Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MBILI YANGA

“N’nakwanilitsa Colinga Canga Cotumikila Yehova”

“N’nakwanilitsa Colinga Canga Cotumikila Yehova”

TINALAILANA na kagulu ka anthu kamene tinacezela pafupi na mudzi wa Granbori, umene unali mkati mwa nkhalango ku Suriname. Kenako tinauyamba ulendo wa pa boti pa Mtsinje wa Tapanahoni. Titafika pamadzi othamanga kwambili, cipolopela ca boti cinagunda mwala n’kuwonongeka. Nthawi yomweyo, mbali yakutsogolo ya botiyo inamila m’madzi, ndipo nafenso tinamila. Mtima wanga unanyamuka! Ngakhale kuti n’nali n’tayendapo maulendo ambili pa boti nili woyang’anila dela, sin’nali kudziŵa kusambila.

N’sanakusimbileni zimene zinacitika pambuyo pake, lekani coyamba nikuuzeni mmene n’nayambila utumiki wanthawi zonse.

N’nabadwa mu 1942 pa cisumbu cokongola ca Curaçao ku Caribbean. Atate kwawo kunali ku Suriname, koma anasamukila ku cisumbuci cifukwa ca nchito. Iwo anabatizika zaka zingapo ine nisanabadwe, ndipo anali mmodzi wa Mboni zoyambilila kubatidwa ku Curaçao. a Anali kutiphunzitsa Baibo mlungu uliwonse, ngakhale kuti nthawi zina sitinali kufuna kuphunzila. N’tafika zaka 14, banja lathu linasamukila ku Suriname cifukwa atate anali kufuna kuti azikasamalila amayi awo okalamba.

MABWENZI ABWINO ANANITHANDIZA

Nili ku Suriname, n’nayamba kuyanjana na acicepele mumpingo amene anali kutumikila Yehova mokangalika. Iwo anali okulilapo pang’ono pa ine, ndipo anali apainiya a nthawi zonse. Akamasimbilana zocitika za mu ulaliki, nkhope zawo zinali kuwala na cimwemwe. Pambuyo pa misonkhano ya mpingo, ine na anzangawo tinali kukambilananso nkhani za m’Baibo, nthawi zina tili khale panja uku tikuyang’ana nyenyezi. Anzangawo, ananithandiza kuzindikila zimene n’nali kufuna paumoyo; n’nali kufuna kutumikila Yehova. Conco n’nabatizika nili na zaka 16. Ndipo n’tafika zaka 18 n’nayamba upainiya wanthawi zonse.

KUPHUNZILA ZINTHU ZOFUNIKA KWAMBILI

Nikucita upainiya ku Paramaribo

N’naphunzila zinthu zambili n’takhala mpainiya, ndipo zimenezo zanithandiza pa utumiki wanga wanthawi zonse. Mwacitsanzo, cinthu coyamba cimene n’naphunzila ni kufunika kophunzitsako ena. N’tayamba upainiya, mmishonale wina dzina lake Willem van Seijl anayamba kunionetsa cidwi. b Iye ananiphunzitsa mosamalila maudindo mu mpingo. Panthawiyo, sin’nali kudziŵa kuti n’nafunikila maphunzilo owonjezela. Caka cotsatila, n’naikidwa kukhala mpainiya wapadela. Ndipo pambuyo pake, n’nayamba kutsogolela tumagulu twakutali tumene tunali mkati mwa nkhalango ku Suriname. Niyamikila kwambili kuti maphunzilo amene n’nalandila kwa abale anali a panthawi yake. Kucokela nthawiyo, nakhala nikutengela citsanzo cawo mwa kupatula nthawi yophunzitsako ena.

