Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 46

Yehova Amatithandiza Kupilila Mwacimwemwe—Motani?

Yehova Amatithandiza Kupilila Mwacimwemwe—Motani?

“Cotelo Yehova azidzayembekezela kuti akukomeleni mtima ndipo adzanyamuka kuti akucitileni cifundo.”—YES. 30:18.

NYIMBO 3 Ndimwe Mphamvu Zathu, Ciyembekezo, na Cidalilo Cathu

ZIMENE TIKAMBILANE a

1-2. (a) Kodi tikambilane mafunso ati? (b) N’ciyani cionetsa kuti Yehova ni wofunitsitsa kutithandiza?

 YEHOVA amatithandiza kupilila mavuto amene tingakumane nawo, na kukhala acimwemwe pom’tumikila. Kodi amatithandiza motani? Nanga tingacite ciyani kuti tipindule kwambili na thandizo limene Yehova amatipatsa? Mafunso amenewa ayankhidwa m’nkhani ino. Koma tisanakambilane mayankho ake, tiyeni tiyankhe funso ili: Kodi Yehova ni wofunitsitsadi kutithandiza?

2 Liwu limene mtumwi Paulo anagwilitsa nchito m’kalata yake yopita kwa Aheberi, lingatithandize kupeza yankho. Paulo analemba kuti: “Yehova ndiye mthandizi wanga; sindidzaopa. Munthu angandicite ciyani?” (Aheb. 13:6) Mabuku ena ofotokozela Baibo amaonetsa kuti tanthauzo la liwu lakuti “mthandizi,” limene lagwilitsidwa nchito pa vesiyi, limakamba za munthu amene akuthamanga kuti akathandize munthu amene akukuwa kupempha thandizo. Yelekezani kuti mukumuona Yehova akuthamanga kuti akapulumutse munthu wosatsika. Mosakayikila, mungavomeleze kuti mafotokozedwe amenewa amaonetsa kuti Yehova ni wofunitsitsa kutithandiza. Inde, amalakalaka kuti akhale mthandizi wathu. Popeza kuti Yehova ali kumbali yathu, tingathe kupilila mavuto alionse mwacimwemwe.

3. Ni zinthu zitatu ziti zimene Yehova amacita potithandiza kupilila mavuto athu mwacimwemwe?

3 Ni zinthu ziti zimene Yehova amacita potithandiza kupilila mavuto mwacimwemwe? Kuti tiyankhe funso limeneli, tiyeni tikambilane buku la Yesaya. Cifukwa ciyani? Cifukwa maulosi ambili amene Yesaya anauzilidwa kulemba, amakhudza atumiki a Mulungu masiku ano. Yesaya pofotokoza mmene Yehova amacitila zinthu, anaseŵenzetsa mawu osavuta kumva pokamba za Yehova. Citsanzo ca zimenezi ticipeza m’caputala 30 ca Yesaya. M’caputala cimeneci, Yesaya anafotokoza momveka bwino mmene Yehova amathandizila anthu ake. Iye analemba kuti Yehova amatithandiza (1) mwa kumvetsela mapemphelo athu mwachelu na kuwayankha, (2) mwa kutitsogolela, komanso (3) mwa kutidalitsa pali pano, na kutilonjeza madalitso ena m’tsogolo. Tsopano, tiyeni tikambilane zinthu zitatuzi zimene Yehova amacita potithandiza.

YEHOVA AMATIMVETSELA

4. (a) Kodi Yehova anawafotokoza motani Ayuda a m’nthawi ya Yesaya? Nanga iye anawalola kuti akumane na zotani? (b) Kodi Yehova anawapatsa ciyembekezo cotani Ayuda okhulupilika? (Yesaya 30:18, 19)

