Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 42

Kodi Mudzalola Yehova Kukucititsani Kukhala Ndani?

Kodi Mudzalola Yehova Kukucititsani Kukhala Ndani?

“Mulungu . . . amalimbitsa zolakalaka zanu [na kukupatsani mphamvu] kuti mucite zinthu zonse zimene iye amakonda.​AFIL. 2:13.

NYIMBO 104 Mphatso ya Mzimu Woyela

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Kodi Yehova angacite ciani kuti akwanilitse colinga cake?

YEHOVA angathe kukhala ciliconse cimene angafune kuti akwanilitse colinga cake. Mwacitsanzo, Yehova ni Mphunzitsi, Wotonthoza, komanso Mlaliki. Apa tangochulako zocepa cabe. (Yes. 48:17; 2 Akor. 7:6; Agal. 3:8) Komabe, nthawi zambili iye amagwilitsila nchito anthu pokwanilitsa cifunilo cake. (Mat. 24:14; 28:19, 20; 2 Akor. 1:3, 4) Komanso, Yehova angapatse aliyense wa ife nzelu na mphamvu, kuti tikhale ciliconse cimene afuna n’colinga cakuti akwanilitse cifunilo cake. Zonsezi ni mbali ya tanthauzo la dzina lake lakuti Yehova, ndipo n’zogwilizana na zimene akatswili ena amakamba.

2. (a) N’cifukwa ciani ena amakayikila kuti Yehova amawagwilitsila nchito? (b) Kodi tidzakambilana ciani m’nkhani ino?

2 Tonse timafuna kuti Yehova atigwilitsile nchito pokwanilitsa cifunilo cake. Komabe, ena amakayikila zakuti Yehova amawagwilitsila nchito. N’cifukwa ciani amakayikila? Ena amaona kuti sangacite zambili cifukwa ca msinkhu wawo. Enanso amaona kuti mikhalidwe siingawalole, kapenanso kuti alibe maluso ofunikila. Koma pali ena amene amakhutila na zimene amacita pali pano, ndipo saona kufunika kowonjezela zocita. M’nkhani ino, tidzakambilana na kuona mmene Yehova amatithandizila kuti tikwanilitse colinga cake. Ndiyeno, tidzakambilana zitsanzo za amuna na akazi ochulidwa m’Baibo. Tidzaona mmene Yehova analimbitsila zolaka-laka zawo na kuwapatsa mphamvu kuti acite cifunilo cake. Potsiliza, tidzakambilana mmene tingaonetsele kuti tifuna kugwilitsidwa nchito na Yehova.

MMENE YEHOVA AMATITHANDIZILA

3. Malinga na Afilipi 2:13, kodi Yehova angalimbitse bwanji zolaka-laka zathu kuti ticite cifunilo cake?

3 Ŵelengani Afilipi 2:13. * Yehova amalimbitsa zolaka-laka zathu kuti ticite cifunilo cake. Kodi amacita bwanji zimenezo? Mwina tingamvele zakuti wina mu mpingo akufunikila thandizo, kapena pali nchito inayake imene ifunika kucitidwa. Mwinanso, akulu angaŵelengele mpingo kalata yocokela ku ofesi ya nthambi, yotidziŵitsa kuti abale kwinakwake akufunikila thandizo. Tikamvela zimenezi, tingadzifunse kuti, ‘Ningacite ciani kuti nithandizeko?’ N’kuthekanso kuti tinapatsidwa utumiki winawake wovuta, koma tikukayikila ngati tingaukwanitse. Kapena tingaŵelenge lemba linalake m’Baibo, na kuyamba kudzifunsa kuti, ‘Kodi mfundo ya pa lembali ningaiseŵenzetse bwanji pothandiza ena?’ Yehova sangatikakamize kucita zimene sitikufuna. Koma akaona kuti tikuganizila zimene tingacite, angalimbitse zolaka-laka zathu kuti tikwanitse kucita zimene tikuganizilazo.

