Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 43

Khalani Wodzipeleka kwa Yehova Yekha

Khalani Wodzipeleka kwa Yehova Yekha

“Yehova ndi Mulungu amene amafuna kuti anthu azidzipeleka kwa iye yekha.”​—NAHUMU 1:2.

NYIMBO 51 Tinadzipeleka kwa Mulungu

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. N’cifukwa ciani tiyenela kukhala wodzipeleka kwa Yehova yekha?

TIMAFUNIKA kukhala odzipeleka kwa Yehova yekha cifukwa ndiye anatilenga na kutipatsa moyo. (Chiv. 4:11) Ndipo timam’konda na kum’lemekeza. Koma ngati sitingasamale, zinthu zina zingatikope na kutilepheletsa kukhala wodzipeleka kwa iye yekha. Kodi zimenezi zingacitike bwanji? Tidzakambilana mmene zingacitikile. Koma coyamba, tiyeni tikambilane tanthauzo la kukhala wodzipeleka kwa Yehova yekha.

2. Malinga na Ekisodo 34:14, n’ciani cimene tidzacita ngati ndife odzipeleka kwa Yehova yekha?

2 M’Baibo, kukhala wodzipeleka kwa Mulungu kumatanthauza kum’konda kwambili. Conco, ngati ndife wodzipeleka kwa Yehova yekha, sitidzalambilanso cinthu cina, koma iye yekha cabe. Sitidzalola munthu wina kapena cinthu cina kukhala patsogolo mu umoyo wathu kuposa Mulungu.—Ŵelengani Ekisodo 34:14.

3. Kodi timatumikila Yehova modzipeleka cifukwa congotengeka maganizo? Fotokozani.

3 Sikuti timatumikila Yehova modzipeleka cifukwa congotengeka maganizo. Koma tinasankha kucita izi cifukwa tinaphunzila za iye na kum’dziŵa bwino. Tinakopeka na makhalidwe ake abwino. Timadziŵa zimene Yehova amakonda na zimene amazonda, ndipo timaona zinthu mmene iye amazionela. Timadziŵanso colinga cake pa anthu, ndipo timacita zinthu mogwilizana na miyezo yake. Komanso, timaona kuti ni mwayi kuti watilola kukhala mabwenzi ake. (Sal. 25:14) Ciliconse cimene taphunzila ponena za Mlengi wathu Yehova, cimatisonkhezela kumukonda kwambili.—Yak. 4:8.

4. (a) Kodi Mdyelekezi amaseŵenzetsa ciani pofuna kutilepheletsa kukonda Yehova na mtima wonse? (b) Tidzakambilana ciani m’nkhani ino?

4 Mdyelekezi ndiye wolamulila wa dzikoli. Ndipo amaliseŵenzetsa potikopa kuti tiyambe kuona zinthu zakuthupi kukhala zofunika kwambili. Amaligwilitsilanso nchito pofuna kutisonkhezela kukhutilitsa zilako-lako zathu zathupi. (Aef. 2:1-3; 1 Yoh. 5:19) Colinga cake ni kutilepheletsa kukonda Yehova na mtima wonse. Tiyeni tikambilane njila ziŵili zimene Mdyelekezi amacitila zimenezi. Yoyamba, amatikopa kuti tiyambe kufuna-funa cuma. Ndipo yaciŵili, amayesa kutisonkhezela kusankha zosangalatsa zoipa.