4 M’mawu oyamba pa Yesaya caputala 30, Yehova anakamba kuti Ayuda anali “ana aamuna osamva,” amene ‘amawonjezela chimo pa chimo.’ Iye anawonjezela kuti: “Amenewa ndi anthu opanduka,. . . amene safuna kumva malamulo a Yehova.” (Yes. 30:1, 9) Popeza anthuwo anali osamvela, Yesaya analosela kuti Yehova adzawalekelela kuti akumane na mavuto. (Yes. 30:5, 17; Yer. 25:8-11) Ndipo anakumanadi nawo. Anatengedwa ukapolo na Ababulo. Ngakhale n’telo, panali anthu ena okhulupilika pakati pa Ayudawo. Ndipo Yesaya anapeleka uthenga wopatsa ciyembekezo kwa iwo. Iye anawauza kuti tsiku lina Yehova adzawakomelanso mtima. (Ŵelengani Yesaya 30:18, 19.) Ndipo zimenezo zinacitikadi. Yehova anawamasula mu ukapolo ku Babulo. Koma panapita zaka zambili kuti iwo amasulidwe. Mawu akuti “Yehova azidzayembekezela kuti akukomeleni mtima,” anaonetsa kuti padzapita nthawi kuti Ayuda okhulupilika amenewo amasulidwe. Aisiraeli anakhala zaka 70 mu ukapolo ku Babulo, otsala ocepa asanaloledwe kubwelela ku Yerusalemu. (Yes. 10:21; Yer. 29:10) Ayudawo atabwelela kwawo, cisoni cimene anali naco cifukwa cokhala ku ukapolo cinasanduka misozi ya cisangalalo.

5. Kodi Yesaya 30:19 imatitsimikizila ciyani?

5 Masiku ano, timalimbikitsidwa na mawu akuti: “Mosakayikila, iye adzakukomela mtima akadzamva kulila kwako.” (Yes. 30:19) Yesaya akutitsimikizila kuti Yehova amamvetsela mwachelu tikamapempha thandizo kwa iye. Ndipo iye adzayankha mapemphelo athu mosazengeleza. Yesaya anati: “Akadzangomva kulila kwakoko, iye adzakuyankha.” Mawu olimbikitsa amenewa amatikumbutsa kuti Atate wathu ni wofunitsitsa, inde amalakalaka kuthandiza anthu amene amam’pempha thandizo. Ndipo kudziŵa izi kumatithandiza kupilila mwacimwemwe.

6. Kodi mawu a Yesaya aonetsa bwanji kuti Yehova amamvetsela pemphelo la mtumiki wake aliyense payekha?

6 N’ciyaninso cina cimene tingaphunzile pa vesiyi ponena za mapemphelo athu? Yehova amamvetsela mwachelu pemphelo la aliyense wa ife. Cifukwa ciyani tikutelo? M’cinenelo coyambilila, liwu lakuti “inu” m’mavesi oyambilila a Yesaya caputala 30, analigwilitsa nchito poonetsa kuti Yehova anali kukamba na gulu la anthu. Koma pa vesi 19, anagwilitsa nchito mawu oonetsa kuti uthengawo unali kupita kwa munthu mmodzi payekha. Mwacitsanzo, Yesaya analemba kuti: “Iwe sudzalilanso,” “iye adzakukomela mtima,” “iye adzakuyankha.” Pokhala Tate wacikondi, Yehova sauza ana ake olefuka kuti, “Uzikhala wolimba monga m’bale kapena mlongo uje.” M’malo mwake, iye amamvetsela mwachelu mapemphelo athu.—Sal. 116:1; Yes. 57:15.

Kodi Yesaya anatanthauza ciyani pamene anati: “Musaleke kumukumbutsa [Yehova]”? (Onani ndime 7)

7. Kodi Yesaya na Yesu anaonetsa bwanji kufunika kopemphela mosalekeza?

7 Tikamufikila Mulungu m’pemphelo, na kumuuza za vuto lathu, nthawi yomweyo iye angatipatse mphamvu zofunikila kuti tipilile. Ndipo ngati vutolo silinathe pa nthawi imene tinali kuyembekezela, tifunika kum’pempha Yehova mosalekeza kuti atipatse mphamvu kuti tipitilize kupilila. Ni zimene iye amafuna kuti tizicita. Tidziŵa zimenezi cifukwa ca mawu a Yesaya akuti: “Musaleke kumukumbutsa [Yehova].” (Yes. 62:7) Kodi izi zitanthauza ciyani? Zitanthauza kuti tiyenela kum’pempha Yehova mosalekeza. Tikatelo, zimakhala ngati kuti tikum’kumbutsa Yehova. Mawu a Yesaya amenewa amatikumbutsa mafanizo a Yesu okamba za pemphelo opezeka pa Luka 11:8-10, 13. Pa lembali, Yesu akutilimbikitsa kuti tizipemphela ‘mokakamila,’ na kupitiliza ‘kupempha’ mzimu wake woyela. Tingam’pemphenso Yehova kuti atitsogolele kuti tipange zisankho zabwino.

