Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 42

“Odala ndi Anthu Osalakwitsa Kanthu” kwa Yehova

“Odala ndi Anthu Osalakwitsa Kanthu” kwa Yehova

“Odala ndi anthu osalakwitsa kanthu . . . , amene akutsatila cilamulo ca Yehova.”—SAL. 119:1.

NYIMBO 124 Tikhale Okhulupilika Nthawi Zonse

ZIMENE TIKAMBILANE *

Ena mwa abale na alongo athu olimba mtima amene anaponyedwapo m’ndende, kapena amene ali m’ndende cifukwa cokhala okhulupilika ku ucifumu wa Yehova (Onani ndime 1-2)

1-2. (a) Kodi maboma ena acita zotani potsutsa anthu a Yehova? Nanga anthu akewo amatani akamatsutsidwa? (b) N’cifukwa ciyani timakhalabe acimwemwe ngakhale atizunze? (Thililam’poni ndemanga pa cithunzi ca pacikuto.)

 PANO tikamba, m’maiko opitilila 30 nchito yathu inaikilidwa ziletso, kapena kutsekedwa kumene. Ena mwa maiko amenewo, anaponya abale na alongo athu m’ndende. Kodi analakwanji? Palibe. Kwa Yehova, iwo alibe mlandu uliwonse. Zimene iwo amangocita ni kuŵelenga na kuphunzila Baibo, kuuzako ena zimene amakhulupilila, komanso kusonkhana na Akhristu anzawo. Cina, iwo sakhalila mbali m’zandale. Olo kuti amatsutsidwa kwambili, atumiki a Mulungu amenewa akhalabe okhulupilika, poonetsa kudzipeleka kwawo kwathunthu kwa Yehova. Ndipo kucita zimenezo kumawapatsa cimwemwe.

2 N’kutheka kuti mwaonapo zithunzi za Mboni zina zolimba mtima zimenezi, nkhope zawo zikuwala na cimwemwe. Iwo ni osangalala cifukwa amadziŵa kuti Yehova amakondwela nawo cifukwa cokhalabe okhulupilika kwa iye. (1 Mbiri 29:17a) Yesu anati: “Odala ndi anthu amene akuzunzidwa cifukwa ca cilungamo . . . Kondwelani, dumphani ndi cimwemwe, cifukwa mphoto yanu ndi yaikulu.”—Mat. 5:10-12.

CITSANZO CIMENE TINGATENGELEKO

Petulo na Yohane anapeleka citsanzo cabwino kwa Akhristu a masiku ano amene amafunika kuimilila m’khoti kuti ateteze cikhulupililo cawo (Onani ndime 3-4)

3. Malinga na Machitidwe 4:19, 20, kodi atumwiwo anatani pamene anali kuzunzidwa m’zaka za zana loyamba? Ndipo anatelo cifukwa ciyani?

3 Abale na alongo athu akupita m’zimene atumwi anakumana nazo m’zaka za zana loyamba, polalikila zokhudza Yesu. Mobweleza-bweleza, oweluza m’khoti yaikulu ya Ayuda ‘anawalamula kuti asiye kulankhula m’dzina la Yesu.’ (Mac. 4:18; 5:27, 28, 40) Kodi atumwiwo anacita bwanji? (Ŵelengani Machitidwe 4:19, 20.) Iwo anadziŵa kuti wolamulila wamkulu ‘anawalamulila kuti alalikile kwa anthu na kupeleka umboni wokwanila’ wokamba za Khristu. (Mac. 10:42) Moimilako atumwi, Petulo na Yohane molimba mtima anakamba kuti ayenela kumvela Mulungu kuposa oweluza amenewo. Ndipo anawatsimikizila kuti sadzaleka kulankhula zokhudza Yesu. Zinali ngati iwo akufunsa oweluzawo kuti, ‘Kodi inu muona kuti muli na ulamulilo waukulu kuposa Mulungu?’

4. Malinga na Machitidwe 5:27-29, kodi atumwi anapeleka citsanzo cotani kwa Akhristu onse oona? Nanga tingatengele bwanji citsanzo cawo?

