Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 44

Yesetsani Kumvetsa Milingo Yonse ya Mawu a Mulungu

Yesetsani Kumvetsa Milingo Yonse ya Mawu a Mulungu

Mungathe “kudziŵa bwino m’lifupi ndi m’litali ndi kukwela ndi kuzama.”—AEF. 3:18.

NYIMBO 95 Kuwala Kuwonjezeleka

ZIMENE TIKAMBILANE a

1-2. Kodi njila yabwino yoŵelengela Baibo ni it? Fotokozani citsanzo.

 YELEKEZANI kuti mufuna kugula nyumba. Kodi mungafune kuona ciyani musanagule nyumbayo? Kodi mungakutile na pikica yoonetsa kutsogolo kwake cabe? Mosakayikila mungafune kudzionela nokha nyumbayo, kuizungulila na kuona milingo yake yonse. Mwina mungafunenso kuona pulani yake kuti mudziŵe mmene anaimangila. Mosakaikila, mungafune kufufuza zambili za nyumbayo kuti muidziŵe bwino musanaigule.

2 Tiyenela kucita cimodzi-modzi poŵelenga na kuphunzila Baibo. Wolemba mabuku wina anayelekezela uthenga wa m’Baibo na “nyumba ya nsanjika yaitali yomangidwa pa pamaziko akuya.” Ndiye tingacite ciyani kuti timvetse mbali zonse za m’Baibo? Mukamaŵelenga mothamanga, mungadziŵe mfundo zocepa cabe—“mfundo zoyambilila za m’mawu opatulika a Mulungu.” (Aheb. 5:12) M’malo mwake, monga mmene mungacitile na nyumba, “fufuzani” kuti mumvetse mfundo zamtengo wapatali. Njila yabwino koposa yoŵelengela mawu a Mulungu ni kuyesa kuona mmene mfundo zosiyana-siyana zikugwilizanila. Muziyesetsa kumvetsa zimene mumakhulupilila komanso cifukwa cake mumazikhulupilila.

3. Kodi mtumwi Paulo analimbikitsa Akhristu anzake kucita ciyani? Nanga n’cifukwa ciyani? (Aefeso 3:​14-19)

3 Kuti timvetse mbali zonse za mawu a Mulungu, tiyenela kuŵelenga mfundo zozama za coonadi. Mtumwi Paulo analimbikitsa Akhristu anzake kuti ayenela kuŵelenga mawu a Mulungu mwakhama ‘kuti athe kudziŵa bwino m’lifupi ndi m’litali ndi kukwela ndi kuzama’ kwa coonadi. Kucita zimenezi kunawathandiza ‘kuti azike mizu mokhazikika’ pa cikhulupililo. (Ŵelengani Aefeso 3:​14-19.) Ifenso tiyenela kucita cimodzi-modzi. Tiyeni tione zimene tingacite kuti timvetse mfundo zamtengo wapatali za m’Mawu a Mulungu.

FUFUZANI MFUNDO ZOZAMA ZA COONADI

4. Tingacite ciyani kuti timuyandikile Yehova? Pelekani zitsanzo.

4 Kwa ife Akhristu kungomvetsa ziphunzitso zoyambilila za m’Baibo si kokwanila. Mwathandizo la mzimu woyela, ndife ofunitsitsa kudziŵa “ngakhale zinthu zozama za Mulungu.” (1 Akor. 2:​9, 10) Pa phunzilo la inu mwini, bwanji osadziikila colinga cophunzila mfudo zozama za mawu a Mulungu kuti mumuyandikile kwambili Yehova? Mwacitsanzo, mungafufuze mmene Yehova anaonetsela cikondi kwa atumiki ake akale na kuona mmene izi zionetsela kuti amakukondani. Mungafufuze za dongosolo la kulambila Yehova m’nthawi ya Aisiraeli na kuliyelekezela na dongosolo la masiku ano. Kapena mungaŵelenge mozama maulosi amene Yesu anakwanilitsa ali padziko lapansi.

5. Kodi pali nkhani imene mungafune kuifufuza pa phunzilo lanu la munthu mwini?

5 Ophunzila Baibo ena akhama anapemphedwa kuti achule mfundo zozama za coonadi zimene angakonde kuphunzila m’mawu a Mulungu. Ena mwa mayankho awo aikidwa pa danga lakuti “ Zimene Mungacite pa Phunzilo la Inu Mwini.” Mungapeze cimwemwe pophunzila nkhani zimenezi poseŵenzetsa Buku Lofufuzila Nkhani la Mboni za Yehova. Kucita phunzilo la Baibo la inu mwini mozama kudzalimbikitsa cikhulupililo canu na kukuthandizani ‘kum’dziŵadi Mulungu.’ (Miy. 2:​4, 5) Lomba tiyeni tikambilane mfundo zozama za coonadi za m’Baibo zimene tingaphunzile.

