Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 41

Mukhoza Kucipeza Cimwemwe Ceniceni

Mukhoza Kucipeza Cimwemwe Ceniceni

“Wodala ndi aliyense woopa Yehova.” —SAL. 128:1.

NYIMBO 110 “Cimwemwe Cimene Yehova Amapeleka”

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Kodi ife anthu tili na ‘cosoŵa cauzimu’ cotani? Nanga cikhudzana bwanji na cimwemwe cathu ceniceni?

 CIMWEMWE ceniceni sikungomva cabe bwino mu mtima kumene kumabwela na kupita. Koma ni cinthu cimene munthu angakhale naco kwa moyo wake wonse. Motani? Yesu pa ulaliki wake wa pa phili anati: “Odala ndi anthu amene amazindikila zosoŵa zawo zauzimu.” (Mat. 5:3) Yesu anadziŵa kuti anthufe tinalengedwa na cikhumbo cofuna kudziŵa Mlengi wathu Yehova Mulungu na kum’lambila. Ici ni ‘cosoŵa cathu cauzimu.’ Popeza Yehova ni “Mulungu wacimwemwe,” nawonso amene amam’lambila angapeze cimwemwe.—1 Tim. 1:11.

“Odala ndi anthu amene akuzunzidwa cifukwa ca cilungamo.”—Mat. 5:10 (Onani ndime 2-3) *

2-3. (a) Kodi Yesu anati ndani ena amene angakhale na cimwemwe? (b) Kodi tikambilane ciyani m’nkhani ino? Nanga n’cifukwa ciyani kukambilana zimenezo n’kofunika?

2 Kodi n’zotheka kukhala acimwemwe pamene tikukumananso na mavuto? Inde. Pa ulaliki wake wa pa phili, Yesu anafotokoza cinacake cocititsa cidwi. Anati “anthu amene akumva cisoni” kaya cifukwa ca macimo awo kapena cifukwa ca mavuto amene akukumana nawo pa umoyo—onse angakhale acimwemwe. Yesu anakambanso cimodzi-modzi ponena za “anthu amene akuzunzidwa cifukwa ca cilungamo” kapena “anthu amene amanyozedwa” cifukwa cokhala otsatila ake. (Mat. 5:4, 10, 11) Koma kodi zitheka bwanji kukhala na cimwemwe ceniceni munthu akamakumana na mavuto ngati amenewa?

3 Apa Yesu anali kuphunzitsa mfundo yakuti cimwemwe cimabwela, osati cifukwa cakuti tilibe mavuto pa umoyo, koma cimabwela cifukwa cokwanilitsa zosoŵa zathu zauzimu na kuyandikila Mulungu. (Yak. 4:8) Kodi tingacite bwanji zimenezi? M’nkhani ino, tikambilane zinthu zitatu zimene zingatithandize kupeza cimwemwe ceniceni.

TIZIDYA CAKUDYA CAUZIMU

4. Kodi cinthu coyamba cimene cingatithandize kupeza cimwemwe ceniceni n’ciyani? (Salimo 1:1-3)

4 CINTHU COYAMBA: Kuti tikhale na cimwemwe ceniceni, tiyenela kudya cakudya cauzimu. Ife anthu komanso nyama timafunika cakudya cakuthupi kuti tikhale na moyo. Koma ni anthu okha amene amadya cakudya cauzimu. Ndipo cakudyaco n’cofunika ngako kwa ife. Ndiye cifukwa cake Yesu anati: “Munthu sangakhale ndi moyo ndi cakudya cokha, koma ndi mawu onse otuluka pakamwa pa Yehova.” (Mat. 4:4) Conco, tsiku siliyenela kupita osadyako cakudya cauzimu cimene ni Mawu a Mulungu amtengo wapatali. Wamasalimo anati: ‘Wodala ndi munthu amene amakodwela ndi cilamulo ca Yehova, ndipo amaŵelenga usana ndi usiku.’—Welengani Salimo 1:1-3.

