Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 44

Pitilizani Kulimbitsa Ciyembekezo Canu

Pitilizani Kulimbitsa Ciyembekezo Canu

“Yembekezela Yehova.”—SAL. 27:14.

NYIMBO 144 Yang’ana pa Mphoto

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Kodi Yehova anatipatsa ciyembekezo cotani?

 YEHOVA anatipatsa ciyembekezo cabwino ngako ca moyo wamuyaya. Ena ciyembekezo cawo n’cokakhala kumwamba kwamuyaya monga zolengedwa zauzimu zosakhoza kufa. (1 Akor. 15:50, 53) Koma ambili ali na ciyembekezo codzakhala na moyo wosatha padziko lapansi, ali na thanzi labwino komanso acimwemwe. (Chiv. 21:3, 4) Kaya tikuyembekezela kukakhala na moyo kwamuyaya kumwamba kapena pano padziko lapansi, ciyembekezo cathu n’camtengo wapatali.

2. Kodi ciyembekezo cathu n’cozikika pa ciyani? Nanga n’cifukwa ciyani tikutelo?

2 Liwu lakuti “ciyembekezo” m’Baibo, lingatanthauze “kuyembekezela zinthu zabwino zimene zidzacitika.” Ciyembekezo cathu ca zam’tsogolo n’cotsimikizika, cifukwa cimacokela kwa Yehova. (Aroma 15:13) Tidziŵa zimene iye anatilonjeza, komanso kuti amakwanilitsa zimene walonjezazo. (Num. 23:19) Ndipo ndife otsimikiza kuti Yehova ni wofunitsitsa kucita zimene ananena, komanso ali na mphamvu zocita zimenezo. Conco, ciyembekezo cathu si maloto cabe kapena nkhambakamwa ayi. Koma n’cozikika pa umboni weniweni.

3. Kodi tikambilane ciyani m’nkhani ino? (Salimo 27:14)

3 Atate wathu wakumwamba amatikonda, ndipo amafuna kuti tizim’khulupilila. (Ŵelengani Salimo 27:14.) Ciyembekezo cathu mwa Yehova cikakhala colimba, tidzakwanitsa kupilila mayeso alionse amene tingakumane nawo, na kukhalabe olimba komanso acimwemwe. Lomba, tiyeni tione mmene ciyembekezo cathu cimatitetezela. Koma coyamba, tikambilane mmene ciyembekezo cathu cilili ngati nangula komanso cisoti. Kenako, tikambilanenso mmene tingalimbitsile ciyembekezo cathu.

CIYEMBEKEZO CATHU CILI NGATI NANGULA

4. Kodi ciyembekezo cathu cili ngati nangula motani? (Aheberi 6:19)

4 M’kalata imene analembela Aheberi, mtumwi Paulo anayelekezela ciyembekezo cathu na nangula. (Ŵelengani Aheberi 6:19.) Popeza iye anali kuyenda ulendo wa pamadzi kaŵili-kaŵili, anali kudziŵa kuti nangula amagwilitsidwa nchito kuti boti isatengeke. Tsiku lina, iye ali pa ulendo m’boti, pa nyanja panacitika cimphepo camkuntho. Mkati mwa cimphepoco, iye anaona amalinyelo (oyendetsa boti) akuponya nangula panyanja kuti boti isatengeke n’kukawomba miyala. (Mac. 27:29, 39-41) Monga mmene nangula amathandizila boti kuti isamatengeketengeke, ciyembekezo cathu naconso cimatithandiza kukhazikika, kuti tisatengeke n’kucoka kwa Yehova tikakumana na mavuto. Ciyembekezo cathu colimba cimatithandiza kusasunthika pokumana na mavuto okhala ngati cimphepo camkuntho, cifukwa timadziŵa kuti zinthu zidzakhala bwino m’tsogolo. Kumbukilani kuti Yesu anakambilatu kuti tidzazunzidwa. (Yoh. 15:20) Conco, kuganizila mphoto imene anatilonjeza m’tsogolo kudzatithandiza kusasunthika pa umoyo wathu wacikhristu.

5. Kodi ciyembekezo cinam’thandiza bwanji Yesu pamene anayang’anizana na imfa?

5 Onani mmene ciyembekezo cinathandizila Yesu kuimabe nji, mosasamala kanthu za imfa yoŵaŵa imene inali patsogolo pake. Pa Pentekosite mu 33 C.E., mtumwi Petulo anagwila mawu ulosi wa m’buku la Masalimo, wofotokoza mmene Yesu analili wodekha komanso wacidalilo. Iye anati: “Ine ndidzakhala ndi ciyembekezo, cifukwa simudzasiya moyo wanga m’Manda, ndipo simudzalola kuti thupi la wokhulupilika wanu livunde. . . . Cifukwa ca nkhope yanu ndidzakhala ndi cimwemwe cosefukila.” (Mac. 2:25-28; Sal. 16:8-11) Ngakhale kuti Yesu anali kudziŵa kuti adzafa, iye anali na ciyembekezo cotsimikizika mwa Mulungu kuti adzamuukitsa, komanso kuti adzabwelela kumwamba kukakhalanso na Atate wake.—Aheb. 12:2, 3.

