Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 44

Kodi Ana Anu Adzatumikilabe Yehova Akakula?

Kodi Ana Anu Adzatumikilabe Yehova Akakula?

“Yesu anali kukulabe m’nzelu ndi mu msinkhu. Ndipo Mulungu ndi anthu anapitiliza kukondwela naye.”—LUKA 2:52.

NYIMBO 134 Ana ni Mphatso Zimene Mulungu Amaikiza kwa Makolo

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Kodi cosankha copambana cimene munthu angapange n’cotani?

NTHAWI zambili, zosankha za makolo zimakhudza ana awo kwa nthawi yaitali. Ngati makolo sapanga zosankha zabwino, angabweletsele ana awo mavuto. Koma ngati amapanga zosankha mwanzelu, amathandiza ana awo kukhala na umoyo wacimwemwe, komanso wokhutilitsa. Koma nawonso ana afunika kupanga zosankha zabwino. Cosankha copambana cimene aliyense angapange, ni kutumikila Atate wathu wacikondi, Yehova.—Sal. 73:28.

2. Kodi Yesu na makolo ake anapanga zosankha zabwino zotani?

2 Mtima wa Yosefe na Mariya unali pa kuthandiza ana awo kutumikila Yehova. Ndipo zosankha zawo monga makolo zinaonetsa kuti ndico cinali colinga cawo cacikulu. (Luka 2:40, 41, 52) Yesu nayenso anapanga zosankha zanzelu zimene zinam’thandiza kucita mbali yake pa colinga ca Yehova. (Mat. 4:1-10) Yesu anakula n’kukhala munthu wokoma mtima, wokhulupilika, komanso wolimba mtima. Inde, anakula monga mwana amene kholo lililonse loopa Mulungu lingam’nyadile na kukondwela naye.

3. Kodi nkhani ino iyankhe mafunso ati?

3 M’nkhani ino, tikambilane mafunso aya: Kodi Yehova anapanga zosankha zabwino ziti zokhudza Yesu? Kodi makolo acikhristu angaphunzilepo ciani pa zosankha zimene makolo a Yesu anapanga? Ndipo Akhristu acinyamata angaphunzile ciani pa zosankha zimene Yesu anapanga?

PHUNZILANI KWA YEHOVA

4. Kodi Yehova anapanga cosankha cofunika citi cokhudza Mwana wake?

4 Yehova anasankhila Yesu makolo abwino koposa. (Mat. 1:18-23; Luka 1:26-38) Mawu a Mariya okhudza mtima opezeka m’Baibo, amaonetsa kukula kwa cikondi cake pa Yehova, na Mawu ake. (Luka 1:46-55) Ndiponso mmene Yosefe anacitila zinthu atapatsidwa malangizo a Yehova, zimaonetsa kuti nayenso anali kuwopa Mulungu, komanso anali kufuna kum’kondweletsa.—Mat. 1:24.

5-6. Kodi Yehova analola Mwana wake kupita m’mavuto otani?

5 Onani kuti Yehova sanasankhile Yesu makolo olemela ayi. Nsembe imene Yosefe na Mariya anapeleka Yesu atabadwa, ionetsa kuti iwo anali osaukila. (Luka 2:24) N’kutheka kuti anali na kashopu pafupi na nyumba yake ku Nazareti, mmene anali kuseŵenzela monga kalipentala. Iwo ayenela kuti anali kukhala umoyo wosalila zambili, maka-maka banja lawo litakula n’kukhala na ana 7 kapena kuposelapo.—Mat. 13:55, 56.

6 Yehova anateteza Yesu ku mavuto ena, koma sanachingilize Mwana wakeyo ku mavuto onse. (Mat. 2:13-15) Mwacitsanzo, Yesu anali na acibale amene sanali kum’khulupilila. Tangoganizani mmene zinalili zovuta kwa Yesu kukhala na a m’banja lake eni-eni, amene poyamba sanakhulupilile kuti iye anali Mesiya. (Maliko 3:21; Yoh. 7:5) Zionekanso kuti imfa ya Yosefe, tate wake womulela, inam’khudza kwambili. Ndiye Yesu pokhala mwana wamkulu m’banja, ayenela kuti sakanacitila mwina koma kuyamba kuyendetsa bizinesi ya banja imene atate ake anasiya. (Maliko 6:3) Pamene Yesu anali kukula, anadziŵa mosamalila banja lawo. Mwa ici, ayenela kuti anali kugwila nchito molimbika. Conco, anadziŵa mmene kulema kumamvekela munthu akagwila nchito tsiku lonse.