Caciŵili cimene n’naphunzila ni ubwino wokhala na umoyo wosalila zambili komanso kukhala wosamala zinthu. Kuciyambi kwa mwezi uliwonse, ine na mpainiya mnzanga wapadela, tinali kupanga bajeti ya zinthu zofunikila zakuthupi zogwilitsa nchito mwezi wonse wathunthu. Kenako, mmodzi wa ife anali kuyenda ulendo wautali kupita ku tauni kukagula zofunikilazo. Tinali kufunika kuseŵenzetsa bwino ndalama imene anali kutipatsa pamwezi na kusamala zinthu zimene tagula kuti zitifikitse kumapeto kwa mwezi. Ngati zofunikilazo zatha tikali m’khalangomo, ni anthu ocepa akanatithandiza ngati analipo n’komwe. Niona kuti zimene n’naphunzila nili wacicepele pankhani yokhala na umoyo wosalila zambili, komanso kusamala zinthu, zanithandiza kuika maganizo anga pa nchito ya Yehova mu umoyo wanga wonse.

Cacitatu cimene n’naphunzila, ni ubwino wophunzitsa anthu m’cinenelo cawo. Nili mwana n’nali kukamba ci Dutch, Cizungu, ci Papiamento, komanso ci Sranantongo (cochedwanso ci Sranan), citundu cofala ku Suriname. Koma pamene tinali m’khalango, n’naona kuti anthu anali kumvetsela uthenga wabwino tikawalalikila m’cinenelo cawo. Cinali kunivuta kulankhula zina mwa zinenelo zimenezi monga ci Saramaccan, cimene cili na mawu ofuna kukweza komanso kutsitsa. Koma n’nayesetsa, ndipo n’nazidziŵa zinenelozo. Kwa zaka zambili, nakhala nikuphunzitsa anthu ambili coonadi cifukwa nimakwanitsa kukamba zinenelo zawo.

Koma nthawi zina, zocititsa manyazi zinali kucitika. Mwacitsanzo, n’nali kufuna kufunsa mayi wina wokamba ci Saramaccan amene anali kuphunzila Baibo mmene anali kumvela cifukwa sanali kumva bwino m’mimba. Koma mmene n’namufunsila, zinamveka monga nikumufunsa ngati ali na pakati. Iye sanayankhe ciliconse cifukwa anacita manyazi. Ngakhale kuti n’nali kulakwitsa pochula mawu, nthawi zonse n’nali kuyesetsa kukamba cinenelo ca anthu a m’gawo langa.

KULANDILA MAUDINDO OWONJEZELA

Mu 1970, n’naikidwa kukhala woyang’anila dela. Caka cimeneco, n’nakhala na mwayi woonetsa tumagulu twakutali m’nkhalangoyo pulogilamu ya zithunzi zoyenda yakuti, “Kuona Malo ku Likulu Lathu la Mboni za Yehova.” Kuti tifikile abale, ine na abale ena tinali kuyenda ulendo wa pamadzi kudutsa mitsinje ya m’nkhalango pogwilitsila nchito boti ya matabwa. Pa ulendowo, tinanyamula jeneleta, petulo, nyale, na pulojekita. Tikafika pa malowo, tinali kunyamula zinthuzo pamanja n’kukazipeleka kumene tinali kuonetsela pulogilamuyo. Koma cimene nikumbukila kwambili pa maulendo onsewo ni mmene anthu anali kukondela mapulogilamu amenewo. N’nali wokondwela kwambili kuthandiza ena kuphunzila za Yehova, na gulu lake la padziko lapansi. Madalitso auzimu amene napeza aposa zinthu zakuthupi zimene nadzimana potumikila Yehova.

KUPOTA CINGWE CA NTHAMBO ZITATU

Ine na Ethel tinakwatilana mu September 1971

Ngakhale kuti n’nali kuona kuti kukhala mbeta kuli na maubwino ake mu utumiki wanga, n’nali kuonabe kuti nifunikila kupeza mnzanga womanga naye banja. Conco, n’nayamba kuipemphelela nkhaniyi, kuti nipeze mkazi amene akanakwanitsa kupilila mwacimwemwe zovuta za mu utumiki wanthawi zonse m’nkhalango imeneyo. Pambuyo pa caka cimodzi, n’natomela mlongo Ethel mpainiya wapadela amene anali na mzimu wodzimana kwambili. Kuyambila ali mwana, mlongo Ethel anali kusilila kwambili mtumwi Paulo, ndipo anadzipeleka mu utumiki wacikhristu potengela citsanzo cake. Kenako, mu September 1971 tinakwatilana, ndipo tinayamba kutumikila m’nchito yadela monga banja.