PEWANI KUKONDA NDALAMA

5. N’cifukwa ciani tifunika kupewa mzimu wokonda ndalama?

5 Mwacibadwa, tonsefe timafuna kukhala na cakudya cokwanila, zovala zooneka bwino, na nyumba yabwino. Komabe, tifunika kupewa mzimu wokonda ndalama. Anthu ambili m’dziko la Satanali ali na mtima ‘wokonda ndalama’ na zinthu zina zakuthupi. (2 Tim. 3:2) Yesu anadziŵa kuti otsatila ake angakopeke n’kuyamba kukonda ndalama. N’cifukwa cake anati: “Kapolo sangatumikile ambuye awili, pakuti adzadana ndi mmodzi ndi kukonda winayo, kapena adzakhulupilika kwa mmodzi ndi kunyoza winayo. Simungathe kutumikila Mulungu ndi Cuma nthawi imodzi.” (Mat. 6:24) Ngati munthu amalambila Yehova, koma pa nthawi imodzi-modziyo amawonongela nthawi na mphamvu zake zoculuka podziunjikila cuma, ndiye kuti akuyesa kutumikila ambuye aŵili. Munthu wotelo sakhala wodzipeleka kwa Yehova yekha.

Umu ni mmene akhristu ena a ku Laodikaya anali kudzionela . .  koma Yehova na Yesu anali kuwaona motele (Onani ndime 6)

6. N’ciani cimene tingaphunzilepo pa mawu amene Yesu anauza mpingo wa ku Laodikaya?

6 Cakumapeto kwa nthawi ya atumwi, Akhristu a mu mpingo wa ku Laodikaya anali kudzitama kuti: “Ndine wolemela, ndapeza cuma cambili ndipo sindikusowa kanthu.” Koma pa maso pa Yehova na Yesu, iwo anali ‘ovutika, omvetsa cisoni, osauka, akhungu, ndi amalisece.’ Yesu anawapatsa uphungu, osati cifukwa cakuti anali olemela, koma cifukwa cakuti kukonda kwawo cuma kunali kuwononga ubale wawo na Yehova. (Chiv. 3:14-17) Cotelo, tikaona kuti tayamba kukonda ndalama, tifunika kuwongolela maganizo athu mwamsanga. (1 Tim. 6:7, 8) Apo ayi, mtima wathu udzakhala wogaŵikana, ndipo kulambila kwathu kudzakhala kosavomelezeka pa maso pa Yehova. Paja iye ni “Mulungu wofuna kuti anthu azidzipeleka kwa iye yekha basi.” (Deut. 4:24) Kodi n’ciani cimene cingapangitse kuti tiyambe kukonda ndalama?

7-9. Kodi mwaphunzila ciani pa nkhani ya mkulu wina dzina lake David?

7 Ganizilani za m’bale wina, dzina lake David. Iye ni mkulu wolimbikila nchito, amene amakhala ku America. Iye anakamba kuti anali kuseŵenza mwakhama pa kampani yawo, moti anamukweza pa nchito. Anachuka m’dziko lawo cifukwa ca luso lake pa nchito imene anali kugwila. M’baleyu anati: “Pa nthawiyo, n’nali kuganiza kuti zimene zinacitikazo cinali cizindikilo cakuti Yehova anali kunidalitsa.” Koma kodi zimenezo zinali zoona?

8 M’bale David anayamba kuona kuti nchito yake inali kumuwonongela ubwenzi na Yehova. Iye anati: “Pa misonkhano ya mpingo, ngakhale mu ulaliki, n’nali kungoganizila za mavuto a ku nchito. N’nali kupeza ndalama zambili. Koma n’nayamba kukhala wopanikizika maganizo kwambili, na kukumana na mavuto m’cikwati.”

