Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 36

Aramagedo ni Nkhani Yokondweletsa!

Aramagedo ni Nkhani Yokondweletsa!

“Anawasonkhanitsa pamodzi [ku] . . . Aramagedo.”​CHIV. 16:16, ftn.

NYIMBO 150 Funani Cipulumutso ca Mulungu

ZIMENE TIKAMBILANE *

1-2. (a) N’cifukwa ciani tikamba kuti Aramagedo ni nkhani yokondweletsa? (b) Ni mafunso ati amene tikambilane m’nkhani ino?

KODI munamvelapo anthu akamba kuti “Aramagedo” ni nkhondo ya nyukiliya kapena kuti ni kuwonongeka kothelatu kwa zacilengedwe? Mosiyana na zimenezi, Baibo imaphunzitsa kuti Aramagedo ni nkhani yabwino ndiponso yokondweletsa. (Chiv. 1:3) Nkhondo ya Aramagedo siidzawononga mtundu wa anthu, koma idzaupulumutsa. N’cifukwa ciani takamba conco?

2 Baibo imaonetsa kuti nkhondo ya Aramagedo idzapulumutsa mtundu wa anthu mwa kuthetsa ulamulilo wa anthu. Nkhondoyi idzapulumutsa mtundu wa anthu mwa kuwononga oipa na kupulumutsa olungama, komanso mwa kuteteza dzikoli kuti lisawonongeke. (Chiv. 11:18) Kuti timvetsetse mfundo zimenezi, tiyeni tikambilane mafunso anayi aya: Kodi Aramagedo n’ciani? Ni zocitika ziti zimene zidzatsogolela ku Aramagedo? Tingacite ciani kuti tikapulumuke pa nthawiyo? Nanga tingacitenso ciani kuti tikhalebe okhulupilika pamene Aramagedo ikuyandikila?

KODI ARAMAGEDO N’CIANI?

3. (a) Kodi liwu lakuti “Aramagedo” litanthauza ciani? (b) Malinga na Chivumbulutso 16:14, 16, n’cifukwa ciani tikamba kuti Aramagedo si malo eni-eni?

3 Ŵelengani Chivumbulutso 16:14, 16. Liwu lakuti “Aramagedo” limapezeka cabe pa vesi imodzi m’Baibo. Liwuli linacokela ku mawu aciheberi amene amatanthauza “Phili la Megido.” (Chiv. 16:16; ftn.) Megido unali mzinda ku Isiraeli wakale. (Yos. 17:11) Koma Aramagedo si malo eni-eni a pa dziko lapansi. Kweni-kweni, Aramagedo itanthauza zocitika za pa nthawi imene “mafumu a dziko lonse lapansi” adzasonkhana kuti alimbane na Yehova. (Chiv. 16:14) Komabe, mawu akuti “Aramagedo” tawagwilitsilanso nchito pokamba za nkhondo imene idzacitika mwamsanga pambuyo pa kusonkhanitsidwa kwa mafumu a dziko lapansi. Nanga tidziŵa bwanji kuti Aramagedo ni malo ophiphilitsa cabe? Coyamba, kulibe phili leni-leni la Megido. Caciŵili, dela la Megido ni locepa kwambili, moti “mafumu a dziko lonse lapansi kumene kuli anthu” komanso magulu awo a asilikali na zida zawo zankhondo sangakwane kumeneko. Cacitatu, monga tionele m’nkhani ino, nkhondo ya Aramagedo idzayamba pamene “mafumu” a dziko lonse lapansi adzaukila anthu a Mulungu, amene sakhala pa malo amodzi, koma amakhala m’madela osiyana-siyana pa dzikoli.

4. N’cifukwa ciani Mulungu anacha nkhondo yaikulu yomaliza kuti Aramagedo, potengela dzina lakuti Megido?

4 N’cifukwa ciani Yehova anacha nkhondo yaikulu yomaliza kuti Aramagedo, potengela dzina lakuti Megido? Dela la Megido na cigwa ca Yezereeli cimene cili pafupi na delali, kunali kucitika nkhondo zambili. Nthawi zina, Yehova anali kuthandiza anthu ake kupambana pa nkhondo zimenezo. Mwacitsanzo, “ndi madzi a ku Megido,” Mulungu anathandiza Woweluza waciisiraeli, Baraki, kugonjetsa gulu la asilikali acikanani lotsogoleledwa na Sisera. Baraki na mneneli wamkazi Debora anaimba nyimbo yoyamikila Yehova powathandiza mozizwitsa kupambana nkhondoyo. Iwo anaimba kuti: “Nyenyezi zinamenya nkhondo zili kumwamba, zinamenyana ndi Sisera . . . Mtsinje wa Kisoni unawakokolola.”—Ower. 5:19-21.

