Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Konzaninso Ubwenzi Wanu na Yehova

Konzaninso Ubwenzi Wanu na Yehova

CAKA ciliconse, nkhosa zambili zamtengo wapatali zimabwezeletsedwa mu mpingo wacikhristu. Tangoganizilani cisangalalo cacikulu cimene cimakhalako kumwamba munthu mmodzi akabwelela! (Luka 15:7, 10) Ngati munabwezeletsedwa mu mpingo, dziŵani kuti Yesu, angelo, komanso Yehova iye mwini, ni okondwela ngako kukuonani kuti mwanyamukanso na kuima kumbali ya coonadi. Komabe, pamene mukonza ubwenzi wanu na Yehova, mungakumane na zopinga. Kodi zina mwa zopingazo n’ziti? Nanga n’ciani cingakuthandizeni kuzigonjetsa?

KODI PAMAKHALA ZOPINGA ZOTANI?

Ambili amakhala na maganizo olefula pambuyo pobwelela mu mpingo. Mwina mungamvetse mmene Mfumu Davide anamvelela. Ngakhale pambuyo pokhululukidwa macimo ake, iye anati: “Zolakwa zanga zandikulila.” (Sal. 40:12; 65:3) Munthu akabwelela kwa Yehova, angakhalebe na maganizo odziimba mlandu, kapena kukhala wamanyazi kwa zaka ndithu. Isabelle, amene anali wocotsedwa kwa zaka zoposa 20, * anati: “Cinali covuta kwambili kwa ine kukhulupilila kuti Yehova anganikhululukile.” Mukalefuka, mungafooke mwauzimu. (Miy. 24:10) Conco, musalole zimenezi kukucitikilani.

Ena amaopa kuti sadzakwanitsa kucita zonse zofunikila kuti abwezeletsecifukwa ca kaamba ka cifukwa ndaŵa ubale wawo na Yehova. Antoine atabwezeletsedwa, anati: “N’nali kuona kuti n’naiŵala zinthu zambili zimene n’nali kucita nili Mboni.” Pa cifukwa cimeneci, ena amazengeleza kutengako mbali mokwanila pa zauzimu.

Mwacitsanzo, munthu amene nyumba yake yawonongeka kwambili na cimphepo camkuntho, angagwe mphwayi akaganizila nthawi na mphamvu zimene ayenela kutailapo kuti amangenso nyumbayo. Mofananamo, ngati ubwenzi wanu na Yehova unawonongeka cifukwa cocita chimo lalikulu, mungamaone kuti muli na cinchito cacikulu kuti mukonzenso ubwenziwo. Koma musade nkhawa, thandizo lilipo.

Yehova akutipempha kuti: “Bwelani tsopano anthu inu. Tiyeni tikambilane.” (Yes. 1:18) Pofika pano, mwayesetsa kukonza zinthu. Yehova ni wokondwa ngako cifukwa ca khama lanu. Ganizilani izi: Cifukwa cakuti munabwelela kwa Yehova, mwakhala citsanzo coonetsa kuti Mdyelekezi ni wabodza.—Miy. 27:11.

Kubwelela kwanu mu mpingo, kwaonetsa kale kuti mwamuyandikila Yehova, ndipo nayenso analonjeza kuti adzakuyandikilani. (Yak. 4:8) Abale na alongo ni okondwela kuti munabwelela mu mpingo. Komabe, palinso zina zimene muyenela kucita. Muyenela kupitiliza kulimbitsa cikondi pa Atate wanu, komanso Bwenzi lanu Yehova. Mungacite bwanji zimenezi?

DZIIKILENI ZOLINGA ZIMEME MUNGAKWANITSE POKONZA UBWENZI WANU

Yesani kudziikila zolinga zimene mungakwanitse. Mwina mukali kukumbukila zimene munaphunzila zokhudza Yehova, komanso lonjezo lake la Paradaiso. Koma lomba muyenela kukhalanso na pulogilamu ya zauzimu, monga kulalikila nthawi zonse, kusonkhana, komanso kuceza na abale na alongo. Ganizilani zolinga izi.

