Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 37

Gonjelani Yehova na Mtima Wonse

Gonjelani Yehova na Mtima Wonse

“Kuli bwanji ndi Atate . . . kodi sitiyenela kuwagonjela koposa pamenepo?”​AHEB. 12:9.

NYIMBO 9 Yehova Ndiye Mfumu Yathu!

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. N’cifukwa ciani tifunika kugonjela Yehova?

TIFUNIKA kugonjela * Yehova cifukwa ndiye anatilenga. Conco, ali na mphamvu yotiuza zocita. (Chiv. 4:11) Palinso cifukwa cina cabwino cimene ciyenela kutisonkhezela kumugonjela. Cifukwa cake n’cakuti, ulamulilo wake ndiwo wabwino koposa. Kuyambila kale, anthu ambili akhala akulamulila anthu anzawo. Koma Yehova ndiye Wolamulila wanzelu, wacikondi, wacisomo, ndiponso wacifundo kwambili kuposa wolamulila wina aliyense.—Eks. 34:6; Aroma 16:27; 1 Yoh. 4:8.

2. Kodi Aheberi 12:9-11 imafotokoza zifukwa ziti zimene ziyenela kutisonkhezela kugonjela Yehova?

2 Yehova amafuna kuti tizimumvela, osati cabe cifukwa coopa kum’khumudwitsa, koma maka-maka cifukwa com’konda ndiponso cifukwa comuona kuti ni Atate wathu wacikondi. M’kalata yake yopita kwa Aheberi, Paulo anafotokoza kuti tiyenela kugonjela Atate wathu Yehova na mtima wonse, cifukwa amatilangiza “kuti tipindule.”—Ŵelengani Aheberi 12:9-11.

3. (a) Timaonetsa bwanji kuti timagonjela Yehova? (b) Ni mafunso ati amene tikambilane?

3 Timagonjela Yehova mwa kuyesetsa kumumvela pa zinthu zonse, komanso mwa kupewa mtima wodalila luso lathu lomvetsa zinthu. (Miy. 3:5) Cimakhala cosavuta kugonjela Yehova tikaphunzila zambili za makhalidwe ake abwino. N’cifukwa ciani zili telo? Cifukwa cakuti pa ciliconse cimene Yehova amacita, amaonetsa makhalidwe ake abwino amenewa. (Sal. 145:9) Tikamaphunzila zambili za Yehova, m’pamenenso timayamba kum’konda kwambili. Ndipo tikayamba kum’konda Yehova, sitimafunikila malamulo ambili-mbili otiuza zoyenela kucita na zosayenela kucita. Timayesetsa kutengela maganizo ake, kukonda zimene amaona kuti n’zabwino, na kupewa zoipa. (Sal. 97:10) Koma nthawi zina, zimakhala zovuta kumvela Yehova. N’cifukwa ciani zimakhala conco? Nanga n’ciani cimene akulu angaphunzile kwa Bwanamkubwa Nehemiya? N’ciani cimene atate angaphunzile kwa Mfumu Davide? Komanso n’ciani cimene amayi angaphunzile kwa Mariya, amayi ake a Yesu? Nkhani ino idzayankha mafunso amenewa.

CIFUKWA CAKE KUGONJELA YEHOVA KUNGAKHALE KOVUTA

4-5. Malinga na Aroma 7:21-23, n’cifukwa ciani cingakhale covuta kumvela Yehova?

4 Cifukwa cimodzi cimene cimapangitsa kuti nthawi zina kugonjela Yehova kukhale kovuta n’cakuti, tonse tinabadwa na ucimo, ndipo ndife opanda ungwilo. Conco, mwacibadwa tilibe mtima wofuna kumvela Yehova. Adamu na Hava atapandukila Mulungu mwa kudya cipatso coletsedwa, anakana kutsatila miyezo ya Mulungu ya cabwino na coipa. (Gen. 3:22) Masiku anonso, anthu ambili safuna kumvela Yehova, ndipo amadzisankhila okha coyenela na cosayenela.

5 Olo anthu amene amam’dziŵa Yehova na kum’konda, nthawi zina zimawavuta kumumvela. Mtumwi Paulo analimbanapo na vuto limeneli. (Ŵelengani Aroma 7:21-23.) Molingana na Paulo, nafenso timafuna kucita zoyenela pamaso pa Yehova. Koma kuti ticite zimenezi, tifunika kupitiliza kulimbana na cilako-lako cofuna kucita zoipa.

