Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 45

Yamikilani Mwayi Wanu Wolambila Yehova M’kacisi Wake Wauzimu

Yamikilani Mwayi Wanu Wolambila Yehova M’kacisi Wake Wauzimu

“Lambilani Iye amene anapanga kumwamba [ndi] dziko lapansi.”—CHIV. 14:7.

NYIMBO 93 Dalitsani Misonkhano Yathu

ZIMENE TIKAMBILANE a

1. Kodi mngelo akunena ciyani? Kodi zimenezo zitanthauza ciyani kwa ife?

 NGATI mngelo afuna kukamba nanu, kodi mungamvetsele kwa iye? Masiku ano, mngelo akulankhula kwa anthu a “kudziko lililonse, fuko lililonse, cinenelo ciliconse, ndi mtundu uliwonse.” Iye akuti, “Opani Mulungu ndi kum’patsa ulemelelo . . . Lambilani Iye amene anapanga kumwamba, [ndi] dziko lapansi.” (Chiv. 14:​6, 7) Yehova ni Mulungu woona yekha amene aliyense afunika kumulambila. Ndife oyamikila ngako kuti iye watipatsa mwayi wamtengo wapatali womulambila m’kacisi wake waukulu wauzimu!

2. Kodi kacisi wauzimu wa Yehova n’ciyani? (Onaninso danga lakuti “ Zimene Kacisi Wauzimu wa Yehova Saimila.”)

2 Kodi kacisi ameneyu n’ciyani? Ndipo n’kuti kumene tingapeze mfundo zofotokoza kacisiyo? Kacisi wauzimu si kacisi weniweni wocita kumangidwa. Ni dongosolo la Yehova lomulambila movomelezeka pa maziko a nsembe ya Yesu Khristu. Mtumwi Paulo anafotokoza dongosolo limeneli kwa Akhristu Aciheberi a m’zaka za zana loyamba a ku Yudeya. b

3-4. Kodi ni khawa iti imene Paulo anali nayo kwa Akhristu Aciheberi? Nanga anawathandiza bwanji?

3 N’cifukwa ciyani Paulo analembela kalata Akhristu Aciheberi a ku Yudeya? Mwina pali zifukwa ziŵili zazikulu. Coyamba, kuti awalimbikitse. Ambili a iwo analeledwa m’cipembedzo ca Ciyuda. Atsogoleli a cipembedzo cawo cakale, mwina anali kuwanyoza cifukwa cokhala Akhristu. Cifukwa cakuti Akristu analibe kacisi wolambililamo, iwo analibe guwa lopelekelapo nsembe kwa Mulungu, analibenso ansembe owatumikila. Izi zikanalefula ophunzila a Khristu na kufooketsa cikhulupililo cawo. (Aheb. 2:1; 3:​12, 14) Ena a iwo akanayesedwa kuti abwelele kucipembedzo cawo ca Ciyuda.

4 Caciŵili, Paulo anaonetsa kuti Akristu Aciheberi sanali kuyesetsa kuti amvetse mfundo zatsopano kapena kuti ziphunzitso zozama zimene ni “cakudya cotafuna” copezeka m’mawu a Mulungu. (Aheb. 5:​11-14) Mwacionekele, ena a iwo anali kutsatilabe Cilamulo ca Mose. Komabe, Paulo anafotokoza kuti nsembe zimene anali kupeleka pansi pa Cilamulo sizinali kufafaniza macimo awo. Pa cifukwa cimeneci, Cilamulo cinali ‘citacotsedwa.’ Conco, Paulo anafuna kuwaphunzitsa ziphunzitso zozama. Ndiye cifukwa cake iye anawakumbutsa za “ciyembekezo cabwino” cozikika pa nsembe ya Yesu cimene cikanawathandizadi ‘kuyandikila kwa Mulungu.’—Aheb. 7:​18, 19.

