Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 41

Mmene Tingatsogozele Phunzilo la Baibo Lotsogolela Munthu ku Ubatizo—Gawo 1

Mmene Tingatsogozele Phunzilo la Baibo Lotsogolela Munthu ku Ubatizo—Gawo 1

“Zikuonekelatu kuti ndinu kalata yocokela kwa Khristu yolembedwa ndi ifeyo kudzela mu utumiki wathu.”​—2 AKOR. 3:3.

NYIMBO 78 Phunzitsani Mau a Mulungu

ZIMENE TIKAMBILANE *

Zimakhala zokondweletsa cotani nanga kwa onse mu mpingo kuona wophunzila Baibo amene amam’konda akubatizika. (Onani ndime 1)

1. Kodi 2 Akorinto 3:1-3 ingatithandize bwanji kuona mwayi umene tili nawo wotsogoza phunzilo la Baibo lotsogolela ku ubatizo? (Onani cithunzi pacikuto.)

KODI mumamvela bwanji wophunzila Baibo wa mumpingo wanu akabatizika? Mosakaikila mumakondwela kwambili! (Mat. 28:19) Ndipo ngati ndimwe amene munali kuphunzila Baibo na wophunzila wa Yesu watsopano ameneyo, cimakhala cokondweletsa ngako kucitila umboni ubatizo wake! (1 Ates. 2:19, 20) Ophunzila obatizika atsopano amenewa ni ‘makalata ocitila umboni,’ kwa amene anali kuwaphunzitsa Baibo, komanso ku mpingo wonse.—Ŵelengani 2 Akorinto 3: 1-3.

2. (a) Kodi tifunika kudzifunsa funso lofunika liti, ndipo cifukwa ciani? (b) Kodi phunzilo la Baibo n’ciani? (Onani mawu am’munsi.)

2 N’zokondweletsa kwambili kuona kuti pazaka zinayi zapitazi, pa avaleji timacitila lipoti maphunzilo a Baibo * pafupi-fupi 10,000,000 mwezi uliwonse padziko lonse. Ndipo m’zaka zimenezi, pa avaleji, anthu opitila 280,000 anali kubatizika caka ciliconse monga Mboni za Yehova komanso ophunzila atsopano a Yesu Khristu. Kodi tingawathandize bwanji maphunzilo a Baibo amenewa ofika mamiliyoni kuti akabatizike? Yehova moleza mtima akupelekabe mwayi kwa anthu kuti akhale ophunzila a Khristu. Conco, tifunika kucita zonse zotheka kuti tiwathandize kupita patsogolo mwamsanga kuti akabatizike. Nthawi yotsalayi ni yocepa kwambili!—1 Akor. 7:29a; 1 Pet. 4:7.

3. Kodi tikambilane ciani m’nkhani ino zokhudza kutsogoza maphunzilo a Baibo?

3 Popeza kuti nchito yopanga ophunzila ifunika kugwilika mwamsanga, maofesi anthambi anapemphedwa kufufuza mmene tingathandizile maphunzilo athu a Baibo kupita patsogolo kuti akabatizike. M’nkhani ino komanso yotsatila, tidzaona zimene tingaphunzile kwa apainiya, amishonale, ndiponso oyang’anila madela amene ni aciyambakale. * (Miy. 11:14; 15:22) Iwo amafotokoza zimene aphunzitsi a Baibo na ophunzila awo angacite kuti phunzilo lawo lizikhala lopindulitsa. M’nkhani ino, tikambilane zinthu zisanu zimene wophunzila Baibo aliyense afunika kucita kuti apite patsogolo na kukabatizika.