6-7. Kodi cifukwa cina cimene cingapangitse kuti cikhale covuta kugonjela Yehova n’citi? Fotokozani citsanzo.

6 Cina cimene cingapangitse kuti cikhale covuta kugonjela Yehova n’cakuti timasonkhezeledwa na cikhalidwe ca kumene tinakulila. Maganizo a anthu ambili m’dzikoli ni osemphana na cifunilo ca Yehova. Conco, timafunika kucita khama nthawi zonse kuti tipewe kutengela maganizo awo. Onani citsanzo ici.

7 M’madela ena, acicepele amakakamizidwa kuwonongela mphamvu na nthawi yawo yoculuka pofuna-funa ndalama zambili. Mlongo wina dzina lake Mary, * anakumanapo na vuto limeneli. Asanaphunzile za Yehova, anacita maphunzilo apamwamba pa univesiti inayake yochuka m’dziko lawo. A m’banja lake anali kum’kakamiza kuti apeze nchito yapamwamba ya ndalama zambili kuti ena azimulemekeza. Iyenso anali kufuna zimenezo. Koma ataphunzila za Yehova na kuyamba kum’konda, anasintha colinga cake. Olo n’telo, zinthu zinali zovutabe kwa iye. Anati: “Nthawi zina, nimapeza mwayi woloŵa nchito yapamwamba komanso ya ndalama zambili. Koma nimadziŵa kuti nchitoyo inganilepheletse kucita zambili potumikila Yehova. Cifukwa ca mmene n’naleledwela, nthawi zina zimanivuta kukana. Nimapempha Yehova kuti anithandize kuti nisagonje, nikayesedwa kuti niloŵe nchito imene ingasokoneze utumiki wanga.”—Mat. 6:24.

8. Kodi tsopano tikambilane ciani?

8 Ndithudi, timapindula ngati tigonjela Yehova. Ndipo Akhristu amene ali na ulamulilo pa ena, monga akulu, atate, na amayi, ali na cifukwa cinanso cokhalila ogonjela kwa Mulungu. Cifukwa cake n’cakuti ngati agonjela Yehova, amapindulitsanso ena. Tiyeni lomba tikambilane zitsanzo zina za m’Baibo, zoonetsa mmene munthu angaseŵenzetsele mphamvu ya ulamulilo imene ali nayo m’njila yokondweletsa Yehova.

ZIMENE AKULU ANGAPHUNZILE KWA NEHEMIYA

Akulu amatengako mbali pa nchito ya pa Nyumba ya Ufumu, monga mmene Nehemiya anacitila pa nchito yokonzanso mpanda wa Yerusalemu(Onani ndime 9-11) *

9. Ni mavuto ati amene Nehemiya anapeza ku Yerusalemu?

9 Yehova anapatsa akulu udindo wofunika kwambili wosamalila anthu ake. (1 Pet. 5:2) Akulu angaphunzile zambili mwa kuona mmene Nehemiya anali kucitila zinthu ndi anthu a Yehova. Pokhala bwanamkubwa wa Ayuda, Nehemiya anali na mphamvu zambili za ulamulilo. (Neh. 1:11; 2:7, 8; 5:14) Ganizilani cabe ena mwa mavuto amene Nehemiya anapeza ku Yerusalemu. Iye anapeza kuti Ayuda anali ataipitsa kacisi, komanso sanali kupeleka zopeleka zothandizila Alevi, monga mmene Cilamulo cinakambila. Cinanso, Ayuda sanali kusunga Sabata, ndipo amuna ena anali atakwatila akazi a mitundu ina osalambila Yehova. Bwanamkubwa Nehemiya anafunika kukonza zinthu zolakwika zimenezi.—Neh. 13:4-30.

10. Kodi Nehemiya anacitapo ciani pa mavuto amene anapeza ku Yerusalemu?

10 Nehemiya sanaseŵenzetse udindo wake molakwika mwa kukakamiza anthu a Mulungu kutsatila maganizo ake. M’malomwake, anapemphela kwa Yehova mocokela pansi pa mtima kuti amutsogolele. Ndiponso anayamba kuphunzitsa Ayuda Cilamulo ca Yehova. (Neh. 1:4-10; 13:1-3) Kuwonjezela apo, modzicepetsa, Nehemiya anaseŵenzela pamodzi na Ayuda, ngakhale pa nchito yomanganso mpanda wa Yerusalemu.—Neh. 4:15.

