Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 41

Zimene Mungacite Kuti Mudzakhalebe Okhulupilika pa “Cisautso Cacikulu”

Zimene Mungacite Kuti Mudzakhalebe Okhulupilika pa “Cisautso Cacikulu”

“Kondani Yehova, inu nonse okhulupilika ake. Yehova amateteza okhulupilika.”​—SAL. 31:23.

NYIMBO 129 Tidzapilila Mosalekeza

ZIMENE TIKAMBILANE *

1-2. (a) Kodi posacedwa atsogoleli a maiko adzalengeza ciani? (b) Kodi tikambilane mafunso ati?

YELEKEZELANI kuti atsogoleli a maiko apeleka cilengezo ca “bata ndi mtendele,” cimene takhala tikuciyembekezela kwa nthawi yaitali. N’kutheka kuti iwo adzayamba kunyadila kuti pa dziko lapansi tsopano pali mtendele kuposa kale lonse. Atsogoleli a maiko adzayesa kutikopa kuti tiyambe kukhulupilila kuti angakwanitse kuthetsa mavuto onse pa dziko lapansi. Komabe, iwo sadzakhala na mphamvu yolepheletsa zinthu zimene zidzacitika pambuyo pa cilengezo ca “bata ndi mtendele.” Cifukwa ciani? Cifukwa malinga na ulosi wa m’Baibo, “ciwonongeko codzidzimutsa cidzafika pa iwo nthawi yomweyo . . . ndipo sadzapulumuka.”—1 Ates. 5:3.

2 Tiyeni tsopano tikambilane mafunso ofunika kwambili awa: Kodi n’ciani cidzacitika pa nthawi ya “cisautso cacikulu”? Kodi Yehova afuna kuti tizikacita ciani pa nthawiyo? Nanga tingakonzekele bwanji pali pano kuti tikakhalebe okhulupilika pa cisautso cacikulu?—Mat. 24:21.

N’CIANI CIDZACITIKA PA “CISAUTSO CACIKULU”?

3. Malinga na Chivumbulutso 17:5, 15-18, kodi Mulungu adzamuwononga bwanji “Babulo Wamkulu”?

3 Ŵelengani Chivumbulutso 17:5, 15-18. “Babulo Wamkulu” adzawonongedwa! Monga takambila kale, atsogoleli a maiko adzakhala alibe mphamvu pa zimene zidzacitika pa nthawiyo. Cifukwa ciani? Cifukwa ‘Mulungu adzaika izi m’mitima yawo kuti acite monga mwa maganizo ake.’ Kodi maganizo ake ni otani? Ni akuti ufumu wa dziko lonse wa cipembedzo conama uwonongedwe, kuphatikizapo Machechi Acikhristu. * Mulungu adzaika maganizo ake m’mitima ya “nyanga 10” za “cilombo cofiila kwambili.” Nyanga 10 zimenezi ziimila maboma onse amene amacilikiza “cilombo.” Cilombo ciimila bungwe la United Nations. (Chiv. 17:3, 11-13; 18:8) Maboma amenewo akadzaukila cipembedzo conama, ndiye cidzakhala ciyambi ca cisautso cacikulu. Ndithudi! Ici cidzakhala cocitika cocititsa mantha cimene cidzakhudza munthu aliyense pa dziko lapansi.

4. (a) Kodi n’kutheka kuti maboma adzakamba kuti n’ciani cawapangitsa kuwononga Babulo Wamkulu? (b) Nanga anthu amene anali m’zipembedzo zimenezo, adzacita ciani?