4. Kodi Yehova angatipatse bwanji mphamvu kuti ticite cifunilo cake?

4 Cinanso, Yehova angatipatse mphamvu kuti ticite cifunilo cake. (Yes. 40:29) Motani? Angatithandize na mzimu wake kuti tikulitse maluso amene tili nawo. (Eks. 35:30-35) Cina, Yehova angaseŵenzetse gulu lake kuti atiphunzitse mmene tingagwilile nchito zina zimene tapatsidwa. Ngati simudziŵa mogwilila nchito imene mwapatsidwa, muyenela kupempha thandizo kwa ena. Komanso, khalani womasuka kupempha thandizo kwa Atate wathu wakumwamba, amene ni woolowa manja, kuti akupatseni “mphamvu yoposa yacibadwa.” (2 Akor. 4:7; Luka 11:13) M’Baibo, muli zitsanzo zambili za amuna na akazi amene Yehova anawathandiza kucita cifunilo cake. Analimbitsa zolaka-laka zawo, na kuwapatsa mphamvu. Pokambilana zina mwa zitsanzo zimenezo, ganizilani mmene Yehova angakuseŵenzetseleni kuti mucite zinthu zolingana na zimene iwo anacita.

ZIMENE AMUNA ENA ANACITA MOTHANDIZIDWA NA YEHOVA

5. Kodi tiphunzilapo ciani tikaganizila nthawi imene Yehova anayamba kuseŵenzetsa Mose kuti apulumutse anthu ake?

5 Yehova anaseŵenzetsa Mose kupulumutsa Aisiraeli. Koma kodi ni liti pamene Yehova anayamba kumuseŵenzetsa? Mose ‘ataphunzila nzelu zonse za Aiguputo,’ mwina anadziona kuti anali woyenela kupulumutsa Aisiraeli. Koma Yehova sanayambe pa nthawi imeneyi kumuseŵenzetsa. (Mac. 7:22-25) Anayamba kumuseŵenzetsa atamuphunzitsa kukhala wodzicepetsa na wofatsa. (Mac. 7:30, 34-36) Yehova anathandiza Mose kukhala wolimba mtima, moti anakwanitsa kukakamba na wolamulila wamphamvu kwambili wa Aiguputo. (Eks. 9:13-19) Kodi tiphunzilapo ciani tikaganizila nthawi imene Yehova anayamba kuseŵenzetsa Mose? Tiphunzilapo kuti Yehova amaseŵenzetsa anthu amene amayesetsa kutengela makhalidwe ake na kum’dalila kuti awapatse mphamvu.—Afil. 4:13.

6. Kodi tiphunzilapo ciani tikaona mmene Yehova anaseŵenzetsela Barizilai kuthandiza Mfumu Davide?

6 Patapita zaka zambili, Yehova anaseŵenzetsa Barizilai kuthandiza Mfumu Davide. Panthawi ina, Davide na asilikali ake anali kuthawa Abisalomu, mwana wa Davide. Iwo anali na njala, ludzu, ndiponso anali otopa. Koma pamodzi na amuna ena, Barizilai, olo kuti anali wokalamba, anaika moyo wake pa ciopsezo mwa kupeleka thandizo kwa Davide na asilikali ake. Iye sanaganize kuti popeza anali wokalamba, ndiye kuti Yehova sakanamugwilitsilanso nchito. M’malomwake, moolowa manja anaseŵenzetsa zinthu zimene anali nazo pothandiza atumiki a Mulungu pa zosoŵa zawo. (2 Sam. 17:27-29) Kodi tiphunzilapo ciani? Olo tili na zaka zingati, Yehova angatigwilitsile nchito kuthandiza okhulupilila anzathu amene alibe zinthu zofunikila mu umoyo, kaya a m’dela lathu kapena a ku dziko lina. (Miy. 3:27, 28; 19:17) Mwina sitingakwanitse kupeleka thandizo la mwacindunji kwa iwo. Ngakhale n’telo, tingapeleke zopeleka zothandizila pa nchito ya padziko lonse, kuti zikagwilitsidwe nchito pothandiza abale na alongo athu kulikonse, komanso nthawi iliyonse imene afunika thandizo.—2 Akor. 8:14, 15; 9:11.