11. Malinga na 1 Atesalonika 2:7, 8, kodi akulu ayenela kucita zinthu motani na abale na alongo mu mpingo?

11 Masiku ano, akulu angatengele citsanzo ca Nehemiya m’njila zambili, ngakhale kuti mwina mu mpingo mwawo mulibe mavuto monga amene Nehemiya anapeza ku Yerusalemu. Mwacitsanzo, akulu amagwila nchito mwakhama posamalila abale na alongo. Iwo sadziona kukhala apamwamba kuposa ena cifukwa ca udindo umene ali nawo. M’malomwake, amacita zinthu mokoma mtima na abale na alongo mu mpingo. (Ŵelengani 1 Atesalonika 2:7, 8.) Amakamba na ena mokoma mtima, cifukwa cakuti ni acikondi na odzicepetsa. M’bale Andrew, amene watumikila monga mkulu kwa nthawi yaitali, anati: “Naona kuti abale na alongo amalimbikitsidwa ngako ngati mkulu ni wokoma mtima ndi wacikondi. Makhalidwe amenewa amasonkhezela mpingo kugwilizana na akulu.” M’bale Tony, amenenso watumikila monga mkulu kwa nthawi yaitali, anati: “Nimacita zonse zotheka kutsatila uphungu wa pa Afilipi 2:3. Nimayesetsa nthawi zonse kuona ena kukhala oniposa. Izi zimanithandiza kupewa mtima wokonda kulamulila ena.”

12. N’cifukwa ciani akulu afunika kukhala odzicepetsa?

12 Akulu ayenela kukhala odzicepetsa, monga mmene Yehova alili wodzicepetsa. Olo kuti iye ni Wolamulila Wamkulu wa cilengedwe conse, “amatsika m’munsi” kuti ‘adzutse munthu wonyozeka kumucotsa m’fumbi.’ (Sal. 18:35; 113:6, 7) Ndipo Yehova amanyansidwa ndi anthu onyada na odzikuza.—Miy. 16:5.

13. N’cifukwa ciani mkulu afunika ‘kulamulila lilime lake’?

13 Mkulu amene amagonjela Yehova ayenela ‘kulamulila lilime lake.’ Apo ayi, angakambe mwaukali kwa munthu amene wacita zinthu mosam’lemekeza. (Yak. 1:26; Agal. 5:14, 15) M’bale Andrew, amene tam’chulapo kale, anati: “Nthawi zina, nimafuna kukamba mwaukali kwa m’bale kapena mlongo amene wacita zinthu mosanilemekeza. Koma kusinkha-sinkha zitsanzo za amuna okhulupilika a m’Baibo, kwanithandiza kuona kufunika kokhala wodzicepetsa na wofatsa.” Akulu amaonetsa kugonjela kwa Yehova mwa kukamba mwacikondi ndi mwaulemu kwa abale na alongo mu mpingo, komanso kwa akulu anzawo.—Akol. 4:6.

ZIMENE ATATE ANGAPHUNZILE KWA MFUMU DAVIDE

14. Ni udindo uti umene Yehova anapeleka kwa tate? Nanga amafuna kuti azicita ciani?

14 Yehova anaika tate kukhala mutu wa banja, ndipo amafuna kuti iye aziphunzitsa na kulangiza ana ake. (1 Akor. 11:3; Aef. 6:4) Komabe, ulamulilo wa tate uli na malile. Iye adzayankha mlandu kwa Yehova, amene amapangitsa banja lililonse kukhala na dzina. (Aef. 3:14, 15) Atate amaonetsa kuti amagonjela Yehova mwa kuseŵenzetsa ulamulilo wawo m’njila imene imakondweletsa Mulungu. Iwo angaphunzile zambili pa nkhaniyi mwa kuŵelenga za umoyo wa Mfumu Davide.

