Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 42

NYIMBO 103 Abusa ni Mphatso za Amuna

Muzionetsa kuti Mumayamikila “Mphatso za Amuna”

Muzionetsa kuti Mumayamikila “Mphatso za Amuna”

“Atakwela kumwamba . . . , anapeleka mphatso za amuna.”AEF. 4:8.

ZOFUNIKA KUMVETSETSA

Mmene atumiki othandiza, akulu, komanso oyang’anila madela amatithandizila. Tiphunzilenso mmene tingaonetsele kuti timayamikila zimene amuna okhulupilikawa amacita.

1. Ni mphatso ziti zimene Yesu anatipatsa?

 PALIBE munthu anakhalapo wowolowa manja kuposa Yesu. Ali pa dziko lapansi, anathandiza ena poseŵenzetsa mphamvu zake zocitila zozizwitsa. (Luka 9:​12-17) Iye anatipatsa mphatso yopambana zonse mwa kupeleka moyo wake potifela. (Yoh. 15:13) Yesu anapitiliza kukhala wowolowa manja ngakhale ataukitsidwa. Iye analonjeza kuti adzapempha Yehova kuti atipatse mzimu woyela kuti utiphunzitse na kutilimbikitsa. Ndipo anacitadi zimenezi. (Yoh. 14:​16, 17, mawu a m’munsi; 16:13) Kuwonjezela apo, pa misonkhano ya mpingo, Yesu amatiphunzitsa mmene tingagwilile nchito yopanga ophunzila pa dziko lonse lapansi.—Mat. 28:​18-20.

2. Kodi “mphatso za amuna” zochulidwa pa Aefeso 4:​7, 8 ni ndani?

2 Koma palinso mphatso ina imene Yesu anatipatsa. Mtumwi Paulo analemba kuti Yesu atakwela kumwamba, “anapeleka mphatso za amuna.” (Ŵelengani Aefeso 4:​7, 8.) Paulo anafotokoza kuti Yesu anapeleka amuna amenewa, kuti athandizile mpingo m’njila zosiyana-siyana. (Aef. 1:​22, 23; 4:​11-13) Masiku ano, “mphatso za amuna” zimenezi ziphatikizapo atumiki othandiza, akulu mu mpingo, komanso oyang’anila madela. a Koma amuna amenewa ni opanda ungwilo. Conco amalakwitsa nthawi zina. (Yak. 3:2) Ngakhale n’telo, Ambuye wathu, Yesu Khristu, amawaseŵenzetsa kuti atithandize. Iwo alidi mphatso kwa ife!

3. Fotokozani citsanzo coonetsa mmene tingathandizile amuna amenewa pamene akugwila nchito zawo.

3 Yesu anapatsa amuna amenewa udindo womanga mpingo. (Aef. 4:12) Koma tonsefe tingathandize amuna amenewa kugwila nchito yofunika imeneyi. Tingayelekezele zimenezi na nchito yomanga Nyumba ya Ufumu. Ena amagwila nchito yomanga pamene ena amawathandiza mwa kupeleka cakudya komanso kuwathandiza pa zinthu zina zofunikila. Mofananamo, tonsefe tingathandize atumiki othandiza, akulu, komanso oyang’anila madela, mwa zokamba komanso zocita zathu. Tiyeni tikambilane mmene timapindulila cifukwa cakuti amuna amenewa amagwila nchito mwakhama. Tikambilanenso mmene tingaonetsele kuti timawayamikila, komanso kuyamikila Yesu amene anatipatsa “mphatso za amuna” zimenezi.

ATUMIKI OTHANDIZA AMACITA “UTUMIKI WOTHANDIZA ANTHU”

4. Kodi atumiki othandiza a m’zaka za zana loyamba anali kuthandiza anthu m’njila ziti?

4 M’zaka za zana loyamba, abale ena anali kuikidwa kukhala atumiki othandiza. (1 Tim. 3:8) N’kutheka kuti amenewa, ni amene anali kucita “utumiki wothandiza anthu” umene Paulo anakambapo. (1 Akor. 12:28) Conco zioneka kuti atumiki othandiza anali kusamalila mbali zina zofunika kuti akulu akhale na nthawi yophunzitsa mu mpingo komanso kuusamalila. Mwacitsanzo, n’kutheka kuti iwo anali kuthandiza kukopolola Malemba kapena kukagula zinthu zoseŵenzetsa pokopolola Malemba.

