Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

1921—Zaka 100 Zapitazo

1921—Zaka 100 Zapitazo

MAGAZINI ya Nsanja ya Mlonda ya January 1, 1921, inali na funso lopita kwa oŵelenga lakuti: “Conco, tili na nchito yanji patsogolo pathu caka cino?” Poyankha funsoli, inagwila mawu lemba la Yesaya 61:1, 2, imene inawakumbutsa za nchito yawo yolalikila. Lembali limati: “Yehova wandidzoza kuti ndikanene uthenga wabwino kwa anthu ofatsa . . . kuti ndikalengeze za caka ca Yehova cokomela anthu mtima, ndi za tsiku lobwezela la Mulungu wathu.”

ALALIKI OLIMBA MTIMA

Kuti akwanilitse nchito yawo, Ophunzila Baibo anafunika kukhala olimba mtima. Iwo anayenela kulengeza “uthenga wabwino” kwa anthu ofatsa, komanso za “tsiku lobwezela” anthu oipa.

M’bale J. H. Hoskin, wa ku Canada, analalikila molimba mtima olo kuti anali kutsutsidwa. Mu 1921, iye anakumana na m’busa wina wacipembedzo. M’bale Hoskin anayambitsa makambilano mwa kunena kuti: “Tikambilane mwamtendele nkhani za m’Baibo. Koma tikalephela kugwilizana, makambilano athu tiwathetsenso mwamtendele.” Koma zimene anagwilizana sizinacitike. M’bale Hoskin anati: “Titakambitsilana kwa mphindi zocepa, [m’busayo] anamenya pa citseko mwamphamvu cakuti n’naona monga galasi ya pa citsekopo idzagwa n’kupwanyika.”

Mwaukali m’busayo anati, “N’cifukwa ciani simulalikila anthu amene si Akhristu?” M’bale Hoskin anangokhala cete, koma atasiyana na m’busayo, mu mtima anati, ‘M’busayu akucita zinthu monga si Mkhristu!’

Tsiku lotsatila, pamene m’busayo anali kulalikila m’chalichi, anakamba zoipa zokhudza m’bale Hoskin. M’baleyu anati: “M’busayo anauza anthu ake kuti n’nali kulankhula mabodza a mkunkhuniza, komanso kuti n’nayenela kuphedwa. M’bale wathu sanabwelele m’mbuyo, koma anapitiliza kulalikila anthu ambili. Iye anati: “N’nali kusangalala kulalikila kumeneko. Anthu ena anafika pokamba kuti, ‘Tidziŵa kuti ndinu munthu wa Mulungu!’ Cina, iwo anadzipeleka kuti azinipatsa zofunikila pa umoyo.”

PHUNZILO LAUMWINI KOMANSO LA BANJA

Pofuna kuthandiza anthu kumvetsa Baibo, Ophunzila Baibo anali kukonza mafunso na mayankho ake, m’magazini imene tsopano imachedwa Galamuka! M’magazini imeneyo munali mafunso a m’Baibo okonzedwela acicepele, amene makolo anali kukambilana na ana awo. Makolowo anali kufunsa ana awo mafunsowo, na kuwathandiza kupeza mayankho m’Baibo. Mafunso ena monga lakuti, “Kodi m’Baibo muli mabuku angati?,” anali kuphunzitsa mfundo zosavuta za m’Baibo. Funso lina linali lakuti, “Kodi Mkhristu woona aliyense ayenela kuyembekezela cizunzo?” Funsoli linakonzekeletsa acicepele kukhala alaliki olimba mtima.

Panalinso mafunso ena na mayankho ake, okonzedwela aja amene anali na cidziŵitso cokulilapo ca m’Baibo. Mayankhowo anali kupezeka m’buku la Cizungu lakuti, Studies in the Scriptures voliyumu yoyamba. Anthu masauzande ambili anapindula na pulogilamu imeneyi. Koma m’magazini ya The Golden Age ya December 21, 1921, munali cilengezo cakuti pulogilamu imeneyi yatha. N’cifukwa ciani panakhala kusintha?

BUKU LATSOPANO

Buku la Zeze wa Mulungu

Makadi oonetsa mbali yoŵelenga

Makadi okhala na mafunso

Amene anali kutsogolela anaona kuti maphunzilo a Baibo atsopano, afunika kuphunzila coonadi mwadongosolo. Conco, mu November 1921, buku lakuti Zeze wa Mulungu linatulutsidwa. Anthu acidwi amene analandila bukuli, naonso analembedwa kuti ayambe kucita maphunzilo a Baibo pa okha poseŵenzetsa bukuli. Maphunzilo amenewo, anathandiza anthu kudziŵa colinga ca Mulungu cakuti adzapatsa anthu moyo wosatha. Kodi anali kucitika motani?

Wophunzila Baibo akalandila bukulo, anali kupatsidwa kakhadi koonetsa masamba amene ayenela kuŵelenga. Mlungu wotsatila, anali kupatsidwa khadi yokhala na mafunso ozikidwa pa mbali imene anali kuŵelenga. Khadiyo inali kukhalanso na mbali imene iye adzaŵelenge mlungu wotsatila.

Mlungu uliwonse kwa milungu 12, wophunzila anali kulandila khadi yatsopano kucokela ku mpingo. Kambili, amene anali kutumiza makadiwo anali okalamba, kapena aja amene sanali kukwanitsa kulalikila nyumba na nyumba. Mwacitsanzo, mlongo Anna K. Gardner, wa ku Millvale, Pennsylvania, U.S.A., anati: “Buku la Zeze wa Mulungu litatulutsidwa, mkulu wanga Thayle, amene sanali kukwanitsa kuyenda anakhala na nchito yaikulu yotumiza makadi a mafunso mlungu uliwonse.” Munthu akatsiliza maphunzilowo, wina mu mpingo anali kupita kwa iye kukam’thandiza kuphunzila zowonjezeleka za m’Baibo.

Mlongo Thayle Gardner pa njinga ya olemala

NCHITO YOFUNIKA KUIGWILA

Kumapeto kwa caka, M’bale J. F. Rutherford anatumiza kalata ku mipingo. Iye anati “nchito yolalikila za Ufumu yayenda bwino kwambili caka cino kuposa zaka za m’mbuyomu.” Anakambanso kuti: “Koma pali nchito yaikulu yofunika kuigwila. Limbikitsani ena kuti agwile nafe nchito yabwino ngako imeneyi.” Ophunzila Baibo anamvela malangizo amenewa. Conco, mu 1922, iwo analengeza uthenga wa Ufumu mopanda mantha kuposa kale lonse.