9 M’bale David anazindikila kuti anafunika kuonanso bwino zinthu zimene anali kuika patsogolo mu umoyo wake. Iye anati: “N’natsimikiza mtima kukonza zinthu.” M’baleyu anaganiza zosintha ndandanda yake ya nchito, ndipo anauza abwana ake za colinga cake. Kodi zotulukapo zake zinali zotani? Anam’cotsa nchito! Kodi iye anacita ciani? M’bale David anati: “Atangonicotsa nchito, tsiku lotsatila n’nafunsila upainiya wothandiza wopitiliza.” Kuti azipeza zofunikila mu umoyo, m’baleyu na mkazi wake anangena nchito yosamalila pa nyumba. Patapita nthawi pang’ono, m’baleyu anayamba upainiya wanthawi zonse. Pambuyo pake, mkazi wake nayenso anayamba upainiya. Banjali linasankha kugwila nchito imene ambili amaiona monga yonyozeka. Koma iwo amaona kuti cofunika kwambili si mtundu wa nchito imene amagwila. Olo kuti ndalama zimene amapeza ni zocepa kwambili tsopano poyelekezela na zimene anali kupeza poyamba, zimene amapezazo zimakwanila kugulila zinthu zofunikila mwezi uliwonse. Iwo amaika Yehova patsogolo mu umoyo wawo. Ndipo adzionela okha kuti iye amasamaliladi anthu amene amaika patsogolo zinthu za Ufumu.—Mat. 6:31-33.

10. Tingateteze bwanji mtima wathu?

10 Kaya ndife olemela kapena ayi, tonse tifunika kuteteza mtima wathu. Motani? Tiyenela kupewa mzimu wokonda cuma. Komanso, sitiyenela kuika patsogolo nchito yathu yakuthupi kuposa utumiki wathu kwa Yehova. Mungadziŵe bwanji kuti mwayamba kuika patsogolo nchito yanu? Mungadzifunse mafunso monga aya: ‘Kodi nimakonda kuganizila za nchito yanga nikakhala pa misonkhano kapena mu ulaliki? Kodi nimakonda kudela nkhawa kuti mwina kutsogolo nidzavutika cifukwa cosoŵa ndalama? Kodi ndalama na cuma zikubweletsa mavuto m’cikwati cathu? Kodi ningalole kugwila nchito imene ena amaiona kukhala yonyozeka, ngati imanipatsa mpata wowonjezela zocita potumikila Yehova?’ (1 Tim. 6:9-12) Pamene tiganizila mafunso amenewa, tiyenela kukumbukila kuti Yehova amatikonda. Ndipo kwa anthu amene amam’tumikila modzipeleka, iye walonjeza kuti: “Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.” Ndiye cifukwa cake mtumwi Paulo analemba kuti: “Moyo wanu ukhale wosakonda ndalama.”—Aheb. 13:5, 6.

MUZISANKHA MOSAMALA ZOSANGALATSA

11. Kodi zosangalatsa zimene timasankha zingatikhudze bwanji?

11 Yehova amafuna kuti tizisangalala na moyo. Ndipo zosangalatsa zimatithandiza kukhala osangalala. Paja Mawu a Mulungu amati: “Kwa munthu, palibe cabwino kuposa kuti adye, amwe, ndi kusangalatsa mtima wake cifukwa coti wagwila nchito mwakhama.” (Mlal. 2:24) Komabe, zosangalatsa zambili m’dzikoli n’zoipa, ndipo zingatiwononge mwauzimu. Zimasukulutsa mfundo za makhalidwe abwino. Komanso zimasonkhezela anthu kulekelela zinthu zoipa zoletsedwa m’Baibo, ngakhalenso kuzikonda kumene.

Kodi n’ndani amakukonzelani zosangalatsa? (Onani ndime 11-14) *

12. Malinga na 1 Akorinto 10:21, 22, n’cifukwa ciani tiyenela kusankha mosamala zosangalatsa?

12 Timafuna kulambila Yehova yekha. Ndiye cifukwa cake, sitingadye “patebulo la Yehova” na “patebulo la ziwanda.” (Ŵelengani 1 Akorinto 10:21, 22.) Kaŵili-kaŵili, kudya cakudya pamodzi na munthu winawake kumaonetsa kuti tili naye pa ubwenzi. Conco, ngati ticita zosangalatsa zolimbikitsa ciwawa, ciwelewele, zamizimu, kapena zilako-lako zina zathupi, ndiye kuti tikudya cakudya cokonzedwa na adani a Mulungu. Tikatelo, timadzivulaza tekha, komanso timawononga ubwenzi wathu na Yehova.

