Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

M’bale Joseph F. Rutherford na abale ena panthawi imene anapita ku Europe

1920—Zaka 100 Zapitazo

1920—Zaka 100 Zapitazo

KUMAYAMBILILO kwa zaka za m’ma 1920, anthu a Yehova anali okonzeka kugwila nchito imene inali patsogolo. Lemba la caka limene iwo anasankha mu 1920 linali lakuti, “AMBUYE ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga.”—Sal. 118:14, King James Version.

Yehova anapeleka nyonga kwa alengezi acangu amenewa. M’caka cimeneco, ciŵelengelo ca akopotala kapena kuti apainiya cinawonjezeka kucoka pa 225 kufika pa 350. Ndipo kwa nthawi yoyamba, anchito opitilila 8,000 a m’makilasi, kapena kuti ofalitsa, anapeleka malipoti awo a ulaliki ku likulu. Yehova anadalitsa nchito yawo cakuti panakhala zotulukapo zabwino kwambili.

ANAONETSA CANGU CAPADELA

Pa 21 March 1920, M’bale Joseph F. Rutherford, amene panthawiyo anali kutsogolela nchito ya Ophunzila Baibo, anakamba nkhani yakuti, “Anthu Mamiliyoni Ambili Amene Ali ndi Moyo Sadzafa.” Ophunzila Baibo anayesetsa kuitanila aliyense ku msonkhano umenewo. Iwo anacita lendi holo ina yaikulu mu mzinda wa New York, ndipo anagaŵila tumapepala twa ciitano pafupi-fupi 320,000.

Kulengeza pa nyuzipepala nkhani yakuti “Anthu Mamiliyoni Ambili Amene Ali ndi Moyo Sadzafa”

Ku msonkhanowo kunafika anthu ambili-mbili—kuposa mmene Ophunzila Baibo anaganizila. Ndipo anthu opitilila 5,000 anadzala m’holomo, cakuti ena ofika 7,000 anapemphedwa kubwelela. Magazini ya Nsanja ya Mlonda inati umenewo unali “msonkhano waukulu komanso wolimbikitsa kwambili wa Ophunzila Baibo, umene sunacitikepo n’kale lonse.”

Ophunzila Baibo anadziŵika kwambili cifukwa ca kulengeza kwawo kuti “anthu mamiliyoni ambili amene ali ndi moyo sadzafa.” Panthawiyo, iwo sanadziŵe kuti uthenga wa Ufumu unafunika kulalikidwa ku madela ena ambili. Ngakhale n’conco, anali okalingalika pa nchito imeneyi. Mlongo Ida Olmstead, amene anayamba kusonkhana mu 1902, anati: “Tinali kudziŵa kuti mtundu wonse wa anthu udzalandila madalitso kutsogolo, ndipo sitinalephele kuuza aliyense amene tinapeza mu ulaliki za uthenga wabwino umenewu.”

ANAYAMBA KUDZIPULINTILA OKHA MABUKU

Pofuna kuonetsetsa kuti cakudya cauzimu cikupelekedwa, abale pa Beteli anayamba kudzipulintila okha zofalitsa. Iwo anagula makina na kukawaika m’cipinda cina ca nyumba ya nsanjika ku 35 Myrtle Avenue, ku Brooklyn, mu mzinda wa New York, kamtunda pang’ono kucoka pa Beteli.

M’bale Leo Pelle na m’bale Walter Kessler, anayamba utumiki wawo wa pa Beteli mu January 1920. M’bale Walter anati: “Titafika, m’bale woyang’anila nchito yopulinta mabuku anatiyang’ana na kutiuza kuti, ‘Kwangotsala ola limodzi na hafu kuti nthawi ya cakudya ca masana ikwane.’ Iye anatipempha kutulutsa makatoni a mabuku m’cipinda capansi.”

M’bale Leo anafotokoza zimene zinacitika tsiku lotsatila. Anati: “Inali nchito yathu kutsuka zipupa za nsanjika yapansi ya nyumbayo. Inali nchito yadothi kwambili imene sin’naicitepo n’kale lonse. Koma inali nchito ya Ambuye, ndipo tinaigwilabe nchitoyo.”

