Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

1924—Zaka 100 Zapitazo

1924—Zaka 100 Zapitazo

“NI NTHAWI yabwino kuciyambi kwa caka kwa mwana aliyense wopatulidwa wa Ambuye . . . kupeza mipata yofutukulila utumiki wake,” inatelo Bulletin ya January 1924. a M’caka cimeneco, Ophunzila Baibo anagwilitsa nchito malangizo amenewa polalikila molimba mtima, komanso kupeza njila zatsopano zolalikilila.

ANAYAMBA KULALIKILA POSEŴENZETSA WAILESI

Kwa zaka pafupi-fupi ziŵili, abale a pa Beteli anagwila nchito yomanga nyumba ya wailesi ya WBBR pa cilumba ca Staten mu mzinda wa New York. Pambuyo podula mitengo, anamanga nyumba yaikulu yokhalamo abale ogwila nchito pamalopo, komanso ina yoikamo zipangizo. Atamaliza kumanga nyumba zimenezi, abale anayamba kugula zipangizo zofunikila kuti ayambe kuulutsa nkhani pa wailesi. Koma anali kudzakumana na mavuto angapo.

Abale anavutika kwambili pamene anali kuimika mlongoti waukulu wa wailesi imeneyi. Mlongoti umenewo wotalika mamita 91, unafunika kumangidwa ku mitengo iŵili yotalika mamita 61. Pamene anayesa kuimika mlongoti umenewu koyamba analephela. Abale anadalila thandizo la Yehova, moti pamapeto pake anakwanitsa kuuimika. Calvin Prosser, amene anagwilako nawo nchito imeneyi anati: “Tikanakwanitsa kuimika mlongoti umeneyu nthawi yoyamba tikanadzitama n’kunena kuti, ‘Onani zimene takwanitsa kucita!’” M’malomwake, abale anatamanda Yehova cifukwa cowathandiza. Koma anali kudzakumana na vuto linanso.

Kuimika umodzi mwa milongoti ya nyumba ya wailesi ya WBBR

Panthawi imeneyo, m’pamene anthu anali kuyamba kuulutsa nkhani poseŵenzetsa wailesi. Ndipo zipangizo zoulutsila nkhani zinali zovuta kupeza. Koma abale anakwanitsa kupeza cipangizo coulutsila cimene munthu wina anali kuseŵenzetsa kumaloko. M’malo mogula maikolofoni yatsopano, iwo anaseŵenzetsa maikolofoni ya mu foni. Tsiku lina usiku, m’mwezi wa February, abale anaganiza zoyesa zipangizo zoulutsila zimene anaika. Anafunika kuulutsa pulogalamu ina yake, conco abale anaimba nyimbo za Ufumu. Mmodzi wa abale amene anali kuimbawo, Ernest Lowe, anafotokoza nkhani yoseketsa imene inacitika pa tsikuli. Iye anati, Judge Rutherford, b amene anali kukhala ku Brooklyn pamtunda wa makilomita 25 kucokela pamene panali nyumba ya wailesiyo, anawatumila foni atamva kuimba kwawo pa wailesi.

M’bale Rutherford anawauza moseka kuti, “Lekani kuimba. Mukumveka ngati pokhoso la acona!” Abalewa anacita manyazi, ndipo mwamsanga anazimitsa wailesi youlutsila nkhani. Koma anadziŵa kuti zonse zinali m’malo kuti ayambe kuulutsa nkhani.

Pa February 24, 1924, poulutsa pulogilamu yawo yoyamba, M’bale Rutherford anapatulila nyumba ya wailesi imeneyo kuti iziseŵenzetsedwa pofalitsa uthenga wa Ufumu wa Mesiya. Iye anafotokoza kuti colinga ca wailesi imeneyo ni “kuthandiza anthu onse kumvetsa coonadi ca m’Baibo komanso nthawi imene tikukhalamo, mosasamala kanthu zimene amakhulupilila.”

