Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 42

Mmene Tingatsogozele Phunzilo la Baibo Lotsogolela Munthu ku Ubatizo—Gawo 2

Mmene Tingatsogozele Phunzilo la Baibo Lotsogolela Munthu ku Ubatizo—Gawo 2

“Nthawi zonse uzisamala ndi zimene umacita komanso zimene umaphunzitsa.”—1 TIM. 4:16.

NYIMBO 77 Kuwala m’Dziko la Mdima

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Tidziŵa bwanji kuti nchito yopanga ophunzila ni yopulumutsa miyoyo?

NCHITO yopanga ophunzila ni yopulumutsa miyoyo. Tidziŵa bwanji? Yesu atapeleka lamulo lopezeka pa Mateyu 28:19, 20 anati: “Pitani mukaphunzitse anthu . . . kuti akhale ophunzila . . . Muziwabatiza.” Kodi ubatizo ni wofunika motani? Ni ciyenelezo kwa onse ofuna cipulumutso. Munthu amene afuna kubatizika, ayenela kukhulupilila kuti cipulumutso n’cotheka kokha cifukwa Yesu anapeleka moyo wake monga nsembe na kuukitsidwa. Ndiye cifukwa cake mtumwi Petulo anauza Akhristu anzake kuti: ‘Ubatizo, ukukupulumutsani mwa kuukitsidwa kwa Yesu Khristu.’ (1 Pet. 3:21) Conco wophunzila watsopano akabatizika, amakhala na ciyembekezo ca moyo wosatha.

2. Kodi 2 Timoteyo 4:1, 2 ionetsa kuti tiyenela kukhala aphunzitsi otani?

2 Kuti tipange ophunzila, tifunika kukulitsa “luso la kuphunzitsa.” (Ŵelengani 2 Timoteyo 4:1, 2.) Cifukwa ciani? Cifukwa Yesu anatilamula kuti: “Pitani [mukapange] . . . ophunzila. . . , ndi kuwaphunzitsa.” Mtumwi Paulo anati “pitiliza kucita” nchitoyi, “cifukwa ukatelo udzadzipulumutsa wekha komanso anthu okumvela.” Ndiye cifukwa cake Paulo anati: “Nthawi zonse uzisamala ndi . . . zimene umaphunzitsa.” (1 Tim. 4:16) Popeza nchito yopanga ophunzila imaphatikizapo kuphunzitsa, kaphunzitsidwe kathu kayenela kukhala kaluso.

3. Kodi m’nkhani ino tikambilane ciani pa nkhani ya kutsogoza maphunzilo a Baibo?

3 Timaphunzitsa anthu mamiliyoni mfundo za coonadi ca m’Baibo. Koma monga tinaonela m’nkhani yapita, tifunika kudziŵa zimene tingacite powathandiza kukhala ophunzila a Yesu Khristu obatizika. M’nkhani ino, tikambilane zinthu zinanso zisanu zimene mphunzitsi aliyense afunika kucita pothandiza wophunzila wake kupita patsogolo kuti akabatizike.

LOLANI KUTI BAIBO IZIPHUNZITSA MUNTHU

Pemphani mphunzitsi waluso kuti akuthandizeni kunola luso lanu mwa kulola Baibo kuphunzitsa munthu (Onani ndime 4-6) *

4. N’cifukwa ciani mphunzitsi afunika kukhala wodziletsa potsogoza phunzilo la Baibo? (Onaninso mawu am’munsi.)

4 Timakonda zimene timaphunzitsa kucokela m’Mawu a Mulungu. Mwa ici, tingamafune kumakambapo kwambili pa zimene tikuphunzitsa. Komabe, kaya ni potsogoza Nsanja ya Mlonda, Phunzilo la Baibo la Mpingo, kapena phunzilo la Baibo lapanyumba, wotsogoza sayenela kukambapo kwambili. Ayenela kulola Baibo kuti ndiyo iziphunzitsa. Kuti mphunzitsi acite zimenezi, ayenela kukhala wodziletsa kuti apewe kumafotokoza zonse zimene akudziŵa pa lemba kapena nkhani iliyonse. * (Yoh. 16:12) Linganizani cidziŵitso ca m’Baibo cimene munali naco pamene munabatizika, na cimene muli naco lelo. Mwacidziŵikile, panthawiyo munali kungodziŵa ziphunzitso zoyambilila za m’Baibo basi. (Aheb. 6:1) Koma lomba muli na cidziŵitso coculuka, ndipo zakutengelani zaka kuti mukhale naco. Conco, musayese kukhutulila wophunzila wanu watsopano zonse panthawi imodzi.