5. N’zinthu ziti zopezeka m’buku la Aheberi zimene tiyenela kumvetsa? Ndipo n’cifukwa ciyani?

5 Paulo anafotokozela Akhristu anzake Aciheberi cifukwa cake kulambila kwa Cikhristu kunali kofunika kwambili kuposa kulambila kumene anali kucita kale. Dongosolo la cipembedzo ca Ciyuda linali cabe “mthunzi wa zimene zinali kubwela, koma zenizeni zake zili mwa Khristu.” (Akol. 2:17) Mthunzi si cinthu ceniceni ayi koma umaimila cinthu cimene cimapanga mthunziwo. Mofananamo, dongosola la cipembedzo ca Ciyuda unali cabe mthunzi wa zinthu zenizeni zimene zinali kubwela. Tiyenela kumvetsa dongosolo limene Yehova wakhazikitsa kuti macimo athu akhululukidwe kuti tizimulambila m’njila yovomelezeka. Tiyeni tiyelekezele “mthunzi” (dongosolo la kulambila la Ciyuda), na “zinthu zenizeni” (m’kalambilidwe ka Cikhristu), malinga na mmene buku la Aheberi limafotokozela. Izi zizatithandiza kudziŵa bwino kacisi wauzimu na mmene amatikhudzila.

CIHEMA

6. Kodi cihema cinali kugwila nchito yanji?

6 Mthunzi wa zakutsogolo. Mfundo yaikulu ya Paulo inali pa cihema cimene cinakozedwa na Mose mu 1512 B.C.E. (Onani danga la kuti “Dongosolo la Kulambila la Ciyuda—Komanso la Cikhristu.”) Cihema cokumanako, cinapangidwa na teti ndipo Aisiraeli anali kucinyamula pomwe anali kusamuka kupita ku malo ena. Iwo anaciseŵenzetsa kwa zaka pafupfupi 500 mpaka pamene anamanga kacisi ku Yerusalemu. (Eks. 25:​8, 9; Num. 9:22) “Cihema cokumanako” anali malo amene Aisiraeli anali kuseŵenzetsa polankhula na Mulungu, popeleka nsembe kwa iye, komanso pom’lambila. (Eks. 29:​43-46) Komabe, cihema cinaimilanso cinthu cacikulu comwe cinali kudzabwela kwa Akhristu.

7. Ni liti pamene kacisi wauzimu anakhazikitsidwa?

7 Zenizeni zake m’nyengo ya Cikhristu. Cihema cakale cinali “mthunzi wa zinthu zakumwamba,” ndipo cinaimila kacisi wauzimu waukulu wa Yehova. Paulo anati “Cihema cimeneco cinali cifanizilo ca nthawi yoikidwilatu imene tsopano yafika.” (Aheb. 8:5; 9:9) Conco panthawi imene anali kulembela kalata Aheberi, kacisi wauzimu anali atakhala kale weniweni kwa Akhristu. Kacisi ameneyu anakhazikitsidwa mu 29 C.E. M’caka cimeneco, Yesu anabatizidwa, anazozedwa na mzimu woyela ndipo anayamba kutumikila Yehova monga “mkulu wansembe” m’kacisi wauzimu cAheb. 4:14; Mac. 10:​37, 38.

MKULU WA ANSEMBE

8-9. Malinga na Aheberi 7:​23-27, ni kusiyana kwakukulu kuti kumene kulipo pakati pa Mkulu Wansembe wa m’nthawi ya Aisiraeli komanso Mkulu wa Ansembe woposa onse Yesu Khristu?

8 Mthunzi wa zakutsogolo. Mkulu wa ansembe anapatsidwa udindo woimilako anthu kwa Mulungu. Mkulu wa ansembe woyamba Aroni, anadzozedwa na Yehova pamene anapatulila cihema cokumanako. Kamabe, monga anakambila Paulo, “panayenela kukhala ansembe ambili oloŵana m’malo cifukwa imfa inali kuwaletsa kupitiliza unsembe wawo.” d (Ŵelengani Aheberi 7:​23-27.) Cifukwa cakuti anali opanda ungwilo, akulu ansembe amenewa anayenela kupeleka nsembe cifukwa ca macimo awo. Pamenepa paonetsa kusiyana kwakukulu komwe kulipo pakati pa akulu ansembe a mu Isiraeli komanso Mkulu wa Ansembe wopambana onse, Yesu Khristu.

