Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 41

NYIMBO 13 Khristu ni Citsanzo Cathu

Zimene Yesu Anacita M’masiku Ake 40 Othela Padziko Lapansi

Zimene Yesu Anacita M’masiku Ake 40 Othela Padziko Lapansi

“Iwo anamuona masiku onse 40 ndipo ankawauza za Ufumu wa Mulungu.”—MAC. 1:3.

ZOFUNIKA KUMVETSETSA

Zimene tingacite potengela citsanzo ca Yesu pa zimene anacita m’masiku ake 40 othela padziko lapansi.

1-2. N’ciyani cinacitika pamene ophunzila aŵili a Yesu anali pa ulendo wopita ku Emau?

 TSIKU lake ni pa Nisani 16, mu 33 C.E. Ophunzila a Yesu ali m’nkhongono zii pokhudzika na cisoni, komanso pokhwethemuka na mantha. Aŵili a iwo akutuluka mu Yerusalemu kuloŵela kumudzi wa Emau, pamtunda wa makilomita 7. Amunawa ni acisoni cifukwa Yesu yemwe akhala akumutsatila wangophedwa cakumene. Mwa ici, ciyembekezo cawo conse pa zimene Mesiya anali kudzawacitila cataika. Koma zinthu zatsala pang’ono kusintha kwa iwo.

2 Mwadzidzidzi, akuona munthu wacilendo akubwela n’kuyamba kuyenda nawo. Ophunzilawo akusimbila munthuyo za kukhumudwa kwawo na zimene zacitika kwa Yesu. Kenako, mlendoyo akuyamba nawo nkhani yomwe isinthiletu zinthu pa moyo wawo. “Kuyambila ndi Zolemba za Mose komanso zonse zimene aneneli analemba,” iye anakufotokozela ophunzilawo cifukwa cake Mesiya anafunika kuvutika komanso kufa. Pofika ku Emau kuja, mlendoyo akudziulula kwa iwo, kuti ni Yesu amene waukitsidwa! Tangoganizani cimwemwe ca ophunzilawo, podziŵa kuti Mesiyayo ali moyo!—Luka 24:​13-35.

3-4. N’ciyani cinacitikila ophunzila a Yesu? Nanga tikambilane ciyani m’nkhani ino? (Machitidwe 1:3)

3 Yesu ataukitsidwa, anakhala masiku 40 pa dziko lapansi asanabwelele kumwamba. M’masiku 40 amenewo, iye anaonekela kwa ophunzila ake maulendo ambili. (Ŵelengani Machitidwe 1:3.) Pa nthawi imeneyo, Yesu analimbikitsa ophunzila ake amene anali acisoni komanso amantha. Iwo anakhalanso acimwemwe komanso olimba mtima kuti apite kukalalikila na kuphunzitsa uthenga wabwino wa Ufumu. a

4 Tingaphunzile zambili pokambilana zinthu zimene Yesu anacita panthawiyo. M’nkhani ino, tikambilane mmene Yesu anaseŵenzetsela nthawi imeneyo (1) kulimbikitsa ophunzila ake, (2) kuwathandiza kumvetsa Malemba mozamilapo, komanso (3) kuwaphunzitsa kuti asenze maudindo aakulu. Pokambilana mbali zitatu zimenezi, tione zimene tingacite kuti titengele citsanzo ca Yesu.

MUZILIMBIKITSA ENA

5. N’cifukwa ciyani ophunzila a Yesu anafunika cilimbikitso?

5 Ophunzila a Yesu anafunika cilimbikitso. Cifukwa ciyani? Cifukwa cakuti ena a iwo anali atasiya nyumba zawo, mabanja awo, komanso mabizinesi awo kuti azitsatila Yesu nthawi zonse. (Mat. 19:27) Ena a iwo anali kucitilidwa zinthu mopanda cilungamo komanso kusalidwa cifukwa cakuti anali atakhala ophunzila ake. (Yoh. 9:22) Iwo anali okonzeka kudzimana zinthu zina komanso kuvutika cifukwa anali kukhulupilila kuti Yesu anali Mesiya wolonjezedwayo. (Mat. 16:16) Koma Yesu ataphedwa, iwo anakhala na cisoni ndipo analefuka cifukwa sanali kudziŵa zomwe zidzacitika.