5-6. (a) Kodi tingaphunzile zotani m’Baibo? (b) Kodi kuŵelenga Baibo kungatithandize m’njila ziti?

5 Kupyolela m’Baibo, Yehova mwacikondi anatipatsa malangizo ofunika okhalila na umoyo wacimwemwe. Timadziŵa colinga cake cokudza moyo umene tili nawo. Timadziŵa mmene tingamuyandikilile, komanso zimene tingacite kuti atikhululukile macimo athu. Kuwonjezela apo, timadziŵanso za ciyembekezo cabwino ca zakutsogolo cimene iye watilonjeza. (Yer. 29:11) Kuphunzila coonadi ca m’Baibo kumadzaza mitima yathu na cimwemwe.

6 Monga tidziŵila, m’Baibo mulinso malangizo ambili otithandiza pa umoyo wa tsiku na tsiku. Tikamatsatila malangizo amenewo, cimwemwe tidzacipeza. Koma tikalefuka na mavuto a pa umoyo, muzipatula nthawi yoŵelenga Mawu a Yehova na kuwasinkhasinkha. Yesu anati: “Odala ndi anthu amene akumva mawu a Mulungu ndi kuwasunga!”—Luka 11:28.

7. Mungacite ciyani kuti muzipindula na zimene mumaŵelenga m’Baibo?

7 Mukamaŵelenga Mawu a Mulungu, musamathamange kuti muzimva kukoma kwa zimene mukuŵelengazo. Tiyelekezele motele: Wina wake waphika cakudya cimene mumacikonda kwambili. Koma cifukwa cakuti ndinu wofulumila komanso wotangwanika, mukudya cakudyaco mothamanga moti mukulephela kumva kukoma kwake. Ndipo pamene mwatsiliza kudya, mwaona kuti cakudyaco mwacidya mothamanga kwambili moti simunamve kukoma kwake. Mofananamo, kodi munayamba mwaŵelengapo Baibo mothamanga cakuti simunamve kukoma kwa uthenga wake? Inde, musamathamange poŵelenga Mawu a Mulungu. Koma muziona m’maganizo mwanu zocitikazo. Muziyelekezela mawu a anthu amene akukamba, komanso muzisinkhasinkha zimene mwaŵelengazo. Mukamaŵelenga mwa njila imeneyi mudzakhala acimwemwe.

8. Kodi “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu” akukwanilitsa bwanji nchito yake? (Mungaonenso mawu a m’munsi.)

8 Yesu anaika “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu” kuti azikonza cakudya cauzimu pa nthawi yoyenela. Ndipo timadyetsedwa bwino mwauzimu. * (Mat. 24:45) Cinthu cacikulu cimene kapolo wokhulupilika amagwilitsa nchito pokonza cakudya cauzimu, ni Malemba ouzilidwa. (1 Ates. 2:13) Cakudya cauzimu cozikika pa Baibo cimeneco, cimatithandiza kudziŵa kaganizidwe ka Yehova. Ndiye cifukwa cake timaŵelenga magazini a Nsanja ya Mlonda na Galamuka!, komanso nkhani za pa jw.org. Timakonzekela misonkhano ya mpingo ya mkati mwa mlungu komanso ya kumapeto kwa mlungu. Ndipo mwezi uli wonse timaonelela pulogilamu ya JW Broadcasting® ngati ilimo m’cinenelo cathu. Tikamadya cakudya cauzimu mokwanila, tidzakwanitsa kucita cinthu caciŵili cimene cingatithandize kupeza cimwemwe ceniceni.