Makolo, konzekeletsani ana anu mocitila na mavuto mu umoyo wawo, mwa kuwaphunzitsa kudalila Mawu a Mulungu (Onani ndime 7) *

7. (a) Kodi okwatilana ayenela kudzifunsa mafunso ati pankhani yolela ana awo? (b) Kodi Miyambo 2:1-6 ingawathandize bwanji makolo pophunzitsa ana awo?

7 Ngati ndimwe okwatilana, ndipo mufuna kukhala ndi ana, dzifunseni kuti: ‘Kodi ndife odzicepetsa, komanso okonda zinthu zauzimu cakuti Yehova angatisankhe kusamalila mwana wakhanda?’ (Sal. 127:3, 4) Ngati ndimwe kholo, dzifunseni kuti: ‘Kodi nimaphunzitsa ana anga za kufunika kolimbikila nchito?’ (Mlal. 3:12, 13) ‘Kodi nimayesetsa kuteteza ana anga ku zinthu zoipa za m’dziko la Satanali?’ (Miy. 22:3) Simungathe kuchingiliza ana anu ku mavuto onse amene iwo angakumane nawo. N’zosatheka zimenezo. Koma mungawakonzekeletse mmene angacitile nawo mavuto pa umoyo, mwa kupitilizabe kuwaphunzitsa mwacikondi kudalila Mawu a Mulungu. (Ŵelengani Miyambo 2:1-6) Mwacitsanzo, ngati wacibululu wanu waleka kutumikila Yehova, thandizani ana anu kucokela m’Mawu a Mulungu, kuona kufunika kokhalabe okhulupilika kwa Yehova. (Sal. 31:23) Kapena ngati munthu amene mumam’konda wamwalila, onetsani ana anu mmene angaseŵenzetsele Mawu a Mulungu kuti apeze citonthozo na mtendele wa maganizo.—2 Akor. 1:3, 4; 2 Tim. 3:16.

PHUNZILANI KWA YOSEFE NA MARIYA

8. Malinga na Deuteronomo 6:6, 7, kodi Yosefe na Mariya anacita ciani?

8 Monga makolo, Yosefe na Mariya anathandiza Yesu kukula monga munthu woyanjidwa na Mulungu. Iwo anatsatila malangizo a Yehova kwa makolo. (Ŵelengani Deuteronomo 6:6, 7.) Yosefe na Mariya anali na cikondi cozama pa Yehova, ndipo colinga cawo cacikulu cinali kulimbikitsa ana awo kukhala na cikondi cofananaco.

9. Kodi Yosefe na Mariya anali kucita zinthu zofunika ziti?

9 Yosefe na Mariya anali na pulogilamu yabwino yocita zauzimu monga banja. Mosakaikila, iwo anali kupezeka pa misonkhano ya wiki na wiki ku sunagoge wa ku Nazareti, komanso pa Pasika wa pacaka ku Yerusalemu. (Luka 2:41; 4:16) Iwo ayenela kuti anali kutengela mwayi maulendo amenewo opita ku Yerusalemu monga banja, kuphunzitsa Yesu na azing’ono ake zokhudza mbili ya anthu a Yehova. N’kutheka kuti pamaulendo amenewo, anali kuyendelanso malo ena ochulidwa m’Malemba. Pamene banja lawo linali kukula, mwacionekele sicinali copepuka kwa Yosefe na Mariya kukhalabe na pulogilamu yabwino yocita zauzimu. Koma cifukwa ca kulimbikila kwawo, iwo anadalitsidwa kwambili. Poika kulambila Yehova patsogolo, banja lawo linakhadi lolimba mwauzimu.

10. Kodi makolo acikhristu angaphunzile ciani kwa Yosefe na Mariya?

10 Kodi inu makolo oopa Mulungu mungaphunzile ciani kwa Yosefe na Mariya? Cofunika koposa, kuphunzitsa ana anu mwa mawu na zocita zanu, kuti mumam’konda kwambili Yehova. Dziŵani kuti mphatso yopambana imene mungapatse ana anu, ni kuwaphunzitsa kukonda Yehova. Ndipo cinthu cimodzi cofunika kwambili cimene mungawaphunzitse, ni mmene angakhalile na pulogilamu yokhazikika ya kuŵelenga, kupemphela, kupezeka pa misonkhano, komanso kutengako mbali mu ulaliki. (1 Tim. 6:6) Komabe, mufunikanso kupezela ana anu zinthu zakuthupi. (1 Tim. 5:8) Koma musaiŵale kuti cimene cidzathandiza ana anu kukapulumuka mapeto a dongosolo lino lakale, na kuloŵa m’dziko latsopano la Mulungu, ni ubale wawo wolimba na Yehova, osati zinthu zakuthupi.—Ezek. 7:19; 1 Tim. 4:8.