YEHOVA AMATITSOGOLELA

8. Kodi mawu a pa Yesaya 30:20, 21 anakwanilitsidwa bwanji m’nthawi zakale?

8 Ŵelengani Yesaya 30:20, 21. Pamene asilikali a Babulo anazinga mzinda wa Yerusalemu kwa caka cimodzi na hafu, anthu a mu mzindawo anakumana na masautso. Ndipo masautsowo anakhala ngati cakudya cawo komanso madzi. Koma malinga na vesi 20 na 21, Yehova analonjeza Ayudawo kuti ngati alapa na kusintha khalidwe lawo, adzawapulumutsa. Yesaya pochula Yehova kuti ‘Mlangizi wawo Wamkulu,’ analonjeza anthuwo kuti Yehova adzawaphunzitsa mmene angam’lambilile movomelezeka. Mawu amenewa anakwanilitsidwa pamene Ayuda anamasulidwa ku ukapolo. Yehova anaonetsadi kuti ni Mlangizi wawo Wamkulu, ndipo motsatila citsogozo cake, anthuwo anakwanitsa kubwezeletsa kulambila koyela. Ndipo masiku ano, ndife odala kuti tili na Yehova Mlangizi wathu Wamkulu.

9. Ni njila ina iti imene Yehova amapelekela malangizo masiku ano?

9 Pa mavesiwa, Yesaya anakamba kuti ife tili ngati ophunzila amene tikuphunzitsidwa na Yehova m’njila ziŵili. Yoyamba, iye anati: “Maso ako adzayamba kuona Mlangizi wako Wamkulu.” Mawu amenewa akupeleka cithunzi cakuti mphunzitsi waimilila kutsogolo kwa ophunzila ake kuti awaphunzitse. Masiku ano, tili na mwayi wopindula na malangizo ake. Kodi Yehova amapeleka motani malangizo kwa ife? Amatelo kupitila m’gulu lake. Ndife oyamikila cotani nanga kulandila malangizo omveka bwino ocokela ku gulu lathu limeneli. Malangizo amene timalandila pa misonkhano ya mpingo, yadela, yacigawo, komanso kupyolela m’zofalitsa zathu, m’pulogilamu ya JW Broadcasting, na njila zina zambili, amatithandiza kupilila mwacimwemwe tikamakumana na mavuto.

10. Kodi timamva “mawu kumbuyo [kwathu]” m’njila yotani?

10 Yesaya anachula njila yaciŵili imene Yehova amatipatsila malangizo. Anati: “Makutu ako adzamva mawu kumbuyo kwako.” Apa mneneliyu akufotokoza Yehova monga mlangizi wachelu amene akuyenda kumbuyo kwa ophunzila ake, na kuwatsogolela njila yoyenela kuyendamo. Masiku ano, timamva mawu a Mulungu kumbuyo kwathu. Motani? Mawu ouzilidwa a Mulungu analembedwa m’Baibo kale kwambili ife tisanakhaleko. Conco, tikamaŵelenga Baibo zimakhala ngati kuti tikumva mawu a Mulungu kumbuyo kwathu.—Yes. 51:4.

11. Ni zinthu ziti zimene tingacite kuti tizipilila mwacimwemwe? Nanga n’cifukwa ciyani?

11 Kodi tingapindule bwanji mofikapo na malangizo amene Yehova amapeleka kupitila m’gulu lake na m’Mawu ake? Onani kuti Yesaya anafotokoza zinthu ziŵili. Coyamba, iye anati: “Njila ndi iyi.” Caciŵili, anati: “Yendani mmenemo.” (Yes. 30:21) Kungodziŵa cabe “njila” sikokwanila. Koma tiyenela ‘kuyendamo.’ Mawu a Yehova komanso zofalitsa za gulu lake, zimatithandiza kudziŵa zimene iye amafuna kwa ife. Timadziŵanso mmene tingagwilitsile nchito zimene timaphunzila. Conco kuti tizipilila mwacimwemwe mu utumiki wathu, tiyenela kucita zonse ziŵili. Tikatelo, mosakayikila Yehova adzatidalitsa.