7. Kodi Yehova anamugwilitsila nchito bwanji Simiyoni? Nanga zimenezi zingatilimbikitse bwanji?

7 Citsanzo cina, ni ca mwamuna wina wokalamba komanso wokhulupilika, dzina lake Simiyoni. Iye anali kukhala ku Yerusalemu, ndipo Yehova anam’lonjeza kuti asanamwalile adzaona Mesiya. Lonjezo limenelo liyenela kuti linam’limbikitsa kwambili Simiyoni, popeza anali atayembekezela Mesiya kwa zaka zambili. Iye anadalitsidwa cifukwa ca kupilila na kukhulupilika kwake. Tsiku lina, “motsogoleledwa ndi mzimu,” anabwela kukacisi. Kumeneko, anaona Yesu ali wakhanda, ndipo Yehova anagwilitsila nchito Simiyoni kulosela za mwanayo, amene anadzakhala Khristu. (Luka 2:25-35) Simiyoni ayenela kuti anamwalila Yesu asanayambe utumiki wake. Olo zinali conco, iye anayamikila ngako kuti Yehova anamugwilitsila nchito mwanjila imeneyi. Ndipo kutsogolo adzalandila madalitso ambili. M’dziko latsopano, Simiyoni wokhulupilikayo adzaona madalitso amene ulamulilo wa Yesu udzabweletsa kwa anthu a mitundu yonse padziko lapansi. (Gen. 22:18) Na ife tiyenela kuyamikila mwayi uliwonse wa utumiki umene Yehova watipatsa.

8. Kodi Yehova angatigwilitsile nchito bwanji monga Baranaba?

8 M’nthawi ya Atumwi, munthu wina woolowa manja, dzina lake Yosefe anadzipeleka kuti Yehova amugwilitsile nchito. (Mac. 4:36, 37) Iye anali kucita bwino kwambili pa nkhani yotonthoza ena. Mwacionekele, ndiye cifukwa cake atumwi anam’patsa dzina lakuti Baranaba, kutanthauza “Mwana wa Citonthozo.” Mwacitsanzo, Saulo atakhala Mkhristu, ambili mwa abale anali kuyopa kugwilizana naye cifukwa anali kudziŵika kuti anali kuzunza mpingo wacikhristu. Komabe, mokoma mtima Baranaba anamulimbikitsa na kumuthandiza. Ndipo Saulo ayenela kuti anayamikila kwambili kukoma mtima kumeneku. (Mac. 9:21, 26-28) Panthawi inanso, akulu ku Yerusalemu anali kufuna kulimbikitsa abale amene anali kukhala ku madela a kutali ku Antiokeya wa ku Siriya. Kodi iwo anatumiza ndani? Anatumiza Baranaba! Ndipo anacita bwino kutumiza iye. Baibo imati iye “anayamba kulimbikitsa onse kuti apitilize kukhala okhulupilika kwa Ambuye motsimikiza mtima.” (Mac. 11:22-24) Mofananamo, masiku ano Yehova angatithandize kukhala “mwana wa citonthozo” kwa Akhristu anzathu. Mwacitsanzo, angatigwilitsile nchito kutonthoza anthu amene anataikilidwa okondedwa awo. Mwinanso angatisonkhezele kulimbikitsa munthu wodwala kapena wovutika maganizo mwa kupita kukam’cezela kapena kungom’tumila foni. Kodi mudzalola kuti Yehova akuseŵenzetseni monga anacitila na Baranaba?—1 Ates. 5:14.

9. Tingaphunzile ciani tikaganizila mmene Yehova anathandizila m’bale Vasily kukhala m’busa wabwino?

9 Yehova anathandizanso m’bale wina, dzina lake Vasily, kukhala m’busa wabwino. Vasily anali na zaka 26 pamene anaikidwa kukhala mkulu. Panthawiyo, anali na mantha cifukwa codziona kuti sangakwanitse kuthandiza abale na alongo mwauzimu, maka-maka ofalitsa amene anali kukumana na mavuto. Komabe, iye anaphunzila zambili kwa akulu ofikapo mwauzimu, komanso m’Sukulu ya Utumiki wa Ufumu imene anangena. Vasily anayesetsa kuti apite patsogolo. Mwacitsanzo, anadziikila zolinga zing’ono-zing’ono. Ndipo pamene anali kukwanilitsa zolingazo, mantha ake anatha pang’ono-pang’ono. Iye tsopano akuti: “Zinthu zimene n’nali kuyopa kale, n’zimene zimanipatsa cimwemwe cacikulu tsopano. Yehova akanithandiza kupeza lemba logwila mtima limene ningagwilitsile nchito polimbikitsa m’bale kapena mlongo mu mpingo, nimakhala na cimwemwe cacikulu.” Abale, mukadzipeleka monga Vasily kuti Yehova akugwilitsileni nchito, iye adzakupatsani mphamvu na maluso kuti muthe kusenza maudindo aakulu mu mpingo.

