NSANJA YA MLONDA—YOPHUNZILA October 2019

Magazini ino ili na nkhani zophunzila wiki ya December 2-29, 2019.

1919—Zaka 100 Zapitazo

Mu 1919, Yehova anapatsa anthu ake mphamvu yolalikila kuposa kale lonse. Koma coyamba, zinthu zina zinafunika kusintha kwambili pakati pa Ophunzila Baibo.

Mulungu Asanapeleke Ciweluzo, Kodi Nthawi Zonse Amacenjeza Anthu Mokwanila?

Masiku ano, Yehova Mulungu akucenjeza anthu za “cimphepo camkuntho” coopsa kwambili kuposa mphepo iliyonse yoopsa imene inacitikapo. Kodi akucita bwanji zimenezi?

Khalanibe Acangu mu Ndime Ino Yothela ya “Masiku Otsiliza”

Kodi padzacitika zotani pa mapeto a “masiku otsiliza”? Nanga Yehova afuna kuti tizicita ciani poyembekezela zocitika zimenezo?

Zimene Mungacite Kuti Mudzakhalebe Okhulupilika pa “Cisautso Cacikulu”

Kodi Yehova afuna kuti tizikacita ciani pa “cisautso cacikulu”? Tingakonzekele bwanji pali pano kuti tikakhalebe okhulupilika pa nthawiyo?

Kodi Mudzalola Yehova Kukucititsani Kukhala Ndani?

M’nthawi yakale, Yehova analimbitsa zolaka-laka za atumiki ake na kuwapatsa mphamvu kuti acite cifunilo cake. Kodi iye amatithandiza bwanji kuti tikwanitse kucita cifunilo cake masiku ano?

Khalani Wodzipeleka kwa Yehova Yekha

Onani mbali ziŵili za umoyo wathu zimene zingatithandize kudziŵa ngati ndifedi odzipeleka kwa Yehova yekha.