4 Sitidziŵa zifukwa zimene maboma adzawonongela Babulo Wamkulu. Mwina iwo adzakamba kuti zipembedzo zikuwalepheletsa kukhazikitsa mtendele pa dziko lapansi, komanso kuti zimakonda kuloŵelela m’ndale. Kapenanso angakambe kuti zipembedzo zadziunjikila cuma cambili na katundu. (Chiv. 18:3, 7) Cioneka kuti pamene maboma adzawononga zipembedzo zonama, sadzapha mamembala onse a m’zipembedzo zimenezo. Koma cioneka kuti iwo adzathetsa zipembedzo zeni-zenizo. Zipembedzo zonama zikadzathetsedwa, anthu amene anali m’zipembedzo zimenezo adzazindikila kuti atsogoleli awo anawagwilitsa mwala. Ndipo mwacionekele adzayamba kukana zakuti anali mamembala a zipembedzo zimenezo.

5. Kodi Yehova analonjeza ciani za cisautso cacikulu? Nanga n’cifukwa ciani adzacita zimenezo?

5 Baibo siifotokoza kuti kuwonongedwa kwa Babulo Wamkulu kudzatenga nthawi yaitali bwanji. Koma cimene tidziŵa n’cakuti sikudzatenga nthawi yaitali kwambili. (Chiv. 18:10, 21) Yehova analonjeza kuti ‘adzafupikitsa masiku’ a cisautso cacikulu, n’colinga cakuti ‘osankhidwa’ ake asakawonongedwe, kuphatikizapo cipembedzo coona. (Maliko 13:19, 20) Koma kodi Yehova afuna kuti tizikacita ciani m’kati mwa cisautso cacikulu Aramagedo isanayambe?

IMANIBE ZOLIMBA KU MBALI YA KULAMBILA KOONA

6. N’cifukwa ciani kuleka kugwilizana na cipembedzo conama pakokha sikokwanila?

6 Monga tinaphunzilila m’nkhani yapita, Yehova amafuna kuti olambila ake azipewa kugwilizana na Babulo Wamkulu. Komabe, kuleka kugwilizana na cipembedzo conama pakokha sikokwanila. Tifunikanso kuimabe zolimba ku mbali ya kulambila koona. Tiyeni tikambilane njila ziŵili zimene tingacitile zimenezi.

MTisaleke kusonkhana pamodzi ngakhale pa nthawi zovuta (Onani ndime 7) *

7. (a) Kodi tingaonetse bwanji kulimba mtima potsatila miyezo yolungama ya Yehova ya makhalidwe abwino? (b) Kodi Aheberi 10:24, 25 ionetsa bwanji kuti kusonkhana n’kofunika kwambili, maka-maka masiku ano?

7 Coyamba, tifunika kupitiliza kucilikiza miyezo yolungama ya Yehova ya makhalidwe abwino. Tiyenela kupewelatu kutengela makhalidwe oipa amene anthu a m’dzikoli ali nawo. Mwacitsanzo, timazonda khalidwe la ciwelewele la mtundu uliwonse, kuphatikizapo vikwati va amuna kapena akazi okha-okha, na makhalidwe ena amathanyula. (Mat. 19:4, 5; Aroma 1:26, 27) Caciŵili, tifunika kupitiliza kulambila Yehova pamodzi na Akhristu anzathu. Timalambila Yehova ku malo aliwonse, kaya ni ku Nyumba ya Ufumu, m’nyumba za abale, ngakhale ku malo ena obisika ngati zinthu n’zovuta. Mulimonse mmene zingakhalile, sitidzaleka kusonkhana. Ndipo tifunika ‘kuwonjezela kucita zimenezi, makamaka pamene tikuona kuti tsikulo likuyandikila.’—Ŵelengani Aheberi 10:24, 25.