Kumanzele: M’bale Rutherford ali mkati mwa nyumba yoyamba youlutsila

Kulamanja: Zipangizo zoulutsila za nyumba ya wailesi

Pulogilamu yoyamba imene anaulutsa inayenda bwino kwambili. Kwa zaka 33, wailesi ya WBBR inagwilitsidwa nchito poulutsa mapulogilamu a pawailesi a anthu a Yehova.

MOLIMBA MTIMA ANATSUTSA ATSOGOLELI ACIPEMBEDZO

Mu July 1924, Ophunzila Baibo anali na msonkhano mu mzinda wa Columbus, ku Ohio. Anthu amene anasonkhana anacokela pa dziko lonse lapansi, ndipo anamva nkhani zokambidwa mu ci Arabic, Cingelezi, ci French, ci German, Cigiriki, ci Hungarian, ci Italian, ci Lithuanian, ci Polish, ci Russian, ci Ukranian, komanso m’zinenelo za ku Scandinavia. Nkhani zina za msonkhanowo zinaulutsidwa pa wailesi, ndipo abale anapempha nyuzipepala ina kuti izifalitsa nkhani za msonkhanowo tsiku lililonse. Dzina la nyuzipepala imeneyo inali Ohio State Journal.

Msonkhano umene unacitikila ku Columbus mu 1924

Pa Cinayi, July 24, abale na alongo oposa 5,000 anapita kukalalikila mu mzinda mmene munali kucitikila msonkhanowo. Iwo anagaŵila mabuku oposa 30,000, ndipo anayambitsa maphunzilo a Baibo ofika m’masauzande. Nsanja ya Mlonda ina inakamba kuti “tsikuli linali losangalatsa pa msonkhano wonse.”

Pa Cisanu, July 25, pamene M’bale Rutherford anali kukamba imodzi mwa nkhani zake, anaŵelenga cikalata coimba mlandu atsogoleli acipembedzo. Iye ananena kuti atsogoleli andale, acipembedzo, komanso amalonda, anali kuletsa anthu kuphunzila coonadi ponena za Ufumu wa Mulungu, Ufumu umene udzabweletsa madalitso kwa anthu onse. M’bale Rutherford ananenanso kuti anthu amenewa anali olakwa cifukwa anali kucilikiza bungwe la League of Nations na kunena kuti ndiyo inali njila imene Mulungu anali kuseŵenzetsa polamulila dziko lapansi. Ophunzila Baibo anafunika kukhala olimba mtima kuti alalikile uthenga umenewo kwa anthu.

Patapita nthawi, Nsanja ya Mlonda ina inanena kuti: “Msonkhano umenewu wa ku Columbus unalimbikitsa cikhulupililo ca kagulu ka abale na alongo okangalika amenewa. . . , unawathandiza kukhala olimba mtima kuti apitilize kulalikila ngakhale kuti anali kutsutsidwa.” Mmodzi wa amene analipo pa msonkhanowo, Leo Claus, anati: “Msonkhanowo utatha, tinali ofunitsitsa kugaŵila kathilakiti kameneka m’gawo lathu.”

Kope la kathilakiti ka Ecclesiastics Indicted

Mu October, Ophunzila Baibo anayamba kugaŵila tumakope topulintidwa twa kathilakiti kakuti Ecclesiastics Indicted (Kuimba Mlandu Zipembedzo), tofika m’mamiliyoni. Kathilakiti kameneka kanali na mfundo za m’cikalata cimene M’bale Rutherford anaŵelenga. M’tauni ina yaing’ono ku Oklahoma, m’dziko la America, Frank Johnson anatsiliza kugaŵila tumathilakiti tumenetu m’gawo limene anapatsidwa kutatsala mphindi 20 kuti akumane na ofalitsa anzake. Sakanayembekezela pamalo oonekela cifukwa anthu a m’tauni imeneyo anali okwiya kwambili na uthenga umene anali kulalikila. Conco anali kumufunafuna. M’bale Johnson anapita kukabisala mu chalichi inayake yapafupi. Popeza m’chalichimo munalibe anthu, iye anasiya tumathilakiti twa Ecclesiastics Indicted m’Baibo ya m’busa komanso pa mipando yonse. Iye anacita zimenezi mofulumila, ndipo anatuluka m’chalichimo mwamsanga. Abale aja anali asanafike, conco iye analoŵanso m’machalichi ena aŵili na kucita cimodzimodzi.

