Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 38

“Bwelani kwa Ine . . . Ndipo Ndidzakutsitsimutsani”

“Bwelani kwa Ine . . . Ndipo Ndidzakutsitsimutsani”

“Bwelani kwa ine nonsenu ogwila nchito yolemetsa ndi olemedwa, ndipo ndidzakutsitsimutsani.”MAT. 11:28.

NYIMBO 17 ‘Nifuna’

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Malinga na Mateyu 11:28-30, kodi Yesu anapeleka lonjezo lotani ku khamu la anthu?

TSIKU lina Yesu anapeleka lonjezo lolimbikitsa ku khamu la anthu amene anali kumvetsela kwa iye. Anati: “Bwelani kwa ine, . . . ndipo ndidzakutsitsimutsani.” (Ŵelengani Mateyu 11:28-30.) Mawu a Yesu amenewa, sanali nkhambakamwa cabe. Mwacitsanzo, ganizilani zimene iye anacitila mayi wina amene anali kudwala matenda osautsa.

2. Kodi Yesu anacita ciani kwa mayi wodwala?

2 Mayi ameneyu anali kufunikila kwambili thandizo. Iye anali atapita kwa madokotala ambili kukafuna-funa thandizo kaamba ka matenda ake. Anavutika na matendawo kwa zaka 12, koma palibe aliyense amene anatha kum’cilitsa. Malinga na Cilamulo ca Mose, iye anali wodetsedwa. (Lev. 15:25) Atamva kuti Yesu akucilitsa anthu, anapita kukam’funa-funa. Atamupeza, anagwila ulusi wopota wa m’mbali mwa malaya ake akunja, ndipo nthawi yomweyo anacila. Kuwonjezela apo, zimene Yesu anacita pocilitsa mayiyu, zinam’thandiza kudziona kuti si wonyozeka, ndiponso kuzindikila kuti anthu amam’konda. Mwacitsanzo, pokamba naye, anaseŵenzetsa mawu aubwenzi akuti “mwanawe.” Kukamba zoona, mayiyu anatsitsimulidwa na kulimbikitsidwa ngako.—Luka 8:43-48.

3. Tikambilane mafunso ati m’nkhani ino?

3 Onani kuti mayiyu anacitapo kanthu mwa kupita kwa Yesu kuti apeze thandizo. N’zimenenso ife tiyenela kucita masiku ano. Tifunika kucita zonse zotheka kuti tipite kwa Yesu. N’zoona kuti pali pano, iye sacilitsa mozizwitsa anthu odwala mwakuthupi amene amapita kwa iye. Ngakhale n’telo, Yesu amatiitana kuti: “Bwelani kwa ine, . . . ndipo ndidzakutsitsimutsani.” M’nkhani ino, tikambilane mafunso asanu aya: Kodi timapita bwanji kwa Yesu? Kodi Yesu anatanthauza ciani pamene anakamba kuti “Senzani goli langa”? Kodi tingaphunzile ciani kwa Yesu? N’cifukwa ciani nchito imene watipatsa imatitsitsimula? Nanga tiyenela kucita ciani kuti tipitilize kutsitsimulidwa na goli la Yesu?

“BWELANI KWA INE”

4-5. Kodi timapita kwa Yesu m’njila zina ziti?

4 Njila imodzi imene timapitila kwa Yesu ni mwa kucita khama kuŵelenga m’Baibo zimene iye anakamba na kucita. (Luka 1:1-4) Ni udindo wathu kucita zimenezi. Timapitanso kwa Yesu mwa kusankha kubatizika kuti tikhale ophunzila ake.

