Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 40

NYIMBO 30 Tate Wanga, Mulungu Wanga, Bwenzi Langa

Yehova “Amacilitsa Anthu Osweka Mtima”

Yehova “Amacilitsa Anthu Osweka Mtima”

“Iye amacilitsa anthu osweka mtima, ndipo amamanga mabala awo.”SAL. 147:3.

ZOFUNIKA KUMVETSETSA

Yehova amasamala kwambili za anthu osweka mtima. M’nkhani ino, tione zimene iye amacita kuti atithandize kucepetsa cisoni, komanso mmene amatithandizila kuti tilimbikitse ena.

1. Kodi Yehova amamva bwanji akaona atumiki ake?

 YEHOVA amaona zonse zimene atumiki ake amapitamo. Amadziŵa tikakhala na cimwemwe komanso tikakhala na cisoni. (Sal. 37:18) Yehova amakondwela kwambili akaona kuti tikucita zonse zomwe tingathe pomutumikila, ngakhale kuti tikukumana na zovuta. Kuwonjezela apo, iye ni wokonzeka kutithandiza komanso kutilimbikitsa.

2. Kodi Yehova amawacitila ciyani anthu osweka mtima? Ndipo tingacite ciyani kuti tipindule na cisamalilo cimene iye amapeleka?

2 Salimo 147:​3, imakamba kuti Yehova “amamanga mabala” a anthu osweka mtima. Lembali lionetsa kuti Yehova amawasamalila mwacikondi anthu osweka mtima. Koma kodi tiyenela kucita ciyani kuti tipindule nalo thandizo la Yehova? Ganizilani citsanzo ici: Munthu akavulala, amapita kwa dokotala waluso kuti amuthandize. Koma kuti wovulalayo acile, ayenela kutsatila mosamala malangizo a dokotala. M’nkhani ino, tione zimene Yehova amakamba m’Mawu ake kwa osweka mtima. Tionenso mmene tingaseŵenzetsele malangizo acikondi amene amatipatsa.

YEHOVA AMATITSIMIKIZILA KUTI NDIFE OFUNIKA KWAMBILI KWA IYE

3. N’cifukwa ciyani anthu ena amadziona kuti ni osafunika?

3 Tikukhala m’dziko lopanda cikondi. Zimenezi zapangitsa kuti anthu ambili ayambe kudziona kuti ni osafunika. Mlongo wina dzina lake Helen a anakamba kuti: “Makolo athu sanali kutionetsa cikondi. Atate anali aciwawa, ndipo tsiku lililonse anali kuniuza kuti ndine wacabe-cabe.” Monga zinalili na Helen, mwina nanunso anthu ena anakucitilam’poni zinthu mwankhanza, kukunyozani mobweleza-bweleza, kapena kukupangitsani kudzimva wosafunika. Ngati n’conco, mwina zimakuvutani kukhulupilila kuti pali wina wake amene angakukondeni.

4. Kodi Yehova amatitsimikizila ciyani pa Salimo 34:18?

4 Ngakhale kuti anthu ena anakucitilam’poni zinthu mwankhanza, dziŵani kuti Yehova amakukondani ndipo amakuonani kukhala wofunika. Iye “ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka.” (Ŵelengani Salimo 34:18.) Conco, ngati mumadziona kukhala wosafunika, muzikumbukila kuti Yehova anaona zabwino mwa inu, ndipo anakukokelani kwa iye. (Yoh. 6:44) Ni wokonzeka kukuthandizani nthawi zonse cifukwa ndinu wofunika kwa iye.

