Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

N’cifukwa Ciyani Ife Sitimenya Nkhondo Ngati Aisiraeli Akale?

N’cifukwa Ciyani Ife Sitimenya Nkhondo Ngati Aisiraeli Akale?

PANTHAWI ya nkhondo yaciŵili ya padziko lonse, msilikali wina wa Nazi mwaukali anauza Mboni za Yehova kuti: “Ngati mukana kumenya nkhondo na dziko la France kapena England, ndithu nonsenu mudzaphedwa!” Ngakhale kuti asilikali a Nazi anali na mfuti m’manja, palibe olo mmodzi wa abale athu anavomela kumenya nkhondo. Uku kunali kulimba mtima! Citsanzo ici cionetsa mmene ife Mboni za Yehova timaonela nkhondo: Timakana kumenya nawo nkhondo. Ngakhale atiwopseze kuti atipha, ife timakana kukhalila mbali m’mikangano yadzikoli.

Komabe, anthu ena amene amati ni Akhristu, sagwilizana nayo mfundo imeneyi. Ambili amakhulupilila kuti Mkhristu ayenela kuteteza dziko lake. Ndipo iwo angafunse kuti, ‘Aisiraeli akale amene anali anthu a Mulungu anali kumenya nkhondo. Nanga Akhristu masiku ano alekelanji?’ Mungayankhe bwanji funsoli? Mungafotokoze kuti mmene zinthu zinalili kwa Aisiraeli kalelo n’zosiyana kutalitali na zocitika za anthu a Mulungu masiku ano. Onani zifukwa zisanu zotsatilazi.

1. AISIRAELI ANALI ANTHU A MTUNDU UMODZI

M’nthawi zakale, Yehova anasankha mtundu wa Isiraeli kukhala anthu ake. Iye anachula Aisiraeli amenewo kuti “cuma canga capadela pakati pa anthu ena onse.” (Eks. 19:5) Cina, Mulungu anawapatsa dziko lawo-lawo losankhidwilatu. Conco, iye akawalamula kupita kukamenya nkhondo na mitundu ina, iwo sanali kupha alambili anzawo. *

Masiku ano, alambili a Yehova oona amacokela “m’dziko lililonse, fuko lililonse, mtundu uliwonse, ndi cinenelo ciliconse.” (Chiv. 7:9) Conco, kuti anthu a Mulungu azimenya nawo nkhondo, zingatanthauze kulimbana, komanso kupha alambili anzawo.

2. YEHOVA NDIYE ANALI KUWALAMULA AISIRAELI KUTI AMENYE NKHONDO

M’nthawi zakale, Yehova ndiye anali kugamula pamene Aisiraeli afunika kumenya nkhondo, komanso cifukwa comenyela nkhondoyo. Mwacitsanzo, Mulungu analamula Aisiraeli kuti akawathile nkhondo Akanani. Iye anacita izi kuti apeleke ciweluzo cake kwa Akananiwo, cifukwa anali kulambila ziŵanda, kucita zaciwelewele, komanso kupeleka ana nsembe. Yehova anauza Aisiraeli kuti awononge anthu ocita zoipa amenewo m’dziko limene anawalonjeza. (Lev. 18:24, 25) Aisiraeli atakhazikika M’dziko Lolonjezedwa, nthawi zina Mulungu anali kuwalamula kukamenya nkhondo kuti adziteteze kwa adani owapondeleza. (2 Sam. 5:17-25) Yehova sanali kulola Aisiraeli kupita kukamenya nkhondo popanda kuwalamula. Koma akadzipitila okha ku nkhondo, nthawi zambili zinthu sizinali kuwayendela bwino.—Num. 14:41-45; 2 Mbiri. 35:20-24.

Masiku ano, Yehova salamula anthu kumenya nkhondo. Maiko amamenyana pofuna kukwanilitsa zolinga zawo, osati cifunilo ca Mulungu ayi. Iwo angamenye nkhondo polimbilana malo, cuma, kapena kusamvana pa nkhani zandale. Nanga bwanji aja amene amati amamenya nkhondo m’dzina la Mulungu pofuna kuteteza kulambila kwawo, kapena kupha adani a Mulungu? Yehova adzateteza alambili ake oona, na kuwononga adani ake onse pa nkhondo yam’tsogolo, yochedwa Aramagedo. (Chiv. 16:14, 16) Amene adzamenye nkhondoyo, ni gulu la asilikali a Mulungu amene ni zolengedwa zokha zauzimu kumwamba, osati alambili aumunthu.—Chiv. 19:11-15.

3. AISIRAELI SANALI KUPHA ANTHU AMENE ANALI KUKHULUPILILA YEHOVA

Pamene Yehova anathila nkhondo Ayeriko, Rahabi pamodzi na banja lake sanaphedwe cifukwa ca cikhulupililo cawo. Kodi ni mmene zimacitikilanso pa nkhondo za masiku ano?

M’nthawi zakale, asilikali aciisiraeli anali kucitila cifundo anthu amene anaonetsa cikhulupililo mwa Mulungu. Koma anali kupha anthu okhawo amene Yehova anawaweluza kuti ni oyenela kuphedwa. Onani zitsanzo ziŵili izi. Ngakhale kuti Yehova analamula kuti mzinda wa Yeriko uwonongedwe, iwo sanaphe Rahabi na banja cifukwa ca cikhulupililo cawo. (Yos. 2:9-16; 6:16, 17) Patapita nthawi, mzinda wonse wa Agibeoni sunawongedwe cifukwa iwo anaonetsa ulemu waukulu kwa Mulungu.—Yos. 9:3-9, 17-19.