MUZISINKHASINKHA MWAKUYA PA COLINGA CA MULUNGU

6. (a) Kodi pali kusiyana kotani pakati pa pulani na colinga? (b) N’cifukwa ciyani tingakambe kuti colinga ca Mulungu ponena za anthu na dziko la pansi ni “camuyaya”? (Aefeso 3:11)

6 Mwacitsanzo, ganizilani zimene Baibo imanena pa colinga ca Mulungu. Pali kusiyana kwakukulu pakati pa pulani na colinga. Pulani ili ngati njila yokutsogolelani kuti mukafike kumene mukufuna kupita. Ngakhale n’telo, pulani ingalephele ngati pali cina cake catseka njila imene mufuna kuseŵenzetsa. Koma colinga tingaciyelekezele na malo enieni amene tikufuna kupitako. Tidziŵa malo enieni amene tifuna kupitako, koma tingaseŵenzetse njila zosiyana-siyana kuti tifike kumeneko. N’zotheka kusintha njila imene tikuseŵenzetsa osati malo amene tikupitako. Ndife oyamikila kuti Yehova mwa pang’ono-pang’ono watiululila ‘colinga cake camuyaya’ m’Baibo. Yehova angaseŵenzetse njila iliyonse kuti akwanilitse colinga cake, cifukwa “anapanga ciliconse n’colinga.” (Miy. 16:4) Ndipo zotulukapo za nchito ya Yehova zimakhalapo kosatha. Kodi colinga ca Yehova n’ciyani? Nanga anapanga masinthidwe otani kuti acikwanilitse?

7. Pambuyo pakuti anthu oyamba am’pandukila, kodi Yehova anapanga masinthidwe otani kuti akwanilitse colinga cake? (Mateyu 25:34)

7 Mulungu anafotokozela anthu oyambilila colinga cake kwa iwo. Iye anawauza kuti “Mubelekane, muculuke, mudzaze dziko lapansi, muyang’anilenso . . . colengedwa ciliconse cokwawa padziko lapansi.” (Gen. 1:28) Kupanduka kwa Adamu na Hava, komanso kubweletsa ucimo padziko lapansi sikunalepheletse colinga ca Yehova. Nthawi yomweyo, iye anatsimikiza kuti adzakhazikitsa Ufumu kumwamba umene udzakwanilitsa colinga cake capolyamba cokudza mtundu wa ana a anthu komanso dziko lapansi . (Ŵelengani Mateyu 25:34.) Panthawi yake yoikika, Yehova mwacikondi anatumiza Mwana wake woyamba kubadwa padziko lapansi kuti adzaphunzitse anthu za Ufumu wa Mulungu na kupeleka moyo wake monga dipo kutiwombola ku ucimo na imfa. Kenako Yesu anaukitsidwa na kupita kumwamba kukakhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Koma pali zambili zimene tingaphunzile pa colinga ca Mulungu.   

Ganizilani nthawi imene atumiki a Yehova apadziko la pansi komanso gulu la kumwamba la Yehova lizayamba kumulambila mogwilidzana (Onani ndime 8)

8. (a) Kodi nkhani yaikulu ya m’Baibo ni yotani (b) Malinga na Aef 1:​8-11, kodi colinga cacikulu ca Mulungu n’ciyani? (Onani cithunzi pacikuto).

8 Nkhani yaikulu ya Baibo ni yakuti dzina la Yehova lidzayeletsedwa pamene iye adzakwanilitsa colinga cake cokhudza dziko lapansi kupitila mu Ufumu wake wolamulidwa na Khristu. Colinga ca Yehova sicingasinthe. Iye anatsimikiza kuti zonse zidzacitika mmene analonjezela. (Yes. 46:​10, 11; Aheb. 6:​17, 18) M’kupita kwa nthawi dziko lapansi lidzakhala Paradaiso mmene ana a Adamu ndi Hava adzasangalala na “moyo kosatha.” (Sal. 22:26) Coposa pamenepa, Yehova alinso na colinga cina cacikulu. Colinga cake cacikulu, ni kugwilizanitsa gulu la atumiki ake padziko lapansi na gulu la kumwamba kuti likhale banja limodzi. Ndipo onse amene adzakhala na moyo panthawiyo, adzagonjela Yehova monga Wolamulila wacilengedwe conse. (Ŵelengani Aefeso 1:​8-11.) Kodi sizikucititsani cidwi kuona mmene Yehova akukwanilitsila colinga cake?