8. Kodi cioneka kuti uthenga wathu udzasintha bwanji kutsogolo?

8 N’zoonekelatu kuti pa nthawi ya cisautso cacikulu, uthenga umene timalalikila udzasintha. Pali pano, timalalikila uthenga wabwino wa Ufumu, ndipo timayesetsa kupanga ophunzila. Koma pa nthawiyo, n’kutheka kuti tidzayamba kulalikila uthenga woŵaŵa ngati matalala. (Chiv. 16:21) Mwina tizikalalikila zakuti dziko la Satana langotsala pang’ono kuwonongedwa. Pa nthawi yoyenelela, tidzauzidwa uthenga weni-weni umene tidzayamba kulalikila komanso mmene tizikalalikilila. Kodi tidzayamba kuseŵenzetsa njila zofanana na zimene takhala tikuseŵenzetsa kwa zaka zoposa 100 polalikila na kuphunzitsa? Kapena tidzaseŵenzetsa njila zina? Pakali pano sitidziŵa. Mulimonsemo, cioneka kuti tidzakhala na mwayi wolengeza molimba mtima uthenga waciweluzo wa Yehova.—Ezek. 2:3-5.

9. Kodi zioneka kuti anthu adzacita ciani akadzamvela uthenga wathu? Nanga ndife otsimikiza za ciani?

9 Mwacionekele, uthenga wathu udzakwiyitsa mitundu ya anthu. Ndipo iwo adzafuna kuthetselatu nchito yathu yolalikila. Masiku ano, timadalila Yehova kuti aticilikize pa utumiki wathu. N’zimenenso tidzafunika kucita pa nthawiyo. Ndife otsimikiza kuti Mulungu adzatipatsa mphamvu kuti tidzathe kucita cifunilo cake.—Mika 3:8.

KONZEKELANI NTHAWI YA KUUKILIDWA KWA ANTHU A MULUNGU

10. Mogwilizana na Luka 21:25-28, kodi anthu ambili adzacita ciani poona zocitika za pa cisautso cacikulu?

10 Ŵelengani Luka 21:25-28. Pa nthawi ya “cisautso cacikulu,” anthu adzakhala na nkhawa kwambili, poona kuti zinthu zonse za m’dzikoli zimene anali kudalila zayamba kusokonezeka. Iwo adzaŵaŵidwa mtima kwambili, podela nkhawa kuti cidzawacitikila n’ciani pa nthawi yoopsa kwambili imeneyo m’mbili yonse ya anthu. (Zef. 1:14, 15) Pa nthawiyo, zinthu mu umoyo ziyenela kuti zidzakhala zovuta kwambili, ngakhale kwa anthu a Yehova. Popeza sitili mbali ya dziko, tingadzakumane na mavuto ena. Zinthu zikhoza kudzafika poipa kwambili, moti n’kusoŵa ngakhale zinthu zina zofunikila kwambili mu umoyo.

11. (a) N’cifukwa ciani mitundu ya anthu idzaika maganizo awo onse pa Mboni za Yehova? (b) N’cifukwa ciani sitifunika kuopa cisautso cacikulu?

11 Pa nthawi ina mkati mwa cisautso cacikulu, anthu amene zipembedzo zawo zidzakhala zitawonongedwa, akhoza kudzakwiya kwambili poona kuti Mboni za Yehova zikupitiliza kulambila. Tangoyelekezelani mkwiyo umene iwo adzaonetsa mwa zokamba zawo, kaya pa intaneti kapena m’njila zina. Mitundu ya anthu na wolamulila wawo, Satana, adzatizonda poona kuti tikupitilizabe kulambila Yehova. Iwo adzazindikila kuti sanakwanilitse colinga cawo cowononga zipembedzo zonse pa dziko lapansi. Conco, maganizo awo onse adzakhala pa ife. Apa m’pamene mitundu ya anthu idzakhala Gogi wa Magogi. * Iwo adzapanga mgwilizano na colinga cakuti awaukile koopsa anthu a Yehova. (Ezek. 38:2, 14-16) N’zomveka kuti tingayambe kuda nkhawa na zimene zidzacitika pa nthawiyo popeza sitidziŵa bwino-bwino mmene zinthu zidzakhalila. Komabe, sitifunika kuopa cisautso cacikulu, cifukwa Yehova adzatipatsa malangizo otithandiza kuti tikapulumuke. (Sal. 34:19) Panthawiyo, ‘tidzaimilila cilili ndi kutukula mitu yathu’, cifukwa tidzadziŵa kuti ‘cipulumutso cathu cayandikila.’ *

12. Kodi “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu” wakhala akutithandiza bwanji kukonzekela zocitika za kutsogolo?