13-14. Malinga na Yakobo 1:14, 15, n’cifukwa ciani tifunika kusamala posankha zosangalatsa? Fotokozani citsanzo.

13 Kodi zosangalatsa zimafanana bwanji na cakudya ceni-ceni? Pamene tikudya, timakhala na ufulu wosankha zakudya zimene tifuna kudya. Koma tikangomeza cakudyaco, zonse zimacitika mwacibadwa, moti sitikhalanso na ufulu kapena mphamvu yosankha mmene thupi lidzacigwilitsila nchito. Kudya cakudya cabwino, kumatithandiza kukhala athanzi. Koma kudya cakudya coipa, kumadwalitsa. Mwina zotulukapo zake sizingaonekele nthawi yomweyo, koma m’kupita kwa nthawi zimadzaonekela.

14 Mofananamo, pamene tisankha zosangalatsa, timakhala na ufulu wosankha zimene tifuna kuloŵetsa mu mtima mwathu. Koma zikangoloŵa, sitikhalanso na mphamvu yosankha, moti zosangalatsazo zimakhudza maganizo na mtima wathu. Zosangalatsa zabwino zimatsitsimula. Koma zoipa zimavulaza. (Ŵelengani Yakobo 1:14, 15.) Nthawi zina, mavuto obwela cifukwa ca zosangalatsa zoipa sangaonekele pamenepo, koma m’kupita kwa nthawi amadzaonekela. N’cifukwa cake Baibo imaticenjeza kuti: “Musanyengedwe, Mulungu sapusitsika. Ciliconse cimene munthu wafesa, adzakololanso comweco. Pakuti amene akufesa ndi colinga copindulitsa thupi lake, adzakolola ciwonongeko kucokela m’thupi lakelo.” (Agal. 6:7, 8) Conco, n’kofunika kwambili kupewa zosangalatsa zonse zimene zimalimbikitsa zinthu zimene Yehova amazonda.—Sal. 97:10.

15. Ni mphatso yanji imene Yehova watipatsa?

15 Atumiki a Yehova ambili amakonda kutamba mapulogilamu olimbikitsa a pa TV yathu ya pa Intaneti yocedwa JW Broadcasting®. Mlongo wina, dzina lake Marilyn anati: “Mapulogilamu a pa TV ya Mboni za Yehova anithandiza kukhala wacimwemwe kwambili. Ningatambe ciliconse pa TV imeneyi cifukwa zonse n’zabwino. Nikasungulumwa kapena kulefuka na zinazake, nimasankha nkhani yolimbikitsa kapena pulogilamu ya Kulambila kwa M’maŵa kuti nimvetsele. Kucita izi kumanithandiza kuyandikila kwambili Yehova na gulu lake. TV imeneyi yasintha kwambili umoyo wanga.” Kodi na imwe mukupindula na mphatso yocokela kwa Yehova imeneyi? Kuwonjezela pa mapulogilamu a pamwezi, pa TV yathu ya JW Broadcasting palinso zofalitsa zambili zomvetsela, mavidiyo, na nyimbo zotsitsimula. Mungamvetsela na kutamba zinthu zimenezi nthawi iliyonse imene mufuna.

16-17. N’cifukwa ciani tifunika kusamala na nthawi imene timathela pa zosangalatsa? Nanga tingacite ciani kuti zosangalatsa zisamatiwonongele nthawi?

16 Kuwonjezela pa kusankha mosamala mtundu wa zosangalatsa, tifunikanso kusamala na kuculuka kwa nthawi imene timathela pa zosangalatsazo. Apo ayi, tingayambe kuwonongela nthawi yoculuka pa zosangalatsa, kuposa pa kutumikila Yehova. Ambili zimawavuta kudziletsa pa nkhani ya nthawi imene amathela pa zosangalatsa. Mwacitsanzo, mlongo wina wa zaka 18, dzina lake Abigail anati: “Kutamba mapulogilamu ena a pa TV yadziko kumanitsitsimula pambuyo pa tsiku lokhala na zocita zambili. Koma ngati siningasamale, ningatenge maawazi nikutamba mapulogilamu amenewo.” M’bale wina wacinyamata, dzina lake Samuel, anati: “Nthawi zina nimataya nthawi yaitali kutamba mavidiyo ambili afupi-afupi a ku dziko pa intaneti. Nimayamba n’kutamba imodzi, kenako ina, ndipo nimangozindikila papita kale maawazi atatu kapena anayi.”