Makina amene anali kupulintila Nsanja ya Mlonda

M’mawiki ocepa cabe, Nsanja ya Mlonda inali kupulintiwa na atumiki odzipeleka olimbika pa nchito. Magazini okwanila 60,000 a Nsanja ya Mlonda ya February 1, 1920, anapulintiwa pa makina opulintila mabuku pa nsanjika yoyamba. Komanso, m’cipinda capansi abale anaikamo makina ena opulintila ochedwa Battleship. Ndipo magazini yakuti The Golden Age inayamba kupulintiwa pa makina athu, kuyambila na kope ya April 14, 1920. Mosakaika konse, Yehova anadalitsa khama la atumiki odzipeleka amenewo.

“Inali nchito ya Ambuye, ndipo tinaigwilabe nchitoyo”

“TIYENI TIKHALE PA MTENDELE”

Anthu a Yehova anayambanso kulalikila mokangalika komanso mogwilizana. Ngakhale n’telo, Ophunzila Baibo ena anasiya kugwilizana na gulu la Mulungu pa nthawi zovutazo, kucoka mu 1917 mpaka 1919. Kodi anthuwo akanathandizidwa bwanji?

Nsanja ya Mlonda ya April 1, 1920, inali na nkhani yakuti, “Tiyeni Tikhale pa Mtendele.” Inali na mawu olimbikitsa akuti: “Ndife otsimikiza . . . kuti aliyense amene ali ndi mzimu wa Ambuye . . . ni wokonzeka kuiŵala zakumbuyo, . . . na kukhala pamodzi mogwilizana komanso kupitiliza kucita zinthu monga thupi limodzi logwilizana.”

Ambili analabadila mawu olimbikitsa amenewa. Banja lina linalemba kuti: “Tikhulupilila kuti kwa caka cimodzi kapena kuposapo tsopano, tinalakwitsa kungokhala n’kumapenyelela ena akugwila nchito [yolalikila]. . . . Ndipo tsopano ndife okonzeka kugwila nchitoyi mwakhama.” Anchito oyambitsidwanso amenewa anali na nchito yaikulu patsogolo yofunika kuigwila.

ANAGAŴILA BUKU LA “ZG”

Pa 21 June, 1920, Ophunzila Baibo anayamba kampeni yaikulu yogaŵila buku la “ZG,” la cikuto capepala lakuti The Finished Mystery. * Ambili mwa mabuku amenewa anangosungidwa bukuli litaletsedwa mu 1918.

Anchito onse osati cabe akopotala, anapemphedwa kutengako mbali pa nchito yogaŵila bukulo. Kope ya June ya 1920 ya Bulletin * inati: “Munthu wobatizika aliyense m’kilasi iliyonse, amene afuna kutengako mbali, ayenela kugwila nchitoyi mosangalala. Aliyense ayendele mfundo yakuti: ‘Cinthu cimene nizicita, ni kugaŵila’ ZG.” Edmund Hooper anakamba kuti pa kampeniyi, kwa ambili kanali koyamba kugwila nchito yolalikila khomo na khomo, imene anali asanaicitepo kumbuyo konseko. Iye anawonjezela kuti: “Apa tsopano tinadziŵa kuti nchitoyo inafunika kucitika kumadela ena ambili ngakhale amene sitinali kuŵaganizila.”

KULINGANIZANSO NCHITO YOLALIKILA KU EUROPE

Popeza kulumikizana na Ophunzila Baibo m’maiko ena kunali kovuta panthawi ya Nkhondo Yoyamba Yapadziko Lonse, M’bale Rutherford anafuna kukalimbikitsa abale m’maiko amenewo na kulinganizanso nchito yolalikila. Conco pa 12 August, 1920, iye na abale ena anayi ananyamuka ulendo wopita ku England na ku maiko ena.

M’bale Rutherford ku Egypt

M’bale Rutherford atafika ku England, Ophunzila Baibo anacita misonkhano itatu ikulu-ikulu, komanso misonkhano 12 ya anthu onse. Anthu pafupi-fupi 50,000 anapezeka pa misonkhano imeneyi. Ponena za ulendo umenewo, magazini ya Nsanja ya Mlonda inati: “Anzathu kumeneko anatsitsimulidwa na kulimbikitsidwa. Anagwilizana kwambili pa cikondi na utumiki, ndipo mitima yambili yacisoni inasangalala.” Mu mzinda wa Paris, M’bale Rutherford anakambanso nkhani yakuti “Anthu Mamiliyoni Ambili Amene Ali ndi Moyo Sadzafa.” Pamene nkhaniyo inali kuyamba, holo yonse inali yodzala. Ndipo anthu 300 anapempha kudziŵa zowonjezeleka.