5. Tiphunzilapo ciyani tikaona mmene Yesu anacitila zinthu na anthu onyozeka?

5 Kukambilana citsanzo ca Yesu kungatithandize kudziŵa mmene Yehova amawaonela anthu osweka mtima. Pamene anali kucita utumiki wake wa padziko lapansi, anaona mmene ena anali kucitila zinthu na anthu amene anali kuoneka onyozeka. Koma iye anacita nawo mokoma mtima anthu onyozekawo. (Mat. 9:​9-12) Pamene mayi wodwala matenda oopsa kwambili anagwila covala ca Yesu, ali na cidalilo cakuti adzacila, Yesu anamutonthoza na kumuyamikila kaamba ka cikhulupililo cake. (Maliko 5:​25-34) Yesu amaonetsa bwino makhalidwe a Atate wake. (Yoh. 14:9) Conco, musakaikile zakuti Yehova amakuonani kukhala wofunika, komanso kuti amaona makhalidwe anu abwino, kuphatikizapo cikhulupililo canu, na cikondi canu pa iye.

6. N’ciyani cingathandize anthu amene amadziona kuti ni osafunika?

6 Kodi mungacite ciyani ngati mumadzionabe kukhala wosafunika? Ŵelengani na kusinkhasinkha mavesi a m’Baibo amene angakutsimikizileni kuti Yehova amakuonani kuti ndinu wofunika. b (Sal. 94:19) Musamadziyelekezele na anthu ena, koma muziganizila zimene mungakwanitse kucita. Yehova sakuyembekezelani kucita zimene simungakwanitse. (Sal. 103:​13, 14) Ngati munthu wina anakucitam’poni nkhanza, kukunyozani, kapena kukucitani nkhanza za kugonana, musamadziimbe mlandu, cifukwa sikunali kufuna kwanu. Kumbukilani kuti Yehova adzaweluza anthu amene amacitila ena zopanda cilungamo. Koma amathandiza amene amacitidwa zopanda cilungamo. (1 Pet. 3:12) Sandra, amene anacitilidwa zinthu mwankhanza ali mwana, ananena kuti, “Nthawi zambili nimapempha Yehova kuti anithandize kudziona moyenela, kudziona mmene iye amanionela.”

7. Kodi zinthu zimene zinaticitikila kumbuyoku zingatithandize bwanji pamene tikutumikila Yehova?

7 Musakaikile kuti Yehova angakuseŵenzetseni pothandiza ena. Iye wakupatsani mwayi wokhala wanchito mnzake pogwila nchito yolalikila. (1 Akor. 3:9) Cifukwa ca zovuta zimene munakumana nazo pa umoyo wanu, mwina cakhala cosavuta kwa inu kuonetsa cifundo kwa anthu amene nawonso amadziona kukhala osafunika. Ndipo mungacite zambili pothandiza anthu otelo. Helen, amene tamuchula mu ndime 3, analandila thandizo, ndipo tsopano nayenso amakwanitsa kuthandiza ena. Iye anati: “Yehova wapangitsa munthu wacabe-cabe ine kuyamba kumva kuti ndine wofunika. Komanso amaniseŵenzetsa kuthandiza ena.” Tsopano Helen akutumikila monga mpainiya wokhazikika.

YEHOVA AMAFUNA KUTI TISAMADZIIMBE MLANDU AKATIKHULULUKILA

8. Kodi Yehova amatiuza ciyani pa Yesaya 1:18?

8 Atumiki ena a Yehova amadziimbabe mlandu mopitilila malile cifukwa ca zoipa zimene anacita asanabatizike kapena atabatizika kale. Koma tisaiŵale kuti Yehova amatikonda kwambili, mwakuti anapeleka dipo kuti macimo athu akhululukidwe. Conco, iye amafuna kuti tiilandile mphatso ya dipo imeneyi. Yehova amatitsimikizila kuti akatithandiza kuti ‘tikhalenso pa ubwenzi wabwino’ c na iye samakumbukilanso macimo athu. (Ŵelengani Yesaya 1:18.) Ndife oyamikila kwambili kuti Atate wathu wacikondi, Yehova, samakumbukila macimo athu akale, ndipo saiŵala zabwino zimene timacita.—Sal. 103:​9, 12; Aheb. 6:10.