5. (a) Malinga na 1 Atesalonika 2:13, timafuna kuti wophunzila wathu azimvetsa ciani tikamaphunzila naye? (b) Nanga tingam’limbikitse bwanji wophunzila wathu kuti azifotokoza zimene akuphunzila?

5 Timafuna kuti ophunzila athu azimvetsa mfundo yakuti zimene akuphunzilazo n’zocokela m’Mawu a Mulungu ouzilidwa. (Ŵelengani 1 Atesalonika 2:13.) Tingacite bwanji zimenezo? Limbikitsani wophunzila wanu kuti azifotokozapo pa zimene akuphunzila. M’malo mofotokozela wophunzila wanu mfundo za coonadi nthawi zonse, m’pempheni kuti akufokozelenkoni zina mwa izo. Thandizani wophunzila wanu kuona mmene angaseŵenzetsele mfundo za m’Mawu a Mulungu. M’funseni mafunso otsogolela ku yankho, komanso mafunso ofuna kudziŵa maganizo ake pa malemba amene akuŵelenga. (Luka 10:25-28) Mwacitsanzo, mungam’funse kuti: “Kodi lembali lakuthandizani kuona khalidwe liti la Yehova?” “Kodi mfundo iyi ya m’Baibo ingakuthandizeni bwanji?” “Kodi mungatipo bwanji pa zimene taphunzilazi?” (Miy. 20:5) Cofunika kwambili, si kuculuka kwa zimene munthu waphunzila, koma kuzikonda na kuzigwilitsila nchito.

6. Kodi kutengako mphunzitsi waluso ku phunzilo lathu la Baibo kuli na ubwino wanji?

6 Pokatsogoza phunzilo la Baibo, kodi mumatengako ofalitsa ena aluso la kuphunzitsa? Mukatengako wofalitsa wotelo, m’funseni za mmene mwatsogozela phunzilo, komanso mmene mwalolela Baibo kuphunzitsa lokha. Kuti munole luso lanu la kuphunzitsa, mufunika kukhala wodzicepetsa. (Yelekezelani na Machitidwe 18:24-26.) Pambuyo pake, funsani wofalitsa walusoyo ngati aona kuti wophunzilayo akumvetsa zimene akuphunzila. Mungapemphenso wofalitsa ameneyo kukakutsogozelani phunzilolo mukadzacokapo kwa wiki imodzi kapena angapo. Izi zidzathandiza kuti phunzilo lisamacitike modukiza-dukiza, ndipo zidzam’thandiza kuona kufunika kwa phunzilo lake. Musamakhale na maganizo akuti ili ni phunzilo “langa,” palibe aliyense ayenela kulitsogoza. Paja ngakhale imwe mufuna kuti wophunzila wanu apite patsogolo m’coonadi.

PHUNZITSANI MWAUMOYO KOMANSO MWACIDALILO

Pothandiza wophunzila wanu kumvetsa mmene angaseŵenzetsele mfundo za m’Baibo, musimbilenkoni za anthu amene anapanga masinthidwe pa umoyo wawo (Onani ndime 7-9) *

7. N’ciani cingathandize wophunzila wanu kuyamba kukonda zimene akuphunzila?

7 Wophunzila wanu afunika aziona kuti mukukamba mwaumoyo komanso mwacidalilo pophunzitsa mfundo za coonadi ca m’Baibo. (1 Ates. 1:5) Kucita izi kudzam’thandiza kukonda zimene akuphunzila. Ngati n’koyenela, m’simbilenkoni mmene mfundo za m’Baibo zakuthandizilani pa umoyo wanu. Pamenepo adzaona kuti m’Baibo muli malangizo amene angam’thandize nayenso.