MUZIMVELA MALAMULO A YEHOVA

9. Kodi cinthu caciŵili cimene cingatithandize kupeza cimwemwe ceniceni n’citi?

9 CINTHU CACIŴILI: Kuti tikhale na cimwemwe ceniceni, tiyenela kumvela malamulo a Yehova. Wamasalimo analemba kuti: “Wodala ndi aliyense woopa Yehova, amene amayenda m’njila za Mulungu.” (Sal. 128:1) Kuwopa Yehova kumatathauza kum’lemekeza kwambili mwa kupewa kucita ciliconse com’khumudwitsa. (Miy. 16:6) Conco, tiyenela kupitiliza kuyesetsa kutsatila malamulo a Mulungu a cabwino na coipa, monga mmene Baibo imafotokozela. (2 Akor. 7:1) Tikamacita zimene Yehova amakonda, na kupewa kucita zimene amadana nazo, tidzakhala na cimwemwe.—Sal. 37:27; 97:10; Aroma 12:9.

10. Malinga na Aroma 12:2, kodi tili na udindo wotani?

10 Ŵelengani Aroma 12:2. Munthu angadziŵe kuti Yehova ndiye ali na mphamvu yotiuza kuti ici n’cabwino, ici n’coipa. Koma munthuyo payekha ayenelanso kutsatila zimene Mulungu amafuna. Mwacitsanzo, munthu angadziŵe kuti boma ndilo lili na ufulu woika malamulo a liŵilo la mamotoka pamsewu. Koma iye angakhale kuti sakufuna kutsatila malamulowo. Ndipo poonetsa kusafuna kwake kuwatsatila, amayendetsa motoka yake mothamanga kwambili. N’cimodzimodzinso ife. Mwa khalidwe lathu, timaonetsa kuti timakhulupililadi kuti kutsatila malamulo a Yehova kumatipindulila. (Miy. 12:28) Umu ni mmene Davide anamvela ponena za Yehova. Iye anati: “Mudzandidziŵitsa njila ya moyo. Cifukwa ca nkhope yanu, munthu adzakondwela mokwanila. Kudzanja lanu lamanja kuli cimwemwe mpaka muyaya.”—Sal. 16:11.

11-12. (a)Tikamada nkhawa na mavuto kapena tikalefulidwa, kodi tiyenela kusamala na ciyani? (b) Kodi mawu a pa Afilipi 4:8 angatithandize bwanji posankha zosangalatsa?

11 Tikakumana na mavuto kapena kulefulidwa, tingaone kuti tiyenela kucitapo kanthu kuti tithetse mavutowo. Izi n’zomveka. Koma tiyenela kusamala kuti tisacite zinthu zimene Yehova amadana nazo.—Aef. 5:10-12, 15-17.

12 M’kalata yake yopita kwa Afilipi, mtumwi Paulo analimbikitsa Akhristu kuti apitilize kuganizila zinthu zimene ni “zolungama, . . . zoyela, . . . zacikondi [komanso] khalidwe labwino lililonse.” (Ŵelengani Afilipi 4:8.) Ngakhale kuti Paulo polemba sanali kukamba za nkhani ya zosangalatsa, zimene iye analemba ziyenela kutithandiza kusankha bwino zosangalatsa. Yesani izi: Pali ponse pamene pali liwu lakuti “zinthu” pa lembali, yesani kuikapo mawu akuti “nyimbo,” “mafilimu,” “mabuku a nthano,” kapena “maseŵelo a pa kompyuta.” Kucita izi kudzakuthandizani kuzindikila zosangalatsa zimene Mulungu amakondwela nazo, komanso zimene amadana nazo. Timafuna kuti umoyo wathu uzikhala wogwilizana na mfundo za Yehova. (Sal. 119:1-3) Ndipo tikacita zimenezi, tidzakhala na cikumbumtima coyela. Izi zitifikitsa pa cinthu cacitatu cimene cingatithandize kupeza cimwemwe ceniceni.—Mac. 23:1.