9 Zenizeni zake m’nyengo ya Cikhristu. Mkulu wathu Wansembe, Yesu Khristu “ndi wanchito wotumikila . . . m’cihema ceniceni, comangidwa ndi Yehova, osati munthu.” (Ahe. 8:​1, 2) Paulo anafotokoza kuti “cifukwa cokhala ndi moyo kosatha [Yesu] palibe womuloŵa m’malo pa unsembe wake.” Anawonjezela kuti Yesu ni “wosaipitsidwa wosiyana ndi anthu ocimwa” ndipo mosiyana na akulu ansembe a mu Isiraeli, “iye safunikila kupeleka tsiku ndi tsiku nsembe zamacimo ake.” Lomba tiyeni tione kusiyana pakati pa maguwa a nsembe na nsembe m’nthawi ya Ayuda komanso m’nthawi ya Akhristu.   

MAGUWA ANSEMBE KOMANSO NSEMBE

10. Kodi kupeleka nsembe pa guwa la mkuwa kunali kuimila ciyani?

10 Mthunzi wa zakutsogolo. Pakhomo pa cihema cokumanako panali guwa lansembe lamkuwa pomwe anali kupelekelapo nsembe zanyama kwa Yehova. (Eks. 27:​1, 2; 40:29) Komabe, nsembezo sizinali kuthandiza anthuwo kuti akukhululukidwe macimo awo kothelatu. (Aheb. 10:​1-4) Nsembe zanyama zimene zinali kupelekedwa mobweleza-bweleza zinaimila nsembe imodzi imene inali kudzayeletselatu mtundu wa anthu ku macimo onse.

11. Ni guwa la nsembe liti limene Yesu anapelekelapo thupi lake nsembe? (Aheberi 10:​5-7, 10)

11 Zenizeni zake m’nyengo ya Cikhristu. Yesu anadziŵa kuti Yehova anam’tuma pa dziko lapansi kuti adzapeleke moyo wake nsembe kuwombola mtundu wa anthu. (Mat. 20:28) Conco, pa ubatizo wake, iye anadzipeleka kuti acite cifunilo ca Yehova. (Yoh. 6:38; Agal. 1:4) Ndipo anapeleka moyo wake pa guwa lophiphilitsa limene linaimila “cifunilo” ca Mulungu cakuti Mwana wake apeleke nsembe moyo wake wagwilo. Yesu anapeleka moyo wake “kamodzi kokha” kuti aphimbe kothelatu macimo ya aliyense amene amaonetsa cikhulupililo mwa Khristu. (Ŵelengani Aheberi 10:​5-7, 10.) Cotsatila, tiyeni tikambilane tanthauzo ya mbali zamkati mwa cihema.

MALO OYELA NA MALO OYELA KOPOSA

12. Ndani anali kuloledwa kuloŵa m’zipinda za cihema?

12 Mthunzi wa zakutsogolo. Akacisi amene anadzamangidwa ku Yerusalemu anali ofanana kwambili na cihema cokumanako. Mkati mwake munali zipinda ziŵili—“Malo Oyela” na “Malo Oyela Koposa”—zomwe zinali kulekanitsidwa na nsalu yochinga. (Aheb. 9:​2-5; Eks. 26:​31-33) Mkati mwa Malo Oyela munali coikapo nyale cagolide, guwa la nsembe lofukizilapo, komanso thebulo yoikapo mkate wacionetselo. “Ansembe odzozedwa” okhawo ni amene anali kuloledwa kukagwila nchito zopatulika m’Malo Oyela. (Num. 3:​3, 7, 10) Malo Oyela Koposa munali likasa la pangano lagolide lomwe linali kuimila kukhalapo kwa Yehova. (Eks. 25:​21, 22) Mkulu wansembe yekha ndiye anali kuloledwa kuloŵa m’Malo Oyela Koposa kamodzi pa caka pa Tsiku la Mwambo Wophimba Macimo. (Lev. 16:​2, 17) Caka ciliconse iye anali kuloŵa m’malo amenewa na magazi anyama kuti akaphimbe macimo ake, komanso ya mtundu wonse wa Isiraeli. Patapita nthawi, Yehova anaseŵenzetsa mzimu wake woyela, kuvumbula tanthauzo la zimenezi.—Aheb. 9:​6-8. e