5. Kodi atumiki othandiza masiku ano amagwila nchito ziti zothandiza?

5 Ganizilani nchito zimene atumiki othandiza amagwila mu mpingo mwanu. (1 Pet. 4:10) Ena angapatsidwe nchito yosamalila maakaunti a mpingo kapena kusamalila magawo. Enanso angapatsidwe nchito yosamalila mabuku kuti ofalitsa azipeza mabuku ofunikila. Atumiki othandiza ena angapatsidwe nchito yosamalila mamaikolofoni, ena ku saundi, ndipo ena angakhale akalinde. Angathandizenso posamalila Nyumba ya Ufumu kuti ikhale yosamalika bwino komanso yaukhondo. Nchito zonsezi zimathandiza kuti mpingo uziyenda bwino. (1 Akor. 14:40) Kuwonjezela apo, atumiki othandiza ena amakamba nkhani za anthu onse. Ndipo amakambanso nkhani pa Msonkhano wa Umoyo na Utumiki. Mtumiki wothandiza angaikidwenso kukhala wothandizila woyang’anila kagulu. Nthawi zina, mkulu angapemphe mtumiki wothandiza woyenelela kuti apite naye ku maulendo aubusa.

6. Tili na zifukwa ziti zowayamikila atumiki othandiza amene amagwila nchito mwakhama?

6 Kodi mpingo umapindula bwanji na nchito za atumiki othandiza? Mlongo wina wa ku Bolivia dzina lake Beberly b anati, “Nimapindula kwambili na misonkhano cifukwa ca nchito zimene atumiki othandiza amacita. Cifukwa ca nchito zawo, nimatha kuimba, kuyankhapo, kumvetsela nkhani, ndipo nimapindula na mavidiyo komanso zithunzi. Iwo amaonetsetsa kuti tonse ndife otetezeka pa misonkhano, ndiponso amalumikiza awo amene akumvetsela misonkhano pa vidiyokomfalensi. Misonkhano ikatha, iwo amakhala patsogolo kuyeletsa, kusamalila maakaunti komanso kutipatsa zofalitsa zimene tikufunikila. Nimawayamikila zedi!” Mlongo Leslie wa ku Colombia amene mwamuna wake ni mkulu anati: “Atumiki othandiza amamuthandiza kwambili mwamuna wanga pamene akucita mautumiki ake. Popanda thandizo lawo, mwamuna wanga akanakhala wotangwanika kwambili. Conco nimawayamikila cifukwa ca kukangalika kwawo komanso kuti ni ofunitsitsa kum’thandiza.” Mosakaikila, inunso mumawayamikila kwambili atumiki othandiza.—1 Tim. 3:13.

7. Tingaonetse bwanji kuti timawayamikila atumiki othandiza? (Onaninso cithunzi.)

7 N’zoona kuti mu mtima mwathu tingayamikile zimene atumiki othandiza amacita. Koma Baibo imatilimbikitsa kuti: “Sonyezani kuti ndinu oyamikila.” (Akol. 3:15) Mkulu wina wa ku Finland dzina lake Cristóvão, anakamba izi poonetsa mmene amayamikila atumiki othandiza, “Nimaŵatumizila khadi kapena meseji yokhala na lemba. Nimachulanso cina cake conilimbikitsa cimene mtumiki wothandiza wacita komanso cifukwa cake nimayamikila utumiki wake.” M’bale Pascal na mkazi wake Jael, amene akhala ku New Caledonia, nthawi zambili amapemphelela atumiki othandiza. Pascal anati, “Posacedwa, takhala tikupemphelela atumiki othandiza a mu mpingo mwathu. Timayamikila Yehova cifukwa ca atumiki othandiza amenewa. Ndipo timamupempha kuti apitilize kuwathandiza.” Yehova amayankha mapemphelo otelo ndipo mpingo wonse umapindula.—2 Akor. 1:11.