9. N’cifukwa ciyani sitiyenela kupitiliza kuganizila macimo amene tinacita kumbuyoku?

9 Ngati mumadziimba mlandu cifukwa ca zimene munacita kumbuyoku, mungacite bwino kuganizila zimene mukucita pali pano na zimene mudzacita m’tsogolo. Ganizilani citsanzo ca mtumwi Paulo. Iye anadziimbapo mlandu kuti panthawi ina anazunzapo Akhristu mwankhanza, koma anadziŵa kuti Yehova anali atamukhululukila. (1 Tim. 1:​12-15) Kodi anakhalila kungoganizila macimo amene anacita kumbuyoko? Mosakaikila, Paulo sanapitilize kuganizila macimo ake akale, monga mmene sanakhalile kuganizila zinthu zimene anacita kuti akhale Mfarisi wolemekezeka. (Afil. 3:​4-8, 13-15) M’malomwake, Paulo anagwila nchito yolalikila mwakhama na kuganizila zimene adzacita m’tsogolo. Mofanana na Paulo, inunso simungasinthe zomwe zinacitika kale. Koma mungatamande Yehova na kumukondweletsa pali pano. Mungamaganizilenso za tsogolo labwino limene wakulonjezani.

10. Tingacite ciyani ngati zocita zathu zinakhumudwitsapo ena kumbuyoku?

10 Mwina mumavutika maganizo cifukwa zinthu zina zimene munacita kumbuyoku zinakhumudwitsapo anthu ena. N’ciyani cingakuthandizeni ngati ni mmene zilili kwa inu? Citani zonse zomwe mungathe kuti mukonzenso zinthu zimene zinalakwika. Izi ziphatikizapo kupepesa mocokela pansi pa mtima. (2 Akor. 7:11) M’pempheni Yehova kuti athandize anthu omwe munawalakwila. Angakuthandizeni inuyo komanso anthu amene munakhumudwitsa kuti nonse mupitilize kumutumikila, komanso kuti mukhalenso na mtendele.

11. Kodi citsanzo ca mneneli Yona citiphunzitsa ciyani? (Onaninso pa cikuto.)

11 Tengam’poni phunzilo pa zolakwa zimene munacita kumbuyoku, ndipo lolani kuti Yehova akugwilitseni nchito m’njila iliyonse imene akufuna. Onani zimene zinacitikila mneneli Yona. M’malo mopita kum’maŵa, kumzinda wa Nineve kumene Yehova anamutuma, Yona anathaŵila kumadzulo, kumzinda wa Tarisi. Yehova anamupatsa cilango Yona, ndipo iye anatengapo phunzilo pa colakwa cake. (Yona 1:​1-4, 15-17; 2:​7-10) Ngakhale n’telo, Yehova anapitiliza kuseŵenzetsa Yona monga mneneli. Mulungu anauzanso Yona kaciŵili kuti apite ku Nineve, ndipo panthawiyi anamvela mwamsanga. Iye sanalole kuti zimene analakwitsa kumbuyoku zimulepheletse kulandila utumiki umene Yehova anamupatsa.—Yona 3:​1-3.

Yehova atapulumutsa mneneli Yona m’mimba mwa cinsomba, anamuuzanso kuti apite ku Nineve kukalengeza uthenga wake (Onani ndime 11)


YEHOVA AMASEŴENZETSA MZIMU WAKE WOYELA POTILIMBIKITSA

12. Kodi Yehova amatipatsa bwanji mtendele zinthu zoipa zikaticitikila? (Afilipi 4:​6, 7)

12 Zinthu zoipa zikaticitikila, Yehova amaseŵenzetsa mzimu wake woyela potilimbikitsa. Onani zimene zinacitikila m’bale Ron na mkazi wake Carol. Iwo anakumana na zinthu zomvetsa cisoni pomwe mwana wawo wamwamuna wa zaka 39 anadzipha. Iwo anati: “Takumanapo na zovuta pa umoyo wathu, koma ici cinaposa zonse. Nthawi zambili tinali kulephela kugona, conco tinali kupemphela kwa Yehova. Tikapemphela tinali kukhala na mtendele wochulidwa pa Afilipi 4:​6, 7.” (Ŵelengani.) Ngati ndinu wosweka mtima cifukwa ca zoipa zina zake zimene zinakucitikilani, mukhuthulileni Yehova zamumtima mwanu. Muzipemphela kwa iye kaŵilikaŵili, komanso mungapemphele kwa utali umene mufuna. (Sal. 86:3; 88:1) M’pempheni Yehova mobweleza-bweleza kuti akupatseni mzimu wake woyela. Iye sadzanyalanyaza pempho lanu.—Luka 11:​9-13.