ZIMENE AKAZI ENA ANACITA MOTHANDIZIDWA NA YEHOVA

10. Kodi Abigayeli anacita ciani? Nanga tiphunzilapo ciani pa citsanzo cake?

10 Panthawi ina, Davide na asilikali ake okhulupilika anali kuthamangitsidwa na Mfumu Sauli. Iwo anali kufunikila thandizo. Asilikali a Davide anapita kukapempha thandizo kwa Mwisiraeli wina wolemela, dzina lake Nabala. Anamupempha kuti awapatseko cakudya cocepa, ciliconse cimene akanakwanitsa kuwapatsa. Anamasuka kumupempha cifukwa anali kum’tetezela nkhosa zake m’cipululu. Koma Nabala wodzikondayo anakana kuwapatsa cakudya ciliconse. Davide anakwiya kwambili cakuti anakonza zakuti akaphe Nabala na amuna onse a m’nyumba yake. (1 Sam. 25:3-13, 22) Komabe, Abigayeli, mkazi wokongola wa Nabala anali wanzelu kwambili. Molimba mtima, iye anapita kukagwada pa mapazi a Davide na kum’condelela kuti asabwezele coipa kuti asakhale na mlandu wa magazi. Mwanzelu, anamulimbikitsa kusiya nkhaniyo m’manja mwa Yehova. Davide anakhudzika mtima kwambili cifukwa cakuti Abigayeli anakamba naye modzicepetsa komanso anacita zinthu mwanzelu. Davide anazindikila kuti Yehova ndiye anatumiza Abigayeli kuti akakumane naye. (1 Sam. 25:23-28, 32-34) Abigayeli anakulitsa makhalidwe amene anali ofunikila kuti Yehova amugwilitsile nchito. Masiku anonso, alongo anzelu na ozindikila, Yehova angawagwilitsile nchito kulimbitsa mabanja awo na Akhristu ena mu mpingo.—Miy. 24:3; Tito 2:3-5.

11. Kodi ana aakazi a Salumu anacita ciani? Nanga n’ndani masiku ano amene amatengela citsanzo cawo?

11 Patapita zaka zambili, ana aakazi a Salumu anali pakati pa anthu amene Yehova anawaseŵenzetsa pa nchito yokonzanso mpanda wa Yerusalemu. (Neh. 2:20; 3:12) Olo kuti atate awo anali kalonga, iwo anadzipeleka kucita nchito yovuta imeneyo, komanso yoika moyo pa ciopsezo. (Neh. 4:15-18) Iwo anali osiyana kwambili ndi anthu ochuka pakati pa Atekowa, amene sanadzicepetse kuti agwile nawo nchitoyo. (Neh. 3:5) Ganizilani cimwemwe cimene ana aakazi a Salumu anakhala naco, pamene nchitoyo inatha m’masiku 52 cabe! (Neh. 6:15) Masiku anonso, pali alongo amene amadzipeleka mwacimwemwe kucita utumiki wapadela, womanga na kukonzanso nyumba zolambilila zopatulidwa kwa Yehova. Thandizo la alongo odzipeleka, aluso, na okhulupilika amenewa ni lofunika kwambili pa nchitoyi.

12. Kodi Yehova angatigwilitsile nchito bwanji mofanana na Tabita?

12 Yehova anasonkhezela Tabita “kucita nchito zabwino zambili, ndi kupeleka mphatso zacifundo zoculuka,” maka-maka kwa akazi amasiye. (Mac. 9:36) Cifukwa cakuti anali woolowa manja kwambili komanso wokoma mtima, anthu ambili anamulila atamwalila. Koma mtumwi Petulo atamuukitsa, anthuwo anakondwela ngako. (Mac. 9:39-41) Tiphunzilapo ciani pa citsanzo ca Tabita? Tiphunzilapo kuti kaya ndife acicepele kapena okalamba, amuna kapena akazi, tonse tingakwanitse kuthandiza abale na alongo athu.—Aheb. 13:16.

