Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

M’bale Rutherford akamba nkhani pa msonkhano waukulu mu 1919, ku Cedar Point, Ohio

1919—Zaka 100 Zapitazo

1919—Zaka 100 Zapitazo

PODZAFIKA mu 1919, Nkhondo Yaikulu (imene pambuyo pake inachedwa Nkhondo Yoyamba Yapadziko Lonse), inatha. Nkhondoyo inatenga zaka zoposa zinayi. Cakumapeto kwa 1918, maiko analeka kumenyana. Ndipo pa January 18, 1919, Msonkhano wokambilana za mtendele unayamba ku Paris. Cimodzi mwa zinthu zazikulu zimene zinacitika pa msonkhanowo ni kukhazikitsidwa kwa pangano la ku Versailles, limene linathetsa mwalamulo nkhondo ya pakati pa Germany na maiko olimbana naye. Panganolo linasainidwa pa June 28, 1919.

Pa nthawiyo, anapangananso zokhazikitsa bungwe latsopano lochedwa League of Nations. Colinga cake cinali “kulimbikitsa mgwilizano wa maiko, komanso kukhazikitsa mtendele na citetezo padziko lonse.” Machechi ambili Acikhristu anayamba kucilikiza bungwe limeneli. Mwacitsanzo, bungwe la Machechi Acikhristu ku America linakamba kuti, League of Nations ni “bungwe la ndale loimilako Ufumu wa Mulungu pano padziko lapansi.” Bungwe la Machechilo linacilikiza kukhazikitsidwa kwa League of Nations, mwa kutumiza nthumwi zake ku msonkhano wokambilana za mtendele ku Paris. Mmodzi mwa nthumwizo anakamba kuti msonkhanowo “unali ciyambi ca nyengo yatsopano m’mbili ya dziko lapansi.”

N’zoona kuti nyengo yatsopano inayamba. Koma sikuti anaiyambitsa ni anthu amene anacita msonkhano wokambilana za mtendele ku Paris. Mu 1919, nyengo yatsopano pa nchito yolalikila inayamba pamene Yehova anapatsa anthu ake mphamvu yolalikila kuposa kale lonse. Koma coyamba, zinthu zina zinafunika kusintha kwambili pakati pa Ophunzila Baibo.

COSANKHA COVUTA

Joseph F. Rutherford

Makonzedwe anapangidwa akuti miting’i ya pa caka yosankha madailekita a Watch Tower Bible and Tract Society idzacitike pa Ciŵelu, pa January 4, 1919. Pa nthawiyo, M’bale Joseph F. Rutherford, amene anali kutsogolela anthu a Yehova, anali ataikidwa m’ndende pa mlandu wabodza ku Atlanta, Georgia, m’dziko la America, pamodzi na abale ena 7. Conco, funso limene abale anali nalo n’lakuti, “Kodi tisankhenso abale amene ali m’ndendewa kuti apitilize kukhala madailekita kapena tisankhe abale ena?”

Evander J. Coward

Ali m’ndendemo, M’bale Rutherford anali kudela nkhawa za tsogolo la gulu la Mulungu. Iye anadziŵa kuti abale ena anali kuona kuti zikanakhala bwino kusankha m’bale wina kuti akhale pulezidenti. Conco, analembela kalata abale amene anali pa miting’iyo. M’kalatayo, anayamikila M’bale Evander J. Coward kuti akhale pulezidenti. M’bale Rutherford anafotokoza kuti M’bale Coward anali munthu “wofatsa,” “wanzelu,” komanso “wokhulupilika kwa Ambuye.” Komabe, abale ambili anali na maganizo osiyanako. Anali kuona kuti tsiku la masankho liyenela kusinthidwa, kuti masankhowo akacitike pambuyo pa miyezi 6. Maloya oimila abale amene anali m’ndendewo anavomeleza zimenezi. Mkati mwa makambilanowo, abale ena anapsa mtima kwambili.

Richard H. Barber

Kenako, panacitika zina zake zimene M’bale Richard H Barber anakamba kuti zinali monga ni ‘kuzima moto.’ Mmodzi wa abale amene anali pa miting’iyo anaimilila na kukamba kuti: “Si ndine katswili wa za malamulo, koma nimadziŵa tanthauzo la kukhala wokhulupilika. Ndipo kukhala wokhulupilika n’kumene Mulungu amafuna. Cinthu cabwino kwambili cimene tingacite poonetsa kuti ndife okhulupilika kwa Mulungu, ni kucita masankho na kusankhanso M’bale Rutherford kukhala pulezidenti.”—Sal. 18:25.