5 Njila inanso imene timapitila kwa Yesu ni mwa kupita kwa akulu ngati tifunikila thandizo. Yesu amaseŵenzetsa “mphatso za amuna” zimenezi posamalila nkhosa zake. (Aef. 4:7, 8, 11; Yoh. 21:16; 1 Pet. 5:1-3) Conco, tifunika kucitapo kanthu mwa kupita kwa iwo kukapempha thandizo. Tisaganize kuti akulu angadziŵe okha zimene zili mu mtima mwathu, komanso zimene tikufunikila. Ganizilani zimene m’bale wina dzina lake Julian anakamba. Anati: “Cifukwa codwala, n’nafunika kusiya utumiki wa pa Beteli. Ndipo mnzanga wina ananilimbikitsa kuti nikapemphe akulu adzacite ulendo waubusa kwa ine kuti anilimbikitse. Poyamba, n’naona ngati kuti sin’nali kufunikila ulendo waubusa. Koma patapita nthawi, n’napita kukapempha thandizo, ndipo ulendo waubusa umenewo ni imodzi mwa mphatso zabwino kwambili zimene n’nalandilapo.” Akulu okhulupilika, monga amene anathandiza Julian, angatithandize kudziŵa “maganizo a Khristu,” kapena kuti kumvetsetsa na kutengela maganizo ake na khalidwe lake. (1 Akor. 2:16; 1 Pet. 2:21) Ndithudi, thandizo limene iwo angatipatse ni mphatso yamtengo wapatali.

“SENZANI GOLI LANGA”

6. Kodi Yesu anatanthauza ciani pamene anati: “Senzani goli langa”?

6 Pamene Yesu anakamba kuti: “Senzani goli langa,” n’kutheka kuti anatanthauza kuti “Muzinimvela monga Mbuye wanu.” N’kuthekanso kuti anatanthauza kuti “Senzani goli pamodzi nane, kuti titumikile Yehova capamodzi.” Mulimonsemo, kusenza goli kutanthauza kuti tiyenela kugwila nchito imene Ambuye wathu anatipatsa.

7. Malinga na Mateyu 28:18-20, ni nchito iti imene tinapatsidwa? Nanga tili na cidalilo cotani?

7 Timasenza goli la Yesu mwa kudzipatulila kwa Yehova na kubatizika. Aliyense ali na mwayi wosenza goli lake. Yesu sangakane aliyense amene amafuna kutumikila Mulungu na mtima wonse. (Yoh. 6:37, 38) Otsatila onse a Khristu ali na mwayi wogwilako nchito imene Yehova anapatsa Yesu. Tili na cidalilo cakuti Yesu adzapitiliza kutithandiza pamene tigwila nchito imeneyi.—Ŵelengani Mateyu 28:18-20.

“PHUNZILANI KWA INE”

Muzitsitsimula ena mmene Yesu anali kucitila(Onani ndime 8-11) *

8-9. N’cifukwa ciani anthu odzicepetsa anali kukopeka na Yesu? Nanga ni mafunso ati amene tiyenela kudzifunsa?

8 Anthu odzicepetsa anali kukopeka na Yesu. (Mat. 19:13, 14; Luka 7:37, 38) Cifukwa ciani? Cabwino, ganizilani kusiyana kumene kunalipo pakati pa Yesu na Afarisi. Afarisi anali onyada ndi opanda cikondi. (Mat. 12:9-14) Koma Yesu anali wacikondi na wodzicepetsa. Afarisi anali okonda kuchuka, ndipo anali kudziona apamwamba kwambili. Yesu analangiza ophunzila ake kuti anayenela kupewa mzimu woipa umenewu. M’malomwake, anawaphunzitsa kukhala odzicepetsa na kutumikila ena. (Mat. 23:2, 6-11) Afarisi anali kupondeleza anthu mwa kuwacititsa kukhala mwamantha. (Yoh. 9:13, 22) Koma Yesu anali kutsitsimula anthu mwa kucita nawo zinthu mwacikondi komanso kukamba nawo mokoma mtima.

9 Kodi mumayesetsa kutsatila citsanzo ca Yesu? Dzifunseni kuti: ‘Kodi anthu ena amaniona kuti ndine wofatsa na wodzicepetsa? Kodi nimadzipeleka kugwila nchito yotsika potumikila ena? Kodi nimacita zinthu mokoma mtima na ena?’

10. Kodi Yesu anali kucita zinthu motani poseŵenza na ena?

10 Poseŵenza na ena, Yesu anali kucita zinthu m’njila yakuti anzake azikhala mwamtendele ndi mwacimwemwe. Komanso, anali kukonda kuphunzitsa ena nchito. (Luka 10:1, 19-21) Cifukwa ca mmene Yesu anali kucitila zinthu, ophunzila ake anali kukhala omasuka kumufunsa mafunso. Ndipo iyenso anali kuwafunsa mafunso kuti amvele maganizo awo. (Mat. 16:13-16) Conco, mofanana na mbewu zimene zimakula bwino ngati zisamalidwa na kutetezedwa, ophunzila a Yesu anakula na kupita patsogolo mwauzimu. Iwo anagwilitsila nchito zimene Yesu anali kuwaphunzitsa, moti anabala zipatso mwa kucita nchito zabwino.