MUZIPHUNZILA WIKI ILIYONSE

Pemphani wophunzila kuti mukhaleko pansi na kukambilana mfundo za m’Baibo (Onani ndime 4-6)

4. Kodi tiyenela kukumbukila ciani za phunzilo la Baibo lotsogoza coimilila?

4 Abale na alongo athu ambili amatsogoza maphunzilo a Baibo acoimilila. Ngakhale kuti ni poyambila pabwino kuti tikope cidwi ca munthu pa Baibo, makambilanowo amakhala acidule, ndipo mwina sangacitike wiki iliyonse. Pofuna kukulitsa cidwi, ofalitsa ena amapempha foni namba ya munthu, ndipo amam’tumila kapena kum’lembela meseji kuti akambilane naye mwacidule mfundo ya m’Malemba nthawi zonse asanapite kukaonana naye. Makambilano apanthawi amenewa angapitilize kwa miyezi popanda kukhala phunzilo la Baibo lopindulitsa. Kodi wophunzila Baibo angapitedi patsogolo n’kudzipatulila na kubatizika, ngati imeneyi ndiye nthawi yokha imene amathela pophunzila Mawu a Mulungu? Osati kwenikweni.

5. Malinga na Luka 14:27-33, kodi Yesu anagogomeza mfundo iti imene ingatithandize pa nchito yathu yopanga ophunzila?

5 Panthawi ina, Yesu anaseŵenzetsa fanizo pofotokoza zimene munthu angacite kuti akhale wophunzila wake. Iye anakamba za munthu wofuna kumanga nsanja, komanso za mfumu yofuna kupita ku nkhondo. Yesu anakamba kuti wofuna kumanga nsanjayo afunika ‘kukhala pansi coyamba na kuŵelengela ndalama zimene angawononge’ kuti atsilize kumanga nsanjayo. Anati mfumuyo nayonso ifunika ‘kukhala pansi coyamba ndi kuganiza mofatsa,’ kuti ione ngati asilikali ake angakwanitse kugonjetsa adani awo. (Ŵelengani Luka 14:27-33.) Yesu anadziŵa kuti munthu wofuna kukhala wophunzila wake, ayenela kumvetsetsa zoloŵetsedwamo. Pa cifukwa cimeneci, tiyenela kulimbikitsa anthu oyembekezeka kukhala ophunzila a Yesu kuti aziphunzila nafe Baibo wiki iliyonse. Kodi tingacite bwanji zimenezi?

6. Kodi tingacite ciani kuti tizitsogoza maphunzilo opita patsogolo?

6 Yambani mwa kutalikitsako makambilano anu potsogoza phunzilo la coimilila. Nthawi zonse mukapita kukaonana naye, m’malo mokambilana cabe mfundo imodzi, mwina mungakambilane naye mfundo ina yowonjezela ya m’Malemba. Ngati mwininyumba wazoloŵela makambilano aataliko amenewa, mungam’funse ngati pali malo amene mungakhaleko pansi kuti mupitilize makambilano anu. Zimene mwininyumba angakambe zidzaonetsa ngati ali na cidwi ceni-ceni cofuna kuphunzila Baibo. Ndiyeno m’kupita kwanthawi, pofuna kuti apite patsogolo mwamsanga, mungam’funse ngati angakonde kuti muziphunzila naye kaŵili pa wiki. Komabe, kuphunzila kamodzi kapena kaŵili cabe sikokwanila.

MUZIKONZEKELA PHUNZILO LILILONSE

Konzekelani bwino phunzilo lanu la Baibo, komanso onetsani wophunzila wanu mokonzekelela (Onani ndime 7-9)

7. Kodi mphunzitsi ayenela kulikonzekela motani phunzilo la Baibo lililonse?

7 Monga mphunzitsi, mufunika kulikonzekela bwino phunzilo la Baibo lililonse. Yambani mwa kuŵelenga nkhani yonse na malemba ake. Ndipo mvetsetsani mfundo zake zikulu-zikulu. Ganizilaninso za mutu wa nkhani, tumitu tung’ono tung’ono, mafunso osindikizidwa, malemba akuti “ŵelengani,” zithunzi, komanso mavidiyo alionse othandiza kumveketsa bwino nkhani imeneyo. Ndiyeno, muli na wophunzila wanu m’maganizo, ganizilani pasadakhale za mmene mudzafotokozela mfundozo mosavuta, komanso momveka bwino. Mukatelo, wophunzila wanu adzamvetsa mosavuta mfundozo na kuziseŵenzetsa. —Neh. 8:8; Miy. 15:28a.