13. Kodi Malo Oyela na Malo Oyela Koposa aimila ciyani m’dongosolo la kulambila la Cikhristu?

13 Zenizeni zake m’nyengo ya Cikhristu. Ophunzila a Khristu oŵelengeka anadzozedwa na mzimu woyela, ndipo amasangalala kukhala paubale wapadela na Yehova. A 144,000 amenewa azikatumikila pamodzi na Yesu kumwamba monga ansembe. (Chiv. 1:6; 14:1) Malo Oyela m’cihema amaimila kudzozedwa kwawo monga ana a Mulungu pa dziko lapansi. (Aroma 8:​15-17) Malo Oyela Koposa amaimila kumwamba kumene Yehova amakhala. “Nsalu yochinga” imene inalekanitsa Malo Oyela na Malo Oyela Koposa inali kuimila thupi la Yesu laumunthu limene linali kumulepheletsa kuloŵa kumwamba monga Mkulu Wansembe woposa onse wakacisi wauzimu. Pomwe Yesu anapeleka nsembe thupi lake laumunthu, anatsegulila Akhristu odzozedwa njila yopita kumwamba. Iwo ayenela kusiya matupi awo aumunthu kuti akalandile mphoto yawo kumwamba. (Aheb. 10:​19, 20; 1 Akor. 15:50) Yesu ataukitsidwa analoŵa m’Malo Oyela Koposa a kacisi wauzimu, kumenenso Akhristu odzozedwa amaloŵa kuti akakhale naye.

14. Malinga na Aheberi 9:​12, 24-26, n’ciyani cipangitsa kacisi wauzimu wa Yehova kukhala wopambana?

14 Pofika pano, taona kuti makonzedwe a Yehova akulambila koyela ni apadela kwambili cifukwa ca nsembe ya dipo komanso unsembe wa Yesu Khristu. Mkulu wansembe mu Isiraeli anali kuloŵa m’Malo Oyela Koposa opangidwa na anthu atanyamula magazi a nsembe za nyama koma Yesu analoŵa “kumwamba kwenikweniko” komwe ni malo oyela koposa, kuti akaonekele pamso pa Yehova. Kumeneko, iye anapeleka mtengo wa moyo wake wangwilo m’malo mwa ife kuti “acotse ucimo kudzela mu nsembe yake.” (Ŵelengani Aheberi 9:​12, 24-26.) Nsembe ya Yesu imacotselatu ucimo kothelatu. Monga mmene tidzaonela, kaya ciyembekezo cathu n’cokakhala kumwamba kapena kudzakhala padziko lapansi, tonsefe tingalambile Yehova m’kacisi wake wauzimu.

MABWALO

15. Kodi ndani anali kutumikila pa mabwalo a cihema?

15 Mthunzi wa zakutsogolo. Cihema cinali na bwalo lomwe linali locingidwa na mpanda mmene ansembe anali kucitila utumiki wawo. Guwa lansembe lamkuwa lofukizilapo nsembe linali m’bwalo limeneli pamodzi na beseni lamkuwa lomwe ansembe anali kuseŵenzetsa podziyeletsa asanayambe kugwila nchito yawo yopatulika. (Eks. 30:​17-20; 40:​6-8) Akacisi omwe anadzamangidwa pambuyo pake anali na bwalo lakunja lomwe anthu amene sanali ansembe anali kuimililamo polambila Mulungu.