8. Kodi mungaphatikizeponso ciani pa phunzilo la Baibo, ndipo zingam’thandize bwanji wophunzila wanu?

8 Pophunzila naye Baibo, m’simbilenkoni wophunzila wanu za anthu amene anakumana na zopinga zolingana na zake ndipo anazigonjetsa. Mungapiteko na munthu wa mu mpingo wanu, amene citsanzo cake cingathandize wophunzila wanu. Apo ayi, mungam’pezeleko zitsanzo zolimbikitsa za pa jw.org, m’nkhani zakuti “Baibulo Limasintha Anthu.” * Nkhani na mavidiyo amenewo adzathandiza wophunzila wanu kuona kuti n’cinthu canzelu kuseŵenzetsa mfundo za m’Baibo pa umoyo wake

9. Mungam’limbikitse bwanji wophunzila wanu kumauzako a m’banja lake na mabwenzi ake zimene amaphunzila?

9 Ngati wophunzilayo ali pabanja, kodi mnzake wa m’cikwati nayenso amaphunzila? Ngati ayi, m’pempheni kuti azikhalapo pa phunzilo. Llimbikitsani wophunzila wanu kuti aziuzako a m’banja lake na mabwenzi ake zimene amaphunzila. (Yoh. 1:40-45) Mungacite bwanji zimenezi? Mungangom’funsa kuti: “Kodi mfundo imeneyi mungaifotokoze bwanji kwa a m’banja lanu?” Kapena kuti, “Kodi mungaseŵenzetse lemba liti kuthandiza mnzanu kuimvetsa mfundoyi?” Mwakutelo, mudzathandiza wophunzila wanu kukhala mphunzitsi. Ndiyeno akadzayenelela, adzayamba kupita mu ulaliki monga wofalitsa wosabatizika. Mungam’funse ngati akudziŵako aliyense amene angafune kuphunzila Baibo. Ngati alipo, kambilanani naye mwamsanga munthuyo na kum’pempha kuti muziphunzila naye. M’tambitseni vidiyo yakuti, Kodi Phunzilo la Baibulo Limacitika Bwanji? *

LIMBIKITSANI WOPHUNZILA WANU KUPEZA MABWENZI MU MPINGO

Limbikitsani wophunzila wanu kupeza mabwenzi mu mpingo (Onani ndime 10-11) *

10. Malinga na 1 Atesalonika 2:7, 8, kodi mphunzitsi angatengele bwanji citsanzo ca Paulo?

10 Monga aphunzitsi, muzikhala na cidwi ceni-ceni pa ophunzila anu. Aoneni monga abale na alongo anu am’tsogolo. (Ŵelengani 1 Atesalonika 2:7, 8.) Si capafupi kwa iwo kusiya mabwenzi awo akudziko na kupanga masinthidwe ofunikila kuti atumikile Yehova. Tiyenela kuwathandiza kupeza mabwenzi eni-eni mu mpingo. Khalani bwenzi kwa wophunzila wanu mwa kumacezako naye pa nthawi zina pamene simukuphunzila naye. Mungam’tumileko foni, meseji, kapena kukamuonako, poonetsa kuti mumam’konda.

11. Kodi timafuna kuti ophunzila athu apeze ciani mu mpingo, ndipo cifukwa ciani?

11 Paja amati: “Kulela mwana n’kwa tonse.” Ifenso tinganene kuti: “Kupanga ophunzila n’kwa mpingo wonse.” Ndiye cifukwa cake aphunzitsi abwino a Baibo amadziŵikitsa ophunzila awo kwa ena mu mpingo amene angakhale zitsanzo zabwino kwa iwo. Pamenepo ophunzilawo angayambe kuyanjana na anthu a Mulungu amene angawalimbikitse mwauzimu, kapenanso akakumana na mavuto. Timafuna kuti wophunzila aliyense azimva kuti ni wofunika mu mpingo wathu komanso m’banja lathu lauzimu. Timafunanso kuti akopeke na cikondi ca ubale wathu wa padziko lonse. Zikatelo, cidzakhala capafupi kwa iye kudula mayanjano ake na anthu amene sangam’thandize kukonda Yehova. (Miy. 13:20) Ngati mabwenzi ake akale angayambe kumusala kapena kum’pewa, sangade nkhawa podziŵa kuti adzapeza mabwenzi eni-eni m’gulu la Yehova.—Maliko 10:29, 30; 1 Pet. 4:4.

