Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Cithunzi coonetsa pulatifomu, komanso cikwangwani pamwamba pake

1922—Zaka 100 Zapitazo

1922—Zaka 100 Zapitazo

“MULUNGU . . . amatithandiza kuti tipambane kudzela . . . mwa Yesu Khristu.” (1 Akor. 15:57) Mawuwa, ndiwo anali lemba la caka ca 1922, ndipo anatsimikizila Ophunzila Baibo kalelo kuti adzalandila mphoto cifukwa ca kukhulupilika kwawo. M’caka cimeneco, Yehova anawafupadi alaliki okangalika amenewo. Anawadalitsa moti anayamba kudzipulintila okha mabuku, komanso kugwilitsa nchito wailesi pofalitsa coonadi ca Ufumu. M’kupita kwa nthawi m’caka cimeneco, zinaonekelanso kuti Yehova anali kudalitsa anthu ake. Ophunzila Baibo amenewo anacita msonkhano waukulu wosaiŵalika, ku Cedar Point, Ohio, ku America. Msonkhanowo unakhudza kwambili nchito ya gulu la Yehova kuyambila nthawi imeneyo mpaka pano.

“LINGALILO LABWINO KWAMBILI”

Pamene nchito yolalikila inapita patsogolo, panali kufunikila mabuku ambili. Abale pa Beteli ya Brooklyn anali kupulinta okha magazini, koma mabuku a cikuto colimba anali kupatsa makampani ena kuti awapulintile. Ndiyeno kwa miyezi yambili, panakhala vuto la kucepa kwa mabuku ogwilitsa nchito mu ulaliki. Conco, M’bale Rutherford anafunsa m’bale Robert Martin, amene anali manejala wa pa fakitale yathu, ngati kunali kotheka kuyamba kudzipulintila tokha mabukuwo.

Fakitale yopulintilamo mabuku ku Brooklyn, mu mzinda wa New York

M’bale Martin anati: “Linali lingalilo labwino kwambili, cifukwa izi zinatanthauza kukhala na fakitale yathu-yathu yopulintilamo mabuku onse.” Conco, abale anayamba kucita lendi malo ena ake ku 18 Concord Street, Brooklyn, ndipo anagula zinthu zonse zofunikila pa nchitoyo.

Si onse amene anakondwela poona kuti tayamba kudzipulintila tokha mabuku. Pulezidenti wa kampani imene inali kutipulintila mabuku, anafika pa fakitale yathu yatsopano. Iye anati: “Muli na makina abwino ngako opulintila. Koma palibe mmodzi wa inu amene amadziŵa mowagwilitsila nchito. Pambuyo pa miyezi 6, makina anu adzawonongeka.”

M’bale Martin anati: “Zimene munthuyo anakamba zinaoneka ngati zoona. Koma tinadziŵa kuti Yehova adzatithandiza, ndipo anatithandizadi.” M’bale Martin anakambadi zoona. Posapita nthawi, makinawo anali kupulinta mabuku 2,000 patsiku.

Abale aimilila pafupi na makina ochedwa linotype mu fakitale

KULALIKILA ANTHU OCULUKA PA WAILESI

Kuwonjezela pa kudzipulintila okha mabuku, anthu a Yehova anayamba kuseŵenzetsa njila yatsopano yofalitsila uthenga wabwino pa wailesi. Pa Sondo masana, pa February 26, 1922, M’bale Rutherford anakamba nkhani pa wailesi kwa nthawi yoyamba. Mutu wake unali wakuti, “Anthu Mamiliyoni Ambili Amene Ali na Moyo Sadzafa,” ndipo anaikambila pa wailesi ya KOG m’tauni ya Los Angeles, ku California, ku America.