Mkazi wanga Ethel sanakulile m’banja lolemela. Conco, sizinamuvute kuzoloŵela m’nchito yadela. Mwacitsanzo, tikamakonzekela kukacezela mipingo ya mkati kwambili mwa nkhalango, sitinali kunyamula katundu wambili. Tinali kusamba na kucapila zovala m’mitsinje. Tinazoloŵelanso kudya cakudya ciliconse cimene iwo atipatsa monga, abuluzi akulu-akulu, nsomba zochedwa piranhas, kapena ciliconse cimene iwo apeza m’nkhalango kapena m’mitsinje. Ngati iwo alibe mbale, tinali kudyela pa masamba a nthoci. Ndipo ngati alibe masipuni kapena mafoloko, tinali kudya na manja. Ine na mkazi wanga Ethel taona kuti kukhala na mzimu wodzimana potumikila Yehova, kwatithandiza kulimbitsa cingwe cathu copotedwa na nthambo zitatu. (Mlal. 4:12) Madalitso amenewa sitikanawasinthanitsa na cina ciliconse.

Tsiku lina tikubwelela kwathu pambuyo pocezela abale na alongo m’nkhalango, m’pamene tinakumana na ngozi imene nafotokoza kuciyambi kwa nkhani ino. Titafika pamadzi othamanga kwambili, boti yathu inagunda mwala n’kumila. Koma posakhalitsa, inayandamanso pa madzi. Mwayi wake, tinavala zovala zothandiza kuti tisamile, ndipo tonse sitinatulukemo m’boti. Koma madzi anali atadzala m’botimo. Conco, tinataya zakudya pamadzi zimene zinali m’mapoto, kuti tigwilitse nchito mapotowo pokapa madzi m’botimo.

Popeza tinalibenso cakudya ciliconse, tinayamba kuŵedza nsomba pa ulendowo. Koma sitinapheko olo imodzi. Conco, tinapemphela kwa Yehova kuti atipatse cakudya ca tsikulo. Pambuyo popemphela, m’bale wina amene tinali naye anaponya mbedza pamadzi, ndipo anapha nsomba yaikulu imene tonse asanu tinadya usikuwo na kukhuta.

KUKHALA MUTU WA BANJA, TATE, KOMANSO WOYANGANILA DELA

Titatumikila m’dela zaka zisanu, ine na mkazi wanga Ethel tinalandila dalitso losayembekezela—tinali kudzakhala makolo. N’nakondwela kwambili n’tamva zimenezo, ngakhale kuti sin’nali kudziŵa kuti umoyo wathu udzakhala bwanji. Ine na Ethel tinali kufunitsitsa kukhalabe mu utumiki wanthawi zonse ngati kunali kotheka. Mu 1976 mwana wathu wamwamuna Ethniël anabadwa. Patapita zaka ziŵili na hafu, mwana wathu waciŵili Giovanni anabadwanso.

Mu 1983 nikupenyelela ubatizo mu Mtsinje wa Tapanahoni pafupi na Godo Holo ku Eastern Suriname

Cifukwa cakuti ku Suriname kunali kosoŵa panthawiyo, ofesi ya nthambi inalinganiza kuti nipitilize kutumikila monga wadela uku tikulela ana athu. Pamene ana athu anali aang’ono, n’nali kutumikila m’dela limene munali mipingo yocepa. Izi zinanipatsa mwayi wotumikila m’dela kwa milungu ingapo mwezi uliwonse, ndipo masiku otsala a mweziwo, n’nali kucita upainiya mu mpingo umene anatipatsa. Mkazi wanga Ethel na ana athu anali kutsagana nane nikamacezela mipingo ya kufupi na kumene tinali kukhala. Koma n’nali kuyenda nekha pokacezela mipingo yakutali komanso pokacititsa misonkhano ikulu-ikulu ku nkhalango.