MUZIKAMBAPO ZA COLINGA CA KUDZIPATULILA NA UBATIZO

Sitepu na sitepu, wophunzila Baibo woona mtima angakwanilitse colinga cake ca kubatizika! (Onani ndime 12-13)

12. N’cifukwa ciani tiyenela kumakambilana na wophunzila wathu za kudzipatulila na ubatizo?

12 Muzikambilana naye za kufunika kodzipatulila na kubatizika. Paja colinga cathu potsogoza phunzilo la Baibo n’kuthandiza munthu kukhala wophunzila wobatizika. Mukaphunzila naye Baibo mokhazikika kwa miyezi ingapo, maka-maka akayamba kupezeka ku misonkhano, m’fotokozeleni colinga ca phunzilo lanu. Wophunzilayo ayenela kumvetsa kuti colinga ni kum’thandiza kuti akayambe kutumikila Yehova monga Mboni yake.

13. Kodi wophunzila amatenga masitepu ati kuti akabatizike?

13 Sitepu na sitepu, wophunzila Baibo woona mtima angakwanilitse colinga cake ca kubatizika! Coyamba, wophunzilayo amafika pom’dziŵa Yehova, kum’konda na kukhulupilila mwa iye. (Yoh. 3:16; 17:3) Kenako amayamba kupanga ubwenzi wolimba na Yehova, na kugwilizana kwambili na mpingo. (Aheb. 10:24, 25; Yak. 4:8) Pothela pake wophunzilayo amalekelatu makhalidwe onse oipa, na kulapa macimo ake. (Mac. 3:19) Panthawiyo, cikhulupililo cake cimam’limbikitsa kuuzako ena mfundo za coonadi. (2 Akor. 4:13) M’kupita kwa nthawi amadzipatulila kwa Yehova, pambuyo pake n’kubatizika kuonetsa umboni wakuti anadzipatulila. (1 Pet. 3:21; 4:2) Ndipo limakhala tsiku lokondweletsa cotani nanga kwa tonsefe! Conco, pamene wophunzila wanu akutenga sitepu iliyonse yotsogolela ku colinga cake, muzimuyamikila mocokela pansi pamtima, na kum’limbikitsa kupitabe patsogolo.

NTHAWI NA NTHAWI MUZIPENDA MMENE WOPHUNZILA WANU AKUPITILA PATSOGOLO

14. Kodi mphunzitsi angam’pende bwanji wophunzila wake kuona ngati akupita patsogolo kapena ayi?

14 Tifunika kukhala oleza mtima pothandiza wophunzila kupita patsogolo kuti akabatizike. Koma pa nthawi inayake, tifunika kudziŵa ngati akufunadi kutumikila Yehova Mulungu. Kodi wophunzila amaonetsa kuti akuyesetsa kumvela malamulo a Yesu? Kapena kodi akungofuna kudziŵa zinthu zocititsa cidwi za m’Baibo?

15. Kodi ni zizindikilo za kupita patsogozo zotani zimene mphunzitsi afunika kuyang’ana mwa wophunzila wake?

15 Nthawi na nthawi, muziona ngati wophunzilayo akupita patsogolo. Mwacitsanzo, kodi zokamba zake zimaonetsa kuti amam’kondadi Yehova? Kodi amapemphela kwa Yehova? (Sal. 116:1, 2) Kodi amakonda kuŵelenga Baibo? (Sal. 119:97) Kodi amasonkhana mokhazikika? (Sal. 22:22) Kodi wapangako masinthidwe ofunikila mu umoyo wake? (Sal. 119:112) Kodi anayamba kuuzako a m’banja lake na mabwenzi ake zimene amaphunzila? (Sal. 9:1) Cofunika koposa, kodi akufunadi kukhala Mboni ya Yehova? (Sal. 40:8) Ngati wophunzilayo sakupita patsogolo pa iliyonse ya mbali zimenezi, yesani kum’funsa cifukwa cake. Ndiyeno kambilanani naye mokoma mtima koma mosam’pita m’mbali. *