5. Ni kusiyana kwakukulu kuti kumene kudzakhalapo pakati pa nkhondo ya Aramagedo na nkhondo imene Baraki anamenya?

5 Baraki na Debora anatsiliza nyimbo yawo na mawu akuti: “Inu Yehova, adani anu onse afafanizidwe cimodzimodzi, ndipo okukondani inu akhale amphamvu ngati mmene dzuwa limakhalila.” (Ower. 5:31) Mofanana na nthawi ya Baraki, pa Aramagedo, adani onse a Mulungu adzawonongedwa kothelatu. Koma anthu amene amakonda Mulungu adzapulumuka. Komabe, pali kusiyana kwakukulu pakati pa Aramagedo na nkhondo imene Baraki anamenya. Pa Aramagedo, anthu a Mulungu sadzamenyako nkhondo. Ndipo sadzakhala na cida ciliconse cankhondo. Adzakhala amphamvu mwa kukhala osatekeseka komanso kukhulupilila Yehova na magulu ake ankhondo akumwamba.—Yes. 30:15; Chiv. 19:11-15.

6. Kodi Mulungu angaseŵenzetse njila ziti powononga adani ake pa Aramagedo?

6 Kodi Mulungu adzawononga bwanji adani ake pa Aramagedo? Iye angagwilitsile nchito njila zosiyana-siyana. Mwacitsanzo, angaseŵenzetse zivomezi, matalala, na mphenzi. (Yobu 38:22, 23; Ezek. 38:19-22) Angacititsenso adani ake kumenyana okha-okha. (2 Mbiri 20:17, 22, 23) Cinanso, angaseŵenzetse angelo kuti awononge anthu oipa. (Yes. 37:36) Olo kuti sitidziŵa njila yeni-yeni imene adzaseŵenzetsa, cimene tidziŵa n’cakuti adzapambana pa nkhondoyo. Mulungu adzawononga adani ake onse, ndipo adzapulumutsa anthu onse olungama.—Miy. 3:25, 26.

NI ZOCITIKA ZITI ZIMENE ZIDZATSOGOLELA KU ARAMAGEDO?

7-8. (a) Mogwilizana na 1 Atesalonika 5:1-6, ni cilengezo capadela citi cimene atsogoleli a maiko adzalengeza? (b) Nanga n’cifukwa ciani cilengezo cimeneci cidzakhala bodza loopsa?

7 Anthu akadzangolengeza “bata ndi mtendele,” nthawi yomweyo “tsiku la Yehova” lidzafika. (Ŵelengani 1 Atesalonika 5:1-6.) “Tsiku la Yehova” lochulidwa pa 1 Atesalonika 5:2 litanthauza “cisautso cacikulu.” (Chiv. 7:14) Kodi tidzadziŵa bwanji kuti cisautso cacikulu catsala pang’ono kuyamba? Baibo imakamba kuti anthu adzapeleka cilengezo capadela kwambili. Cilengezoco cikadzapelekedwa, posapita nthawi cisautso cacikulu cidzayamba.

8 Kodi ni cilengezo cotani cimeneco? Ni cilengezo ca “bata ndi mtendele,” cimene Baibo inakambilatu. N’cifukwa ciani atsogoleli a maiko adzalengeza zimenezi? Kodi nawonso atsogoleli a zipembedzo adzatengako mbali? N’kutheka. Komabe, tidziŵa kuti cilengezo ca “bata ndi mtendele” cidzakhala bodza lina louzilidwa na ziŵanda. Bodzali lidzakhala loopsa kwambili cifukwa lidzapangitsa anthu kuona ngati kuti ali pa mtendele, pamene m’ceni-ceni angotsala pang’ono kuyang’anizana na cisautso cacikulu kwambili m’mbili yonse ya anthu. Inde, “ciwonongeko codzidzimutsa cidzafika pa iwo nthawi yomweyo monga zowawa za pobeleka za mkazi wapakati.” Nanga n’ciani cidzacitikila atumiki okhulupilika a Yehova? N’kutheka kuti adzadzidzimutsidwa na kuyamba kwa tsiku la Yehova, koma adzakhala okonzeka.