Alexander H. Macmillan

M’bale A. H. Macmillan amene nayenso anali m’ndende, anakamba kuti tsiku lotsatila M’bale Rutherford anagogoda pa cipinda cake ca ndende, na kumuuza kuti, “Tulutsa dzanja lako panja.” Kenako, anamupatsila kalata imene abale analembela m’bale Rutherford, yofotokoza zotsatila za masankho. M’bale Macmillan ataona mawu ocepa a m’kalatayo, nthawi yomweyo anamvetsa tanthauzo lake. Mawuwo anali akuti: “RUTHERFORD WISE VAN BARBER ANDERSON BULLY NA SPILL PULEZIDENTI ATATU OYAMBA MAOFISALA TIKUKONDANI NONSE.” Mawu amenewa anatanthauza kuti madailekita onse a Watch Tower Society anasankhidwanso, ndipo M’bale Joseph Rutherford na William Van Amburgh anaikidwanso kukhala maofisala. Conco, M’bale Joseph Rutherford anapitiliza kukhala pulezidenti.

ANATULUTSIDWA M’NDENDE!

Pamene abale 8 aja anali m’ndende, Ophunzila Baibo okhulupilika anayamba kupempha anthu kuti asaine cikalata cocondelela boma kuti litulutse abalewo m’ndende. Abale na alongo olimba mtima amenewa anakwanitsa kupeza anthu oposa 700,000 amene analola kusaina cikalataco. Pa Citatu, pa March 26, 1919, akalibe kupeleka cikalataco ku boma, M’bale Rutherford na abale enawo anatulutsidwa m’ndende.

Pokamba kwa abale amene anamucingamila, M’bale Rutherford anati: “Sinikayikila kuti zimene zaticitikilazi zangotithandiza kukonzekela mavuto aakulu amene tidzakumana nawo kutsogolo. . . . Colinga cacikulu ca nchito imene mwacita, sikuthandiza abale anu kuti atulutsidwe m’ndende. Izi zinangolowetsedwamo cabe. . . . Colinga cacikulu cinali kucitila umboni za Coonadi. Ndipo abale amene agwila nchitoyi alandila dalitso lalikulu.”

Zimene zinacitika ponena za mlandu umene abale athu anali kuimbidwa, zionetsa kuti Yehova anali kuŵatsogolela. Pa May 14, 1919, khoti ya apilu inapeleka cigamulo cotele: “Oimbidwa mlandu pa nkhani iyi anamanidwa . . . ufulu woweluzidwa mwacilungamo, ndipo pa cifukwa cimeneci milandu yawo yafafanizidwa.” Ici cinali ciweluzo cabwino. Cifukwa ciani? Abalewo anali kuimbidwa milandu yoopsa, ndipo akanati angowakhululukila kapena kuwacepetsela zaka zokhala m’ndende, akanakhalabe na mbili yoipa yophwanya malamulo. Koma popeza khoti inagamula kuti milandu yawo yafafanizidwa, ndipo sanazengedwenso mlandu pambuyo pake, maina awo anafafanizidwa pa mndandanda wa anthu ophwanya malamulo. Conco, M’bale Rutherford

anakhalabe na ziyenelezo zoteteza anthu a Yehova pa milandu mu Khoti Yaikulu Kwambili ku America. Iye anacita izi kambili-mbili pambuyo potulutsidwa m’ndende.

ANATSIMIKIZA MTIMA KUGWILA NCHTO YOLALIKILA

M’bale Macmillan anati: “Sitikanakhala manja lende n’kumayembekezela kuti Ambuye abwele kudzatitenga kupita kumwamba. Tinazindikila kuti tinafunika kucitapo kanthu kuti tidziŵe zimene Ambuye anali kufuna kweni-kweni.”

Koma zinali zovuta kuti abale ayambenso kugwila nchito imene anali kucita kwa zaka m’mbuyomo. Cifukwa ciani? Cifukwa pa nthawi imene abale ena anali m’ndende, zipangizo zosindikizila zimene anali kuseŵenzetsa posindikiza mabuku, zinali zitawonongedwa. Zimenezi zinali zolefula. Ndipo abale ena anayamba kuganiza kuti mwina amenewo ndiwo anali mapeto a nchito yolalikila.

Ophunzila Baibo anafuna kudziŵa ngati panali anthu ena amene anali kufunabe kumvetsela uthenga wa Ufumu umene iwo anali kulalikila. Motelo, M’bale Rutherford anakonza zakuti akambe nkhani. Anakonzanso zoitanila aliyense ku nkhaniyo. M’bale Macmillan anati: “Abale anali na maganizo akuti ngati sikudzabwela aliyense wokamvetsela nkhaniyo, ndiye kuti nchito yolalikila yatha.”