16. N’ciani cingaonetse kuti ni bwino kuleka kuphunzila na munthu?

16 Pakapita nthawi, onani ngati mufunikila kupitiliza kuphunzila na munthuyo. Dzifunseni kuti: ‘Kodi wophunzilayu amalephela kukonzekela phunzilo? Kodi alibe cidwi cofuna kupezeka ku misonkhano? Kodi akali na makhalidwe oipa? Kodi akali mu cipembedzo conyenga? Ngati yankho ni inde, kupitiliza kuphunzila na munthuyo kungakhale ngati kuphunzitsa kunyaya munthu amene amadana n’kuloŵa pamadzi! Ngati wophunzila saonetsa kuyamikila zimene akuphunzila, ndiponso safuna kusintha, n’kwanji kupitiliza naye?

17. Malinga na 1 Timoteyo 4:16, kodi aphunzitsi onse a Baibo afunika kucita ciani?

17 Udindo wathu wopanga ophunzila sitiutengela kucala ayi. Timafuna kuthandiza ophunzila athu kupita patsogolo kuti akabatizike. Ndiye cifukwa cake timalola Baibo kuphunzitsa yokha, ndipo timafuna kuphunzitsa mwaumoyo komanso mwacidalilo. Tidzalimbikitsa wophunzila wathu kupanga mabwenzi mu mpingo. Cina, tidzagogomeza colinga codzipatulila na kubatizika. Komanso nthawi na nthawi, tizipenda mmene wophunzila wathu akupitila patsogolo. (Onani bokosi lakuti “ Zimene Aphunzitsi Afunika Kucita Kuti Atsogolele Ophunzila Awo ku Ubatizo.”) Kwa ife ni mwayi wosaneneka, kutengako mbali m’nchito yopulumutsa miyoyo imeneyi! Tiyeni ticite zonse zotheka, kuti tizitsogoza maphunzilo a Baibo otsogolela ku ubatizo.

NYIMBO 79 Aphunzitseni Kucilimika

^ ndime 5 Tikamatsogoza maphunzilo a Baibo, timakhala na mwayi wothandiza anthu kudziŵa kuti Yehova afuna kuti iwo asinthe kaganizidwe kawo, mmene amamvelela, komanso kacitidwe kawo ka zinthu. Nkhani ino ipitiliza kufotokoza mmene tinganolele luso lathu la kuphunzitsa.

^ ndime 4 Onani nkhani yakuti “Zimene Tiyenela Kupewa Pocititsa Phunzilo la Baibulo” m’kabuku ka Umoyo na Utumiki ka September 2016.

^ ndime 8 Pitani pa LAIBULALI > MAGAZINI.

^ ndime 9 Pa JW Library®, pitani pa MEDIA > OUR MEETINGS AND MINISTRY > TOOLS FOR THE MINISTRY.

^ ndime 15 Onani nkhani yakuti, “Kukonda Yehova na Kum’yamikila Kudzakusonkhezelani Kubatizika,” komanso yakuti “Kodi Ndimwe Wokonzeka Kubatizika?” mu Nsanja ya Mlonda ya March 2020.

^ ndime 77 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Pambuyo potsogoza phunzilo la Baibo, mlongo amene ni ciyambakale akuthandiza mlongo amene watsogoza phunzilo, mmene angapewele kukambapo kwambili pophunzitsa.

^ ndime 79 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Paphunzilo la Baibo, wophunzila aphunzilapo mmene angakhalile mkazi wabwino. Pambuyo pake, auzako mwamuna wake zimene waphunzila.

^ ndime 81 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Wophunzila na mwamuna wake akusangalala na maceza kunyumba kwa mmodzi wa mabwenzi ake amene anadziŵana ku Nyumba ya Ufumu.