N’zolimbikitsa kuona kuti makolo ambili acikhristu amapanga zosankha zauzimu zothandiza mabanja awo (Onani ndime 11) *

11. (a) Kodi uphungu wa pa 1 Timoteyo 6:17-19, ungawathandize bwanji makolo kupanga zosankha zabwino polela ana awo? (b) Ni zolinga ziti zimene mungadziikile monga banja? Ndipo mungapeze nazo madalitso otani? (Onani bokosi lakuti “ Kodi Mudzadziikila Zolinga Ziti?”)

11 N’zolimbikitsa kuona kuti makolo ambili acikhristu amapanga zosankha zabwino zauzimu zothandiza mabanja awo. Iwo amalambila Yehova pamodzi nthawi zonse. Amapezeka pa misonkhano yampingo komanso yacigawo. Ndiponso amalalikila uthenga wabwino. Mabanja ena amapita ngakhale kukalalikila ku magawo osafoledwa kaŵili-kaŵili. Ena amapita kukaona Beteli, kapena kukathandiza pa nchito zomanga. Mabanja amene amasankha kucita zimenezi amaseŵenzetsa ndalama zawo, ndipo nthawi zina amakumana na zopinga. Koma mapindu amene amapeza amawalemeletsa mwauzimu. (Ŵelengani 1 Timoteyo 6:17-19.) Ana okulila m’mabanja otelo, nthawi zambili amakula na makhalidwe abwino, ndipo amakhala oyamikila kuti analeledwa mwa njila imeneyi. *Miy. 10:22.

PHUNZILANI KWA YESU

12. Kodi Yesu anafunika kucita ciani pamene anali kukula?

12 Atate a Yesu akumwamba amapanga zosankha zabwino nthawi zonse. Komanso makolo ake a padziko lapansi nawonso anali kupanga zosankha zanzelu. Komabe, pamene Yesu anali kukula anafunikila kumapanga zosankha zake. (Agal. 6:5) Mofanana na aliyense wa ife, iye anali na ufulu wodzisankhila zocita. Akanasankha kuika zofuna zake patsogolo. Koma m’malomwake, iye anasankha kukhalabe paubale wabwino na Yehova. (Yoh. 8:29) Kodi citsanzo cake cingawathandize bwanji acicepele masiku ano?

Acicepele, musakane cilangizo ca makolo anu (Onani ndime 13) *

13. Kodi Yesu anapanga cosankha cofunika citi ali wamng’ono?

13 Ali wamng’ono, Yesu anasankha kukhala wogonjela kwa makolo ake. Iye sanakanepo cilangizo ca makolo ake poganiza kuti anali kudziŵa zambili kuposa iwo. M’malomwake, “anapitiliza kuwamvela.” (Luka 2:51) Mosakaikila, Yesu anayesetsa kukwanilitsa udindo wake monga mwana wamkulu m’banja. Analimbikilanso kuphunzila nchito ya atate ake omulela ya ukalipentala, kuti azithandizila pa zofunika za banja.

14. Tidziŵa bwanji kuti Yesu anali woŵelenga Mawu a Mulungu wakhama?

14 Zioneka kuti Yesu anauzidwa na makolo ake za kubadwa kwake kozizwitsa, komanso mauthenga amene angelo a Mulungu anabweletsa okamba za iye. (Luka 2:8-19, 25-38) Yesu sanadalile cabe zimene anali kuuzidwa. Iye anali kuŵelenganso Malemba payekha. Tidziŵa bwanji kuti Yesu anali woŵelenga Mawu a Mulungu wakhama? Cifukwa ali wamng’ono, aphunzitsi ku Yerusalemu “anadabwa kwambili ndi mayankho ake komanso poona kuti anali womvetsa zinthu kwambili.” (Luka 2:46, 47) Ndipo ali na zaka 12 cabe, Yesu anali atadziŵa kale kuti Yehova anali Tate wake.—Luka 2:42, 43, 49.

15. Kodi Yesu anaonetsa bwanji kuti anasankha kucita cifunilo ca Yehova?

15 Yesu atadziŵa mbali yake pa colinga ca Yehova, anasankha kuvomela utumiki umene anapatsidwa. (Yoh. 6:38) Anadziŵa kuti anthu ambili adzamuzonda, ndipo zioneka kuti zimenezi zinam’vutitsa maganizo. Ngakhale n’conco, iye anasankhabe kumvela Yehova. Yesu atabatizika mu 29 C.E., colinga cake cacikulu mu umoyo cinali kucita cifunilo ca Yehova. (Aheb. 10:5-7) Ngakhale pamene anali kufa pa mtengo wozunzikilapo, Yesu sanasunthike pa kucita cifunilo ca Atate wake.—Yoh. 19:30.