12 “Kapolo wokhulupilika ndi wanzelu” wakhala akutikonzekeletsa kuti tikakhalebe okhulupilika pa nthawi ya cisautso cacikulu. (Mat. 24:45) Iye wacita zimenezi m’njila zambili. Mwacitsanzo, ganizilani za misonkhano yacigawo ya pa nthawi yake ya mu 2016 mpaka 2018. Misonkhanoyi inatithandiza kukulitsa makhalidwe ofunikila pamene tsiku la Yehova likuyandikila. Tiyeni tikambilanenso mwacidule za makhalidwe amenewa.

PITILIZANI KUKULITSA MAKHALIDWE A KUKHULUPILIKA, KUPILILA, NA KULIMBA MTIMA

Konzekelani pali pano kuti mukapulumuke “cisautso cacikulu”(Onani ndime 13-16) *

13. Kodi tingakulitse bwanji khalidwe la kukhulupilika? Nanga n’cifukwa ciani tiyenela kucita zimenezo pali pano?

13 Kukhulupilika: Mutu wa msonkhano wacigawo wa 2016 unali wakuti, “Khalanibe Wokhulupilika kwa Yehova.” Pa msonkhano umenewo, tinaphunzila kuti ngati tili pa ubale wolimba na Yehova, tidzakhalabe wokhulupilika kwa iye. Tinaphunzilanso kuti cimene cingatithandize kukhala pa ubwenzi wolimba na Yehova, ni kupemphela kwa iye mocokela pansi pa mtima na kuŵelenga Mawu ake mwakhama. Kucita izi, kudzatithandiza kupilila mayeselo amene tingakumane nawo, ngakhale aakulu kwambili. Pamene mapeto a dziko la Satana ayandikila, tiyembekezela kukumana na mavuto aakulu, amene adzayesa kukhulupilika kwathu kwa Mulungu na Ufumu wake. Mwacidziŵikile, anthu adzapitiliza kutinyoza. (2 Pet. 3:3, 4) Cifukwa cimodzi cacikulu cimene amacitila zimenezi n’cakuti sititengako mbali m’zandale. Conco, lomba ndiyo nthawi yofunika kukulitsa khalidwe la kukhulupilika. Ndipo tikatelo, tidzakhalebe okhulupilika pa cisautso cacikulu.

14. (a) Kodi padzakhala kusintha kotani ponena za abale otsogolela gulu la Mulungu pano pa dziko lapansi? (b) N’cifukwa ciani tidzafunika kukhala okhulupilika pa nthawiyo?

14 Pa nthawi ya cisautso cacikulu, padzakhala kusintha kwa abale otsogolela gulu la Mulungu pano pa dziko lapansi. Pa nthawi ina mkati mwa cisautsoco, odzozedwa onse amene adzakhala akali pa dziko lapansi, adzasonkhanitsidwa kupita kumwamba kuti akamenye nawo nkhondo ya Aramagedo. (Mat. 24:31; Chiv. 2:26, 27) Izi zitanthauza kuti pa nthawiyo sitidzakhalanso na Bungwe Lolamulila pano pa dziko lapansi. Ngakhale n’conco, khamu lalikulu lidzapitilizabe kucita zinthu mwadongosolo. Abale oyenelela a m’gulu la nkhosa zina ndiwo adzayamba kutsogolela. Tidzafunika kuonetsa kuti ndife okhulupilika kwa Yehova mwa kucilikiza abale amenewa, ndiponso kutsatila malangizo ocokela kwa Mulungu amene adzayamba kutipatsa. Cipulumutso cathu cidzadalila pa kumvela malangizo awo!

