Kodi Mudziŵa?
Kodi nyimbo zinali zofunika motani kwa Aisiraeli akale?
NYIMBO zinali zofunika kwambili m’cikhalidwe ca Aisiraeli. Baibo imachula zocitika zingapo zoonetsa anthu akuimba nyimbo poseŵenzetsa zipangizo zoimbila, komanso akuimba popanda zipangizo. Mbali yaikulu ya Baibo ni nyimbo. Mwacitsanzo, mabuku a Masalimo, Nyimbo ya Solomo, komanso Maliro analembedwa kuti aziimbidwa. Buku lina lokamba za umoyo wa m’nthawi ya m’Baibo, linakamba kuti Baibo imaonetsa bwino kuti Aisiraeli anali kuimba nyimbo pa zocitika zosiyana-siyana pa umoyo wawo.—Music in Biblical Life.
Nyimbo mu umoyo wawo wa tsiku na tsiku. Aisiraeli anali kuimba nyimbo pofuna kuonetsa mmene anali kumvela. (Yes. 30:29) Azimayi anali kuimba masece, kuimba nyimbo mwacisangalalo, ndipo analinso kuvina pa nthawi ya zikondwelelo. Zikondwelelozo zinaphatikizapo nthawi yolonga mfumu yatsopano, asilikali akapambana nkhondo, komanso pa zikondwelelo za kulambila. (Ower. 11:34; 1 Sam. 18:6, 7; 1 Maf. 1:39, 40) Aisiraeli analinso kuimba nyimbo za malilo poonetsa cisoni cacikulu. (2 Mbiri 35:25) Monga inakambila Cyclopedia ya McClintock and Strong, n’zoonekelatu kuti “Aisiraeli anali kukonda kwambili kuimba nyimbo.”
Nyimbo m’bwalo la mfumu. Mafumu aciisiraeli anali kukonda kumvetsela nyimbo. Mfumu Sauli anaitanitsa Davide kuti azimuimbila nyimbo m’bwalo lacifumu. (1 Sam. 16:18, 23) Patapita nthawi pomwe Davide anakhala mfumu, anapanga zipangizo zoimbila, ndipo anapeka nyimbo zogwila mtima. Iye analinganizanso gulu la oimba kuti liziimba pa kacisi wa Yehova. (2 Mbiri 7:6; Amosi 6:5) Mfumu Solomo anali na amuna komanso akazi oimba m’bwalo lake lacifumu.—Mlal. 2:8.
Kuseŵenzetsa nyimbo polambila. Koposa zonse, Aisiraeli anali kuseŵenzetsa nyimbo polambila Yehova. Ndipo panali anthu oimba okwana 4,000 amene anali kuimba pa kacisi ku Yerusalemu. (1 Mbiri 23:5) Iwo anali kuimba poseŵenzetsa zinganga, zoimbila za zingwe, azeze, komanso malipenga. (2 Mbiri 5:12) Koma amuna aluso amenewa sindiwo okha anali kuimba nyimbo polambila Yehova. Mwacionekele, Aisiraeli ambili anali kuimba nyimbo popita ku zikondwelelo ku Yerusalemu. Nyimbo zimenezi zimachedwa Nyimbo Zokwelela Kumzinda. (Sal. 120-134) Malinga na zolemba za Ciyuda, Aisiraeli anali kuimba Masalimo ya Haleluya a pakudya cakudya ca Pasika.
Nyimbo zikali zofunika kwambili kwa anthu a Mulungu masiku ano. (Yak. 5:13) Timaimba nyimbo polambila Yehova. (Aef. 5:19) Ndipo kuimba nyimbo zotamanda Yehova pamodzi na abale kumatigwilizanitsa. (Akol. 3:16) Kuwonjezela apo, timamvako bwino tikamvetsela kapena kuimba nyimbo pamene tikumana na mavuto. (Mac. 16:25) Kuimba ni njila yabwino kwambili yoonetsela kuti timamukhulupilila Yehova ndiponso kuti timamukonda.
a Ayuda anali kuchula Masalimo 113 mpaka 118 kuti Masalimo ya Haleluya. Ndipo anali kuimba nyimbozi potamanda Yehova.