16. Kodi ana angaphunzile ciani kwa Yesu?

16 Mvelani makolo anu. Mofanana ndi Yosefe na Mariya, makolo anu ni opanda ungwilo. Komabe, iwo anapatsidwa udindo na Yehova kuti akutetezeni, kukuphunzitsani, komanso kukulangizani. Ngati mumvela cilangizo cawo na kulemekeza ulamulilo wawo, ‘zinthu zidzakuyendelani bwino.’—Aef. 6:1-4.

17. Malinga na Yoswa 24:15, kodi acicepele ayenela kupanga okha cosankha citi?

17 Sankhani amene mufuna kutumikila. Mufunika kum’dziŵa bwino Yehova, cifunilo cake, komanso mmene mungacitile cifunilo cake mu umoyo wanu. (Aroma 12:2) Mukatelo, mudzapanga cosankha cofunika kopambana mu umoyo wanu, ca kutumikila Yehova. (Ŵelengani Yoswa 24:15; Mlal. 12:1) Ngati mukhala na pulogilamu yokhazikika ya kuŵelenga na kuphunzila Baibo, cikondi canu pa Yehova cidzakula ndipo cikhulupililo canu mwa iye cidzalimbila-limbila.

18. Ni cosankha citi cimene acicepele afunika kupanga, nanga cotulukapo cake cidzakhala cotani?

18 Sankhani kuika cifunilo ca Yehova patsogolo mu wanu. Dziko la Satanali limalonjeza kuti ngati museŵenzetsa maluso anu kuti mudzipindulitse nokha, mudzakhala acimwemwe. Koma zoona zake n’zakuti, amene amaika mtima wonse pa zolinga za kuthupi ‘amadzibweletsela zopweteka zambili pathupi lawo.’ (1 Tim. 6:9, 10) Koma ngati mumvela Yehova na kusankha kuika cifunilo cake patsogolo, mudzakhala na umoyo wopindulitsa, ndipo ‘mudzacita zinthu mwanzelu.’—Yos. 1:8.

MUDZASANKHA KUCITA CIANI?

19. Kodi makolo afunika kukumbukila ciani?

19 Inu makolo, citani zonse zotheka kuti muthandize ana anu kutumikila Yehova. M’dalileni, ndipo adzakuthandizani kupanga zosankha zanzelu. (Miy. 3:5, 6) Kumbukilani kuti ana anu adzatengela kwambili zocita zanu kuposa zokamba zanu. Conco, pangani zosankha zimene zidzawathandiza kuti Yehova awayanje.

20. Kodi acicepele adzapeza madalitso otani ngati asankha kutumikila Yehova?

20 Inu acicepele, makolo anu angakuthandizeni kupanga zosankha zanzelu mu umoyo wanu. Koma kuti muyanjidwe na Mulungu, cosankha n’canu. Telo tengeleni citsanzo ca Yesu na kusankha kutumikila Atate wanu wacikondi wakumwamba. Mukacita izi, mudzakhala na umoyo wa zocita zambili, waphindu, komanso wokondweletsa palipano. (1 Tim. 4:16) Ndipo kutsogolo mudzakhala na umoyo wokhutilitsa koposa!

NYIMBO 133 Lambila Yehova Ukali Wacicepele

^ ndime 5 Makolo acikhristu amafuna kuti ana awo akadzakula, akapitilizebe kutumikila Yehova mokondwa. Kodi makolo angapange zosankha zotani kuti athandize ana awo kupitilizabe kutumikila Yehova ngakhale akadzakula? Nanga Akhristu acinyamata afunika kupanga zosankha zotani kuti akakhale na umoyo wopambana kweni-kweni? Nkhani ino iyankha mafunso amenewa.

^ ndime 11 Onani bokosi lakuti, “Makolo Anga Ndi Anthu Abwino Kwambiri” mu Galamukani! ya October 2011, peji. 20, komanso nkhani yakuti, “Kalata Yapadera Yopita kwa Makolo Awo” mu Galamukani! ya March 8, 1999, peji. 25.

^ ndime 65 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Mariya anathandiza kwambili Yesu ali wamng’ono kukhala na cikondi cozama pa Yehova. Masiku anonso, amayi angathandize ana awo kukhala na cikondi cacikulu pa Yehova.

^ ndime 67 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Yosefe ayenela kuti anali kukonda kupita ku sunagoge na banja lake. Nawonso atate a masiku ano ayenela kukonda kupita kumisonkhano yampingo na mabanja awo.

^ ndime 69 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Yesu anaphunzila maluso a nchito kwa atate ake. Nawonso acicepele a masiku ano angaphunzile maluso kwa atate awo.