Muzipemphela kwa Yehova nthawi zonse. Atate wanu adziŵa kuti mukamapitiliza kudziimba mlandu, cingakuvuteni kupemphela kwa iye. (Aroma 8:26) Ngakhale conco, “limbikilani kupemphela,” muuzeni Yehova kuti mufunitsitsa kukhala naye paubwenzi wolimba. (Aroma 12:12) Andrej anati: “N’nali kudziimba mlandu kwambili, komanso n’nali kucita manyazi. Koma pambuyo pa pemphelo lililonse n’nali kumvelako bwino. N’nali kukhala na mtendele wamaganizo.” Ngati simudziŵa zimene mungachule m’pemphelo, phunzilani pa mapemphelo amene Mfumu Davide yolapa inapeleka, olembedwa pa Salimo 51 na 65.

Muziŵelenga Baibo nthawi zonse. Izi zidzakuthandizani kukhala na cikhulupililo colimba, komanso kukulitsa cikondi canu pa Yehova. (Sal. 19:7-11) Felipe anati: “Cifukwa cosakhala na pulogilamu yoŵelenga Baibo nthawi zonse, n’nafooka ndipo n’namgwilitsa mwala Yehova. Sin’nafune kubwelezanso colakwaco. Conco, n’naonetsetsa kuti nikucita phunzilo laumwini nthawi zonse.” Na imwe mungacite cimodzi-modzi. Ngati mufuna thandizo pa nkhani zimene mungaŵelenge pa phunzilo lanu laumwini, bwanji osapempha mnzanu wofikapo mwauzimu kuti akuthandizeni.

Konzaninso ubwenzi wanu na abale na alongo. Ena amene anabwelela mu mpingo, anali na nkhawa yakuti abale na alongo adzayamba kuwaona mosayenela. Larissa anati: “N’nali kucita manyazi kwambili. N’nali kuona kuti n’nakhumudwitsa mpingo. Maganizo amenewa n’nakhala nawo kwa nthawi yaitali.” Dziŵani kuti akulu komanso Akhristu ena okhwima, ni ofunitsitsa kukuthandizani kukonzanso ubwenzi wanu na Yehova. (Onani bokosi lakuti, “ Zimene Akulu Angacite”) Iwo ni okondwela kuti munabwelela, ndipo afuna kuti zizikuyendelani bwino.—Miy. 17:17.

N’ciani cingakuthandizeni kuyandikila mpingo? Muzicita mokwanila zimene abale na alongo amacita, monga kupezeka ku misonkhano, komanso kulalikila nthawi zonse. Kodi izi zingakuthandizeni bwanji? Felix anati: “Mpingo unali kuniyembekezela mwacidwi kuti nibwelele. N’naona kuti ndine wofunika. Onse ananithandiza kuti nikhalenso m’banja lauzimu, kuona kuti Yehova ananikhululukila, komanso kupitiliza kum’tumikila.”—Onani bokosi lakuti, “ Zimene Mungacite.”

MUSATAYE MTIMA!

Satana adzapitiliza kukuponyelani “zimphepo zamkuntho” za mayeso kuti akufooketseni pamene mukonzanso ubwenzi wanu na Yehova. (Luka 4:13) Konzekelani kulimbana na mavutowo mwa kulimbitsa ubwenzi wanu na Yehova pali pano.

Ponena za nkhosa zake, Yehova analonjeza kuti: “Nkhosa zosocela ndidzazifunafuna, zomwazika ndidzazibweza. Yothyoka mwendo ndidzaimanga mwendo wothyokawo. Yodwala ndidzailimbitsa.” (Ezek. 34:16) Yehova wathandiza anthu osaŵelengeka kukonzanso ubale wawo na iye. Dziŵani kuti amafuna kukuthandiza kupitiliza kulimbitsa ubale wanu na iye.

^ ndime 4 Maina m’nkhani ino asinthidwa.