6. Kodi Yesu anacita ciyani ataukitsidwa?

6 Mosakaikila, Yesu anali kumvetsa cifukwa cake ophunzila ake anali na cisoni iye atamwalila. Iye anali kudziŵanso kuti cisoni cawo sicinali umboni woonetsa kuti analibe cikhulupililo ayi. Conco atangoukitsidwa, anayamba kulimbikitsa mabwenzi ake. Mwacitsanzo, Yesu anaonekela kwa Mariya Magadala. Pa nthawiyi n’kuti Mariya akulila pa manda a Yesu. (Yoh. 20:​11, 16) Anaonekelanso kwa ophunzila aŵili amene tawachula m’nkhani ino. Ndipo anaonekelanso kwa mtumwi Petulo. (Luka 24:34) Tiphunzilapo ciyani pa zimene Yesu anacitazi? Onani zinacitika iye ataonekela kwa Mariya Magadala.

7. Kodi Yesu anaona Mariya akucita ciyani? Ndipo zimenezo zinam’sonkhezela kucita ciyani? (Yohane 20:​11-16) (Onaninso cithunzi.)

7 Ŵelengani Yohane 20:​11-16. Pa Nisani 16 m’mawa, azimayi angapo anapita kumanda a Yesu. (Luka 24:​1, 10) Tiyeni tikambilane zimene zinacitikila Mariya Magadala amene anali mmodzi wa azimayiwo. Mariya atafika pa mandawo, anapeza kuti mtembo wa Yesu mulibe. Conco iye anapita kukauza Petulo na Yohane za nkhaniyi. Amuna aŵiliwo anathamanga kupita kumanda a Yesu. Ndipo Mariya anali kuwalondola. Amunawo anapezadi kuti mtembo wa Yesu mulibe. Conco iwo anabwelela kunyumba. Koma Mariya sanabwelele nawo. Anakhalabe ku mandako, ndipo anayamba kulila. Iye sanadziŵe kuti Yesu anali pomwepo. Yesu anaona pamene mzimayi wokhulupilikayu anali kulila ndipo anakhudzika kwambili. Conco anaonekela kwa Mariya ndipo anacita zinthu zina zake zimene zinamulimbikitsa. Yesu anauza mzimayiyu kuti apite akauze abale ake uthenga wofunika. Uthengawo unali wakuti Yesu waukitsidwa.—Yoh. 20:​17, 18.

Tengelani citsanzo ca Yesu mwa kukhala chelu komanso okoma mtima kwa acisoni (Onani ndime 7)


8. Tingacite ciyani potengela citsanzo ca Yesu?

8 Tingacite ciyani kuti titengele citsanzo ca Yesu? Tingatengele citsanzo ca Yesu mwa kulimbikitsa abale na alongo athu kuti apitilize kutumikila Yehova. Mofanana na Yesu, tiyenela kudziŵa zovuta zimene abale athu amakumana nazo, kuyesetsa kumvetsa mmene akumvela, komanso kuwalimbikitsa. Ganizilani citsanzo ca mlongo wina dzina lake Jocelyn, amene mlongosi wake anamwalila pangozi. Iye anati: “Kwa miyezi yambili, n’nali na cisoni cacikulu.” Komabe, m’bale wina na mkazi wake anaitana mlongo Jocelyn kunyumba kwawo, ndipo mwacifundo anali kumvetsela pomwe mlongo Jocelyn anali kufotokoza mmene anali kumvela. Iwo anamuuza kuti Mulungu amamuona kukhala wofunika. Jocelyn anati: “Cisoni cimene n’nali naco zinali ngati n’nali panyanja yacimphepo camkuntho. Koma Yehova anaseŵenzetsa banjali kunipulumutsa. Ananithandiza kukhalanso na cifuno copitiliza kutumikila Yehova.” Nafenso tingalimbikitse ena mwa kumvetsela mwachelu pamene akutikhutulila za mumtima mwawo, komanso mwa kuwaonetsa cifundo pokamba nawo. Tikacita zimenezi, tidzawalimbikitsa komanso kuwathandiza kupitiliza kutumikila Yehova.—Aroma 12:15.

MUZITHANDIZA ENA KUMVETSA MALEMBA

9. N’ciyani cinacitikila ophunzila a Yesu? Nanga Yesu anawathandiza bwanji?

9 Ophunzila a Yesu anakhulupilila Mawu a Mulungu, ndipo anacita zonse zimene akanatha kuti azicita zimene mawuwo amanena. (Yoh. 17:6) Ngakhale n’telo, maganizo awo anali osokonezeka cifukwa sanamvetse cifukwa cake Yesu anafa monga cigaŵenga. Yesu anadziŵa kuti ophunzila ake anali na cikhulupililo komanso kuti anali kumukonda Yehova. Koma anazindikila kuti iwo anafunika kumvetsa bwino Malemba. (Luka 9:​44, 45; Yoh. 20:9) Conco anathandiza ophunzilawo kumvetsa zimene anali kuŵelenga m’Malemba. Onani mmene anacitila zimenezi pomwe anaonekela kwa ophunzila aŵili omwe anali pa ulendo wopita ku Emau.