4 Atumwiwo anapeleka citsanzo cabwino kwambili. Ndipo kuyambila nthawi imeneyo, Akhristu onse oona akhala akutsatila citsanzo cawo. Atumwiwo anali ofunitsitsa “kumvela Mulungu monga wolamulila, osati anthu.” (Ŵelengani Machitidwe 5:27-29.) Pambuyo pomenyedwa cifukwa cokhalabe okhulupilika, atumwiwo anacoka pamaso pa khoti lalikulu la Ayuda, “ali osangalala cifukwa cakuti Mulungu anawaona kuti ndi oyenela kucitilidwa cipongwe cifukwa ca dzina la Yesu,” ndipo sanaleke kulalikila!—Mac. 5:40-42.

5. Ni mafunso ati amene tiyenela kupeza mayankho ake?

5 Citsanzo cimene atumwiwo anapeleka cimabutsa mafunso. Mwacitsanzo, kodi cisankho cawo comvela Mulungu osati anthu, cigwilizana bwanji na lamulo la m’Malemba lakuti ‘muzimvela olamulila akulu-akulu’? (Aroma 13:1) Kodi ‘tingamvele bwanji maboma na olamulila’ monga mmene Paulo anakambila, koma n’kukhalabe wokhulupilika kwa Mulungu wathu amene ni Wolamulila wamkulukulu?—Tito 3:1.

“OLAMULILA AKULU-AKULU”

6. (a) Kodi “olamulila akulu-akulu” ochulidwa pa Aroma 13:1 ndani? Nanga tiyenela kucita nawo motani? (b) Kodi mfundo yosatsutsika yokhudza maulamulilo onse a anthu ni yotani?

6 Ŵelengani Aroma 13:1. Pa lembali, mawu akuti “olamulila akulu-akulu,” akamba za anthu amene ali na mphamvu zolamulila anzawo. Ndipo Akhristu ayenela kuwagonjela olamulila amenewo, cifukwa iwo amakhazikitsa mtendele m’dziko, amaonetsetsa kuti malamulo akutsatilidwa, ngakhale kuteteza anthu a Yehova nthawi zina. (Chiv. 12:16) Conco, tiyenela kupeleka misonkho, mitulo, kuwaopa, na kuwapatsa ulemu umene amafuna. (Aroma 13:7) Komabe, maboma a anthu amenewa ali na ulamulilo, cabe cifukwa Yehova wawalola kuti akhale nawo. Yesu anamveketsa bwino mfundo imeneyi pamene Bwanamkubwa waciroma, Pontiyo Pilato, anali kumufunsa mafunso. Pamene Pilato anauza Yesu kuti ali na mphamvu zom’masula kapena zom’peleka kuti akaphedwe, Yesu anamuyankha kuti: “Simukanakhala ndi mphamvu iliyonse pa ine mukanapanda kupatsidwa kucokela kumwamba.” (Yoh. 19:11) Monga mmene zinalili kwa Pilato, ulamulilo wonse umene maboma a anthu komanso atsogoleli andale ali nawo, uli na malile.

7. Ni pa zocitika ziti zimene pamene sitingamvele maulamulilo a anthu? Nanga olamulila amenewo ayenela kudziŵa ciyani?

7 Akhristu ayenela kumvela malamulo a boma, malinga ngati sasemphana na malamulo a Mulungu. Koma sitingamvele anthu amenewo ngati akutiuza kucita zimene Mulungu amaletsa, kapena kutiletsa kucita zimene Mulungu amafuna. Mwacitsanzo, iwo angafune kuti anyamata onse m’dziko akamenye nkhondo kuti ateteze dziko lawo. * Kapena angaletse Baibo yathu, na zofalitsa zozikika pa Baibo. Komanso, angatiletse kulalikila na kulambila kwathu Mulungu. Olamulila amenewa akamaseŵenzetsa mphamvu zawo molakwika, mwacitsanzo kuzunza ophunzila a Khristu, adzayankha mlandu kwa Mulungu. Ndipo Yehova amaona zocita zawo.—Mlal. 5:8.