Khalani aubwenzi na ofikilika

Khalani okangalika

Khalani odzicepetsa ndi wolimbikila nchito *

11. Ni mafunso ati amene tiyenela kudzifunsa?

11 Kodi muli na udindo woyang’anila anthu ena? Ngati n’telo, mungacite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi nimacita bwanji zinthu na ena ku nchito kapena ku nyumba? Kodi nimalimbikitsa mtendele? Kodi kacitidwe kanga ka zinthu kamapangitsa ena kukhala omasuka kufunsa mafunso? Kodi nimaonetsa kuti nifuna kumvelako malingalilo awo?’ Sitifuna kukhala ngati Afarisi, amene anali kukwiya anthu akawafunsa mafunso, ndiponso kucitila nkhanza anthu amene apeleka malingalilo osiyana ndi awo.—Maliko 3:1-6; Yoh. 9:29-34.

“MUDZATSITSIMULIDWA”

12-14. N’cifukwa ciani nchito imene Yesu anatipatsa ni yotsitsimula?

12 N’cifukwa ciani n’zotsitsimula kugwila nchito imene Yesu anatipatsa? Pali zifukwa zambili zimene zimapangitsa nchitoyi kukhala yotsitsimula. Tiyeni tikambilaneko zifukwa zocepa cabe.

13 Tili na oyang’anila abwino kwambili. Yehova ni Woyang’anila Wamkulu. Iye si mbuye wankhanza kapena wosayamika. Koma amayamikila nchito imene timacita. (Aheb. 6:10) Ndipo amatipatsa mphamvu zimene timafunikila kuti tigwile nchito imene watipatsa. (2 Akor. 4:7; Agal. 6:5) Mfumu yathu Yesu, anatipatsa citsanzo cabwino ca mmene tiyenela kucitila zinthu na ena. (Yoh. 13:15) Nawonso akulu amatengela citsanzo ca Yesu, “m’busa wamkulu,” pamene akutisamalila. (Aheb. 13:20; 1 Pet. 5:2) Amayesetsa kucita zinthu mokoma mtima, molimba mtima, na molimbikitsa pamene akutitsogolela na kutiteteza.

14 Tili na mabwenzi abwino kwambili. Kuposa anthu ena onse, ife atumiki a Mulungu tili na mabwenzi acikondi kwambili na nchito yokondweletsa ngako. Ganizilani cabe: Tili na mwayi wogwila nchito pamodzi na abale na alongo a makhalidwe abwino. Iwo sadziona apamwamba kuposa ena. Ali na maluso ambili, koma ni odzicepetsa. Ndipo amaona ena kukhala owaposa. Iwo amationa monga anchito anzawo, komanso monga mabwenzi awo. Amatikonda kwambili cakuti ni okonzeka ngakhale kutifela.

15. Kodi tiyenela kuiona bwanji nchito imene timagwila?

15 Tili na nchito yabwino kwambili. Timaphunzitsa anthu coonadi ponena za Yehova, na kuvumbula mabodza a Mdyelekezi. (Yoh. 8:44) Satana amacitila anthu nkhanza mwa kuwaphunzitsa mabodza amene amawapangitsa kukhala opanda ciyembekezo. Mwacitsanzo, iye amakamba kuti Yehova sangatikhululukile macimo athu, ndiponso kuti ndife oipa kwambili moti Mulungu sangatikonde. Awa ni mabodza amkunkhuniza komanso ofooketsa kwambili. Zoona n’zakuti, tikapita kwa Khristu, macimo athu amakhululukidwa. Ndipo Yehova amatikonda kwambili ife tonse. (Aroma 8:32, 38, 39) N’zokondweletsa kwambili kuthandiza anthu kuyamba kudalila Yehova na kuwaona akusintha umoyo wawo.