MUZIIKA KULAMBILA YEHOVA PATSOGOLO

13. N’ciyani cacitatu cimene cingatithandize kupeza cimwemwe ceniceni? (Yohane 4:23, 24)

13 CINTHU CACITATU: Muzionetsetsa kuti mukuika kulambila Yehova patsogolo mu umoyo wanu. Yehova pokhala Mlengi wathu, ni woyenela kuti ife tizim’lambila. (Chiv. 4:11; 146, 7) Conco, tiyenela kuika patsogolo kulambila Mulungu m’njila imene iye amavomeleza, “motsogoleledwa ndi mzimu ndi coonadi.” (Ŵelengani Yohane 4:23, 24.) Timafuna kuti mzimu woyela wa Mulungu uzititsogolela pa kulambila kwathu kuti kulambilako kukhale kogwilizana na mfundo za coonadi copezeka m’Mawu ake. Tiyenela kuika patsogolo kulambila kwathu olo kuti tikhala m’dziko limene nchito yathu inaikilidwa ziletso kapena kutsekedwa. Pano tikamba, abale na alongo oposa 100 ali m’ndende cabe cifukwa ni Mboni za Yehova. * Ngakhale n’telo, iwo amacita mwacimwemwe zonse zimene angathe kuti azipemphela, kuŵelenga Mawu a Mulungu, na kuuzako ena za iye na Ufumu wake. Anthu akatinyoza kapena kutizunza, tingakhale acimwemwe podziŵa kuti Yehova ali nafe, ndiponso kuti adzatifupa.—Yak. 1:12; 1 Pet. 4:14.

CITSANZO CA ZOCITIKA ZENIZENI

14. N’ciyani cinacitikila m’bale wina wa cinyamata ku Tajikistan? Nanga n’cifukwa ciyani?

14 Zocitika zenizeni zimatsimikizila kuti zinthu zitatu zimene tangokambilana kumene, zimatithandizadi kupeza cimwemwe ceniceni, kaya zinthu zikhale motani pa umoyo wathu. Onani zimene zinacitikila mnyamata wa zaka 19, dzina lake Jovidon Bobojonov, wa ku Tajikistan, amene anakana kuloŵa usilikali. Pa October 4, 2019, iye anatengedwa mwacikakamizo panyumba pawo n’kukamusunga m’ndende kwa miyezi ndithu, ndipo anali kum’cita nkhanza ngati kuti anali cigaŵenga. Maiko ambili anamva za kupanda cilungamo kumene kunacitikila m’bale Bobojonov. Lipoti linaonetsa kuti anam’menya pofuna kum’kakamiza kuti avomele kuloŵa usilikali, n’kuyamba kuvala yunifomu ya usilikali. Pambuyo pake, khoti linam’peza na mlandu, ndipo anam’gamula kuti apite kundende yacibalo. Anakhala m’ndendemo mpaka pamene pulezidenti wadzikolo anam’khululukila, na kulamula kuti atulutsidwe. Kwa nthawi yonseyo, Jovidon anakhalabe wokhulupilika, ndipo sanataye cimwemwe cake. Motani? Mwa kuzindikila zosoŵa zake zauzimu.

M’bale Jovidon anali kudya cakudya cauzimu, kutsatila mfundo za Mulungu, komanso anali kuika patsogolo kulambila Yehova mu umoyo wake (Onani ndime 15-17)

15. Kodi m’bale Jovidon anali kudya bwanji cakudya cauzimu pamene anali m’ndende?

15 Ali m’ndende, m’bale Jovidon anapitiliza kudya cakudya cauzimu, ngakhale kuti analibe Baibo kapena cofalitsa ciliconse. Kodi zimenezo zinali kutheka bwanji? Abale na alongo anali kum’pelekela cakudya mu zola zawo. Ndipo pa zola za cakudyazo anali kulembapo lemba latsikulo. Conco, iye anali kukwanitsa kuŵelenga Baibo tsiku lililonse na kusinkhasinkha. Atatuluka m’ndende, iye analimbikitsa abale na alongo amene sanakumanepo namayeso aakulu kuti: “Mufunika kugwilitsa nchito ufulu umene muli nawo popitiliza kuphunzila zambili zokhudza Yehova poŵelenga Mawu ake, ndiponso mabuku athu.”