17 Mungacite ciani kuti musamawonongele nthawi yambili pa zosangalatsa? Coyamba, mufunika kupenda kuti mudziŵe kuculuka kwa nthawi imene mumathela pa zosangalatsa. Mwacitsanzo, bwanji osalemba ciŵelengelo ca maawazi amene mumathela pocita zosangalatsa pa wiki? Mungalembe pa kalenda ciŵelengelo ca maawazi amene mumathela potamba TV, kufufuza zinthu pa Intaneti, na kuchaya magemu pa foni kapena pa tabuleti. Mukaona kuti mumawononga nthawi yoculuka pocita zimenezi, mungalembe ndandanda. Pa ndandandayo, coyamba dziikileni nthawi yocita zinthu zofunika kwambili. Kenako, dziikileni nthawi yocita zosangalatsa. Cina, pemphelani kwa Yehova kuti akuthandizeni kuyesetsa kutsatila ndandanda yanu. Mukatelo, mudzakhala na mphamvu komanso nthawi yokwanila yocita phunzilo la Baibo laumwini, kulambila kwa pabanja, kusonkhana, na kutumikila Yehova mwa kugwila nchito yolalikila na kuphunzitsa. Komanso, simudzadziimba mlandu cifukwa ca nthawi imene mumathela pa zosangalatsa.

KHALANIBE ODZIPELEKA KWA YEHOVA YEKHA

18-19. Tingaonetse bwanji kuti ndife odzipeleka kwa Yehova yekha?

18 Mtumwi Petulo anafotokoza za kuwonongedwa kwa dziko la Satanali ndiponso za dziko latsopano limene lidzabwela. Kenako anati: “Okondedwa, pakuti mukuyembekezela zinthu zimenezi, citani ciliconse cotheka kuti iye adzakupezeni opanda banga, opanda cilema ndiponso muli mu mtendele.” (2 Pet. 3:14) Tifunika kumvela malangizo amenewa mwa kuyesetsa kukhala na khalidwe loyela, komanso kulambila Yehova mmene iye amafunila. Tikatelo, tidzaonetsa kuti ndifedi odzipeleka kwa Yehova yekha.

19 Satana na dziko lake sadzaleka kutikopa kuti tiike zinthu zina patsogolo m’malo mwa Yehova. (Luka 4:13) Komabe, kaya tikumane na mayeselo otani, sitidzalola ciliconse kapena aliyense kukhala patsogolo mu umoyo wathu kuposa Yehova. Tatsimikiza mtima kukhala odzipeleka kwa Yehova yekha, cifukwa iye yekha ndiye woyenela kum’lambila!

NYIMBO 30 Tate Wanga, Mulungu Wanga, Bwenzi Langa

^ ndime 5 Ife tonse timakonda kutumikila Yehova. Koma kodi ndife odzipeleka kwa iye yekha? Zosankha zathu n’zimene zimaonetsa ngati ndifedi odzipeleka kwa Yehova yekha. Conco, tiyeni tikambilane zosankha zimene timapanga pa nkhani ya zosangalatsa na ndalama. Kukambilana zimenezi kudzatithandiza kuona ngati ndifedi odzipeleka kwa Yehova yekha.

^ ndime 53 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Sitingafune kudya cakudya coipa cimene aciphikila m’khichini yauve. Ndiye n’kutambilanji zosangalatsa zoipa zophatikizapo ciwawa, zamizimu, kapena ciwelewele?