Anthu pafupifupi 25,000 anamvetsela nkhaniyo. Ena analemba makalata oyamikila M’bale Rutherford. Kalata ina inacokela kwa Willard Ashford, wa m’tauni ya Santa Ana, ku California. Iye anayamikila M’bale Rutherford cifukwa ca nkhani yake “yosangalatsa komanso yocititsa cidwi.” M’kalatayo iye anati: “Nili na odwala atatu panyumba amene sakwanitsa kuyenda. Conco, sizikanatheka kubwela kudzamvetsela nkhani yanu, ngakhale nkhaniyo ikanakambidwa kufupi na kwathu. Zikomo kuti nkhani yanu munaikambila pa wailesi.”

M’milungu yotsatila, nkhani zinanso zinaulutsidwa pa wailesi. Podzafika kumapeto kwa caka ca 1922, Nsanja ya Mlonda inati anthu “pafupifupi 300,000 anamvetsela uthenga wabwino pa wailesi.”

Polimbikitsidwa na makalata komanso ndemanga za anthu, Ophunzila Baibo amenewo anaganiza zokhazikitsa nyumba ya wailesi pa malo a Staten Island, kufupi na Beteli ya ku Brooklyn. M’zaka zotsatilapo, Ophunzila Baibo anali kugwilitsa nchito nyumba ya wailesi imeneyo yochedwa WBBR, pofalitsa uthenga wa Ufumu kwa anthu ambili.

ZILEMBO ZA “ADV”

Mu Nsanja ya Mlonda ya June 15, 1922, munali cilengezo cakuti kudzakhala msonkhano waukulu ku Cedar Point, Ohio, kuyambila pa September 5 mpaka 13, 1922. Ophunzila Baibo anakondwela kwambili atakhamukila ku Cedar Point.

M’nkhani yake yolonjela anthu, M’bale Rutherford anati: “Ndine wotsimikiza na mtima wonse kuti Ambuye . . . adzadalitsa msonkhano uno, kuti upeleke umboni waukulu kwa anthu kuposa kale lonse.” Alankhuli a nkhani pa msonkhanowo mobweleza-bweleza anagogomeza nchito yolalikila.

Khamu la anthu limene linapezeka pa msonkhano waukulu mu 1922 ku Cedar Point, Ohio

Ndiyeno pa Cisanu, September 8, anthu 8,000 anadzaza bwalo la msonkhano, kuyembekezela mwacidwi kumvetsela nkhani ya M’bale Rutherford. Anali kuyembekezela kuti iye adzafotokoza tanthauzo la zilembo zakuti “ADV,” zolembedwa pa tumapelala twa ciitano. Pamene anakhala pansi, ambili a iwo anaona cinsalu cacikulu pamwamba pa pulatifomu. M’bale Arthur Claus, amene anacoka ku tauni ya Tulsa, ku Oklahoma, ku America anapezeka msonkhanowo. Iye anakhala pamalo akuti azimva bwino-bwino, cifukwa panthawiyo kunalibe zokuzila mawu.

“Tinali kumvetsela nkhaniyo mwachelu”

Pofuna kuonetsetsa kuti pasakhale cosokoneza ciliconse, cheyamani analengeza kuti palibe aliyense wobwela mocedwa adzaloledwa kuloŵa m’bwalo la msonkhano nkhani ya M’bale Rutherford ili mkati. Pa 9:30 a.m, anayamba nkhani yake mwa kugwila mawu a Yesu pa Mateyu 4:17 akuti: “Ufumu wakumwamba wayandikila.” Pofotokoza njila imene anthu adzamvele za Ufumu umenewu, iye anati: “Yesu iye mwini anakamba kuti pa nthawi ya kukhalapo kwake, iye adzatsogolela pa nchito yokolola anthu ake, na kusonkhanitsa kwa iye Akhristu oona komanso okhulupilika.”

M’bale Claus, amene anali kumvetsela m’gulu, anati: “Tinali kumvetsela nkhaniyo mwachelu.” Koma mwadzidzidzi iye anadwala moti anatuluka m’bwalo la msonkhano mokwinyilila, podziŵa kuti sadzaloledwa kuloŵanso.