8. Kodi mawu a mtumwi Paulo a pa Akolose 1:9, 10, atiphunzitsa ciani za kupemphelela maphunzilo athu a Baibo?

8 Pokonzekela, pemphelani kwa Yehova za wophunzila wanu na zosoŵa zake. M’pempheni kuti akuthandizeni kukaphunzitsa zocokela m’Baibo, mwa njila yom’fika pamtima wophunzila wanu. (Ŵelengani Akolose 1:9, 10.) Yesani kuganizila mfundo iliyonse imene ingakhale yovuta kwa wophunzila wanu kuimvetsa kapena kuivomeleza. Musaiŵale kuti colinga canu ni kum’thandiza kupita patsogolo mpaka kukabatizika.

9. Kodi mphunzitsi angathandize bwanji wophunzila wake kukonzekela phunzilo? Fotokozani.

9 Tikhulupilila kuti kucita phunzilo la Baibo kaŵili-kaŵili na wophunzila wanu, kudzam’thandiza kuyamikila zimene Yehova na Yesu aticitila, ndipo adzafuna kudziŵa zambili. (Mat. 5:3, 6) Kuti apindule mokwanila na zimene akuphunzila, wophunzilayo afunika kusumika maganizo pa zimene akuphunzila. Conco, m’gogomezeleni kuti azikonzekela phunzilo lililonse mwa kuliŵelenga pasadakhale, komanso kuona mmene angaseŵenzetsele mfundo za m’nkhaniyo. Kodi monga mphunzitsi mungam’thandize bwanji? Konzekelani naye phunzilo limodzi wophunzila wanu kuti mumuonetse mmene angacitile zimenezi. * M’fotokozeleni mmene angapezele mayankho pa mafunso osindikizidwa, komanso muonetseni mmene kuconga liwu kapena mawu ofunika kungam’thandizile kukumbukila yankho. Ndiyeno m’pempheni kuti ayankhe m’mawu ake-ake. Akamacita zimenezi, mudzadziŵa ngati akumvetsetsa zimene akuphunzila. Koma palinso cina cimene mungalimbikitse wophunzila wanu kucita.

M’PHUNZITSENI KUKAMBILANA NA YEHOVA TSIKU LILILONSE

Phunzitsani wophunzila Baibo wanu kumakambilana na Yehova (Onani ndime 10-11)

10. N’cifukwa ciani kuŵelenga Baibo tsiku na tsiku n’kofunika? Nanga cofunika n’ciani kuti wophunzila apindule na kuŵelenga Baibo?

10 Kuwonjezela pa kuphunzila wiki iliyonse na mphunzitsi wake, wophunzila angapindulenso ngati acita zina payekha tsiku lililonse. Iye afunika azikambilana na Yehova. Motani? Mwa kumvetsela kwa Yehova, komanso kukamba naye. Angamvetsele kwa Mulungu mwa kuŵelenga Baibo tsiku na tsiku. (Yos. 1:8; Sal. 1:1-3) Muonetseni mmene angaseŵenzetsele “Ndandanda ya Kuŵelenga Baibo” imene angaipulinte kucokela pa jw.org. * Koma kuti apindule kwambili na kuŵelenga Baibo kwake, m’limbikitseni kusinkha-sinkha pa zimene Baibo ikum’phunzitsa ponena za Yehova, na mmene angaseŵenzetsele zimenezo mu umoyo wake.—Mac. 17:11; Yak. 1:25.

11. Kodi wophunzila angadziŵe bwanji kupemphela moyenelela? Nanga n’cifukwa ciani afunika kumapemphela kwa Yehova kaŵili-kaŵili?

11 Limbikitsani wophunzila wanu kuti azikamba na Yehova mwa kupemphela tsiku lililonse. Muzipeleka mapemphelo okhudza mtima kuciyambi na kumapeto kwa phunzilo. Komanso, muzipemphela naye limodzi na kum’chula m’pemphelo. Pamene amvetsela mapemphelo anu, iye adzaphunzila kupemphela mocokela pansi pa mtima na kupeleka mapemphelo ake kwa Yehova Mulungu, kupitila m’dzina la Yesu Khristu. (Mat. 6:9; Yoh. 15:16) Tangoganizani mmene kuŵelenga Baibo tsiku na tsiku (ndiko kumvetsela kwa Yehova), komanso kupemphela kwa iye (ndiko kukamba na Yehova) kungathandizile wophunzila wanu kumuyandikila kwambili Mulungu! (Yak. 4:8) Kucita zimenezi kudzathandiza wophunzila wanu kupita patsogolo mpaka kufika podzipatulila na kubatizika.