AKULU “AMENE AKUGWILA NCHITO MWAKHAMA PAKATI PANU”

8. N’cifukwa n’ciyani Paulo anakamba kuti akulu a m’zaka za zana loyamba anali “kugwila nchito mwakhama?” (1 Atesalonika 5:​12, 13)

8 M’zaka za zana loyamba, akulu anali kuseŵenza mwakhama mu mpingo. (Ŵelengani 1 Atesalonika 5:​12, 13; 1 Tim. 5:17) Iwo anali kutsogolela mpingo mwa kucititsa misonkhano komanso kupanga zigamulo monga bungwe la akulu. Iwo analinso kulangiza abale na alongo awo mwa kuwapatsa uphungu mosapita mbali koma mwacikondi n’colinga coti ateteze mpingo. (1 Ates. 2:​11, 12; 2 Tim. 4:2) Kuwonjezela apo, amuna amenewa analinso kugwila nchito molimbika kuti asamalile mabanja awo komanso kuti iwo eni apitilize kukhala olimba kuuzimu.—1 Tim. 3:​2, 4; Tito 1:​6-9.

9. Kodi akulu amagwila nchito ziti masiku ano?

9 Akulu masiku ano amakhala na zocita zambili. Iwo ni alaliki a uthenga wabwino. (2 Tim. 4:5) Amapeleka citsanzo cabwino mwa kulalikila mwakhama. Amalinganizanso ofalitsa kuti akalalikile m’gawo la mpingo, amatiphunzitsa mmene tingagwilile nchito yolalikila, komanso kuphunzitsa mwaluso. Iwo amagwilanso nchito yoweluza. Ndipo amacita izi mwacifundo komanso mosakondela. Munthu akacita chimo lalikulu mu mpingo, akulu amayesetsa kum’thandiza kuti akonzenso ubwenzi wake na Yehova. Panthawi imodzi-modzi, iwo amaonetsetsa kuti akusungitsa ciyelo mu mpingo. (1 Akor. 5:​12, 13; Agal. 6:1) Koposa zonse, akulu amadziŵika kuti ni abusa. (1 Pet. 5:​1-3) Iwo amakonzekela bwino kuti akakambe nkhani za Baibo zogwila mtima. Amayesetsanso kudziŵa aliyense mu mpingo komanso kucita maulendo aubusa. Kuwonjezela pa maudindo amene ali nawo, akulu ena amathandizila pa nchito zomanga, kusamalila Nyumba za Ufumu, ndipo amathandizanso kulinganiza misonkhano ya cigawo. Akulu ena amatumikilanso m’Makomiti Okambilana na Acipatala komanso m’Tumagulu Toyendela Odwala. Ndithudi, akulu amagwila nchito molimbika kaamba ka ife!

10. Tili na zifukwa ziti zoyamikilila akulu amene amagwila nchito mwakhama?

10 Yehova anakambilatu kuti abusa adzasamalila bwino kwambili nkhosa zake, komanso kuti nkhosazo “sizidzaopa kanthu kapena kucita mantha.” (Yer. 23:4) Mlongo wina wa ku Finland dzina lake Johanna, anaona kukwanilitsika kwa mawu amenewa pamene amayi ake anadwala matenda aakulu. Iye anati: “Cimanivuta kuuzako ena mmene nikumvela. Koma mkulu wina anaonetsa kuleza mtima mwa kuniyembekezela mpaka pamene n’nali wokonzeka kumuuza nkhawa zanga. Iye anapemphela nane, ndipo ananitsimikizila kuti Yehova amanikonda. Sinikumbukila kwenikweni zimene iye anakamba, koma cimene nikumbukila n’cakuti nkhawa yanga inatha. Nikhulupilila kuti Yehova ndiye anatuma mkuluyo kuti adzanithandize pa nthawi yoyenela.” Kodi akulu a mu mpingo mwanu anakuthandizankoni m’njila ziti?