6. Kodi m’bale wina anati ciyani za ciyembekezo?

6 Ciyembekezo cathu cimeneci cathandiza abale na alongo oculuka kupilila mayeso. Mwacitsanzo, onani citsanzo ici ca m’bale wina wokhulupilika dzina lake Leonard Chinn, wa ku England. Panthawi ya nkhondo yoyamba ya padziko lonse, iye anaponyedwa m’ndende cifukwa cokana kuloŵa usilikali. Kwa miyezi iŵili anakhala m’cipinda cayekha ku ndendeko. Pambuyo pake, anayamba kum’gwilitsa nchito yakalavulagaga. Iye anati: “Zimene napitamo zanithandiza kudziŵa kuti ciyembekezo n’cofunikila kwambili kuti tipilile. Tili na citsanzo ca Yesu, atumwi, na aneneli, cimene tingatengeleko. Tilinso na malonjezo abwino kwambili a m’Baibo. Zonsezi zimatipatsa ciyembekezo cabwino ca zam’tsogolo, komanso zimatilimbitsa kuti tipile.” Ciyembekezo cinali ngati nangula kwa m’bale Leonard. Ndipo cingakhalenso nangula kwa ife.

7. Kodi mayeso amalimbitsa bwanji ciyembekezo cathu? (Aroma 5:3-5; Yakobo 1:12)

7 Ciyembekezo cathu cimalimbilako tikapilila mayeso, komanso tikaona mmene Yehova watithandizila na kutiyanja. (Ŵelengani Aroma 5:3-5; Yakobo 1:12.) Inde, ciyembekezo cathu cimakhala colimba kwambili kuposa pamene tinalandila coonadi poyamba. Satana amafuna kuti tigonje pa mayeso. Koma na thandizo la Yehova tingathe kupilila mayeso alionse.

CIYEMBEKEZO CATHU CILI NGATI CISOTI COLIMBA

8. Kodi ciyembekezo cathu cili monga cisoti motani? (1 Atesalonika 5:8)

8 Baibo imayelekezelanso ciyembekezo cathu na cisoti colimba. (Ŵelengani 1 Atesalonika 5:8.) Msilikali pa nkhondo amavala cisoti colimba kuti ateteze mutu wake. Pa nkhondo yathu yauzimu, tiyenela kuteteza maganizo athu ku misampha ya Satana. Iye amagwilitsa nchito zinthu zosiyana-siyana kuti atiike pa mayeselo, n’colinga cakuti asokoneze maganizo athu. Monga mmene cisoti cimatetezela mutu wa msilikali, naconso ciyembekezo cathu cimateteza maganizo athu kuti tikhalebe okhulupilika kwa Yehova.

9. Kodi pamakhala zotulukapo zotani ngati anthu alibe ciyembekezo?

9 Ciyembekezo cathu codzakhala na moyo kwamuyaya, cimatithandiza kukhala anzelu komanso ozindikila. Koma ciyembekezo cimeneci cikafooka, ndipo ngati maganizo athu akhazikika pa zokhumba mtima wathu, tingaiŵale za ciyembekezo cathu cimeneco. Onani citsanzo ici ca Akhristu ena mu mzinda wakale wa Korinto. Iwo anasiya kukhulupilila lonjezo lofunika kwambili la Mulungu, limene ni ciyembekezo ca ciukitso. (1 Akor. 15:12) Paulo analemba kuti anthu amene sakhulupilila za ciukitso, amangokhalila zalelo basi. (1 Akor. 15:32) Masiku ano, anthu ambili amene sakhulupilila malonjezo a Mulungu, saganizila za m’tsogolo, ndipo amacita zonse zotheka kuti akhale na umoyo wabwino pali pano. Koma ife timakhulupilila malonjezo a Mulungu onena zam’tsogolo. Ciyembekezo cathu cili ngati cisoti cophiphilitsa cimene cimateteza maganizo athu, na kutithandiza kupewa umoyo wongofuna kudzisangalatsa, umene ungawononge ubale wathu na Yehova.—1 Akor. 15:33, 34.