M’THANDIZENI KUPALANA UBWENZI NA YEHOVA

12. Kodi mphunzitsi angam’thandize bwanji wophunzila wake kupalana ubwenzi na Yehova?

12 Mukamaphunzila Baibo na wophunzila wanu, zimene akuphunzila zizim’fika pamtima, osati cabe kum’kopa maganizo. Cifukwa ciani? Mtima wathu, umene uphatikizapo zolakalaka zathu, komanso mmene timvelela, umatilimbikitsa kucitapo kanthu. Yesu anali mphunzitsi waluso amene anali kukopa maganizo a anthu. Koma anthu anali kum’tsatila cifukwa analinso kuwafika pamtima. (Luka 24:15, 27, 32) Wophunzila wanu afunika aziona Yehova kukhala weniweni, amene angapalane naye ubwenzi, ndipo azimuona kukhala Take wake, Mulungu wake, komanso Bwenzi lake. (Sal. 25:4, 5) Pamene mukuphunzila Baibo, gogomezani za makhalidwe abwino a Mulungu wathu. (Eks. 34:5, 6; 1 Pet. 5:6, 7) Pankhani iliyonse imene mukuphunzila, gogomezani za makhalidwe a Yehova. Thandizani wophunzila wanu kuyamikila makhalidwe abwino a Yehova monga cikondi, kukoma mtima, na cifundo. Yesu anakamba kuti “lamulo lalikulu kwambili komanso loyamba,” n’lakuti “uzikonda Yehova Mulungu wako.” (Mat. 22:37, 38) Thandizani wophunzila wanu kukhala na cikondi cozama pa Mulungu.

13. Pelekani citsanzo ca mmene mungathandizile wophunzila kum’dziŵa bwino Yehova.

13 Pokambilana na wophunzila wanu, muzionetsa kuti mumam’konda kwambili Yehova. Zimenezi zidzathandiza wophunzila wanu kuzindikila kuti nayenso afunika kulimbitsa ubwenzi wake na Mulungu. (Sal. 73:28) Mwacitsanzo, kodi pali mawu m’cofalitsa cophunzililamo kapena m’lemba, amene aonetsa makhalidwe a Yehova monga cikondi, nzelu, cilungamo, kapena mphamvu, amene amakukhudzani mtima? Ngati n’conco, muuzeni wophunzila wanu kuti cimeneco, n’cimodzi mwa zifukwa zambili zimene mumam’kondela Atate wathu wakumwamba. Koma palinso cina cimene wophunzila Baibo afunika kucita kuti apite patsogolo na kubatizika.

M’LIMBIKITSENI KUMAPEZEKA PA MISONKHANO YAMPINGO

Mwamsanga limbikitsani wophunzila wanu kuyamba kupezeka pa misonkhano (Onani ndime 14-15)

14. Kodi Aheberi 10:24, 25, imatiuza ciani za misonkhano yampingo imene ingathandize wophunzila Baibo kupita patsogolo?

14 Tonsefe timafuna kuti ophunzila athu apite patsogolo kuti akabatizike. Njila imodzi imene tingawathandizile, ni mwa kuwalimbikitsa kumapezeka pa misonkhano yampingo. Aphunzitsi aluso amakamba kuti ophunzila amene amafulumila kuyamba kusonkhana, ndiwo amapita patsogolo mwamsanga. (Sal. 111:1) Aphunzitsi ena amauza ophunzila awo kuti zimene akuphunzila ni hafu cabe ya maphunzilo a Baibo, hafu ina angailandile ku misonkhano ya mpingo. Ŵelengani Aheberi 10:24, 25 na wophunzila wanu, na kum’fotokozela mapindu amene angapeze akamapezeka pa misonkhano. M’tambitseni vidiyo yakuti N’ciani Cimacitika ku Nyumba ya Ufumu? * Thandizani wophunzila wanu kuona kuti kupezeka ku misonkhano wiki iliyonse, ni mbali yofunika kwambili mu umoyo wake.