M’bale Johnson mofulumila, anabwelela kumalo kumene anapangana kuti akumane na abale aja. Iye anabisala kumbuyo kwa malo omwetsela mafuta, kwinaku akukhala chelu kuti anthu amene anali kumufunafuna asamuone. Anthu amene anali kumufunafunawo anadutsa pamalo amenewo na galimoto yawo koma sanamuone. Patapita kanthawi kocepa anthuwo atadutsa, abale anzake a Frank amene anali kulalikila pafupi na malo aja, anafika na galimoto na kumutenga.

M’bale wina anakamba kuti, “Pomwe tinali kucoka m’tauni imeneyi, tinadutsa pa machalichi atatu aja. Pabwalo pa chalichi iliyonse panali anthu pafupifupi 50. Anthu ena anali kuŵelenga thilakiti imeneyo pomwe ena anali kuinyamula m’mwamba kuti abusa awo aione. Tinacokadi panthawi yoyenela! Tinayamikila Yehova Mulungu wathu potiteteza, komanso potipatsa nzelu zotithandiza kudziŵa zocita kuti tisagwidwe na adani a Ufumu amenewa.”

OPHUNZILA BAIBO ANALALIKILA MOLIMBA MTIMA M’MAIKO ENA

Józef Krett

Ophunzila Baibo amene anali m’maiko ena, nawonso anali kulalikila molimba mtima. Kumpoto kwa dziko la France, m’bale Józef Krett analalikila anchito a ku migodi ocokela ku dziko la Poland. Kumeneko anali kufunika kukamba nkhani ya mutu wakuti “Akufa Adzaukitsidwa Posacedwa.” Pomwe abale na alongo anapeleka ciitanilo ca nkhani imeneyi kwa anthu a m’tauni imeneyo, wansembe wina wa kumaloko anauza anthu a m’chalichi yake kuti asakapite kukamvetsela nkhani imeneyo. Koma anthuwo sanacite zimene anauzidwa. M’malomwake, anthu oposa 5,000 anapita kukamvetsela nkhaniyo, kuphatikizapo wansembe uja! M’bale Krett anauza wansembe uja kuti akhalile kumbuyo zimene amakhulupilila, koma iye anakana. Pambuyo pa nkhaniyo, m’bale Krett anakwanitsa kugaŵila zofalitsa zonse zimene anali nazo kwa anthu poona kuti anthuwo anali na njala ya Mawu a Mulungu.—Amosi 8:11.

Claude Brown

M’bale Claude Brown anapita ku Africa ku dziko limene tsopano limachedwa Ghana, kukalalikila uthenga wabwino. Nkhani zimene anali kukamba komanso zofalitsa zimene anali kugaŵila zinathandiza kuti coonadi cifalikile mwamsanga m’dzikolo. John Blankson, amene anali kucita maphunzilo ogulitsa mankhwala, anamvetselako nkhani imodzi ya m’bale Brown. Posapita nthawi, iye anazindikila kuti wapeza coonadi. John anakamba kuti, “Coonadi cinanisangalatsa kwambili, ndipo n’nauzako ena coonadi cimeneco momasuka kusukulu.”

John Blankson

John anali ataphunzila kuti ciphunzitso ca Utatu cinali cabodza. Conco tsiku lina, iye anapita ku chalichi ca Anglican kuti akafunse wansembe za ciphunzitso cimeneci. Wansembeyo anapitikitsa John mokwiya kwinaku akukamba kuti: “Sindiwe Mkhristu, ndiwe mwana wa Mdyelekezi. Coka muno!”

Atafika kunyumba, John analembela kalata wansembeyo yomupempha kuti akakumane pamalo ena ake pomwe padzakhala anthu ambili kuti wansembeyo akakhalile kumbuyo ciphunzitso ca Utatu. Wansembeyo anauza John kuti apite ku ofesi ya mphunzitsi wamkulu wa pa sukuluyo. John atafika kumeneko, mphunzitsiyo anamufunsa ngati analembeladi wansembe uja kalata.