Cilengezo ca mu nyuzipepala cokamba za nkhani ya M’bale Rutherford ya mutu wakuti, “Ciyembekezo ca Mtundu wa Anthu Umene Uli pa Mavuto,” yokambidwila ku Los Angeles, California, mu 1919

Olo kuti M’bale Rutherford anali kudwala, anakambabe nkhaniyo pa Sondo, pa May 4, 1919 ku Los Angeles, California. Mutu wake unali wakuti, “Ciyembekezo ca Mtundu wa Anthu Umene Uli pa Mavuto.” Anthu pafupi-fupi 3,500 anapezekapo, ndipo anthu mahadiledi ambili anabwezedwa cifukwa ca kucepa kwa malo. Tsiku lotsatila, anthu ena 1,500 anapezekapo. Apa abale anaona kuti anthu anali kufunabe kumvetsela uthenga wa Ufumu.

Zimene abalewo anacita pambuyo pake zinayala maziko a nchito yolalikila imene Mboni za Yehova zakhala zikucita mpaka lelo.

KUKONZEKELA KUKULA KWA GULU

Nsanja ya August 1, 1919, inalengeza kuti kuciyambi kwa September, kudzacitika msonkhano waukulu. Inakamba kuti msonkhanowo udzacitikila ku Cedar Point, Ohio. Wophunzila Baibo wacicepele, dzina lake Clarence B. Beaty, amene anali kukhala ku Missouri anati: “Aliyense anali kufunitsitsa kukapezekapo.” Abale na alongo oposa 6,000 anapezekapo. Ici cinali ciŵelengelo cacikulu kwambili kuposa cimene anali kuyembekezela. Cina cokondweletsa kwambili cinali cakuti anthu oposa 200 anabatizika. Iwo anabatizikila m’nyanja yapafupi ya Erie.

Cikuto ca kope yoyamba ya The Golden Age ya October 1, 1919

Pa tsiku lacisanu la msonkhanowo, pa September 5, 1919, M’bale Rutherford anakamba nkhani ya mutu wakuti “Mawu kwa Anchito Anzathu.” M’nkhaniyo, iye analengeza za magazini yatsopano, yochedwa The Golden Age. * Kalata yofotokoza za magaziniyo inati mudzayamba “kupezeka nkhani zatsopano zofunika kwambili, komanso kufotokoza mwa Malemba cifukwa cake pa dzikoli [panali] kucitika zinthu zazikulu.”

Ophunzila Baibo onse analimbikitsidwa kulalikila molimba mtima pogwilitsila nchito magazini yatsopano imeneyi. Kalata yofotokoza mmene nchitoyi inayenela kucitikila inati: “Mkhristu aliyense wodzipeleka [komanso wobatizika] ayenela kukumbukila kuti ni mwayi waukulu kwambili kutumikila Mulungu. Ndipo afunika kuyamba kucita zimenezo palipano, mwa kucita zilizonse zimene angathe polalikila kwa anthu m’dzikoli.” Ophunzila Baibo ambili analabadila malangizo amenewa. Ofalitsa Ufumu okangalika anagwila nchitoyi mwakhama, cakuti podzafika mu December caka cimeneco, anthu oposa 50,000 analembetsa kuti azilandila magazini yatsopanoyi.

Abale ku Brooklyn, New York, ali na thilaki yodzala na magazini ya The Golden Age

Pakutha kwa caka ca 1919, anthu a Yehova anali atakhalanso gulu lolinganizidwa mwadongosolo, komanso anali atalimbikitsidwa. Kuwonjezela apo, maulosi angapo ofunika kwambili onena za masiku otsiliza anali atakwanilitsidwa. Nthawi yoyesa anthu a Mulungu na kuwayenga, imene inanenedwelatu pa Malaki 3:1-4, inali itatha. Anthu a Yehova anali atamasulidwa mu ukapolo wophiphilitsa kwa “Babulo Wamkulu.” Ndipo Yesu anali ataika “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu.” * (Chiv. 18:2, 4; Mat. 24:45) Apa tsopano Ophunzila Baibo anali okonzeka kugwila nchito imene Yehova anali kufuna kuti acite.

^ ndime 23 Magazini ya The Golden Age inayamba kuchedwa Consolation mu 1937, ndipo mu 1946, inayamba kuchedwa Galamukani!