16. Kodi ndani amatumikila pa bwalo lakunja komanso lamkati pa kacisi wauzimu?

16 Zenizeni zake m’nyengo ya Cikhristu. Otsalila odzodzedwa amatumikila mokhulupilika padziko lapansi m’bwalo lamkati la kacisi wauzimu asanapite kukatumikila monga ansembe na Yesu kumwamba. Beseni la madzi lomwe linali pacihema limakumbutsa odzodzedwa komanso Akhristu onse kuti ayenela kukhala oyela m’makhalidwe komanso mwauzimu. Koma kodi “a khamu lalikulu” amene amacilikiza abale odzozedwa a Khristu, amalambilila kuti? Mtumwi Yohane anawaona “ataimilila pamaso pa mpando wacifumu,” limene ni bwalo lakunja la kacisi wa Yehova, komwe “akumucitila utumiki wopatulika usana ndi usiku m’kacisi wake.” (Chiv. 7:​9, 13-15) Ndife oyamikila ngako kuti tili na malo m’makozedwa a Yehova akulambila koyela!

MWAYI WATHU WOLAMBILA YEHOVA

17. Kodi tili na mwayi wopeleka nsembe ziti kwa Yehova?

17 Masiku ano Akhristu onse ali na mwayi wopeleka nsembe kwa Yehova mwa kuseŵenzetsa nthawi yawo, mphamvu zawo, komanso cuma cawo, popititsa patsogolo ucifumu wa Mulungu. Mtumwi Paulo anauza Akhristu Aciheberi kuti “tiyeni nthawi zonse tizitamanda Mulungu. Tizicita zimenezi monga nsembe imene tikupeleka kwa Mulungu, yomwe ndi cipatso ca milomo yathu. Timagwilitsa nchito milomo imeneyi polengeza dzina lake kwa anthu ena.” (Aheb. 13:15) Tingaonetse kuti timayamikila mwayi wathu wolambila Yehova mwa kum’patsa nsembe zabwino koposa.

18. Malinga na Aheberi 10:​22-25, kodi tiyenela kupitiliza kucita ciyani? Nanga sitiyenela kuiŵala ciyani?

18 Ŵelengani Aheberi 10:​22-25. Cakumapeto kwa kalata imene Paulo analembela Aheberi, anachula zinthu zina zimene sitifunika kunyalanyaza pa kulambila kwathu. Zimene ziphatikizapo kumufikila Yehova m’pemphelo, kulengeza poyela ciyembekezo cathu, kusonkhana capamodzi monga mpingo, komanso kulimbikitsana ‘makamaka pamene tiukuona kuti tsiku la [Yehova] likuyandikila.’ Cakumapeto kwa buku la Chivumbulutso, mngelo wa Yehova anachula mawu akuti: “Lambilani Mulungu,” kaŵili konse pofuna kuwagogomezela! (Chiv. 19:10; 22:9) Tiyeni ticite zonse zotheka kuti tisaiŵale mfundo yozama ya coonadi yonena za kacisi wauzimu wa Yehova, komanso mwayi wamtengo wapatali umene tili nawo wolambila Mulungu wathu wamkulu!

NYIMBO 88 N’dziŵitseni Njila Zanu

a Cimodzi mwa ziphunzitso zozama za mawu a Mulungu n’cokhudza kacisi wauzimu wa Yehova. Kodi kacisi ameneyu n’ciyani? Nkhani ino ifotokoza mfundo zopezeka m’buku la m’Baibo la Aheberi zofotokoza kacisi ameneyu. Lolani kuti nkhani ino ikulitse ciyamikilo canu cimene muli naco pa mwayi wanu wolambila Yehova.

b Kuti mupeze mfundo zokuthandizani kumvetsa buku la Aheberi, onelelani vidiyo yakuti Mfundo Zokhudza Buku la Aheberi pa jw.org

c M’malemba Acigiriki Acikhristu ni buku la Aheberi lokha limene limachula Yesu kuti ni Mkulu wa Ansembe.

d Malinga na buku lina, zioneka kuti panali akulu ansembe 84 amene anatumikila mu Isiraeli kudzafika panthawi pamene kacisi wa ku Yerusalemu anawonongedwa mu 70 C.E.

e Kuti mudziŵe tanthauzo la zimene mkulu wa ansembe anali kucita pa tsiku lophimba macimo, onelelani vidiyo yakuti The Tent pa pa jw.org ku cizungu.

g Onani bokosi yakuti “Mmene Mzimu Woyera Unaululira Tanthauzo la Kachisi Wauzimu” mu Nsanja ya Olonda ya July 15, 2010.