10. Kodi Yesu anathandiza bwanji ophunzila ake kumvetsa kuti iye analidi Mesiya? (Luka 24:​18-27)

10 Ŵelengani Luka 24:​18-27. Onani kuti Yesu sanafulumile kuwauza amunawo kuti iye anali ndani. M’malomwake, anawafunsa mafunso. N’cifukwa ciyani anatelo? Mwina anali kufuna kuti iwo amuuze zimene zinali m’maganizo mwawo na mmene anali kumvela. Ndipo iwo anamuuzadi. Anamuuza kuti anali kuyembekezela kuti Yesu adzamasula Aisiraeli ku ulamulilo wopondeleza wa Roma. Yesu anawalola kufotokoza maganizo awo. Atamaliza kufotokoza, Yesu anaseŵenzetsa Malemba pothandiza amunawo kumvetsa zimene zinacitika. b Tsiku limenelo madzulo, Yesu anapita kwa ophunzila enanso kukawathandiza kumvetsa zimene zinacitikazo. (Luka 24:​33-48) Tiphunzilapo ciyani pa zimene zinacitikazi?

11-12. (a) Tiphunzilapo ciyani tikaona mmene Yesu anaphunzitsila coonadi ca m’Baibo? (Onaninso zithunzi.) (b) Kodi m’bale wina anathandiza bwanji wophunzila wake?

11 Kodi tingacite ciyani kuti titengele citsanzo ca Yesu? Coyamba, pamene mukuphunzila Baibo na munthu, muzimufunsa mafunso aluso amene angakuthandizeni kudziŵa maganizo ake komanso mmene akumvela. (Miy. 20:5) Mukamvetsa mmene munthuyo akumvela, muonetseni mmene angapezele Malemba omwe angamuthandize. Ndipo pewani kumuuza zocita. M’malomwake, muthandizeni kuti azimvetsa Malemba. Muthandizeni kuona mmene angaseŵenzetsele mfundo za m’Baibo pa umoyo wake. Tiyeni tikambilane zimene zinacitikila m’bale wina wa ku Ghana dzina lake Nortey.

12 Pamene Nortey anali na zaka 16 anayamba kuphunzila Baibo. Koma posapita nthawi, a m’banja lake anayamba kumutsutsa. N’ciyani cinamuthandiza kukhalabe olimba? Mphunzitsi wake wa Baibo anali atakambilana naye kale Mateyo caputala 10, imene imaonetsa kuti Akhristu enieni adzazunzidwa. Nortey anati: “Conco pamene n’nayamba kuzunzidwa, n’nakhala wotsimikiza kuti napezadi coonadi.” Mphunzitsi wake wa Baibo anam’thandizanso mwa kukambilana naye Mateyo 10:16. Anamuonetsa kuti anafunika kucita zinthu mocenjela, komanso mwaulemu pokambilana nkhani za cipembedzo panyumba. Nortey atabatizika anafuna kuyamba upainiya. Koma atate ake anali kufuna kuti iye apite ku yunivesite. M’malo mouza Nortey zocita, mphunzitsi wake wa Baibo anaseŵenzetsa mafunso omuthandiza kuganizila mfundo za m’Baibo kuti apange cisankho canzelu. Kodi Nortey anacita ciyani? Nortey anasankha kuyamba upainiya wokhazikika. Conco atate ake anamuuza kuti acoke panyumba. Kodi Nortey amamva bwanji akaganizila zimene zinam’citikilazi? Iye anati: “Sinikaikila kuti n’napanga cisankho coyenela.” Nafenso tikamapatula nthawi yothandiza ena kumvetsa Malemba, tidzawathandiza kukhala Akhristu okhwima.—Aef. 3:​16-19.