13. Kodi Yehova anamuseŵenzetsa bwanji mlongo Ruth, amene anali ni wamanyazi? Nanga pamapeto pake iye anati ciani?

13 Mlongo wina wamanyazi, dzina lake Ruth, anali kufuna kukhala mmishonale. Ali wacicepele, anali wacangu kwambili kugaŵila tumapepala twauthenga ku nyumba na nyumba. Iye anati: “N’nali kuikonda kwambili nchito imeneyi.” Koma cifukwa ca manyazi, akapeza anthu pa nyumba, sanali kukambako nawo kuti awauze za Ufumu wa Mulungu. Olo kuti anali wamanyazi, Ruth anakhala mpainiya wanthawi zonse atafika zaka 18. Mu 1946, anangena Sukulu ya Giliyadi Yophunzitsa Baibo. Ndipo pambuyo pake anakatumikila ku Hawaii na ku Japan. Yehova anamuseŵenzetsa mwapadela kulengeza uthenga wabwino m’maiko amenewo. Atagwila nchito yolalikila kwa zaka pafupi-fupi 80, iye anati: “Nthawi zonse Yehova wakhala akunilimbikitsa. Wanithandiza kuthetsa manyazi. Nikhulupilila na mtima wonse kuti Yehova angagwilitsile nchito munthu aliyense amene amam’dalila.”

LOLANI KUTI YEHOVA AKUGWILITSILENI NCHITO

14. Malinga na Akolose 1:29, kodi tifunika kucita ciani kuti Yehova atigwilitsile nchito?

14 Kuyambila kale-kale, Yehova wakhala akugwilitsila nchito atumiki ake m’njila zambili zosiyana-siyana. Nanga bwanji imwe? Kodi mudzalola Yehova kukugwilitsilani nchito monga ndani? Kwakukulu-kulu, zidzadalila pa mzimu wanu wodzipeleka kucita zambili. (Ŵelengani Akolose 1:29.) Ngati mudzipeleka, Yehova angakucititseni kukhala wolengeza ufumu wacangu, mphunzitsi wogwila mtima, munthu wotonthoza ena mokoma mtima, wanchito waluso, bwenzi lolimbikitsa, kapena ciliconse cimene angafune kuti akwanilitse cifunilo cake.

15. Malinga na malangizo a pa 1 Timoteyo 4:12, 15, kodi abale acicepele afunika kupempha Yehova kuti awathandize kucita ciani?

15 Nanga bwanji imwe abale acicepele amene mukukula? Dziŵani kuti pafunika abale ambili amphamvu kuti akalamile na kuyamba kutumikila monga atumiki othandiza. M’mipingo yambili, muli akulu ambili kuposa atumiki othandiza. Imwe abale acicepele, yesetsani kukalamila kuti musenze maudindo mu mpingo. Nthawi zina, abale ena amakamba kuti, “Nimakhutila kutumikila cabe monga wofalitsa mu mpingo.” Ngati na imwe mumamvela conco, pemphani Yehova kuti akuthandizeni kukhala na cifuno cokalamila kuti mukhale mtumiki wothandiza, komanso kuti akupatseni mphamvu kuti mucite zonse zimene mungathe pom’tumikila. (Mlal. 12:1) Tikufunikila kwambili thandizo lanu!—Ŵelengani 1 Timoteyo 4:12, 15.

16. Kodi tiyenela kum’pempha ciani Yehova? Nanga n’cifukwa ciani?

16 Yehova angakucititseni kukhala ciliconse cimene angafune kuti akwanilitse cifunilo cake. Conco, m’pempheni kuti alimbitse zolaka-laka zanu kuti mugwile nchito yake. Kenako, m’pempheni kuti akupatseni mphamvu zimene mungafunikile. Kaya ndimwe wacicepele kapena wacikulile, yesetsani kuseŵenzetsa nthawi yanu, mphamvu, maluso, na cuma canu polemekeza Yehova. (Mlal. 9:10) Musalole mantha kapena kudzikayikila, kukutaitsani mwayi wocita zonse zimene mungathe potumikila Yehova. Ndithudi! Ni mwayi waukulu kwambili kucita zonse zimene tingathe kuti tibweletse ulemelelo kwa Atate wathu wacikondi, amene ni woyeneladi kulandila ulemelelo.

NYIMBO 127 Mtundu wa Munthu Amene Niyenela Kukhala

^ ndime 5 Kodi mumafuna kucita zambili potumikila Yehova? Kodi mumakayikila zakuti iye akali kukugwilitsilani nchito? Kapena simuona kufunika kuwonjezela zocita potumikila Yehova? M’nkhani ino, tidzakambilana njila zosiyana-siyana zimene Yehova amalimbitsila zolaka-laka zathu, na kutipatsa mphamvu kuti tikhale ciliconse cimene angafune kuti akwanilitse cifunilo cake.

^ ndime 3 Olo kuti Paulo analembela Akhristu a m’nthawi ya atumwi kalatayi, mfundo zake zimagwila nchito kwa atumiki onse a Yehova.