8. Kodi pali kusiyana kotani pakati pa Yehova na “olamulila akulu-akulu”?

8 Liwu lakuti “akulu-akulu,” limatanthauza munthu amene ali na udindo waukulu, koma osati waukulu kopambana. Ngakhale kuti maboma a anthu amachedwa kuti “olamulila akulu-akulu,” pali wina wake amene ali na ulamulilo waukulu kopambana. Kanayi konse m’Baibo, Yehova Mulungu amachedwa “Wamkulukulu.”—Dan. 7:18, 22, 25, 27.

“WAMKULUKULU”

9. Kodi mneneli Danieli anaona ciyani m’masomphenya?

9 Mneneli Danieli anaona masomphenya, amene anaonetsa ukulu wa Yehova kuposa maulamulilo ena onse. Coyamba, iye anaona zilombo zinayi zikulu-zikulu, zimene ziimila maulamulilo a mphamvu padziko lonse amene anakhalako, komanso amene alipo. Maulamulilowo anali Babulo, Amedi na Aperesiya, Girisi, na Roma, komanso ulamulilo wamphamvu umene ulipo masiku ano wa Britain na America. (Dan. 7:1-3, 17) Kenako, Danieli anaona Yehova Mulungu atakhala pampando wacifumu kumwamba. (Dan. 7:9, 10) Zotsatila zimene mneneli wokhulupilikayu anaona, ni cenjezo kwa olamulila onse masiku ano.

10. Malinga na Danieli 7:13, 14, 27, kodi Yehova adzapatsa ndani mphamvu zolamulila dziko lonse lapansi? Nanga kodi zimenezi zimatiuza ciyani zokhudza iye?

10 Ŵelengani Danieli 7:13, 14, 27. Mulungu akucotsa mphamvu na ulamulilo wonse ku maboma a anthu n’kuupeleka kwa oyenelela komanso amphamvu kwambili. Kodi amenewo ndani? Ni wina wake “wooneka ngati mwana wa munthu” amene ni Yesu Khristu, pamodzi na “oyela a Wamkulukulu” a 144,000, amene adzalamulile “mpaka kalekale.” (Dan. 7:18) N’zoonekelatu kuti Yehova ni “Wamkulukulu,” cifukwa ni yekhayo ali na mphamvu yocita zimenezi.

11. N’ciyani cina cimene Danieli analemba coonetsa kuti Yehova ali na ulamulilo wopambana pa mitundu ya anthu?

11 Zocitika zimene Danieli anaona m’masomphenya, n’zogwilizana na zimene anakamba asanaone masomphenyawo. Iye anati: “Mulungu wakumwamba . . , amacotsa mafumu ndi kuika mafumu.” Iye anawonjezela kuti: “Wam’mwambamwamba ndiye Wolamulila wa maufumu a anthu, ndiponso . . . , akafuna kupeleka ulamulilo kwa munthu aliyense, amamupatsa.” (Dan. 2:19-21; 4:17) Kodi pakhalako zocitika pamene Yehova anacotsa mafumu na kuika mafumu? Inde!

Yehova anacotsa ufumu wa Belisazara na kuupeleka kwa Amedi na Perisiya (Onani ndime 12)

