Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 39

“Taonani! “Khamu Lalikulu la Anthu”

“Taonani! “Khamu Lalikulu la Anthu”

“Ndinaona khamu lalikulu la anthu, limene palibe munthu aliyense amene anatha kuliwelenga, . . . ataimilila pamaso pa mpando wacifumu ndi pamaso pa Mwanawankhosa.”CHIV. 7:9.

NYIMBO 60 Ni Moyo Wawo

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Kodi zinthu zinali bwanji mu umoyo wa mtumwi Yohane ca m’ma 95 C.E?

CA M’MA 95 C.E., zinthu zinali zovuta kwambili mu umoyo wa mtumwi Yohane. Iye anali wokalamba, anali mkaidi pa cisumbu ca Patimo, ndipo ayenelanso kuti anali atatsala yekha mtumwi wa Yesu. (Chiv. 1:9) Yohane anali kudziŵa kuti ampatuko anali kusoceletsa mipingo na kuyambitsa magaŵano. Zinali kuoneka monga kuti mpingo wacikhristu, umene unali waung’ono pa nthawiyo, unali utangotsala pang’ono kufafanizidwa.—Yuda 4; Chiv. 2:15, 20; 3:1, 17.

Mtumwi Yohane anaona “khamu lalikulu” litavala mikanjo yoyela, ndiponso litanyamula nthambi za kanjedza m’manja mwawo (Onani ndime 2)

2. Malinga na Chivumbulutso 7:9-14, ni masomphenya aulosi ati okondweletsa amene Yohane anaona? (Onani cithunzi pa cikuto.)

2 Mkati mwa nthawi yovutayo, Yohane anaona masomphenya aulosi okondweletsa. M’masomphenya amenewo, iye anamva mngelo wina akuuza angelo anayi kuti agwile mphepo zowononga za cisautso cacikulu, mpaka atadinda cidindo comaliza pa kagulu ka akapolo a Mulungu. (Chiv. 7:1-3) Kagulu kameneka ni ka Akhristu a 144,000, amene adzalamulila pamodzi na Yesu kumwamba. (Luka 12:32; Chiv. 7:4) Ndiyeno, Yohane anakamba kuti anaona gulu lina lalikulu kwambili la anthu, cakuti anati: “Zimenezi zitatha, nditayang’ana ndinaona khamu lalikulu la anthu, limene palibe munthu aliyense amene anatha kuliwelenga, locokela m’dziko lililonse, fuko lililonse, mtundu uliwonse, ndi cinenelo ciliconse. Iwo anali ataimilila pamaso pa mpando wacifumu ndi pamaso pa Mwanawankhosa.” (Ŵelengani Chivumbulutso 7:9-14.) Ganizilani cabe cimwemwe cimene Yohane anali naco atadziŵa zakuti kutsogolo, anthu masauzande ambili-mbili adzayamba kulambila Mulungu m’coonadi!

3. (a) N’cifukwa ciani masomphenya a Yohane ayenela kulimbitsa cikhulupililo cathu? (b) Tiphunzile ciani m’nkhani ino?

3 N’zosacita kufunsa kuti cikhulupililo ca Yohane cinalimba kwambili ataona masomphenya amenewa. Koma kuposa Yohane, ife ndiye tiyenela kulimbikitsidwa kwambili cifukwa tikukhala m’nthawi ya kukwanilitsidwa kwa masomphenyawa. Taona khamu la anthu ofika m’mamiliyoni likusonkhanitsidwa. Iwo ali na ciyembekezo cokapulumuka cisautso cacikulu na kudzakhala na moyo wamuyaya pa dziko lapansi. M’nkhani ino, tiphunzile mmene Yehova anathandizila anthu ake zaka zoposa 80 zapitazo, kudziŵa bwino kuti khamu lalikulu n’ndani. Pambuyo pake, tikambilane mbali ziŵili zokhudza khamu limeneli: (1) kukula kwake, na (2) mitundu yosiyana-siyana ya anthu amene ali m’gululi. Mfundo zimenezi ziyenela kulimbitsa cikhulupililo ca onse amene ali m’gulu lodalitsika limeneli.

KODI KHAMU LALIKULU LIDZAKHALA KUTI?

4. Ni mfundo ya coonadi iti imene Machechi Acikhristu saimvetsetsa? Nanga Ophunzila Baibo anasiyana bwanji na Machechi Acikhristu pa nkhani imeneyi?

4 Machechi ambili acikhristu saphunzitsa mfundo ya coonadi ya m’Malemba, yakuti kutsogolo anthu omvela adzakhala na moyo wosatha pa dziko lapansi. (2 Akor. 4:3, 4) Masiku ano, machechi ambili acikhristu amaphunzitsa kuti anthu onse abwino amapita kumwamba akamwalila. Koma izi n’zosiyana na zimene kagulu kocepa ka Ophunzila Baibo kanali kuphunzitsa. Iwo anayamba kufalitsa magazini ya Nsanja ya Mlonda m’caka ca 1879. Ophunzila Baibo anali kukhulupilila kuti Mulungu adzabwezeletsa Paradaiso pa dziko lapansi. Anali kukhulupililanso kuti anthu omvela mamiliyoni ambili adzakhala pano pa dziko lapansi, osati kumwamba. Komabe, panatenga nthawi yaitali kuti iwo amvetsetse kuti anthu omvela amenewa ni ati maka-maka.—Mat. 6:10.