Tengelani citsanzo ca Yesu mwa kuthandiza ena kumvetsa Malemba (Onani ndime 11) e


THANDIZANI ABALE KUKHALA “MPHATSO ZA AMUNA”

13. Kodi Yesu anacita ciyani pofuna kuti nchito yolalikila ipitilizebe ngakhale pambuyo pakuti wabwelela kumwamba? (Aefeso 4:8)

13 Pamene anali pa dziko lapansi, Yesu anacita zonse zimene Atate wake anamutuma. (Yoh. 17:4) Koma iye sanaganize kuti ndiye yekha akanakwanitsa kucita zimene Yehova anali kufuna. Pocita utumiki wake wa zaka zitatu na hafu, Yesu anaphunzitsako ena nchito zosiyana-siyana. Yesu anali kuwakhulupilila ophunzila ake. Iye anawapatsa udindo wotsogolela nchito yolalikila na kuphunzitsa uthenga wabwino. Anapatsanso ophunzilawo udindo wosamalila nkhosa zamtengo wapatali za Yehova. Ndipo n’kutheka kuti ena mwa ophunzilawo, anali asanakwanitse zaka 30. (Ŵelengani Aefeso 4:8.) Amuna amenewa anagwila nchito na Yesu molimbika, ndipo anali okhulupilika kwa iye. Koma asanabwelele kumwamba, iye anawaphunzitsa zinthu zina zimene zikanawayeneleza kukhala “mphatso za amuna.” Kodi anacita bwanji zimenezi?

14. Kodi Yesu anathandiza bwanji ophunzila ake kukula kuuzimu m’masiku ake 40 othela padziko lapansi? (Onaninso cithunzi.)

14 Yesu anapatsa ophunzila ake uphungu wosapita m’mbali, koma anacita zimenezi mokoma mtima. Mwacitsanzo, iye anazindikila kuti ophunzila ake ena anali kukaikila zakuti iye anali ataukitsidwa. Conco anawathandiza kukhulupilila kuti anali ataukitsidwadi mwa kuwapatsa uphungu. (Luka 24:​25-27; Yoh. 20:27) Anawaunzanso kuti aziika maganizo awo pa kusamalila anthu a Yehova m’malo moganizila kwambili nchito yakuthupi. (Yoh. 21:15) Anawakumbutsanso kuti sayenela kuganizila kwambili za maudindo amene ena angalandile pamene akutumikila Yehova. (Yoh. 21:​20-22) Iye anawongolela maganizo olakwika amene ophunzila ake anali nawo ponena za Ufumu wa Mulungu. Ndipo anawathandiza kuika maganizo awo pa kulalikila uthenga wabwino. (Mac. 1:​6-8) Kodi akulu angaphunzile ciyani kwa Yesu?

Tengelani citsanzo ca Yesu mwa kuphunzitsa ena kuyenelela maudindo (Onani ndime 14)


15-16. (a) Kodi akulu angacite ciyani kuti atengele citsanzo ca Yesu? Fotokozani. (b) Kodi uphungu unam’thandiza bwanji Patrick?

15 Kodi akulu angacite ciyani kuti atengele citsanzo ca Yesu? Iwo ayenela kuphunzitsa komanso kuthandiza amuna ngakhale acinyamata kuti akhale oyenela kusenza maudindo aakulu mumpingo. c Akulu sayembekezela kuti awo amene akuwaphunzitsa nchito, azicita bwino-bwino zinthu popanda kulakwitsa zina zake. Pophunzitsa abale acinyamatawa, akulu ayenela kupeleka uphungu wacikondi. Kucita izi kudzathandiza abale acinyamatawa kuona kufunika kokhala odzicepetsa, odalilika, komanso ofunitsitsa kutumikila ena.—1 Tim. 3:1; 2 Tim. 2:2; 1 Pet. 5:5.

16 Onani mmene uphungu unathandizila m’bale wina dzina lake Patrick. Ali wacinyamata, iye anali kulankhula mwaukali, komanso mosakomela ena mtima, kuphatikizapo alongo. Mkulu wina anaona zimene Patrick anali kucita, ndipo anam’patsa uphungu wosapita m’mbali. Koma anacita zimenezo mokoma mtima. Patrick anati: “Nimayamikila kuti mkulu uja ananithandiza. N’nali kukhumudwa nikaona abale ena akulandila maudindo amene n’nali kufuna. Koma uphungu umene mkulu uja ananipatsa, unanithandiza kuona kufunika kotumikila abale na alongo modzicepetsa. Uphunguwo unan’thandiza kupewa kuika kwambili maganizo anga pa maudindo amene ningakhale nawo mumpingo.” Zotsatila zake zinali zakuti Patrick anaikidwa kukhala mkulu ali na zaka 23.—Miy. 27:9.