15. Tingakulitse bwanji khalidwe lopilila? Nanga n’cifukwa ciani tifunika kucita zimenezo pali pano?

15 Kupilila: Mutu wa msonkhano wacigawo wa 2017 unali wakuti, “Limbikani, Musafooke!” Msonkhano umenewo unatithandiza kukulitsa khalidwe lopilila tikakumana na mayeselo. Tinaphunzila kuti tifunika kukhala opilila, kaya zinthu zili bwino kapena ayi. Tingakulitse khalidwe lopilila mwa kudalila Yehova. (Aroma 12:12) Ndipo tisaiŵale mawu a Yesu akuti: “Amene adzapilile mpaka pa mapeto, ndiye amene adzapulumuke.” (Mat. 24:13) Mawu amenewa atanthauza kuti tifunika kukhalabe okhulupilika, mosasamala kanthu za mavuto amene tingakumane nawo. Ngati tipilila mayeselo pali pano, tidzakhala na cikhulupililo colimba, cisautso cacikulu cikalibe kuyamba.

16. Kodi n’ciani cimapangitsa munthu kukhala wolimba mtima? Nanga tingakulitse bwanji khalidwe limeneli pali pano?

16 Kulimba mtima: Mutu wa msonkhano wacigawo wa 2018 unali wakuti, ‘Khalani Olimba Mtima.’ Pa msonkhano umenewo, tinaphunzila kuti maluso kapena nzelu si ndiye zimapangitsa munthu kukhala wolimba mtima. Mofanana na khalidwe la kupilila, kuti tikhale olimba mtima zeni-zeni, timafunika kudalila Yehova. Kodi tingacite ciani kuti tizim’dalila kwambili Yehova? Tiyenela kumaŵelenga Mawu ake tsiku lililonse, ndiponso kusinkha-sinkha mmene Yehova anapulumutsila anthu ake akale. (Sal. 68:20; 2 Pet. 2:9) Mitundu ya anthu ikadzatiukila pa cisautso cacikulu, tidzafunika kukhala olimba mtima na kudalila Yehova kuposa kale lonse. (Sal. 112:7, 8; Aheb. 13:6) Ngati tidalila Yehova pali pano, tidzakhala olimba mtima Gogi akadzatiukila. *

MUZIYEMBEKEZELA MWACIDWI CIPULUMUTSO CANU

Yesu na gulu lake la nkhondo lakumwamba akwela mahosi oyela. Iwo abwela kudzamenya nkhondo ya Aramagedo kuti awononge adani a Mulungu(Onani ndime 17)

17. N’cifukwa ciani sitiyenela kuopa Aramagedo? (Onani cithunzi pa cikuto.)

17 Monga mmene tinaphunzilila m’nkhani yapita, ambili a ife takhala moyo wathu wonse m’masiku otsiliza. Koma tilinso na ciyembekezo cokapulumuka cisautso cacikulu. Nkhondo ya Aramagedo idzathetselatu dongosolo lino la zinthu. Komabe, palibe cifukwa cocitila mantha. Yehova ndiye mwini nkhondoyo, ndipo ife sitidzafunika kutengako mbali. (Miy. 1:33; Ezek. 38:18-20; Zek. 14:3) Yehova akadzangolamula, Yesu Khristu adzatsogolela gulu la nkhondo la Mulungu kuti liyambe kumenya nkhondo. Pa gululo, padzakhala odzozedwa oukitsidwa komanso makamu a angelo. Capamodzi, iwo adzamenya nkhondo yolimbana na Satana, ziwanda zake, na magulu a nkhondo a pa dziko lapansi.—Dan. 12:1; Chiv. 6:2; 17:14.

18. (a) Kodi Yehova anatitsimikizila ciani? (b) Kodi Chivumbulutso 7:9, 13-17 ionetsa bwanji kuti palibe cifukwa cokhalila na nkhawa?