13. Kodi mzimu woyela ungatithandize bwanji kupitiliza kutumikila Yehova mokhulupilika? (Aefeso 3:16)

13 Kodi munakumanapo na vuto lalikulu limene linakufooketsani? Mzimu woyela ungakupatseni mphamvu kuti mupitilize kutumikila Yehova mokhulupilika. (Ŵelengani Aefeso 3:16.) Ganizilani zinacitikila mlongo wina dzina lake Flora. Iye na mwamuna wake anali kutumikila monga amishonale. Kenako mwamuna wake anacita cigololo ndipo anasudzulana. Iye anati: “N’nali na cisoni cacikulu cifukwa ca zimene anacita. Cifukwa cakuti n’nali kungoganizila nkhaniyi, n’nali kulephela kucita zinthu zina. N’nali kupemphela kwa Yehova kuti anipatse mzimu wake woyela kuti unithandize kupilila. Yehova ananilimbikitsa ndipo ananithandiza kuti nipilile, ngakhale kuti poyamba zinali kuoneka zosatheka kupilila.” Tsopano mlongo Flora amaona kuti Mulungu anamuthandiza kukhala na cikhulupililo colimba, ndipo ali na cidalilo cakuti Mulungu adzamuthandiza ngakhale pa mavuto a m’tsogolo. Mlongo Flora anakamba kuti mawu a pa Salimo 119:32 amafotokoza bwino mmene Yehova anamuthandizila. Lembali limati: “Ndidzatsatila malamulo anu ndi mtima wonse, cifukwa mwandithandiza kuti ndiwamvetse bwino.”

14. Tingalole bwanji mzimu woyela kugwila nchito pa ife?

14 Pambuyo popemphela kuti Yehova akupatseni mzimu wake woyela, kodi muyenela kucita ciyani? Muzicita zinthu zimene zingacititse mzimu woyela kugwila nchito pa inu. Zimenezi ziphatikizapo kusonkhana komanso kulalikila. Muziŵelenga Mawu a Yehova tsiku lililonse. Izi zidzakuthandizani kuti muzisinkhasinkha pa kaganizidwe kake. (Afil. 4:​8, 9) Pamene mukuŵelenga, ganizilani mmene Yehova anathandizila anthu ochulidwa m’Baibo kupilila pamene anakumana na mavuto. Sandra amene tamuchula m’ndime 6 anakumana na mavuto aakulu motsatizana. Iye anati: “Nkhani ya Yosefe inanilimbikitsa kwambili. Yosefe sanalole kuti mavuto komanso zopanda cilungamo zimene zinamucitikila ziwononge ubwenzi wake na Yehova.”—Gen. 39:​21-23.

YEHOVA AMATILIMBIKITSA POSEŴENZETSA OKHULUPILILA ANZATHU

15. Kodi ndani angatilimbikitse? Nanga angatithandize bwanji? (Onaninso cithunzi.)

15 Pamene tikuvutika, okhulupilila anzathu ‘amatilimbikitsa kwambili.’ (Akol. 4:11) Yehova amaseŵenzetsa abale na alongo athu potionetsa kuti amatikonda. Okhulupilila anzathu angatilimbikitse mwa kupatula nthawi yoceza nafe komanso kutimvetsela pamene tikuwafotokozela mmene tikumvela. Angatilimbikitsenso mwa kutiŵelengela lemba kapena kupemphela nafe. d (Aroma 15:4) Nthawi zina, m’bale kapena mlongo angatikumbutse kaganizidwe ka Yehova, ndipo zimenezi zingatithandize kupitiliza kupilila. Akhristu anzathu angatithandizenso m’njila zina, monga kutipatsa cakudya tikakumana na mavuto.