Koma m’mphindi zocepa, iye anayamba kumvako bwino, ndipo anatembenuka kubwelelanso ku bwalo la msonkhano. Pamene anali kubwelela anamva anthu akuomba m’manja. Atamva zimenezo, anakondwela kwambili. Anati anali wokonzeka ngakhale kukwela pamwamba pa bwalo la msonkhano limenelo kuti asaphonye nkhani yolimbikitsa imeneyo. M’bale Claus, ali mnyamata wa zaka 23 panthawiyo, anakwela pawindo la bwalo la msonkhanolo. Mawindo a bwalo limenelo anali otsegula. Conco, iye anati “anakwanitsa kumvetsela nkhaniyo bwino-bwino.”

Koma m’bale Claus sindiye yekha anakwela m’mwamba mwa bwalo limenelo. Panalinso abale ena. Ndipo mmodzi wa iwo anali Frank Johnson. M’bale Johnson anapita kwa m’bale Claus na kum’funsa kuti: “Kodi uliko na kampeni kakuthwa?”

M’bale Claus anayankha kuti, “Inde, nili nako.”

M’bale Frank anati, “Ndiwe yankho pa zimene tinali kufuna. Kodi waciona cinsalu copinda ici? Ni cikwangwani comangilila kumwambaku. Umvetsele mwachelu kwa Woweluza. * Akanena kuti, ‘Lengezani, lengezani,’ udule nthambo zinayi izi.”

Conco, M’bale Claus na abale ena, anali kuyembekezela M’bale Rutherford kukamba mawu aja monga cizindikilo kuti adule nthambozo. Kenako, M’bale Rutherford anafika pacimake penipeni pa nkhani yake. Iye atatentha nayo nkhaniyo, mokweza mawu anati: “Mukhale mboni za Ambuye zokhulupilika komanso zoona. Pitilizani kumenya nkhondo mpaka mbali iliyonse ya Babulo itawonongedwa. Lengezani uthengawu kwina kulikonse. Dziko lonse lidziŵe kuti Yehova ndiye Mulungu, ndipo Yesu Khristu ndiye Mfumu ya mafumu, ndi Mbuye wa ambuye. Lelo ndi tsiku lalikulu kuposa masiku onse. Onani, Mfumu yayamba kale kulamulila ndipo inu ndinu atumiki ake olengeza ufumuwo. Conco lengezani, lengezani, lengezani Mfumu ndi ufumu wake!”

M’bale Claus anati iye na abale ena anadula nthambozo, ndipo cinsaluco cinatambasuka bwino-bwino. Mogwilizana na zilembo zija za “ADV,” pa cinsalupo panali polemba kuti: “Lengezani Mfumu na Ufumu Wake.” Zilembo za “ADV” ni cidule ca liwu la Cizungu lakuti ‘advertise,’ limene litanthauza kuti ‘lengezani’ kapena ‘lalikilani.’

NCHITO YOFUNIKA KWAMBILI

Msonkhano waukulu umenewo wa ku Cedar Point, unathandiza abale na alongo kuika maganizo awo pa nchito yofunika kwambili yolalikila za Ufumu. Ndipo awo amene anali mtima wodzipeleka anali okondwa kutengako m’mbali pa nchitoyo. Kopotala wina (tsopano timati mpainiya) wa ku tauni ya Oklahoma, ku America analemba kuti, “Tinali kulalikila m’dela limene anthu ambili anali kuseŵenza pa migodi ya malasha amiyala, ndipo anali osauka.” Iye anati nthawi zambili anthuwo akamvetsela uthenga wopezeka m’magazini ya Golden Age, “anali kugwetsa misozi.” Kopotalayo anati, “Tinaona kuti linali dalitso lalikulu kuwalimbikitsa.”

Ophunzila Baibo amenewo anaona kufunika kwa mawu a Yesu a pa Luka 10:2 akuti: “Zokolola n’zoculukadi, koma anchito ndi ocepa.” Kumapeto kwa cakaco, iwo anali ofunitsitsa kuposa kale lonse kulengeza uthenga wa Ufumu m’madela ambili.

^ Nthawi zina, M’bale Rutherford analil kucedwa “Woweluza” cifukwa anagwilapo nchito yoweluza ku Missouri, America.