18 Yehova anatitsimikizila kuti: “Cida ciliconse cimene cidzapangidwe kuti cikuvulaze sicidzapambana.” (Yes. 54:17) “Khamu lalikulu” la atumiki okhulupilika a Yehova lidzapulumuka ‘cisautso cacikulu.’ Ndipo lidzapitiliza kumutumikila. (Ŵelengani Chivumbulutso 7:9, 13-17.) Ndithudi, palibe cifukwa cokhalila na nkhawa! Baibo imatipatsa cidalilo cakuti tidzapulumuka. Tidziŵa kuti “Yehova amateteza okhulupilika.” (Sal. 31:23) Anthu onse amene amakonda Yehova na kum’tamanda adzasangalala kuona kuti iye wacotsa citonzo pa dzina lake loyela.—Ezek. 38:23.

19. Ni madalitso otani amene tidzalandila posacedwapa?

19 Ganizilani cabe mmene mawu a pa 2 Timoteyo 3:2-5 angalembedwele pofotokoza za anthu m’dziko latsopano limene simudzakhala cisonkhezelo ca Satana. (Onani kabokosi kakuti Makhalidwe a Anthu M’dziko Latsopano.) M’bale George Gangas * amene anatumikilapo m’Bungwe Lolamulila, anafotokoza motele: “Posacedwa, tidzaloŵa m’dziko latsopano. Lidzakhala dziko labwino cotani nanga mmene aliyense adzakhala m’bale na mlongo! Tidzakhala na moyo kwamuyaya.” Kodi si ciyembekezo cokondweletsa cimeneci?

NYIMBO 122 Cilimikani, Musasunthike!

^ ndime 5 Tidziŵa kuti posacedwa, “cisautso cacikulu” cidzayamba. Kodi n’ciani cidzaticitikila pa nthawi imeneyo? Kodi Yehova afuna kuti tizikacita ciani pa nthawiyo? Nanga ni makhalidwe ati amene tifunika kukulitsa pali pano kuti tikakhalebe okhulupilika? Nkhani ino idzayankha mafunso amenewa.

^ ndime 3 KUFOTOKOZELA MAWU ENA: Tikanena kuti Machechi Acikhristu, titanthauza zipembedzo zonse zimene zimadzinenela kuti zimatsatila Khristu, koma siziphunzitsa anthu kulambila Yehova mmene iye amafunila.

^ ndime 11 KUFOTOKOZELA MAWU ENA: Mawu akuti Gogi wa Magogi (mwacidule, Gogi) atanthauza mgwilizano wa mitundu ya anthu amene adzaukila atumiki a Yehova pa cisautso cacikulu.

^ ndime 11 Kuti mudziŵe zambili pa zimene zidzacitika nkhondo ya Aramagedo ikadzatsala pang’ono kuyamba, onani nkhani 21 m’buku lakuti Ufumu wa Mulungu Ukulamulila. Ndipo kuti mudziŵe zambili za kuukila kwa Gogi wa Magogi, na mmene Yehova adzatetezela anthu ake pa Aramagedo, onani Nsanja ya Mlonda ya July 15, 2015, mapeji 14-19, komanso mutu 17 na 18 m’buku la Cizungu lakuti Pure Worship of Jehovah—Restored At Last!

^ ndime 16 Pa msonkhano wacigawo wa caka cino ca 2019, wa mutu wakuti “Cikondi Sicitha!” tinaphunzila kuti sitifunika kukhala na nkhawa cifukwa Yehova, Mulungu wathu wacikondi amatiteteza.—1 Akor. 13:8.

^ ndime 19 Onani nkhani yakuti “Zochita Zake Zimtsata” mu Nsanja ya Olonda ya December 1, 1994.

^ ndime 65 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Pa nthawi ya cisautso cacikulu, molimba mtima kagulu ka abale na alongo kakucita msonkhano wa mpingo kusanga.

^ ndime 67 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: A khamu lalikulu la atumiki okhulupilika a Yehova adzatuluka m’cisautso cacikulu ali amoyo komanso acimwemwe!