9. Kodi Mulungu adzawononga dziko lonse la Satana pa nthawi imodzi? Fotokozani.

9 Yehova sadzawononga dziko lonse la Satana pa nthawi imodzi, monga anacitila m’nthawi ya Nowa. Koma adzayambila kuwononga mbali imodzi. Ndipo pambuyo pake, adzawononga mbali ina yotsala. Coyamba, adzawononga Babulo Wamkulu, ufumu wa dziko lonse wa cipembedzo conama. Kenako, pa Aramagedo, adzawononga mbali yotsala ya dziko la Satana, imene iphatikizapo magulu a zankhondo, a zandale, na a zamalonda. Tiyeni lomba tikambilane zambili zokhudza zocitika ziŵili zikulu-zikulu zimenezi.

10. Malinga na Chivumbulutso 17:1, 6 na 18:24, n’cifukwa ciani Yehova adzawononga Babulo Wamkulu?

10 “Ciweluzo ca hule lalikulu.” (Ŵelengani Chivumbulutso 17:1, 6; 18:24.) Babulo Wamkulu wabweletsa citonzo cacikulu pa dzina la Mulungu. Wakhala akuphunzitsa anthu mabodza ponena za Mulungu. Iye wakhalanso akucita cigololo cauzimu mwa kupanga mgwilizano na olamulila a dziko. Komanso wakhala akupondeleza mamembala ake na kuwadyela masuku pa mutu. Kuwonjezela apo, Babulo Wamkulu wakhetsa magazi ambili, kuphatikizapo magazi a atumiki a Mulungu. (Chiv. 19:2) Kodi Yehova adzamuwononga bwanji Babulo Wamkulu?

11. Kodi “cilombo cofiila kwambili” ciimila ciani? Nanga Mulungu adzaciseŵenzetsa bwanji powononga Babulo Wamkulu?

11 Yehova adzaseŵenzetsa “nyanga 10” za “cilombo cofiila kwambili” powononga “hule lalikulu” limeneli. Cilombo cophiphilitsa cimeneci ciimila bungwe la United Nations. Nyanga 10 ziimila maboma onse andale amene amacilikiza bungwe limeneli. Pa nthawi ya Mulungu yoikika, maboma amenewa adzaukila Babulo Wamkulu. Iwo ‘adzamusakaza ndi kumusiya wamalisece’ mwa kumulanda cuma cake, ndiponso kuonetsa poyela kuipa kwake. (Chiv. 17:3, 16) Babulo Wamkulu adzawonongedwa mofulumila kwambili, ngati kuti ni m’tsiku limodzi, moti onse amene anali kumucilikiza adzadabwa. Iwo adzadabwa cifukwa iye wakhala akudzitama kuti: “Ine ndine mfumukazi. Sindine mkazi wamasiye, ndipo sindidzalila ngakhale pang’ono.”—Chiv. 18:7, 8.

12. Kodi Yehova sadzalola maboma a anthu kucita ciani? Nanga n’cifukwa ciani?

12 Mulungu sadzalola kuti mitundu ya anthu iwononge atumiki ake. Iwo amanyadila kuchedwa na dzina lake, ndipo anamvela lamulo lake lakuti atuluke mu Babulo Wamkulu. (Mac. 15:16, 17; Chiv. 18:4) Kuwonjezela apo, iwo ayesetsa kuthandiza ena kuti atulukemo. Conco, atumiki a Yehova sadzalandilako milili imene Babulo Wamkulu adzalandila. Olo n’telo, cikhulupililo cawo cidzayesedwa.

Kulikonse pa dziko lapansi kumene anthu a Mulungu adzakhala, adzadalila iye pamene Gogi adzawaukila(Onani ndime 13) *

13. (a) Kodi Gogi n’ndani? (b) Mogwilizana na Ezekieli 38:2, 8, 9, ni liti pamene Gogi adzasonkhana pa malo ophiphilitsa ochedwa Aramagedo?