11. Kodi tingawaonetse bwanji akulu kuti timawayamikila? (Onaninso cithunzi.)

11 Yehova amafuna kuti tiziwayamikila akulu mocokela pansi pa mtima “cifukwa ca nchito yawo.” (1 Ates. 5:​12, 13) Henrietta amene akhala ku Finland, anakamba kuti: “Akulu amathandiza ena modzipeleka. Koma izi sizitanthauza kuti iwo ali na nthawi kapena mphamvu zoculuka kuposa ena. Ndipo sizitanthauzanso kuti iwo sakumana na mavuto pa umoyo wawo. Nthawi zina nimawauza kuti, ‘Mudziŵa, ndinu mkulu wabwino kwambili. N’nali kungofuna kukuuzani zimenezi.’” Mlongo wina wa ku Türkiye c dzina lake Sera anati: “Akulu nawonso ayenela kulimbikitsidwa kuti apitilize kugwila bwino nchito yawo. Conco tingaŵalembele khadi la mawu acilimbikitso, kuwaitanila ku cakudya, kapena kupita nawo mu ulaliki.” Kodi pali mkulu wina wake mu mpingo mwanu amene mumayamikila nchito imene amagwila? Ngati alipo, muonetseni kuti mumayamikila zimene amacita.—1 Akor. 16:18.

Mungawalimbikitse akulu kuti apitilize kugwila bwino nchito yawo (Onani ndime 7, 11, 15)


OYANG’ANILA MADELA AMALIMBIKITSA MIPINGO

12. Ni amuna enanso ati amene Yesu anapeleka kuti alimbikitse mipingo? (1 Atesalonika 2:​7, 8)

12 Khristu Yesu anapelekanso amuna ena amene analimbikitsa mpingo m’njila ina. Motsogoleledwa na Yesu, akulu a ku Yerusalemu anasankha Paulo, Baranaba, komanso ena kuti akhale oyang’anila oyenda-yenda. (Mac. 11:22) N’cifukwa ciyani? Kuti agwile nchito imodzi-modzi imene atumiki othandiza komanso akulu anali kugwila, yomwe ni kulimbikitsa mipingo. (Mac. 15:​40, 41) Amuna amenewa anadzimana zambili kuti agwile nchito imeneyi. Nthawi zina iwo anafika poika miyoyo yawo pa ciopsezo kuti aphunzitse na kulimbikitsa ena.—Ŵelengani 1 Atesalonika 2:​7, 8.

13. Kodi oyang’anila madela amacita nchito ziti?

13 Oyang’anila madela amayenda malo osiyana-siyana mlungu uliwonse. Ena amayenda maulendo atali-atali pocoka pa mpingo wina kupita kwina. Mlungu uliwonse, woyang’anila dela amakamba nkhani zingapo komanso kucita maulendo aubusa. Amacititsanso msonkhano wa apainiya, miting’i ya akulu, ndipo amatsogoza makambilano a ulaliki. Iye amakonzekela nkhani za pa msonkhano wa dela komanso wa cigawo. Ndipo amalinganizanso misonkhano imeneyi. Amaphunzitsa pa masukulu ya apainiya, ndipo amacititsanso msonkhano wapadela wa apainiya m’dela lake. Kuwonjezela pa izi, nthawi zina amacitanso nchito zofunika mwamsanga zimene ofesi ya nthambi ingamupatse.

14. Tili na zifukwa ziti zoyamikila oyang’anila madela amene amagwila nchito mwakhama?

14 Kodi mipingo imapindula bwanji na nchito zimene oyang’anila madela amacita? Ponena za maulendo amene oyang’anila madela amacita, m’bale wina wa ku Türkiye anati: “Pa maulendowo, oyang’anila madela amanilimbikitsa kuseŵenzetsa nthawi yanga yoculuka pothandiza abale na alongo anga. Nakumanapo na oyang’anila madela ambili, koma palibe ngakhale mmodzi amene anali kuoneka wosafikilika kapena wotangwanika kwambili moti n’kulephela kuceza nane.” Johanna, amene tam’chula kale, anapita mu ulaliki na woyang’anila dela koma sanapeze munthu pa nyumba iliyonse. Komabe Johanna anati: “Sinidzaiŵala tsikuli. Pa nthawiyi, alongo anga aŵili anali atasamukila kudela lina. Conco n’nali kuŵasoŵa kwambili. Wadela ananilimbikitsa mwacikondi. Iye ananithandiza kuona kuti ngakhale kuti pali pano sitingakhale pafupi na a m’banja lathu komanso anzathu, m’dziko latsopano tidzakhala na mipata yoculuka yoceza nawo.” Ambili a ife timawakonda kwambili oyang’anila madela amene atumikilapo m’dela lathu.—Mac. 20:37–21:1.

