Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Pamene cimphepo coopsa camkuntho cocokela kwa Mulungu ciyandikila, anthu afunika kumvela cenjezo!

Mulungu Asanapeleke Ciweluzo, Kodi Nthawi Zonse Amacenjeza Anthu Mokwanila?

Mulungu Asanapeleke Ciweluzo, Kodi Nthawi Zonse Amacenjeza Anthu Mokwanila?

KATSWILI wazanyengo akuona pa makina ake opimila nyengo. Iye akuzindikila kuti cimphepo coopsa camkuntho cikuyandikila dela limene muli anthu ambili. Powadela nkhawa anthuwo, akuwacenjeza mwamphamvu kuti athaŵe mwamsanga m’delalo.

Masiku ano, Yehova akucita zofanana na zimenezi. Akucenjeza anthu za “cimphepo camkuntho” coopsa kwambili kuposa mphepo iliyonse yoopsa imene inacitikapo. Kodi iye akucita bwanji zimenezi? Nanga tingatsimikizile bwanji kuti akucenjeza anthu mokwanila kuti acitepo kanthu? Kuti tiyankhe mafunso amenewa, tiyeni coyamba tikambilane za macenjezo ena amene Yehova anapelekapo m’nthawi yakale.

NTHAWI PAMENE MULUNGU ANACENJEZAPO ANTHU

M’nthawi yakale, Yehova anacenjezapo anthu za ‘mphepo zamkuntho’ kapena kuti ziweluzo zimene anafuna kupeleka kwa anthu amene anali kuphwanya malamulo ake mwadala. (Miy. 10:25; Yer. 30:23) Pa cocitika ciliconse, iye anali kucenjezelatu anthu pasadakhale na kuwauza zoyenela kucita pomvela malamulo ake. (2 Maf. 17:12-15; Neh. 9:29, 30) Pofuna kulimbikitsa anthu kusintha, Mulungu anali kutumiza atumiki ake okhulupilika kuti akalengeze za ciweluzo cake kwa anthuwo, na kuwathandiza kuona kuti anafunika kucitapo kanthu mwamsanga.—Amosi 3:7.

Mmodzi wa atumiki a Mulungu okhulupilika amenewo anali Nowa. Kwa zaka zambili, iye mopanda mantha anacenjeza anthu a m’nthawi yake, amene anali aciwelewele na aciwawa, kuti kudzabwela Cigumula ca padziko lonse. (Gen. 6:9-13, 17) Anawauzanso zimene anafunika kucita kuti akapulumuke. Nowa analalikila mwakhama kwambili, cakuti pambuyo pake anachedwa “mlaliki wa cilungamo.”—2 Pet. 2:5.

Olo kuti Nowa anawacenjeza mwakhama, anthuwo ananyalanyaza uthenga wocokela kwa Mulungu. Iwo anaonetsa kuti analibiletu cikhulupililo. Conco, anafa pamene Cigumula “cinafika n’kuwaseselatu onsewo.” (Mat. 24:39; Aheb. 11:7) Cigumula citafika, iwo analibenso cifukwa codandaulila kuti Mulungu sanawacenjeze.

Nthawi zina, Yehova anali kucenjeza anthu atangotsala pang’ono kupeleka ciweluzo. Olo zinali conco, anali kuonetsetsa kuti anthuwo apatsidwa nthawi yokwanila yolabadila macenjezo ake. N’zimene anacita asanabweletse Milili 10 kwa Aiguputo. Iye anawacenjezelatu. Mwacitsanzo, Yehova anatuma Mose na Aroni kuti akacenjeze Farao na atumiki ake za mlili wa 7, womwe unali mvula yamphamvu kwambili ya matalala. Popeza mvula ya matalalayo inafunika kuyamba tsiku lotsatila, kodi tinganene kuti Mulungu anawapatsadi nthawi yokwanila yopeza pothaŵila? Baibo imati: “Aliyense amene anaopa mawu a Yehova pakati pa atumiki a Farao anaonetsetsa kuti ziweto zake ndi anchito ake athawila m’nyumba. Koma aliyense amene sanalabadile mawu a Yehova anasiya atumiki ake ndi ziweto zake kunja.” (Eks. 9:18-21) Conco, n’zoonekelatu kuti Yehova anawacenjeza mokwanila, kotelo kuti amene anacitapo kanthu mwamsanga, sanavutike kwambili na mlili umenewo.