10. Kodi ciyembekezo cimatiteteza bwanji ku maganizo olakwika?

10 Ciyembekezo cathu cingatithandizenso kupewa maganizo akuti sitingathe kukondweletsa Yehova olo pang’ono. Mwacitsanzo, ena angamaganize kuti: ‘N’zosatheka ine kukhala pakati pa anthu amene adzakhala na moyo kwamuyaya. Siningakwanitse kucita zimene Mulungu amafuna.’ Kumbukilani kuti maganizo amenewa, ni amene Elifazi wotonthoza wabodza anawagwilitsa nchito pokamba na Yobu. Elifazi anati: “Kodi munthu ndani kuti akhale woyela?” Ponena za Mulungu, iye anati: “Iyetu alibe cikhulupililo mwa angelo ake, ndipo kumwamba si koyela m’maso mwake.” (Yobu 15:14, 15) Ili linali bodza lamkunkhuniza! Kumbukilani kuti Satana amafuna kuti muziganiza conco. Iye adziŵa kuti mukamaganizila kwambili zimenezi, mudzataya ciyembekezo canu. Conde, kanizani mabodza amenewo, ndipo ikani maganizo anu pa malonjezo a Yehova. Musakayikile ngakhale pang’ono kuti iye afuna kuti mukakhale na moyo kwamuyaya, komanso kuti adzakuthandizani kucita zimenezo.—1 Tim. 2:3, 4.

MUSALEKE KULIMBITSA CIYEMBEKEZO CANU

11. N’cifukwa ciyani tiyenela kuleza mtima pamene tikuyembekezela malonjezo a Mulungu?

11 Nthawi zina, n’covuta kusungabe ciyembekezo cathu cili colimba. Tingalephele kukhala oleza mtima pamene tikuyembekezela Mulungu kuti akwanilitse zimene anatilonjeza. Komabe, Yehova ni wamuyaya, ndipo nthawi amaiona mosiyana na mmene ife timaionela. (2 Pet. 3:8, 9) Iye adzakwanilitsa malonjezo ake, mwina osati pa nthawi imene ife tikufuna. Ndiye n’ciyani cingatithandize kulimbitsabe ciyembekezo cathu pamene tikuyembekezela Mulungu moleza mtima kuti akwanilitse malonjezo ake?—Yak. 5:7, 8.

12. Malinga na Aheberi 11:1, 6, kodi tiyenela kucita ciyani kuti tikhale na ciyembekezo?

12 Tikakhalabe pa ubwenzi wabwino na Yehova, amene adzakwanilitsa zimene anatilonjeza, ciyembekezo cathu cidzakhala colimba. Ndipo kuti tikhale na ciyembekezo, tiyenela kukhulupilila kuti Yehova alikodi, komanso kuti “amapeleka mphoto kwa anthu omufuna-funa ndi mtima wonse.” (Ŵelengani Aheberi 11:1, 6.) Tikamaona kuti Yehova ni weniweni kwa ife, cidalilo cathu cakuti iye adzakwanilitsa zonse zimene analonjeza cadzalimbilako. Tiyeni tikambilane zinthu zimene zingatithandize kulimbitsa ubale wathu na Yehova, kuti ciyembekezo cathu cikhalebe colimba.

Kupemphela na kusinkhasinkha kudzathandiza kuti ciyembekezo cathu cikhalebe colimba (Onani ndime 13-15) *

13. Kodi tingayandikane naye motani Mulungu?

13 Tizipemphela kwa Yehova na kuŵelenga Mawu ake. Olo kuti Yehova sitingathe kumuona, tingamuyandikile. Tingakambe naye m’pemphelo, tili na cidalilo cakuti adzatimvetsela. (Yer. 29:11, 12) Timamvetsela kwa Mulungu pamene tiŵelenga Baibo na kusinkhasinkha zimene taŵelenga. Ndipo ciyembekezo cathu cimalimbilako tikamaŵelenga za mmene Yehova anathandizila anthu m’nthawi zakale amene anali okhulupilika kwa iye. Inde, zonse zimene zinalembedwa m’Baibo, “zinalembedwa kutilangiza, kuti mwa cipililo ndi citonthozo ca malembo, tikhale ndi ciyembekezo.”—Aroma 15:4. Buku Lopatulika.

14. N’cifukwa ciyani tiyenela kusinkhasinkha zimene Yehova anacitilapo anthu ena?

14 Tizisinkhasinkha mmene Yehova anakwanilitsilapo malonjezo ake. Ganizilani zimene Mulungu anacitila Abulahamu na Sara. Iwo anafika pa msinkhu wakuti sakanabeleka ana. Koma Mulungu anawalonjeza kuti adzakhala na mwana. (Gen. 18:10) Kodi Abulahamu anacita ciyani? Baibo imati: “[Anali na] cikhulupililo cakuti adzakhala tate wa mitundu yambili.” (Aroma 4:18) Malinga na kaonedwe ka anthu, zimenezo zinaoneka zosatheka. Koma Abulahamu anali na cidalilo cakuti Yehova adzakwanilitsa lonjezo lake. Munthu wokhulupilika ameneyu sanagwilitsidwe mwala. (Aroma 4:19-21) Nkhani zotelo zimatiphunzitsa kuti nthawi zonse tingam’dalile Yehova kuti adzakwanilitsa malonjezo ake, ngakhale tione ngati n’zosatheka.