12. Fotokozani citsanzo ca mmene Yehova anacotsela mafumu pa ulamulilo wawo m’nthawi zakale. (Onani cithunzi.)

12 Yehova waonetsapo kuti ali na ulamulilo waukulu wopambana “olamulila akuluakulu.” Ganizilani zitsanzo zitatu izi. Farao, mfumu ya Iguputo, anaika anthu a Yehova mu ukapolo. Ndipo mobwelezabweleza iye anakana kuwamasula. Ngakhale n’telo, Mulungu anawamasulabe anthu ake, koma Farao anam’miza pa Nyanja Yofiira. (Eks. 14:26-28; Sal. 136:15) Mfumu Belisazara ya Babulo atakonza phwando ‘anadzikweza pamaso pa Ambuye wakumwamba.’ Ndipo ‘anatamanda milungu wamba yasiliva komanso yagolide,’ m’malo motamanda Yehova. (Dan. 5:22, 23) Koma Mulungu anatsitsa munthu wodzikuza ameneyo. “Usiku womwewo” Belisazara anaphedwa ndipo ufumu wake unapelekedwa m’manja mwa “Amedi ndi Aperisiya.” (Dan. 5:28, 30, 31) Herode Agiripa Woyamba, mfumu ya Palesitina, anagamula kuti mtumwi Yakobo aphedwe. Ndipo anaponya mtumwi Petulo m’ndende n’colinga cakuti nayenso akamuphe. Koma Yehova anacilepheletsa colinga ca Herode. “Mngelo wa Yehova anamukantha,” ndipo anafa.—Mac. 12:1-5, 21-23.

13. Fotokozani citsanzo coonetsa mmene Yehova anagonjetsela mgwilizano wa mafumu olamulila.

13 Yehova anaonetsanso kuti ali na ulamulilo waukulu koposa pa mgwilizano wa mafumu. Iye anamenyela nkhondo Aisiraeli, powathandiza kugonjetsa mgwilizano wa mafumu acikanani okwana 31, komanso kugonjetsa madela aakulu a dziko lolonjezedwa. (Yos. 11:4-6, 20; 12:1, 7, 24) Cina, Yehova anaonetsa Mfumu Beni-hadadi zakuda pamodzi na mafumu ena a Asuri okwana 32, amene anali kulimbana na Isiraeli.—1 Maf. 20:1, 26-29.

14-15. (a) Kodi Mfumu Nebukadinezara, komanso Dariyo, anati ciyani ponena za ucifumu wa Yehova? (b) Kodi wamasalimo anati ciyani za Yehova na mtundu wake?

14 Mobwelezabweleza, Yehova wakhala akuonetsa kuti ni Wamkulukulu. Pamene Mfumu Nebukadinezara ya Babulo inadzitama cifukwa ca ‘mphamvu zake zazikulu na ulemelelo wake waukulu,’ m’malo movomeleza modzicepetsa kuti Yehova ndiye woyenela kutamandidwa, Mulungu anamucititsa misala. Koma Nebukadinezara atacila misala yake ‘anatamanda Wam’mwambamwamba,’ ndipo iye anavomeleza kuti “ulamulilo [wa Yehova] udzakhalapo mpaka kalekale.” Anakambanso kuti: “Palibe aliyense amene angaletse dzanja lake.” (Dan. 4:30, 33-35) Danieli atayesedwa pa kukhulupilika kwake, komanso Yehova atamupulumutsa m’dzenje la mikango, Mfumu Dariyo analengeza kuti: “Anthu azinjenjemela ndi kucita mantha pamaso pa Mulungu wa Danieli. Pakuti iye ndi Mulungu wamoyo, amene adzakhalapo mpaka kalekale ndipo ufumu wake sudzawonongeka komanso ulamulilo wake udzakhalapo kwamuyaya.”—Dan. 6:7-10, 19-22, 26, 27.

15 Wamasalimo anati: “Yehova wasokoneza zolinga za anthu a mitundu ina. Walepheletsa maganizo a mitundu ya anthu.” Ndipo anawonjezela kuti: “Wodala ndi mtundu umene Mulungu wawo ndi Yehova, anthu amene iye wawasankha kukhala colowa cake.” (Sal. 33:10, 12) Ha! tili na cifukwa cabwino cotani nanga cosungila umphumphu wathu kwa Yehova.