16. Kodi m’bale Jovidon anaika maganizo ake pa ciyani?

16 M’bale wathuyu anali kutsatila malamulo a Yehova. M’malo mokhala na maganizo olakwika na kuyamba kucita zinthu zoipa, iye anaika maganizo ake pa Yehova na mfundo zake. M’bale Jovidon anali kucita cidwi na zinthu zokongola zimene Mulungu analenga. M’mawa ulionse akauka, anali kumvetsela kulila kwa mbalame. Ndipo usiku, anali kucita cidwi na kuwala kwa mwezi komanso nyenyezi. Iye anati: “Mphatso zocokela kwa Yehova zimenezi zinali kunithandiza kukhala wosangalala, ndiponso zinali kunilimbikitsa.” Tikamayamikila zinthu zauzimu komanso zakuthupi zimene Yehova amatipatsa, timakhala na cimwemwe cacikulu mumtima, ndipo cimwemweco cimatithandiza kupilila.

17. Kodi munthu amene akukumana na mavuto monga a m’bale Jovidon angawagwilitse nchito bwanji mawu a pa 1 Petulo 1:6, 7?

17 Cina, m’bale Jovidon anaika kulambila Yehova patsogolo. Iye anadziŵa kufunika kokhala wokhulupilika kwa Mulungu woona. Yesu anati: “Yehova Mulungu wako ndi amene uyenela kumulambila, ndipo uyenela kutumikila iye yekha basi.” (Luka 4:8) Akulu-akulu a asilikali pamodzi na asilikali ena anafuna kuti m’bale Jovidon aleke kukhala wa Mboni za Yehova. Koma iye anali kupemphela mocokela pansi pa mtima usana na usiku, kupempha Yehova kuti am’thandize kukhalabe wokhulupilika kwa iye. Ngakhale kuti anacitidwa zinthu zopanda cilungamo, m’bale Jovidon sanagonje. Zotulupo zake n’zakuti iye tsopano ali na cimwemwe cacikulu cifukwa cikhulupililo cake cinayesedwa, ndipo anapambana olo kuti anagwidwa, kumenyedwa, na kuponyedwa m’ndende.—Ŵelengani 1 Petulo 1:6, 7.

18. Kodi tingapitilize bwanji kukhala acimwemwe?

18 Yehova amadziŵa zimene timafunikila kuti tikhale na cimwemwe ceniceni. Tikamayesetsa kucita zinthu zitatu zimene zingatithandize kupeza cimwemwe ceniceni, tidzacipezadi ngakhale kuti tikukumana na mavuto. Tikatelo, tizatha kukamba kuti: “Odala ndi anthu amene Mulungu wawo ndi Yehova.”—Sal. 144:15.

NYIMBO 89 Mvela Udalitsike

^ Anthu ambili amavutika kucipeza cimwemwe ceniceni cifukwa amacifuna-funa kolakwika. Iwo amaona kuti angacipeze m’zosangulutsa, cuma, kuchuka, kapena mwa kukhala na mphamvu. Koma pamene Yesu anali padziko lapansi, anauza anthu mmene angacipezele cimwemwe ceniceni. Ndiye cifukwa cake m’nkhani ino, tikambilane zinthu zitatu zimene zingatithandize kupeza cimwemwe ceniceni.

^ Onani nkhani yakuti, “Kodi Mumalandila Cakudya ‘pa Nthawi Yoyenela’?” mu Nsanja ya Mlonda ya August 15, 2014.

^ Kuti mudziŵe zambili, fufuzani pa jw.org ku Chichewa nkhani yakuti, “Anamangidwa Chifukwa Chotsatila Zimene Amakhulupilila.

^ MAWU OFOTOKOZELA CITHUNZI: M’citsanzo ici, Mboni zikulimbikitsa m’bale womangidwa amene akupita kukaonekela pamaso pa khoti.