John anayankha kuti, “Inde n’natelo.”

Mphunzitsiyo anauza John kuti alembe kalata yopepesa kwa wansembeyo. Conco John analemba izi m’kalata yake:

“Bambo, mphunzitsi wanga waniuza kuti nilembe kalata yokupepesani, ndipo ndine wokonzeka kucita zimenezo pokhapo mukavomeleza kuti ziphunzitso zanu n’zabodza.”

Mphunzitsiyo anadabwa ndipo anamufunsa kuti, “John, kodi izi n’zimene ufuna kulemba?”

Iye anayankha kuti, “Inde, cifukwa sin’nalakwe ciliconse.”

Mphunzitsiyo anayankha kuti, “Udzacotsedwa sukulu. Sungapitilize kuphunzila pasukulu lino ngati sulemekeza wansembe wa cipembedzo ca boma.”

John anayankha kuti, “Koma mphunzitsi, . . . mukamaphunzitsa ndipo sitinamvetse zina zake, timakufunsani mafunso, si conco?”

Mphunzitsiyo anayankha kuti, “Inde mumatelo.”

John anakamba kuti, “Zimenezo n’zimene zacitika. Bamboyo anali kuniphunzitsa Baibo, conco ninam’funsa funso. Ngati bambo uja walephela kuyankha funso langa, sinionapo cifukwa colembela kalata yomupepesa.”

John sanacotsedwe sukulu, ngakhale kuti sanalembe kalata yopepesa.

ANALI KUFUNITSITSA KUCITA ZAMBILI PA NCHITO YOLALIKILA

Pofotokoza zimene zinacitika caka cimeneco, Nsanja ya Mlonda ina inanena kuti: “Tingagwilizane na mawu amene Davide anakamba akuti: ‘Inu mudzandipatsa mphamvu kuti ndithe kumenya nkhondo.’ (Sal. 18:39) Caka cimeneci, cakhala cotilimbikitsa kwambili, cifukwa taona mmene Yehova watithandizila pamene tikugwila nchito yolalikila. Atumiki ake okhulupilika akhala akulalikila uthenga wabwino mosangalala.”

Cakumapeto kwa caka cimeneco, abale anapanga makonzedwe akuti atsegule nyumba ina yawailesi kuti aziigwilitsa nchito polalikila. Nyumba yawailesi imeneyi yatsopano, anaimangila mumzinda wa Chicago ku America. Nyumba ya wailesi imeneyi inali na cikwangwani colembedwa kuti WORD kutanthauza kuti MAWU. Anaipatsa dzina limeneli cifukwa anali kudzaigwilitsa nchito polalikila Mawu a Mulungu. Panyumba yatsopano imeneyi, anagwilitsa nchito cipangizo camphamvu coulutsila. Cipangizo cimeneci cinatheketsa kuti anthu amve uthenga wa Ufumu ngakhale kumadela akutali monga kumpoto kwa Canada.

M’caka ca 1925, Yehova anali kudzabweletsa kuwala kwa coonadi. Kuwalako kunali kudzathandiza Ophunzila Baibo kumvetsa zinthu za pa Chivumbulutso caputala 12. Cifukwa ca kamvedwe katsopano ka palembalo, ambili anasiya kutumikila Yehova. Komabe ambili anasangalala na kamvedwe katsopano kameneka, cifukwa anamvetsa mmene zinthu zimene zinacitika kumwamba zinakhudzila atumiki a Mulungu padziko lapansi.

a Kabukuka tsopano kamachedwa Umoyo na Utumiki Wathu WacikhristuKabuku ka Msonkhano.

b M’bale J. F. Rutherford, amene anali kutsogolela Ophunzila Baibo pa nthawiyo, anali kudziŵika kuti “Judge” Rutherford. Zinali conco cifukwa asanayambe kutumikila pa Beteli, nthawi na nthawi anagwilapo nchito monga woweluza wapadela m’khoti la Eighth Judicial Circuit mu mzinda wa Missouri.