Masiku ano, anthu amene amamenya nkhondo sacitila cifundo anthu amene aonetsa cikhulupililo mwa Mulungu. Nthawi zina, anthu osalakwa amaphedwa pamene maiko akulimbana.

4. AISIRAELI ANALI KUTSATILA MALANGIZO A KAMENYEDWE KA NKHONDO

M’nthawi zakale, Yehova anafuna kuti Aisiraeli azimenya nkhondo motsatila malangizo ake. Mwacitsanzo, nthawi zina Mulungu anali kuwauza kucita “pangano la mtendele” na mtundu wina. (Deut. 20:10) Kuwonjezela apo, Yehova anali kufuna kuti asilikali aciisiraeli azisunga misasa yawo mwaunkhondo, komanso kukhala oyela mwamakhalidwe. (Deut. 23:9-14) Asilikali a mitundu yowazungulila anali kugwilila akazi m’madela amene iwo agonjetsa. Koma Yehova sanali kuwalola Aisiraeli kucita zimenezo. Ndipo sanali kuwalola ngakhale kukwatila mkazi amene watengedwa ukapolo kufika mwezi umodzi utatha pambuyo pogonjetsa mzindawo.—Deut. 21:10-13.

Masiku ano, maiko ambili anasainila cipangano ca malamulo a kamenyedwe ka nkhondo. Ngakhale kuti amacita zimenezi pofuna kuteteza anthu, n’zacisoni kuti malamulowo amaphwanyidwa na maikowo.

5. MULUNGU ANALI KUMENYELA NKHONDO MTUNDU WAKE

Kodi Mulungu amamenyela nkhondo mtundu uliwonse masiku ano muja anacitila kwa Aisiraeli pogonjetsa Ayeriko

M’nthawi zakale, Yehova anali kumenyela nkhondo Aisiraeli, ndipo nthawi zina anali kucita cozizwitsa kuti iwo apambane. Mwacitsanzo, kodi Yehova anathandiza bwanji Aisiraeli kugonjetsa mzinda wa Yeriko? Potsatila malangizo a Yehova, Aisiraeli ‘anafuula mwamphamvu mfuu yankhondo, ndipo mpanda wa mzindawo unayamba kugwa mpaka pansi.’ Mwakutelo, kunakhala kosavuta kuulanda mzindawo. (Yos. 6:20) Nanga pa nkhondo yolimbana na Aamori anapambana bwanji? “Yehova anawagwetsela miyala ikuluikulu ya matalala kucokela kumwamba yomwe inawagwela ndi kuwapha . . . Amene anaphedwa ndi matalalawo anali ambili kuposa amene ana a Isiraeli anapha ndi lupanga.”—Yos. 10:6-11.

Masiku ano, Yehova samenyela nkhondo mtundu uliwonse padziko lapansi. Ufumu wake, umene Yesu ndiye Mfumu ya Ufumuwo, “suli mbali ya dziko lino.” (Yoh. 18:36) Mosiyana na zimenezi, Satana ndiye ali na mphamvu pa maulamulilo onse a anthu. Nkhondo zoopsa za padzikoli zimaonetsa maganizo ake oipa kwambili.—Luka 4:5, 6; 1 Yoh. 5:19.

AKHRISTU OONA NI ANTHU OBWELETSA MTENDELE

Monga taonela, mmene zinthu zilili kwa ife masiku ano, n’zosiyana kutalitali na mmene zinali kwa Aisiraeli. Komabe, zimenezi si zifukwa zokhazo zimene sitimenyela nkhondo. Palinso zina. Mwacitsanzo, Mulungu analosela kuti m’masiku otsiliza, anthu amene adzaphunzitsidwa na iye “sadzaphunzilanso nkhondo,” ngakhale kutengako mbali. (Yes. 2:2-4) Kuwonjezela apo, Yesu anati ophunzila ake sadzakhala “mbali ya dzikoli.” Iwo sadzakhalila mbali m’mikangano ya m’dzikoli.—Yoh. 15:19.

Cina, Khristu analimbikitsa otsatila ake kucita zoposa pamenepo. Iye anawauza kupewa khalidwe limene limatsogolela ku mkwiyo komanso nkhondo. (Mat. 5:21, 22) Cinanso, iye analangiza otsatila ake kukhala anthu ‘obweletsa mtendele,’ komanso kukonda adani awo.—Mat. 5:9, 44.

Koma bwanji ifeyo aliyense payekha? N’zoona kuti sitingakhale na cifuno comenya nkhondo. Koma kodi n’kutheka kukhala na maganizo acidani mu mtima mwathu amene angayambitse mikangano na magaŵano mu mpingo? Conde, tiyeni tiyesetse kuwacotselatu mu mtima mwathu.—Yak. 4:1, 11.

M’malo mocita nawo mikango ya maiko, timalimbikitsa mtendele na cikondi pakati pathu. (Yoh. 13:34, 35) Conco, tiyeni tipitilize kusakhalila mbali pamene tikuyembekezela Yehova kuti akathetseletu nkhondo zonse kwamuyaya.—Sal. 46:9.

^ Nthawi zina, mafuko aciisiraeli inali kumenyana okha-okha. Koma nkhondo zimenezo Yehova sanali kukondwela nazo. (1 Maf. 12:24) Ngakhale n’conco, iye anali kulola nkhondo zimenezo akaona kuti mafuko ena amupandukila, kapena akacita macimo aakulu.—Ower. 20:3-35; 2 Mbiri. 13:3-18; 25:14-22; 28:1-8.