Mapemphelo a tate wacikhristu ayenela kuonetsa kuti ni wodzicepetsa(Onani ndime 15-16) *

15. N’cifukwa ciani Mfumu Davide ni citsanzo cabwino cimene atate ayenela kutengela?

15 Davide anali mutu wa banja, ndipo Yehova anamuikanso kukhala mfumu ya mtundu wonse wa Isiraeli. Pokhala mfumu, Davide anali na mphamvu zambili za ulamulilo. Pa nthawi ina, iye anaseŵenzetsa molakwika mphamvu zake, moti anacita zolakwa zazikulu. (2 Sam. 11:14, 15) Komabe, Davide anagonjela Yehova. Motani? Analandila uphungu umene anapatsidwa. Komanso anakhuthulila Yehova nkhawa zake m’pemphelo. Ndipo anayesetsa kumvela uphungu wa Yehova. (Sal. 51:1-4) Kuonjezela apo, anaonetsa kudzicepetsa mwa kulandila uphungu wanzelu wocokela kwa amuna, ngakhalenso kwa akazi. (1 Sam. 19:11, 12; 25:32, 33) Davide anaphunzilapo kanthu pa zolakwa zake, ndipo anasumika maganizo ake pa kutumikila Yehova.

16. Ni zinthu zina ziti zimene atate angaphunzile kwa Davide?

16 Kodi ni zinthu zina ziti zimene imwe atate mungaphunzile kwa Mfumu Davide? Musamagwilitsile nchito molakwa mphamvu za ulamulilo zimene Yehova anakupatsani. Muzivomeleza zolakwa zanu, na kulandila uphungu wa m’Baibo wocokela kwa ena. Mukatelo, banja lanu lidzakulemekezani kwambili cifukwa ca kudzicepetsa kwanu. Popemphela na banja lanu, m’khuthulileni Yehova nkhawa zanu. A m’banja lanu aziona kuti mumam’dalila kwambili. Ndipo koposa zonse, muziona kutumikila Yehova kukhala kofunika ngako mu umoyo wanu. (Deut. 6:6-9) Citsanzo canu cabwino ni mphatso ina yamtengo wapatali imene mungapatse banja lanu.

ZIMENE AMAYI ANGAPHUNZILE KWA MARIYA

17. Kodi Yehova anapatsa mayi udindo wotani?

17 Yehova anapatsa mayi mbali yofunika kwambili m’banja. Anam’patsa udindo wolangiza ana. (Miy. 6:20) Ndipo zimene mayi amakamba na kucita zingakhudze anawo kwa moyo wawo wonse. (Miy. 22:6) Onani zimene amayi angaphunzile kwa Mariya, amayi ake a Yesu.

18-19. Kodi amayi angaphunzile ciani kwa Mariya?

18 Mariya anali kuwadziŵa bwino Malemba. Iye anali kulemekeza Yehova kwambili ndiponso anali naye pa ubwenzi wolimba. Analolela kucita zimene Yehova anamuuza, olo kuti izi zinali kudzasintha umoyo wake wonse.—Luka 1:35-38, 46-55.

Ngati mayi walema kapena wakhumudwa, amafunika kuugwila mtima kuti acitebe zinthu mwacikondi kwa a m’banja lake(Onani ndime 19) *

19 Masiku ano, imwe amayi mungatengele citsanzo ca Mariya m’njila zingapo. Yoyamba, muzicita phunzilo laumwini na kupemphela kwa Yehova pamwekha kuti mukhalebe pa ubwenzi wolimba na iye. Yaciŵili, yesetsani kuwongolela mbali zimene simucita bwino kuti mukondweletse Yehova. Mwacitsanzo, mwina munaleledwa na makolo okwiya msanga amene anali kukonda kukukalipilani. Pa cifukwa ici, n’kutheka kuti munakula na maganizo akuti umu ni mmene ana ayenela kuleledwela. Olo pambuyo pophunzila miyezo ya Yehova, mwina zimakuvutani kucita zinthu modekha na moleza mtima ndi ana anu, maka-maka ngati sakumvelani pamene mwalema. (Aef. 4:31) Pa nthawi ngati zimenezi, m’pamene mufunika kudalila kwambili Yehova mwa kupemphela kwa iye. Mayi wina dzina lake Lydia anati: “Nthawi zina, nimacita kupemphela kwambili kuti nisakam’kalipile mwana wanga ngati sakunimvela. Pa nthawi ina, nili mkati mokamba, n’nacita kudzigwila pakamwa kuti nisakambe mawu oipa, n’kuyamba kupemphela kwa Yehova ca mu mtima kuti anithandize. Pemphelo limanithandiza kukhala wodekha.”—Sal. 37:5.