13 Kuukila kwa Gogi. (Ŵelengani Ezekieli 38:2, 8, 9.) Zipembedzo zonse zonama zikadzawonongedwa, anthu a Mulungu sadzawonongedwa. Adzakhala ngati mtengo umene watsala wokha-wokha pambuyo pa cimphepo coopsa cam’kuntho. Koma Satana adzakwiya kwambili na zimenezi. Iye adzawonetsa mkwiyo wake mwa kufalitsa mabodza, kapena kuti ‘mauthenga onyansa ouzilidwa,’ pofuna kusonkhezela mitundu ya anthu kupanga mgwilizano kuti aukile atumiki a Yehova. (Chiv. 16:13, 14) Mgwilizano wa mitundu umenewu ni umene umachedwa “Gogi wa kudziko la Magogi.” Mitundu ya anthu ikadzaukila atumiki a Mulungu, ndiye kuti idzakhala kuti yasonkhana pa malo ophiphilitsa ochedwa Aramagedo.—Chiv. 16:16.

14. Kodi Gogi adzazindikila ciani?

14 Gogi adzadalila “mphamvu za anthu,” kapena kuti magulu ake a nkhondo. (2 Mbiri 32:8) Koma ife tidzadalila Yehova Mulungu wathu, olo kuti pa nthawiyo, anthu adzaona ngati kucita zimenezi n’kupusa. Iwo adzakhala na maganizo amenewa cifukwa coona kuti Babulo Wamkulu amene poyamba anali wamphamvu, milungu yake siinamupulumutse kwa “cilombo” na “nyanga 10.” (Chiv. 17:16) Conco, Gogi adzaona kuti n’zosavuta kutiwononga. Iye adzabwela ngati mitambo yophimba dziko kuti atiwononge. (Ezek. 38:16) Koma posakhalitsa, iye adzazindikila kuti wadzikola mu msampha. Mofanana na Farao pa Nyanja Yofiila, Gogi adzazindikila kuti akumenyana na Yehova.—Eks. 14:1-4; Ezek. 38:3, 4, 18, 21-23.

15. Kodi Khristu adzacita ciani pa Aramagedo?

15 Khristu na magulu ake a nkhondo akumwamba adzateteza anthu a Mulungu na kuwononga mitundu ya anthu na magulu awo a nkhondo. (Chiv. 19:11, 14, 15) Nanga n’ciani cidzacitikila mdani wamkulu wa Yehova, Satana, amene pogwilitsila nchito mabodza adzasonkhezela mitundu ya anthu kuukila atumiki a Mulungu pa Aramagedo? Yesu adzaponya Satana na viŵanda vake ku phompho. Iwo adzakhala kumeneko kwa zaka 1,000, ndipo sadzakhalanso na mphamvu yosoceletsa anthu.—Chiv. 20:1-3.

TINGACITE CIANI KUTI TIKAPULUMUKE PA ARAMAGEDO?

16. (a) Timaonetsa bwanji kuti ‘timam’dziŵa Mulungu’? (b) Kodi kudziŵa Mulungu kudzatithandiza bwanji pa Aramagedo?

16 Kaya takhala m’coonadi kwa zaka zambili kapena ayi, kuti tikapulumuke pa Aramagedo tifunika kuonetsa kuti ‘timam’dziŵa Mulungu,’ ndiponso kuti ‘timamvela uthenga wabwino wonena za Ambuye wathu Yesu.’ (2 Ates. 1:7-9) Kudziŵa Mulungu kumatanthauza kudziŵa miyezo yake, zimene amakonda, na zimene amazonda. Timaonetsa kuti timam’dziŵa ngati timam’konda, kumumvela, na kukhala wodzipeleka kwa iye yekha cabe. (1 Yoh. 2:3-5; 5:3) Ngati tikonda Mulungu, timakhala na mwayi ‘wodziwika kwa’ iye. Ndipo kudziŵika kwa Mulungu kudzatithandiza kuti tikapulumuke pa Aramagedo. (1 Akor. 8:3) N’cifukwa ciani takamba conco? Cifukwa cakuti ngati ndife odziŵika kwa Mulungu, ndiye kuti iye amatikonda.

17. Kodi kumvela “uthenga wabwino wonena za Ambuye wathu Yesu” kutanthauza ciani?

17 “Uthenga wabwino wonena za Ambuye wathu Yesu” utanthauza mfundo zonse za coonadi zimene Yesu anaphunzitsa, zimene zinalembedwa m’Baibo. Timaonetsa kuti timamvela uthenga wabwino umenewu mwa kuseŵenzetsa mfundo zimene Yesu anaphunzitsa mu umoyo wathu. Izi ziphatikizapo kuika zinthu za Ufumu patsogolo, kutsatila miyezo yolungama ya Mulungu, na kulengeza za Ufumu wake. (Mat. 6:33; 24:14) Ziphatikizaponso kuthandiza abale a Khristu odzozedwa, pamene akugwila nchito yaikulu imene anapatsidwa, yolalikila uthenga wabwino na kupanga ophunzila.—Mat. 25:31-40.