15. Tingacite ciani kuti tilimbikitse wophunzila wathu kumapezeka pa misonkhano mokhazikika?

15 Kodi mungacite ciani ngati wophunzila wanu sanayambe kupezeka pa misonkhano, kapena amasonkhana mwa apo na apo? Mwacimwemwe, muuzenkoni zimene munaphunzila pa misonkhano yaposacedwa. Izi zingakhale zolimbikitsa kuposa kungom’pempha kuti akapezeke ku misonkhano. M’patseni Nsanja ya Mlonda kapena kabuku ka Umoyo na Utumiki kamene mudzaphunzila pa misonkhano. Muonetseni zimene zidzaphunzilidwa pa msonkhano wotsatila, ndipo m’funseni mbali imene wacita nayo cidwi. Zimene wophuzila wanu adzaona pa msonkhano wake woyamba, zidzaposa msonkhano uliwonse wa cipembedzo umene anapezekapo. (1 Akor. 14:24, 25) Iye adzapeza abale na alongo amene ni zitsanzo zabwino kwa iye, ndipo angam’thandizenso kupita patsogolo kuti akabatizike.

16. Kodi cofunika n’ciani kuti tizitsogoza maphunzilo a Baibo otsogolela ku ubatizo? Nanga tidzaphunzila ciani m’nkhani yotsatila?

16 Kodi tingatsogoze bwanji maphunzilo a Baibo otsogolela ku ubatizo? Tingathandize wophunzila Baibo kuona kufunika kwa phunzilo la Baibo, mwa kum’limbikitsa kuti tiziphunzila naye wiki na wiki, komanso kuti azikonzekela phunzilo lililonse. Tingam’limbikitsenso kumakambilana na Yehova tsiku lililonse kuti akhale naye pa ubwenzi. Cina, tiyenela kum’limbikitsa kuti azipezeka pa misonkhano yampingo. (Onani bokosi lakuti “ Zimene Wophunzila Afunika Kucita Kuti Apite Patsogolo na Kukabatizika.”) Komabe, monga mmene nkhani yotsatila idzafotokozela, palinso zinthu zina zisanu zimene aphunzitsi a Baibo angacite kuti athandize ophunzila awo kukabatizika.

NYIMBO 76 Kodi Mumamvela Bwanji?

^ ndime 5 Kuphunzitsa munthu kumatanthauza kum’thandiza “kuganiza, kumvela, kapena kucita zinthu m’njila yatsopano kapena yosiyanako.” Lemba lathu la caka ca 2020 la Mateyu 28:19, lakhala likutikumbutsa kufunika kophunzila Baibo ndi anthu, komanso kuwathandiza mmene angakhalile ophunzila a Yesu Khristu obatizika. M’nkhani ino komanso yotsatila, tidzaphunzila mmene tinganolele maluso athu panchito yofunika kwambili imeneyi.

^ ndime 2 KUFOTOKOZELA MAWU ENA: Ngati mumakambilana na munthu za m’Baibo nthawi zonse, mwa mafunso na mayankho, ndiye kuti mukutsogoza phunzilo la Baibo. Mungacitile lipoti phunzilo ngati mwalitsogoza maulendo aŵili, kucokela pamene munamuonetsa mmene phunzilo limacitikila, ndipo muona kuti phunzilo limenelo lidzapitiliza.

^ ndime 3 M’nkhani zimenezi mulinso mfundo zocokela m’nkhani zakuti “Kucititsa Maphunzilo a Baibulo Opita Patsogolo,” za mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa July 2004 mpaka May 2005.

^ ndime 9 Tambani vidiyo ya mamineti anayi yakuti, Kuthandiza Maphunzilo Athu a Baibo Kukonzekela. Pa JW Library®, yendani pa MEDIA > OUR MEETINGS AND MINISTRY > IMPROVING OUR SKILLS.

^ ndime 10 Yendani pa LAIBULALI > MABUKU NA MABULOSHA.

^ ndime 14 Pa JW Library®, yendani pa MEDIA > OUR MEETINGS AND MINISTRY > TOOLS FOR THE MINISTRY.