N’zimenenso Yehova anacita asanabweletse mlili wa namba 10. Anacenjeza Farao na atumiki ake. Koma iwo anacita zinthu mopanda nzelu mwa kusamvela cenjezo limeneli. (Eks. 4:22, 23) Mapeto ake, ana awo aamuna oyamba kubadwa anaphedwa. Zinalidi zomvetsa cisoni kwambili. (Eks. 11:4-10; 12:29) Kodi iwo anali na mpata wolabadila cenjezo limeneli? Inde! Mwamsanga, Mose anacenjeza Aisiraeli za mlili wa namba 10 umene unali kubwela, komanso anawauza zimene anafunika kucita kuti apulumutse mabanja awo. (Eks. 12:21-28) Cifukwa cakuti anamvela Yehova, anthu 3 miliyoni anatuluka mu Iguputo. Panali Aisiraeli na “khamu la anthu a mitundu yosiyanasiyana,” kuphatikizapo Aiguputo.—Eks. 12:38.

Monga taonela m’zitsanzo zimenezi, nthawi zonse Yehova anali kuonetsetsa kuti anthu ali na nthawi yokwanila yolabadila macenjezo ake. (Deut. 32:4) Kodi colinga cake cinali ciani pocita zimenezi? Mtumwi Petulo anafotokoza kuti Yehova “safuna kuti wina aliyense adzawonongedwe, koma amafuna kuti anthu onse alape.” (2 Pet. 3:9) Inde, Mulungu anali kuwafunila zabwino anthu. Anali kufuna kuti asanapeleke ciweluzo, anthuwo alape na kumvela uphungu wake.—Yes. 48:17, 18; Aroma 2:4.

KULABADILA CENJEZO LA MULUNGU MASIKU ANO

Masiku anonso, anthu onse afunika kulabadila cenjezo lofunika kwambili limene likupelekedwa pa dziko lonse. Pamene anali pa dziko lapansi, Yesu anakambilatu kuti dzikoli lidzawonongedwa pa nthawi ya “cisautso cacikulu.” (Mat. 24:21) Ponena za nthawi ya ciweluzo imeneyo, iye anakamba ulosi womveka bwino wofotokoza zimene otsatila ake adzaona na kukumana nazo, nthawiyo ikadzatsala pang’ono kukwana. Iye anakambilatu zocitika zikulu-zikulu za pa dziko lonse zimene tikuziona masiku ano.—Mat. 24:3-12; Luka 21:10-13.

Mogwilizana na ulosi umenewu, Yehova lomba akulimbikitsa aliyense kugonjela ulamulilo wake wacikondi. Iye amafuna kuti anthu omvela akhale na moyo wabwino pali pano, ndiponso kuti kutsogolo akasangalale na madalitso m’dziko latsopano lolungama. (2 Pet. 3:13) Pofuna kuthandiza anthu kukhulupilila malonjezo ake, Yehova wapeleka uthenga wopulumutsa moyo. Uwu ni “uthenga wabwino . . . wa Ufumu,” umene Yesu anakambilatu kuti “udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse.” (Mat. 24:14) Mulungu wakhazikitsa gulu la olambila ake oona kuti apeleke “umboni,” kapena kuti kulalikila uthenga wocokela kwa Mulungu umenewu m’maiko pafupi-fupi 240. Yehova afuna kuti anthu ambili alabadile cenjezo lake kuti akapulumuke ciweluzo cake, cimene cili monga cimphepo coopsa camkuntho.—Zef. 1:14, 15; 2:2, 3.

Conco, n’zoonekelatu kuti Yehova amapeleka nthawi yokwanila kwa anthu yolabadila macenjezo ake. Maumboni amene tapenda, aonetselatu kuti n’zimene iye amacita nthawi zonse. Koma funso lofunika kwambili n’lakuti, Kodi anthu adzalabadila cenjezo la Mulungu nthawi isanathe? Monga amithenga a Mulungu, tiyeni tipitilize kuthandiza anthu ambili mmene tingathele kuti akapulumuke mapeto a dzikoli.