MUZISINKHA-SINKHA MWAKUYA ZATSOGOLO LANU

9. Kodi kuŵelenga Baibo kumatithandiza kuziŵa ciyani za mtsogolo?

9 Gazilani ulosi umene Yehova ananena m’munda wa Edeni wopezeka pa Genesis 3:15. b Unachula zocitika zimene zinali kudzakwanilitsa colinga cake. Koma zinali kudzacitika zaka masauzande mtsogolo. Zocitika zimenezi zinapatikizapo kubadwa kwa mbadwa za Abulahamu, mzele umene munadzabadwila Khristu. (Gen. 22:​15-18) Koma m’caka ca 33 C.E., Yesu anavulazidwa cidendene, monga mmene ulosiwo unanenela. (Mac. 3:​13-15) Mbali yothela ya ulosiwo, imene ni kupwanyidwa mutu kwa Satana, idzakwanilitsidwa pambuyo pa zaka 1000 za ulamulilo wa Yesu. (Chiv. 20:​7-10) Baibo imavumbula zimene zidzacitike pamene udani pakati pa gulu la Satana komanso gula la Yehova udzafike pacimake.

10. (a) Kodi ni zocitika ziti za mtsogolo zimene zicitike posacedwa? (b)  Kodi tingakonzekeletse bwanij maganizo na mtima wathu? (Onani mawu a m’munsi)

10 Ganizilani zocitika zapadela izi zimene Baibo inalosela. Coyamba, olamulila adzalengeza “bata ndi mtendele!” (1 Ates. 5:​2, 3) “Nthawi yomweyo,” cisautso cacikulu cidzayamba pamene olamulila adzaukila cipembedzo conyenga. (Chiv. 17:16) Pambuyo paizo, tidzaona zodabwitsa pamene “mwana wa munthu akubwela pamitambo ya kumwamba ndi mphamvu ndi ulemelelo waukulu.” (Mat. 24:30) Yesu adzapeleka ciweluzo pa mtundu wa ana a anthu mwa kulekanitsa nkhosa na mbuzi. (Mat. 25:​31-33, 46) Satana sadzakhala phee osacitapo kali konse. Cifukwa ca mkwiyo iye adzasonkhezela mgwilizano wa a mitundu umene Baibo imacha Gogi wa kudziko la magogi kuti aukile kulambila koona. (Ezek. 38:​2, 10, 11) Panthawi ina, odzozedwa adzasonkhanitsidwa kumwamba kuti agwilizane na Yesu na gulu lake la nkhondo pomenya nkhondo ya Aramagedo yomwe ni mbali yothela ya cisautso cacikulu. c (Mat. 24:31; Chiv. 16:​14, 16) Kenako Ulamulilo wa Yesu wa Zaka 1000 wolamulila dziko lapansi udzayamba.—Chiv. 20:6.

Kuphunzila za Yehova kwa zaka ma biliyoni kuzakuthandizani kuti mumuyandikile ngako. (Onani ndime 11)

11. Kodi ciyembekezo ca moyo wosatha cimatanthauzanji kwa inu? (Onaniso cithunzi.)

11 Yesani kuganizila mmene zinthu zidzakhalile pambuyo pa ulamulilo wa Yesu wa zaka 1,000. Baibo imatiuza kuti Mlengi wathu anatipatsa “mtima wofuna kukhala na moyo mpaka kalekale” (Mlal. 3:11) Kodi izi zidzakhuza bwanji umoyo wanu, komanso ubwenzi wanu na Yehova? Buku lakuti Yandikilani kwa Mulungu, pa tsamba 319, imafotokoza mfundo yocitsa cidwi yakuti: “Pambuyo pokhala na moyo kwa zaka mahandiledi, masauzande, mamiliyoni, ngakhale mamiliyoni ambili-mbili, tizadziŵa zinthu zochuluka zokhudza Yehova Mulungu kuposa mmene tikudziŵila panopa. Koma tidzaonabe kuti pali zinthu zodabwitsa zosaŵelengeka zofunika kuphunzila. . . . Moyo wamuyaya udzakahala watanthauzo kwambili komanso wazocita zosiyana-siyana. Ndipo nthawi zonse kuyandikana na Yehova kudzakhala mbali yofunika kwambili ya moyo umenewu.” Komabe pakalipano, n’ciyaninso cina cimene tingaphunzile pamene tipitiliza kuŵelenga mawu a Mulungu?

LIDZIŴENI BWINO GULU LA KUMWAMBA

12. N’ciyani cingatithandize kudziŵa gulu la kumwamba? Fotokozani citsanzo.

12 Mawu a Mulungu amatipatsako kadyonkho ponena za Yehova, amene “amakhala pa malo apamwamba.” (Yes. 33:5) Baibo imavumbula zinthu zocititsa cidwi za Yehova, komanso gulu lake la kumwamba. (Yes. 6:​1-4; Dan. 7:​9, 10; Chiv. 4:​1-6) Mwacitsanzo, tingaŵelenge zinthu zocititsa mantha zimene Ezekieli anaona pamene “kumwamba kunatseguka, ndipo anayanba kuona masomphenya a Mulungu.”—Ezek. 1:1.