15. N’cifukwa ciyani tiyenela kuganizila zimene Mulungu waticitila?

15 Ganizilani zimene Yehova wakucitilani inuyo pacanu. Ganizilani cabe mmene mwapindulila na malonjezo a m’Mawu a Mulungu amene akwanilitsidwa kale. Mwacitsanzo, Yesu analonjeza kuti Atate wake adzakupatsani zofunikila pa umoyo. (Mat. 6:32, 33) Cina, Yesu anakutsimikizilani kuti Yehova adzakupatsani mzimu woyela mukam’pempha. (Luka 11:13) Yehova wakwanilitsadi malonjezo amenewa. Mungaganizilenso malonjezo ena amene iye wakwanilitsa pa inu. Mwacitsanzo, anakulonjezani kuti adzakukhululukilani, kukutonthozani, na kukudyetsani mwauzimu. (Mat. 6:14; 24:45; 2 Akor. 1:3) Conco, mukamaganizila zimene Mulungu wakucitilani, ciyembekezo canu pa zimene adzakucitilani m’tsogolo cidzalimbilako.

KONDWELANI NA CIYEMBEKEZOCO

16. N’cifukwa ciyani ciyembekezo ni mphatso ya mtengo wapatali?

16 Ciyembekezo cathu codzakhala na moyo kwamuyaya, ni mphatso yamtengo wapatali yocokela kwa Mulungu. Tiyembekezela mwacidwi tsogolo labwino limeneli, limene ndife otsimikiza kuti lidzabweladi. Ciyembekezoci cili monga nangula. Cimatithandiza kuti tisasunthike polimbana na mayeso, pozunzidwa, ngakhale poyang’anizana na imfa. Cilinso ngati cisoti colimba cimene cimateteza maganizo athu kuti tikanize zosayenela na kumamatila ku zabwino. Ciyembekezo cathu cozikika pa Baibo cimeneci, cimatiyandikilitsa kwa Mulungu, komanso cimaonetsa kukula kwa cikondi cathu pa iye. Timapindula kwambili tikamasunga ciyembekezo cathu cili colimba.

17. N’cifukwa ciyani ciyembekezo cathu cimatipangitsa kukhala okondwela?

17 M’kalata yake yopita kwa Aroma, mtumwi Paulo anatilimbikitsa kuti: “Kondwelani ndi ciyembekezoco.” (Aroma 12:12) Paulo anakondwela na ciyembekezoci cifukwa anali wotsimikiza kuti akakhalabe wokhulupilika, adzakhala na moyo kwamuyaya kumwamba. Nafenso tingakondwele na ciyembekezo cathu cifukwa sitikayikila kuti Yehova adzakwanilitsa malonjezo ake. Wamasalimo analemba kuti: “Wodala ndi munthu . . . amene ciyembekezo cake cili mwa Yehova Mulungu wake, . . . Wosunga coonadi mpaka kalekale.”—Sal. 146:5, 6.

NYIMBO 139 Yelekeza Uli M’dziko Latsopano

^ Yehova anatipatsa ciyembekezo cabwino ngako ca zam’tsogolo. Ciyembekezo cimeneci cimatilimbikitsa, na kutithandiza kupewa kumangoganizila za mavuto athu. Cimatithandizanso kukhalabe okhulupilika kwa Mulungu, kaya tikumane na mavuto otani. Cina, ciyembekezo cimeneci cimatiteteza ku zinthu zimene zingasokoneze maganizo athu. Monga tionele m’nkhani ino, zonsezi ni zifukwa zabwino zotithandiza kulimbitsabe ciyembekezo cathu cimeneci.

^ MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Monga mmene cisoti colimba cimatetezela mutu wa msilikali, komanso mmene nangula amathandizila kuti boti isatengeke na mafunde kapena cimphepo, ciyembekezo cathu naconso cimateteza maganizo athu, na kutithandiza kukhala osasunthika tikakumana na mayeso. Mlongo akupemphela kwa Yehova mwacidalilo. M’bale akusinkhasinkha mmene Mulungu anakwanilitsila malonjezo ake kwa Abulahamu. M’bale winanso akuganizila mmene Mulungu wamudalitsila.