18. Kodi abale a Khristu odzozedwa adzacita ciani poyamikila zimene a nkhosa zina anawacitila?

18 Posacedwa, atumiki a Mulungu odzozedwa adzaonetsa kukoma mtima kwa Akhristu a “nkhosa zina,” cifukwa ca zabwino zimene iwo akuwacitila pano pa dziko lapansi. (Yoh. 10:16) Kodi adzacita bwanji zimenezo? Nkhondo ya Aramagedo isanayambe, onse a 144,000 adzakhala ataukitsidwa kale kupita kumwamba, monga zolengedwa zauzimu zosakhoza kufa. Ndipo pa nkhondo ya Aramagedo, iwo adzakhala mbali ya gulu lankhondo lakumwamba, limene lidzaphwanya Gogi na kuteteza “khamu lalikulu” la a nkhosa zina. (Chiv. 2:26, 27; 7:9, 10) Ndithudi! A khamu lalikulu adzakondwela kwambili podziŵa kuti anathandiza atumiki a Mulungu odzozedwa, pamene iwo anali pa dziko lapansi.

TINGACITE CIANI KUTI TIKHALEBE OKHULUPILIKA PAMENE MAPETO AKUYANDIKILA?

19-20. Olo kuti timakumana na mayeselo, n’ciani cingatithandize kukhalabe okhulupilika pamene Aramagedo ikuyandikila?

19 M’masiku otsiliza ovuta ano, atumiki ambili a Yehova akukumana na mayeselo. Ngakhale n’conco, n’zotheka kupilila mwacimwemwe. (Yak. 1:2-4) Kodi n’ciani cingatithandize? Cimodzi cofunika kwambili ni kulimbikila kupemphela mocokela pansi pa mtima. (Luka 21:36) Tifunikanso kucita zinthu mogwilizana na mapemphelo athu, mwa kuŵelenga Mawu a Mulungu tsiku lililonse na kusinkha-sinkha zimene timaŵelenga, kuphatikizapo maulosi ocititsa cidwi okamba za nthawi yathu ino. (Sal. 77:12) Cinanso, tifunika kucita zonse zimene tingathe pa nchito yolalikila. Tikacita zonsezi, tidzakhalabe na cikhulupililo colimba ndiponso ciyembekezo camphamvu.

20 Tangoganizilani cisangalalo cimene mudzakhala naco pamene Babulo Wamkulu adzawonongedwa, komanso pamene nkhondo ya Aramagedo idzatha! Koposa pamenepo, ganizilani cimwemwe cimene mudzakhala naco pamene dzina la Mulungu lidzayeletsedwa, ndiponso pamene anthu onse adzalemekeza ucifumu wake. (Ezek. 38:23) Inde, Aramagedo ni nkhani yokondweletsa kwa anthu amene amadziŵa Mulungu, kumvela Mwana wake, na kupilila mpaka pa mapeto.—Mat. 24:13.

NYIMBO 143 Musaleke Kugwila Nchito, Kuyang’anila, na Kuyembekezela

^ ndime 5 Anthu a Yehova akhala akuyembekezela Aramagedo kwa nthawi yaitali. M’nkhani ino, tikambilane kuti Aramagedo n’ciani. Tikambilanenso zocitika zimene zidzatsogolela ku Aramagedo, ndiponso zimene tingacite kuti tikhalebe okhulupilika pamene mapeto akuyandikila.

^ ndime 71 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Pamene zinthu zoopsa zikucitika, (1) sitidzaleka kulalikila malinga ngati zidzakhala zotheka kutelo, (2) tidzapitiliza kucita phunzilo laumwini na kulambila kwa pabanja, komanso (3) tidzapitiliza kudalila citetezo ca Mulungu.

^ ndime 85 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Apolisi atsala pang’ono kuthyola nyumba ya banja lacikhristu, ndipo banjalo likukhulupilila kuti Yesu na angelo ake akuona zimene zikucitikazo.