17. Kodi Yesu anaonetsa bwanji kuti anali kuwadalila ophunzila ake?

17 Yesu sanangopatsa ophunzila ake udindo wolalikila, koma anawapatsanso udindo wophunzitsa. (Mat. 28:20.) N’kutheka kuti ophunzilawo anali kuganiza kuti sangakwanitse kucita utumikiwo. Koma Yesu sanali kukaikila kuti iwo angakwanitse kucita nchito imeneyi. Anali kuwadalila kwambili moti anawauza kuti: “Mofanana ndi mmene Atate ananditumila, inenso ndikukutumani.”—Yoh. 20:21.

18. Kodi akulu angacite ciyani potengela citsanzo ca Yesu?

18 Kodi akulu angacite ciyani kuti atengele citsanzo ca Yesu? Akulu ozindikila amagaŵilako ena nchito. (Afi. 2:​19-22). Mwacitsanzo, akulu angapemphe acinyamata kuti athandize kuyeletsa komanso kukonzanso zinthu pa Nyumba ya Ufumu. Akulu akapatsa abale nchito, ayenela kuwaphunzitsa moigwilila komanso kuwadalila kuti adzaigwila bwino. Mkulu wina watsopano dzina lake Matthew, amayamikila kuti akulu ena amam’phunzitsa nchito zosiyana-siyana mumpingo, komanso amamudalila kuti adzaigwila bwino nchito imene amupatsa. Iye anati: “Nikalakwitsa zina zake pogwila nchitozo, iwo anali kunithandiza kuona pamene nifunika kuwongolela.” d

19. Tiyenela kukhala ofunitsitsa kucita ciyani?

19 Yesu anaseŵenzetsa masiku ake 40 othela padziko lapansi kulimbikitsa ena, kuwaphunzitsa, komanso kuwaonetsa mogwilila nchito. Tiyeni tikhale ofunitsitsa kutsatila citsanzo cake mosamala kwambili. (1 Pet. 2:21) Iye adzatithandiza kucita zimenezi. Ndi iko komwe, iye analonjeza kuti: “Nili nanu pamodzi masiku onse mpaka cimalizilo ca nthawi ino.—Mat. 28:20.

NYIMBO 15 Tamandani Woyamba Kubadwa wa Yehova

a Mabuku a Uthenga Wabwino komanso mabuku ena a m’Baibo amaonetsa maulendo angapo pamene Yesu anaonekela kwa ophunzila ake pambuyo poukitsidwa. Iye anaonekela kwa: Mariya Magadala (Yoh. 20:​11-18); kwa azimayi ena (Mat. 28:​8-10; Luka 24:​8-11); kwa ophunzila aŵili (Luka 24:​13-15); kwa Petulo (Luka 24:34); komanso kwa atumwi koma Thomasi sanalipo. (Yoh. 20:​19-24) Anaonekelanso kwa atumwi ndipo Thomasi analipo (Yoh. 20:26); kwa ophunzila 7 (Yoh. 21:​1, 2); kwa ophunzila oposa 500 (Mat. 28:16; 1 Akor. 15:6); kwa m’bale wake Yakobo (1 Akor. 15:7); kwa atumwi onse (Mac. 1:4); komanso kwa atumwi pomwe anali pafupi na mzinda wa Betaniya. (Luka 24:​50-52) N’kutheka kuti olemba Baibo sanachule maulendo onse amene Yesu anaonekela kwa ophunzila ake pambuyo poukitsidwa.—Yoh. 21:25.

b Kuti muone maulosi onse okhudza Mesiya, onani nkhani yakuti, “Kodi Maulosi Onena za Mesiya Amatsimikizila Kuti Yesu Analidi Mesiya?” pa jw.org ku Chichewa.

c Nthawi zina, ngakhale akulu acinyamata a zaka zoyambila 25 mpaka 30 angaikidwe kukhala oyang’anila dela. Komabe, amuna amenewa ayenela kukhala oti atumikila monga akulu kwa nthawi ndithu, ndipo afika poidziŵa bwino nchito yawo.

d Kuti mupeze mfundo zina za mmene mungathandizile abale acinyamata kuyenelela maudindo, onani Nsanja ya Mlonda ya August 2018 masamba 11-12, ndime 15-17, komanso ya April 15, 2015, masamba 3-13.

e MAWU OFOTOKOZELA CITHUNZI: M’bale akuthandiza wophunzila wake wa Baibo kuganizila zimene Malemba amanena na kudziŵa mmene angakondweletsele Yehova.