PITILIZANI KUTSITSIMULIDWA NA GOLI LA YESU

16. Kodi goli limene Yesu akutipempha kunyamula n’losiyana bwanji na magoli ena amene timanyamula?

16 Goli limene Yesu akutipempha kunyamula n’losiyana na magoli ena amene timanyamula. Mwacitsanzo, ambili pokomboka ku nchito, amakhala olema komanso opanda cimwemwe. Mosiyana na zimenezi, tikakomboka pa nchito yotumikila Yehova na Khristu, timakhala acimwemwe kwambili. Nthawi zina, timakhala olema kwambili pocoka ku nchito yakuthupi, ndipo timacita kudzikakamiza kuti tipite ku misonkhano ya mkati mwa wiki madzulo. Olo n’telo, pocoka kumeneko, nthawi zambili timakhala titatsitsimulidwa na kulimbikitsidwa. Mofananamo, ngati timayesetsa kulalikila mwakhama na kucita phunzilo laumwini, timatsitsimulidwa na kulimbikitsidwa.

17. Kodi sitiyenela kuiŵala ciani? Nanga tiyenela kusamala na ciani?

17 Tisaiŵale kuti aliyense wa ife ali na malile pa zimene angakwanitse kucita. Conco, tiyenela kuganizila mosamala zinthu zimene timasankha kucita. Mwacitsanzo, tingawononge mphamvu zathu poyesa-yesa kudziunjikila cuma. Koma kumbukilani zimene Yesu anauza mnyamata wina wolemela amene anamufunsa kuti: “Ndicite ciani kuti ndikapeze moyo wosatha?” Mnyamata ameneyu anali kale kutsatila Cilamulo. Ayenela kuti anali munthu wabwino ndithu, cifukwa buku la Uthenga Wabwino la Maliko limakamba mosapita m’mbali kuti Yesu “anam’konda.” Yesu anapempha mnyamatayo kuti abwele kwa iye. Anati “Pita kagulitse zilizonse zimene uli nazo, . . . ndiyeno ubwele udzakhale wotsatila wanga.” Mnyamatayo anali kufuna kutsatila Yesu, koma sanakwanitse cifukwa sanafune kusiya “katundu wambili” amene anali naye. (Maliko 10:17-22) Cotelo, anakana kusenza goli limene Yesu anamupatsa, ndipo anapitiliza kutumikila “Cuma.” (Mat. 6:24) Kodi imwe mukanasankha ziti?

18. Kodi nthawi na nthawi tiyenela kucita ciani? Ndipo n’cifukwa ciani?

18 Nthawi na nthawi, tiyenela kudzifufuza kuti tione zimene timaika patsogolo mu umoyo wathu. Cifukwa ciani? Kucita zimenezi kungatithandize kuti tiziseŵenzetsa bwino mphamvu zathu. Ganizilani zimene m’bale wina wacinyamata, dzina lake Mark, anakamba. Iye anati: “Kwa zaka zambili, n’nali kuganiza kuti nili na umoyo wosalila zambili. N’nali kucita upainiya, koma nthawi zonse n’nali kuganizila za ndalama na kulaka-laka umoyo wapamwamba. Sin’nali kumvetsa cifukwa cake sin’nali kukhala wacimwemwe. Ndiyeno, n’nazindikila kuti vuto linali lakuti n’nali kuthela nthawi na mphamvu zanga zoculuka pofuna kukwanilitsa zofuna zanga, koma Yehova n’nali kungom’patsa zotsala cabe.” M’bale Mark anasintha maganizo ake na zocita zake, n’colinga cakuti acite zambili potumikila Yehova. Iye anati: “Nimakhala na nkhawa nthawi zina, koma mwa thandizo la Yehova na Yesu, lomba nimakwanitsa kusumika maganizo anga potumikila Yehova.”