15. (a) Malinga na 3 Yohane 5-8, tingaonetse bwanji kuti timawayamikila oyang’anila madela? (Onaninso cithunzi.) (b) N’cifukwa ciyani tiyenela kuwayamikila akazi a amuna apaudindo? Nanga tingacite bwanji zimenezi? (Onani mbali yakuti “ Muzikumbukila Akazi Awo.”)

15 Mtumwi Yohane analimbikitsa Gayo kuceleza abale oyendela mipingo na “kuwathandiza m’njila imene Mulungu angasangalale nayo.” (Ŵelengani 3 Yohane 5-8.) Njila imodzi tingacitile zimenezi ni kuitanila oyang’anila dela ku cakudya. Njila ina ni kupezekapo pa makambilano a ulaliki mu mlungu wapadela. Leslie, amene tam’chula uja amaonetsa kuyamikila m’njila zinanso. Iye anati: “Nimapemphelanso kuti Yehova awapatse zimene akufunikila. Ine na mwamuna wanga timawalembela makalata yowauza mmene timapindulila akaticezela.” Kumbukilani kuti nawonso oyang’anila madela ali mavuto yawo ndipo amalema monga ife. Nthawi zina nawonso amadwala, amakhala na nkhawa, ndipo amalefuka. Conco amapemphela kuti Mulungu awathandize. Mawu anu okoma mtima, kapena mphatso yanu yocepa ingakhale ngati yankho la mapemphelo awo!—Miy. 12:25.

TIFUNIKILA “MPHATSO ZA AMUNA”

16. Malinga na Miyambo 3:​27, ni mafunso ati amene abale angadzifunse?

16 Kuzungulila dziko lonse lapansi, tikufunikila abale ambili amene angakhale “mphatso za amuna.” Ngati ndinu m’bale wobatizika, mungadzifunse ngati ‘mungathe kuthandiza’ mwa njila imeneyi. (Ŵelengani Miyambo 3:27.) Kodi mukuyesetsa kuti muyenelele kukhala mtumiki wothandiza? Ngati ndinu kale mtumiki wothandiza, kodi mukuyesetsa kuti muyenelele kukhala mkulu? d Kodi mungasintheko zinthu zina pa umoyo kuti mufunsile kuloŵa Sukulu ya Alengezi a Ufumu? Sukulu imeneyi idzakuthandizani kuti Yesu akugwilitseni nchito mokwanila. Ngati muona kuti simungakwanitse kucita zimenezi, pemphelani kwa Yehova. M’pempheni kuti akupatseni mzimu wake woyela umene ungakuthandizeni kukwanilitsa nchito iliyonse imene mungapatsidwe.—Luka 11:13; Mac. 20:28.

17. Kodi “mphatso za amuna” zimene Mfumu yathu, Yesu Khristu, wapeleka zionetsa ciyani za iye?

17 Abale omwe Yesu watipatsa monga “mphatso za amuna”, ni umboni wakuti iye akutitsogolela masiku ano otsiliza. (Mat. 28:20) Timayamikila kwambili kuti tili na Mfumu yacikondi komanso yowolowa manja, imene imadziŵa zimene tikufunikila na kutipatsa amuna oyenelela amene amatithandiza. Conco funafunani mipata yoyamikila abale amene amagwila nchito molimbika amenewa. Ndipo musamaiwale kumuyamikila Yehova, amene ndiye Gwelo la “mphatso iliyonse yabwino ndi yangwilo.”—Yak. 1:17.

NYIMBO 99 Abale Miyanda Miyanda

a Akulu amene amatumikila m’Bungwe Lolamulila, othandizila Bungwe Lolamulila, a m’Komiti ya Nthambi, komanso amene amacita mautumiki ena, nawonso ni “mphatso za amuna.”

b Maina ena asinthidwa.

c Dzikoli linali kuchedwa Turkey.

d Kuti mudziŵe zimene mungacite kuti muyenelele kutumikila monga mtumiki wothandiza kapena mkulu, ŵelengani nkhani yakuti “Abale—Kodi Mukuyesetsa Kuti Muyenelele Kukhala Mtumiki Wothandiza?” komanso yakuti “Abale—Kodi Mukuyesetsa Kuti Muyenelele Kukhala Mkulu?” mu Nsanja ya Mlonda ya November 2024.