NKHONDO YOTHELA

Mgwilizano wa mitundu sudzapambana polimbana na magulu ankhondo akumwamba a Yehova (Onani ndime 16-17)

16. Kodi tingakhale otsimikiza za ciyani ponena za “cisautso cacikulu”? Nanga n’cifukwa ciyani? (Onani cithunzi.)

16 Taona zimene Yehova anacita kumbuyoko. Nanga kutsogoloku kudzacitike zotani? Tili na cidalilo cakuti Yehova adzapulumutsa atumiki ake okhulupilika pa “cisautso cacikulu” cimene cikubwela. (Mat. 24:21; Dan. 12:1) Iye adzacita zimenezi pamene mgwilizano wa maiko wochedwa Gogi wa Magogi adzaukila mwankhanza atumiki okhulupilika a Yehova padziko lonse. Mgwilizano wa maiko umenewu, ngakhale kuti ukaphatikizepo mamembala onse 193 a bungwe la United Nations, sudzapambana podzalimbana na Wamkulukulu pamodzi na magulu ake ankhondo akumwamba. Yehova analonjeza kuti: “Ndidzadzilemekeza, kudziyeletsa ndi kucititsa kuti mitundu yambili ya anthu indidziŵe, ndipo iwo adzadziŵa kuti ine ndine Yehova.”—Ezek. 38:14-16, 23; Sal. 46:10.

17. Kodi Baibo inalosela ciyani zokhudza tsogolo la mafumu a dziko lapansi, komanso la anthu okhulupilika kwa Yehova?

17 Kuukila kwa Gogi kudzayambitsa nkhondo ya Yehova yothela ya Aramagedo. Pa nkhondoyo, iye adzawononga “mafumu a dziko lonse lapansi kumene kuli anthu.” (Chiv. 16:14, 16; 19:19-21) Koma “owongoka mtima ndi amene adzakhale m’dziko lapansi, ndipo opanda colakwa ndi amene adzatsalemo.”—Miy. 2:21.

TIYENI TIKHALEBE OKHULUPILIKA

18. Kodi Akhristu oona oculuka akhala ofunitsitsa kucita ciyani? Nanga n’cifukwa ciyani? (Danieli 3:28)

18 Kwa zaka mahandiledi, Akhristu ambili oona aika miyoyo yawo pa ciwopsezo cifukwa cokonda Yehova monga Wolamulila wawo Wamkulu. Akhristu amenewa amasungabe umphumphu wawo ndipo amafanana na Akhristu atatu aciheberi amene anapulumutsidwa m’ng’anjo yamoto cifukwa cokhalabe wokhulupilika kwa Wamkulukulu.—Ŵelengani Danieli 3:28.

19. Kodi Yehova adzaweluza anthu ake pamaziko otani? Nanga kodi ife tiyenela kucita ciyani palipano?

19 Wamasalimo Davide analemba za kufunika kokhalabe okhulupilika kwa Mulungu. Anati: “Yehova adzapeleka cigamulo ku mitundu ya anthu. Ndiweluzeni inu Yehova, mogwilizana ndi cilungamo canga, komanso mogwilizana ndi mtima wanga wosagawanika.” (Sal. 7:8) Iye analembanso kuti: “Mtima wanga wosagawanika ndiponso wowongoka unditeteze.” (Sal. 25:21) Kuti tikhale na umoyo wabwino, tiyenela kukhalabe okhulupilika kwa Yehova na kusagonja pa cikhulupililo cathu kwa iye, ngakhale zivute zitani! Tikatelo, tidzamva monga mmene wamasalimo anamvela amene analemba kuti: “Odala ndi anthu osalakwitsa kanthu . . . , amene akutsatila cilamulo ca Yehova.”—Sal. 119:1.

NYIMBO 122 Cilimikani, Musasunthike!

^ Baibo imalangiza Akhristu kuti azimvela olamulila akulu-akulu, kutanthauza maboma a m’dzikoli. Koma maboma ena amatsutsa Yehova poyela na atumiki ake. Kodi tingatani kuti tizimvela olamulila amenewo, koma panthawi imodzimodzi n’kukhalabe okhulupilika kwa Yehova?

^ Onani nkhani yakuti, “N’cifukwa Ciyani Ife Sitimenya Nkhondo Ngati Aisiraeli Akale?” m’magazini ino.