19. N’cifukwa ciani kuona zinthu moyenela n’kofunika kwambili?

19 Pali zinthu zitatu zimene tifunika kucita kuti tipitilize kutsitsimulidwa na goli la Yesu. Coyamba, tiziona zinthu moyenela. Timagwila nchito ya Yehova. Conco, tifunika kuigwila mogwilizana na malangizo ake. Ife ndife anchito cabe, koma Yehova ndiye Mwini wa nchito. (Luka 17:10) Ngati tigwila nchito ya Mulungu popanda kutsatila malangizo ake, tingakhale ngati ng’ombe imene ikulimbana na goli. Ngakhale ng’ombe yamphamvu kwambili ingadzivulaze na kulema kwambili, ngati nthawi zonse imalimbana na goli limene aimangamo na kukana kuyenda m’njila imene mbuye wake akufuna. Koma ngati titsatila malangizo a Yehova pogwila nchito yake, tingakwanitse kucita zinthu zimene tinali kuona kuti sitingathe, na kugonjetsa zopinga zilizonse zimene zingakhalepo. Tizikumbukila kuti palibe aliyense amene angalepheletse Yehova kukwanilitsa cifunilo cake.—Aroma 8:31; 1 Yoh. 4:4.

20. Kodi colinga cathu posenza goli la Yesu ciyenela kukhala ciani?

20 Caciŵili, tizitumikila tili na colinga cabwino. Colinga cathu ni kupeleka ulemelelo kwa Atate wathu wacikondi, Yehova. Anthu ena a m’nthawi ya atumwi, amene anali kutsatila Yesu na zolinga zadyela, posapita nthawi cimwemwe cawo cinatha, ndipo anasiya kusenza goli lake. (Yoh. 6:25-27, 51, 60, 66; Afil. 3:18, 19) Koma anthu amene anali kutsatila Yesu cifukwa cokondadi Mulungu ndi anthu anzawo, anapitiliza kutumikila Yehova mwacimwemwe kwa moyo wawo wonse. Ndipo anakhala na ciyembekezo cokalamulila na Khristu kumwamba. Nafenso n’cimodzi-modzi. Kuti tikhalebe acimwemwe, tifunika kusenza goli la Yesu na colinga cabwino.

21. Mogwilizana na Mateyu 6:31-33, kodi tili na cikhulupililo cakuti Yehova adzacita ciani?

21 Cacitatu, tikhale na cikhulupililo cakuti Yehova adzakhala nafe. Tinasankha kukhala umoyo wodzimana na kugwila nchito ya Yehova modzipeleka. Yesu anakambilatu kuti tidzazunzidwa. Koma tili na cikhulupililo cakuti Yehova adzatipatsa mphamvu kuti tikwanitse kupilila mavuto aliwonse amene tingakumane nawo. Ndipo pamene tipilila mavuto, m’pamene cikhulupililo cathu cimalimbila-limbila. (Yak. 1:2-4) Tilinso na cikhulupililo cakuti Yehova adzatipatsa zosoŵa zathu, ndipo Yesu adzatiŵeta, komanso abale na alongo athu adzatilimbikitsa. (Ŵelengani Mateyu 6:31-33; Yoh. 10:14; 1 Ates. 5:11) Ndithudi! Tili na zonse zofunikila zimene zingatithandize kupilila mavuto alionse amene tingakumane nawo.

22. N’ciani cimatipangitsa kukhala okondwela?

22 Mayi amene Yesu anacilitsa, anatsitsimulidwa pa tsiku limene anacilitsidwa. Koma kuti atsitsimulidwe kwamuyaya, anafunika kukhala wophunzila wokhulupilika wa Khristu. Kodi muganiza kuti anacita ciani? Ngati anasankha kusenza goli la Yesu, ndiye kuti anakhala na mwayi wokalandila mphoto yapamwamba kwambili, yokalamulila na Yesu kumwamba. Ndipo zilizonse zimene anasiya kuti ayambe kutsatila Khristu n’zosanunkha kanthu poyelekezela na mphoto imeneyi. Kaya tili na ciyembekezo cokakhala na moyo wosatha kumwamba kapena padziko lapansi, ndife okondwela kwambili kuti tinalabadila ciitano ca Yesu cakuti: “Bwelani kwa ine.”

NYIMBO 13 Khristu ni Citsanzo Cathu

^ ndime 5 Yesu amatiitana kuti tipite kwa iye. Kodi timapita bwanji kwa Yesu? Nkhani ino iyankhe funso limeneli. Itikumbutsenso mmene kugwila nchito na Khristu kumatitsitsimulila.

^ ndime 60 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Yesu anatsitsimula anthu m’njila zosiyana-siyana.

^ ndime 66 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Mofananamo, m’bale akutsitsimula ena m’njila zosiyana-siyana.