Mabwenzi abwino, amene ni odalilika komanso okonda Yehova amatithandiza kwambili na kutilimbikitsa (Onani ndime 15)


16. Kodi tiyenela kucita ciyani kuti tilandile thandizo kucokela kwa ena?

16 Nthawi zina tingafunike kucita kupempha ena kuti atithandize. Abale na alongo athu amatikonda ndipo amafuna kutithandiza. (Miy. 17:17) Koma nthawi zina sangadziŵe zimene tikufunikila komanso mmene tikumvela. (Miy. 14:10) Ngati cina cake cikukuvutitsani maganizo, uzankoni anzanu odalilika mmene mukumvela. Auzeni zimene zingakuthandizeni. Mungasankhe kuuzako mkulu mmodzi kapena aŵili amene mumamasukilana nawo. Alongo ena apeza kuti n’zothandiza kukambilana na mlongo wokhwima kuuzimu.

17. Kodi ni zovuta ziti zingatilepheletse kulandila cilimbikitso? Nanga tingazigonjetse bwanji zovutazo?

17 Pewani kukhala kwanokha kwa nthawi yaitali. Nthawi zina simungafune kukhala na anthu ena cifukwa cokhala wokhumudwa kwambili. Ndipo nthawi zina abale na alongo anu sangakumvetseni, kapena angaseŵenzetse mawu olakwika pokamba nanu. (Yak. 3:2) Koma musalole kuti zimenezi zikulepheletseni kulandila cilimbikitso cimene mukufunikila. Mkulu wina dzina lake Gavin, amene ali na matenda a maganizo anati: “Nthawi zambili sinimafuna kuceza na anzanga.” Koma Gavin amapezabe nthawi yoceza na abale ake, ndipo amamvako bwino akacita zimenezi. Mlongo wina dzina lake Amy anati: “Cifukwa ca zoipa zimene zinanicitikila kumbuyoku, cimanivuta kukhulupilila anthu. Koma nikuyesetsa kuonetsa cikondi kwa abale na alongo komanso kuwakhulupilila monga mmene Yehova amacitila. Nidziŵa kuti kucita zimenezi kumamukondweletsa Yehova, ndipo inenso kumanibweletsela cimwemwe.”

MALONJEZO A YEHOVA A ZA M’TSOGOLO ANGATILIMBIKITSE

18. Kodi tikuyembekezela ciyani m’tsogolo? Nanga tingacite ciyani pali pano?

18 Posacedwa, Yehova adzacotsapo mavuto onse komanso zonse zimene zimatipangitsa kusweka mtima. (Chiv. 21:​3, 4) Pa nthawi imeneyo, zinthu zonse zoipa zimene zinaticitikilapo ‘sizidzativutitsanso maganizo.’ (Yes. 65:17) Monga taonela kale, Yehova “amamanga mabala” athu ngakhale pali pano. Landilani thandizo lililonse limene Yehova amapeleka kuti akulimbikitseni na kukutonthozani. Musakaikile ngakhale pang’ono kuti iye “amakufunilani zabwino.”—1 Pet. 5:7.

NYIMBO 7 Yehova Ndiye Mphamvu Zathu

a Maina ena asinthidwa.

b Onani danga lakuti “ Yehova Amakuonani Kuti Ndinu Ofunika.”

c Kuti Yehova ‘atithandize kukhalanso pa ubwenzi wabwino’ na iye, tiyenela kuonetsa kuti ndife olapa na kumupempha kuti atikhululukile macimo athu. Tiyenelanso kusintha makhalidwe athu. Tikacita chimo lalikulu, tiyenelanso kupempha thandizo kwa akulu mu mpingo.—Yak. 5:​14, 15.

d Mwacitsanzo, ganizilani malemba opezeka m’buku la Chichewa lakuti Malemba Othandiza pa Moyo wa Chikhristu, pa mutu wakuti “Chitonthozo” komanso wakuti “Nkhawa.”