Cikwangwani colengeza nkhani imene inakambidwa mu holo ya Royal Albert ku London

M’mawiki okonkhapo, M’bale Rutherford na abale enawo anapita ku Athens, ku Cairo, komanso ku Jerusalem. Pofuna kukulitsa cidwi ca anthu m’madela amenewa, M’bale Rutherford anakhazikitsa malo ofikilapo mabuku m’tauni ya Ramallah, pafupi na Jerusalem. Ndiyeno anabwelela ku Europe na kukakhazikitsa ofesi yanthambi ya Central Europe, na kukonza zakuti mabuku azipulintiwa kumeneko.

KUVUMBULA KUPANDA CILUNGAMO PAMLANDU

Mu September 1920, Ophunzila Baibo anafalitsa magazini yapadela yochedwa The Golden Age ya namba 27, imene inavumbula kuzunzidwa kwa Ophunzila Baibo mu 1918. Ndipo makina amene tawachula kumayambililo ochedwa Battleship, anali kugwila nchito usana ndi usiku, kupulinta makope a magazini imeneyi opitilila 4 miliyoni.

Pikica ya Mlongo Emma Martin ali ku polisi

Oŵelenga magaziniyi anadziŵa za mlandu umene boma linam’semela mlongo Emma Martin. Mlongo Martin anali kopotala mu mzinda wa San Bernardino, ku California. Pa 17 March, 1918, iye na abale ena atatu, m’bale E. Hamm, m’bale E. J. Sonnenburg, komanso m’bale E. A. Stevens, anapita ku msonkhano waung’ono wa Ophunzila Baibo.

Koma munthu wina sanabwele pamsonkhanowo na colinga cophunzila Baibo. Munthuyo pambuyo pake anaulula kuti: “N’napita ku msonkhanowo . . . motumidwa na boma, kuti nipeze umboni wa kukhoti.” Iye anapeza buku lakuti The Finished Mystery limene anali kuti ndiwo umboni. Patapita masiku ocepa cabe, Mlongo Martin na abale atatuwo anagwidwa. Iwo anaimbidwa mlandu wakuti anali akazitape, mwa kugaŵila buku loletsedwa.

Mlongo Martin na abale enawo anaweluzidwa kuti ali na mlandu, ndipo anagamulidwa kukapika ndende kwa zaka zitatu. Iwo anayamba kupika ndende pa 17 May, 1920, cifukwa analibenso mwayi uliwonse wocita apilu. Koma posapita nthawi zinthu zinasintha.

Pa 20 June, 1920, M’bale Rutherford anasimba cokumana naco cawo pa msonkhano mu mzinda wa San Francisco. Posakondwela na mmene nkhani ya Akhristuwo inayendela, opezeka pa msonkhanowo anavomeleza zakuti alembele telegilamu pulezidenti wa America. Mu telegilamuyo iwo anati: “Tiona kuti kumangidwa . . . kwa amayi Martin . . . pamlandu waukazitape n’kupanda cilungamo . . . Zimene akulu-akulu a boma anacita kuseŵenzetsa mphamvu za udindo wawo . . . kuchela msampha . . . amayi Martin . . . na kuwasemela mlandu n’colinga cakuti akapike ndende, tiona kuti n’zosayenela . . . ngakhale pang’ono.”

Tsiku lotsatila lomwelo, pulezidenti wa America, Woodrow Wilson, anathetsa mlandu wa Mlongo Martin, komanso wa M’bale Hamm, M’bale Sonnenburg, na M’bale Stevens. Kumangidwa kwawo kopanda cilungamo kunathela pamenepo.

Pamene caka ca 1920 cinali kufika kumapeto, Ophunzila Baibo anali na zifukwa zambili zokhalila acimwemwe. Nchito ku likulu inapitabe patsogolo. Ndipo kuposa n’kale lonse, Akhristu oona analengeza mwacangu kuti Ufumu wa Mulungu wokha ndiwo udzathetsa mavuto a anthu. (Mat. 24:14) Caka cotsatila ca 1921, cinakhala capadela pa kulengeza coonadi ca Ufumu.

^ ndime 18 Buku lakuti The Finished Mystery inali voliyumu ya namba 7 ya buku lakuti Studies in the Scriptures. Buku la “ZG” la cikuto capepala, linapulintiwa monga Nsanja ya Mlonda ya March 1, 1918. Cilembo ca “Z” cinali kuimila Zion’s Watch Tower, ndipo “G” kuimila cilembo ca namba 7 pa alifabeti, kutanthauza voliyumu ya namba 7.

^ ndime 19 Kamene tsopano ni kabuku ka Umoyo na Utumiki.