YEHOVA AMATIDALITSA

12. Malinga na Yesaya 30:23-26, kodi Yehova anawadalitsa bwanji anthu ake?

12 Ŵelengani Yesaya 30:23-26. Kodi ulosiwu unakwanilitsidwa bwanji kwa Ayuda amene anabwelela ku Isiraeli pambuyo pomasulidwa mu ukapolo ku Babulo? Iwo analandila madalitso oculuka kuuzimu komanso kuthupi. Yehova anadalitsa anthu ake powapatsa cakudya coculuka. Coposa zonse, anawapatsa cakudya cauzimu coculuka pamene kulambila koona kunali kubwezeletsedwa pang’ono-pang’ono. Madalitso auzimu amene anthu a Mulungu analandila anali oculuka kuposa amene analandilapo kumbuyoko. Monga vesi 26 ionetsela, Yehova anacititsa kuti kuwala kwauzimu kuwonjezeke kwambili. (Yes. 60:2) Madalitso amene Yehova anapatsa atumiki ake anawathandiza kupitiliza kum’tumikila mokondwela, komanso ali na mtendele wa maganizo “cifukwa cokhala ndi cimwemwe mumtima.”—Yes. 65:14.

13. Kodi ulosi wokamba za kubwezeletsa kulambila koyela ukukwanilitsidwa bwanji masiku ano?

13 Kodi ulosi wokamba za kubwezeletsa kulambila koyela umatikhudza masiku ano? Inde! Motani? Kungoyambila mu 1919, anthu mamiliyoni amasuka mu ukapolo wa Babulo Wamkulu, amene ni ufumu wa dziko lonse wa cipembedzo conyenga. Iwo atsogoleledwa ku malo abwino kwambili kuposa Dziko Lolonjezedwa la Isiraeli. Malo amenewo ni paradaiso wauzimu. (Yes. 51:3; 66:8) Kodi paradaiso wauzimu ameneyo n’ciyani?

14. Kodi paradaiso wauzimu n’ciyani? Nanga ndani amene amakhala mmenemo? (Onani mawu akuti Kufotokozela Mawu Ena.)

14 Kungoyambila mu 1919, Akhristu odzozedwa akhala akusangalala m’paradaiso wauzimu ameneyu. b Nawonso amene ali na ciyembekezo codzakhala padziko lapansi, amene ni a nkhosa zina, aloŵa m’paradaiso wauzimu ameneyu, ndipo akusangalala na madalitso a Yehova oculuka.—Yoh. 10:16; Yes. 25:6; 65:13.

15. Kodi paradaiso wauzimu amapezeka kuti?

15 Kodi paradaiso wauzimu ameneyu ali kuti masiku ano? Alambili a Yehova amapezeka m’maiko osiyana-siyana padziko lapansi. Conco, paradaiso wauzimu amene iwo alimo ali padziko lonse lapansi. Motelo, kaya tikukhala dziko liti, tingakhale m’paradaiso wauzimu ameneyu malinga ngati ticilikiza kulambila koona mokhulupilika.

Kodi aliyense wa ife angawonjezele bwanji kukongola kwa paradaiso wauzimu? (Onani ndime 16-17)

16. N’ciyani cingatithandize kupitiliza kuona kukongola kwa paradaiso wauzimu?

16 Cimodzi mwa zimene tingacite kuti tikhalebe m’paradaiso wauzimu, ni kupitiliza kukulitsa ciyamikilo cathu pa ubale wacikhristu wa padziko lonse. Kodi tingacite bwanji zimenezi? Mwa kuyang’ana pa zabwino, osati pa zophophonya za anthu amene ali m’paradaiso ameneyu. (Yohane 17:20, 21) N’cifukwa ciyani kucita izi n’kofunika? Ganizilani citsanzo ici. Tikamayenda m’paki, timayembekezela kuona mitengo yosiyana-siyana yokongola. Mofananamo, paradaiso wauzimu amene ali m’mipingo masiku ano, ni wokongoletsedwa na abale na alongo osiyana-siyana amene awayelekezela na mitengo. (Yes. 44:4; 61:3) Timafunika kuika maganizo athu pa kukongola kwa nkhalango, m’malo moyang’ana zolakwika pa “mitengo” imene ili pafupi nafe. Conco, tisalole zophophonya zathu kapena za ena mu mpingo kutilepheletsa kuona kukongola kwa mpingo wacikhristu wogwilizana wa padziko lonse.