M’nchito yadela, nthawi zambili n’nali kuyenda pa boti pokacezela mipingo yakutali

N’nafunika kulinganiza bwino zinthu kuti nizisamalila maudindo anga onse. N’nali kuonetsetsa kuti mlungu uliwonse tikucita kulambila kwa pabanja. Nikapita kukacezela mipingo ku nkhalango, mkazi wanga Ethel ndiye anali kucititsa kulambila kwa pabanja. Koma nthawi zambili, tinali kucitila zinthu pamodzi monga banja. Ine na mkazi wanga, tinali kucitanso zosangalatsa na ana athu, monga kucita maseŵela, kapena kukaona malo ocititsa cidwi a kufupi na kumene tinali kukhala. Nthawi zambili n’nali kugona mocedwa cifukwa cokonzekela zinthu zina zauzimu. Ndipo Ethel, mofanana na mkazi wochulidwa pa Miyambo 31:15, anali kuuka m’mamaŵa na kuonetsetsa kuti taŵelenga lemba la tsiku, komanso tadyela pamodzi cakudya ca m’maŵa ana athu asanapite kusukulu. Niyamikila kwambili kukhala na mkazi wodzimana, amene nthawi zonse anali kunithandiza kukwanilitsa maudindo amene Yehova ananipatsa.

Monga makolo, tinayesetsa kuthandiza ana athu kukonda Yehova komanso ulaliki. Tinali kufuna kuti ana athu adzacite utumiki wanthawi zonse, osati cifukwa cakuti n’zimene ife tinali kufuna, koma cifukwa cakuti iwo aukonda. Nthawi zonse tinali kuwauza kuti utumiki wanthawi zonse ni wosangalatsa. Tinali kuwauzanso mavuto amene tinali kukumana nawo, komanso mmene Yehova anali kutithandizila na kutidalitsa monga banja. Tinalinso kuonetsetsa kuti ana athu akuceza na mabwenzi amene anali kuika Yehova patsogolo mu umoyo wawo.

Yehova anali kutipatsa zonse zofunikila polela ana athu. Ndipo ine n’nali kucita zonse zotheka kuti nisamalile banja langa. Kutumikila ku nkhalango monga mpainiya wapadela kunaniphunzitsa mopangila bajeti ya zinthu zofunikila zakuthupi. Koma ngakhale n’telo, nthawi zina tinali kupeleŵela zinthu zina zofunikila. Panthawi ngati zimenezo, Yehova anali kutithandiza kwambili. Mwacitsanzo, cakumapeto kwa m’ma 1980 komanso ca kuciyambi kwa m’ma 1990, ku Suriname kunabuka cipolowe. M’zaka zimenezo, cinali covuta kupeza zinthu zofunikila paumoyo. Ngakhale n’conco, Yehova anali kutisamalila.—Mat. 6:32.

NIKAYANG’ANA KUMBUYO, SINIMADZIIMBA MLANDU PA CISANKHO CANGA

Kucokela kumanzele kupita ku lamanja: Ine na mkazi wanga Ethel

Mwana wathu wamkulu Ethniël na mkazi wake Natalie

Mwana wathu Giovanni na mkazi wake Christal

Paumoyo wathu wonse, Yehova wakhala akutisamalila. Ndipo watithandiza kukhala acimwemwe komanso okhutila. Ana athu timawanyadila kwambili, ndipo timayamikila kwambili kuti tinakwanitsa kuwaphunzitsa kutumikila Yehova. Timakondwela kuti nawonso anasankha kucita utumiki wanthawi zonse pa umoyo wawo. Ethniël komanso Giovanni, onse analoŵapo masukulu aumulungu. Ndipo tsopano akutumikila pa ofesi ya nthawi ku Suriname pamodzi na azikazi awo.

Ine na mkazi wanga Ethel takalamba tsopano. Koma tikali kutumikila Yehova monga apainiya apadela. Timakhala otangwanika kwambili cakuti nikali kufuna-funabe nthawi yakuti niphunzile kusambila! Koma sinimadziimba mlandu pa cisankho canga. Nikayang’ana kumbuyo, kukamba zoona nimaona kuti cisankho cimene n’napanga nili wacicepele cotumikila Yehova mu utumiki wanthawi zonse kwa moyo wanga wonse, cinali cabwino ngako!

b Mbili ya m’bale Willem van Seijl yakuti Reality Has Exceeded My Expectations, inafalitsidwa mu Galamukani! yacizungu ya October 8, 1999.