20. Kodi amayi ena amakumana na vuto lanji? Nanga angacite ciani kuti alithetse?

20 Vuto lina limene amayi ena amakhala nalo n’lakuti amavutika kuonetsa cikondi kwa ana awo. (Tito 2:3, 4) Ambili mwa amayi amenewo, analeledwa na makolo amene sanali kuonetsa cikondi kwa ana awo. Ngati umu ni mmene imwe munaleledwela, musatengele citsanzo colakwika ca makolo anu. Mayi amene amagonjela Yehova na kucita cifunilo cake, amafunika kuphunzila kuonetsa cikondi kwa ana ake. N’zoona kuti zingakhale zovuta kusintha kaganizidwe kanu, mmene mumamvelela, komanso mmene mumacitila zinthu. Komabe, n’zotheka kusintha, ndipo kusintha kumeneko kungapangitse kuti imwe na banja lanu mukhale acimwemwe kwambili.

PITILIZANI KUGONJELA YEHOVA

21-22. Malinga na Yesaya 65:13, 14 ni mapindu ati amene timapeza ngati tigonjela Yehova?

21 Mfumu Davide anali kudziŵa mapindu amene amakhalapo ngati tigonjela Yehova. Iye anati: “Malamulo ocokela kwa Yehova ndi olungama, amasangalatsa mtima. Cilamulo ca Yehova ndi coyela, cimatsegula maso. Ndiponso mtumiki wanu amacenjezedwa nazo. Munthu wosunga zigamulozo amapeza mphoto yaikulu.” (Sal. 19:8, 11) Masiku ano, timaona kusiyana pakati pa anthu amene amagonjela Yehova, ndi anthu amene amakana uphungu wake wacikondi. Anthu amene amagonjela Yehova, amafuula “mokondwa cifukwa cokhala ndi cimwemwe mumtima.”—Ŵelengani Yesaya 65:13, 14.

22 Ngati akulu, atate, na amayi amagonjela Yehova na mtima wonse, amakhala na umoyo wabwino, mabanja awo amakhala acimwemwe, ndipo mpingo nawonso umakhala wogwilizana kwambili. Koposa zonse, amakondweletsa mtima wa Yehova. (Miy. 27:11) Kunena zoona, palibe cina cosangalatsa kuposa kucita zinthu zokondweletsa mtima wa Yehova!

NYIMBO 123 Gonjelani Dongosolo la Mulungu

^ ndime 5 M’nkhani ino, tikambilane zifukwa zimene ziyenela kutisonkhezela kugonjela Yehova. Tikambilanenso mmene akulu, atate, na amayi, angaseŵenzetsele mphamvu ya ulamulilo imene Yehova anawapatsa. Iwo angaphunzile zambili kwa Bwanamkubwa Nehemiya, Mfumu Davide na Mariya, amayi ake a Yesu.

^ ndime 1 KUFOTOKOZELA MAWU ENA: Anthu amene amacita kukamizidwa kumvela munthu wina, sakondwela na mfundo yakuti tiyenela kugonjela. Koma anthu a Mulungu amaona kuti kugonjela kuli cabe bwino, cifukwa amacita kusankha okha kumvela Yehova.

^ ndime 7 M’nkhani ino, maina ena asinthidwa.

^ ndime 62 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Mkulu aseŵenzela pamodzi na mwana wake pa nchito yokonza zowonongeka pa Nyumba ya Ufumu, monga mmene Nehemiya anathandizila pa nchito yomanganso mpanda wa Yerusalemu.

^ ndime 64 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Tate akupemphela kwa Yehova mocokela pansi pa mtima pamodzi na banja lake.

^ ndime 66 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Kamnyamata kataila nthawi yaitali kucita maseŵela a pa kompyuta, koma sikanatsilize kugwila nchito zapakhomo na homuweki yake. Amayi ake abwela ku nchito ali olema, ndipo akumulangiza modekha, popanda kukamba mawu aukali.