17. Kodi aliyense wa ife angacite ciyani polimbikitsa mgwilizano mumpingo?

17 Kodi aliyense wa ife angacite ciyani kuti alimbikitse mgwilizano mumpingo? Tiyenela kukhala anthu obweletsa mtendele. (Mat. 5:9; Aroma 12:18) Nthawi iliyonse tikacitapo kathu kuti tikhazikitse mtendele na ena mumpingo, timapangitsa kuti paradaiso wauzimu akongoleleko. Tizikumbukila kuti Yehova ndiye anakokela aliyense m’paradaiso wauzimu ameneyu, mmene muli kulambila koyela. (Yoh. 6:44) Tangoganizani mmene Yehova amasangalalila akaona kuti tikuyesetsa kulimbikitsa mtendele na mgwilizano pakati pa atumiki ake, amene amawaona kuti ni amtengo wapatali!—Yes. 26:3; Hag. 2:7.

18. Kodi tiyenela kusinkhasinkha ciyani kaŵili-kaŵili? Nanga n’cifukwa ciyani?

18 Kodi tingacite ciyani kuti tizipindula kwambili na madalitso amene timalandila monga atumiki a Mulungu? Tiyenela kuganizila mozama zimene timaŵelenga m’Mawu a Mulungu, komanso m’zofalitsa zathu zozikika pa Baibo. Kuŵelenga na kusinkhasinkha, kudzatithandiza kukulitsa makhalidwe acikhristu amene adzatilimbikitsa kukonda abale athu na “cikondi ceniceni” mumpingo. (Aroma 12:10) Tikamaganizila madalitso amene talandila pali pano, ubale wathu na Yehova udzalimbilako. Ndipo kusinkhasinkha madalitso amene Yehova watisungila m’tsogolo, kudzatithandiza kusungabe ciyembekezo cathu com’tumikila kwamuyaya. Zonsezi zidzawonjezela cimwemwe cathu pom’tumikila Yehova pali pano.

KHALANI OKONZEKA KUPILILA

19. (a) Malinga na Yesaya 30:18, kodi tingakhale otsimikiza za ciyani? (b) N’ciyani cingatithandize kupilila mwacimwemwe?

19 Yehova “adzanyamuka” kuti atithandize pamene adzawononga dziko loipali. (Yes. 30:18) Ndife otsimikiza kuti Yehova amene ni ‘Mulungu wa cilungamo,’ sadzalola dziko la Satanali kukhalapo mpaka kale-kale. (Yes. 25:9) Conco, tiziyembekezela moleza mtima tsiku la cipulumutso la Yehova. Koma pali pano, ndife ofunitsitsa kupitiliza kuyamikila mwayi wa pemphelo, kuphunzila na kugwilitsa nchito zimene timaŵelenga m’Mawu a Mulungu, komanso kusinkhasinkha madalitso athu. Tikatelo, Yehova adzatithandiza kupilila mwacimwemwe pom’lambila.

NYIMBO 142 Tigwilitsitse Ciyembekezo Cathu

a Nkhani ino, ifotokoza zinthu zitatu zimene Yehova amacita pothandiza alambili ake kupilila mavuto mwacimwemwe. Kuti tizidziŵe zinthu zimenezo, tikambilane mfundo za mu Yesaya caputala 30. Pokambilana caputala cimeneci, tidzakumbutsidwa kufunika kopemphela kwa Yehova, kuŵelenga Mawu ake, na kusinkhasinkha madalitso amene watipatsa, komanso amene watisungila m’tsogolo.

b KUFOTOKOZELA MAWU ENA: “Paradaiso wauzimu” ni mkhalidwe wacitetezo cauzimu umene tilimo mmene tikulambila Yehova mogwilizana. M’paradaiso wauzimu ameneyu tili na cakudya cauzimu camwana alilenji cosaipitsidwa na mabodza a zipembedzo zonyenga. Cina, timagwilanso nchito yokhutilitsa yolalikila uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Tili pa ubale wolimba na Yehova, ndiponso timakhala mwamtendele na abale komanso alongo athu acikondi amene amatithandiza kupilila mwacimwemwe zovuta za paumoyo. Timaloŵa m’paradaiso wauzimu ameneyu tikayamba kulambila Yehova m’njila yoyenela, komanso pamene ticita zonse zotheka kuti titengele citsanzo cake.