13. Mumayamikila ciyani zokhudza udindo wa Yesu kumwamba mogwilizana na Aheberi 4:​14-16?

13 Ganizilanso za udindo umene Yesu ali nawo monga Mfumu kumwamba komanso Mkulu wathu wa Ansembe, amene amatimvela cisoni. Kupitila mwa iye, timatha kufikila “mpando wacifumu wa kukoma mtima kwakulu” wa Mulungu m’pemphelo, kupempha kucitilidwa cifundo na thandizo “pa nthawi imene tikufunika thandizo.” (Ŵelengani Aheberi 4:​14-16.) Tisalole tsiku kudutsa osaganizilapo zimene Yehova na Yesu anaticitila, komanso zimene akuticitila pamene ali kumwambako. Cikondi cawo pa ife, ciyenela kutikhudza mtima na kutilimbikitsa kukhala a cangu pa utumiki wathu na kulambila kwathu.—2 Akor. 5:​14, 15.

Ganizilani cimwemwe cimene m’zakhala naco m’dziko la tsopano podziŵa kuti munathandiza anthu kukhala Mboni za Yehova komanso ophunzila a Yesu! (Onani ndime 14)

14. Ni njila imodzi iti imene tingaonetsele kuyamkila kwathu Yehova na Yesu? (Onaninso cithunzi.)

14 Njila imodzi imene tingaonetsele kuti timayamikila Yehova na mwana wake Yesu, ni mwa kuyesetsa kuthandiza anthu ena kuti akhale Mboni za Yehova komanso ophunzila a Khristu. (Mat. 28:​19, 20) Izi n’zimene mtumwi Paulo anacita poonetsa ciyamikilo cake kwa Mulungu na Khristu. Iye anadziŵa kuti cifunilo ca Yehova “n’cakuti anthu kaya akhale a mtundu wotani apulumuke ndi kukhala odziwa coonadi molondola.” (1 Tim. 2:​3, 4) Iye anacita zonse zotheka mu utumiki wake na colinga cakuti ngati n’zotheka ‘apulumutseko ena.’—1 Akor. 9:​22, 23.

PEZANI CIMWEMWE POŴELENGA MAWU A MULUNGU

15. Malinga na Salimo 1:​2, n’ciyani cingatipatse cimwemwe?

15 Wa Masalimo anafotokoza kuti munthu wa cimwemwe, “amakondwela ndi cilamulo ca Yehova,” ndipo ‘amasinkhasinkha cilamulo cake usana ndi usiku.’ (Sal. 1:​1-3) Pothilila ndemanga pa lembali, womasulila Baibo wina dzina lake Joseph Rotherham m’buku lake lakuti Studies in the Psalms anati “pezani cimwemwe pa citsogozo cimene mwafufuza, ciphunzileni ndipo muziciganizilapo.” Anawonjezela kuti “ngati tsiku langopita popanda munthu kumvetsa mfundo inayake poŵelanga Baibo, ndiye kuti tsikulo langopita pacabe.” Mungapeze cimwemwe pamene muŵelenga Baibo ngati mukuyesetsa kumvetsa zimene mukuŵelengazo na kuona mmene mfundo zofunikazo zikugwilizanila. N’zosangalatsa ngako kumvetsa milingo yonse ya mawu a Mulungu!

16. Kodi tizakambilana ciyani m’nkhani yotsatila?

16 N’zotheka kumvetsa mfundo zabwino za coonadi zimene Yehova amatiphunzitsa kupitila m’Mawu ake. M’nkhani yotsatila tizakambilana imodzi mwa mfundo zozama za coonadi—Kacisi wauzimu wa Yehova, umene Paulo anaufotokoza m’kalata yake yopita kwa Akhristu Aciheberi. Kuphunzila nkhaniyi kudzakubweletselani cimwemwe coculuka.

NYIMBO 94 Tiyamikila Mau a Mulungu

a Kuŵelenga Baibo ni kosangalatsa. Kumatipindulila na kutilimbikitsa kuyandikila Atate wathu wakumwamba. Mkhani ino tione zimene tingacite kuti tidziŵe bwino “mlifupi, mlitali, kukwela ndi kuzama” kwa Mawu a Mulungu

b Onani nkhani yakuti “Ulosi Wamakedzana Umene Umakukhudzani” mu Nsanja ya Mlonda ya July 2022.

c Kuti mudziŵe zimene mungacite pokonzekela zinthu zocititsa mantha zimene zidzacitika mtsogolo, onani buku lakuti Ufumu wa Mulungu Ukulamulila tsamba 230.