5. Kodi Ophunzila Baibo anali kukhulupilila ciani za a 144,000?

5 Kuwonjezela apo, Ophunzila Baibo anali kudziŵa kuti malinga n’zimene Malemba amakamba, anthu ena ‘adzagulidwa pa dziko lapansi’ kuti akalamulile na Yesu kumwamba. (Chiv. 14:3) Anthu amenewo ni kagulu ka Akhristu odzipatulila komanso okangalika okwana 144,000, amene amatumikila Mulungu mokhulupilika pano pa dziko lapansi. Nanga kodi iwo anali kukhulupilila ciani za khamu lalikulu?

6. Kodi Ophunzila Baibo anali kukhulupilila ciani za khamu lalikulu?

6 M’masomphenya ake, Yohane anaona a khamu lalikulu “ataimilila pamaso pa mpando wacifumu ndi pamaso pa Mwanawankhosa.” (Chiv. 7:9) Mawu amenewa anapangitsa Ophunzila Baibo kuyamba kukhulupilila kuti nawonso a khamu lalikulu adzakhala kumwamba, mofanana na a 144,000. Koma funso limene linabwelapo linali lakuti, ‘Ngati a 144,000 na a khamu lalikulu, onse adzakhala kumwamba, kodi adzasiyana bwanji?’ Ophunzila Baibo anali kukhulupilila kuti a khamu lalikulu ni Akhristu amene anali kumvela Mulungu pamene anali pa dziko lapansi, koma osati na mtima wawo onse. Anali kukhulupililanso kuti anthu ena amene anali kutsatila mfundo za m’Baibo, koma anali m’Machechi Acikhristu, naonso anali mbali ya khamu lalikulu. Ophunzila Baibo anali kuona kuti ngakhale kuti a khamu lalikulu anali kum’konda Mulungu, cikondi cawo sicinali cokwanila moti n’kukhala oyenelela kukalamulila na Yesu. Conco, anali kukhulupilila kuti a khamu lalikulu adzapita ndithu kumwamba, koma cifukwa ca kucepa kwa cikondi cawo, adzangokhala pamaso pa mpando wacifumu, osati pa mipando yacifumu.

7. Kodi Ophunzila Baibo anali kukhulupilila kuti n’ndani adzakhala pa dziko lapansi mu Ulamulilo wa Khristu wa Zaka 1000? Nanga anali kukhulupilila ciani za anthu akale okhulupilika?

7 Nanga Ophunzila Baibo anali kukhulupilila kuti n’ndani adzakhala pa dziko lapansi? Anali kukhulupilila kuti a 144,000 na a khamu lalikulu akadzatengedwa kupita kumwamba, anthu ena mamiliyoni ambili adzakhala na moyo pano pa dziko lapansi, kuti asangalale na madalitso a Ulamulilo wa Khristu wa Zaka 1000. Ophunzila Baibo sanali kukhulupilila kuti anthu mamiliyoni amenewa adzayamba kutumikila Yehova, Ulamulilo wa Khristu wa Zaka 1000 usanayambe. M’malomwake, anali kukhulupilila kuti anthuwa adzaphunzitsidwa za Yehova mkati mwa Zaka 1000. Ndipo amene adzamvela Yehova, adzakhala na moyo wosatha pano pa dziko lapansi, koma amene sadzamvela, adzawonongedwa. Cinanso, Ophunzila Baibo anali kuganiza kuti mwina ena mwa anthu amene adzatumikila monga “akalonga” pa dziko lapansi mu Ulamulilo wa Khristu, kuphatikizapo anthu akale okhulupilika amene anafa Khristu asanabwele, adzalandila mphoto ya moyo wakumwamba kumapeto kwa Ulamulilo wa Zaka 1000.—Sal. 45:16.

8. Kodi Ophunzila Baibo anali kukhulupilila kuti ni magulu atatu ati amene ali na mbali pa colinga ca Mulungu?

8 Conco, Ophunzila Baibo anali kukhulupilila kuti pali magulu atatu a anthu: (1) a 144,000, amene adzalamulila na Yesu kumwamba; (2) khamu lalikulu la Akhristu acikhulupililo cocepelapo, amene adzaima pamaso pa mpando wacifumu kumwamba; ndiponso (3) anthu mamiliyoni ambili amene adzaphunzitsidwa njila za Yehova pa dziko lapansi, mkati mwa Ulamulilo wa Khristu wa Zaka 1000. * Pa nthawi yake yoyenela, Yehova anathandiza Ophunzila Baibo kumvetsetsa coonadi pa nkhani imeneyi.—Miy. 4:18.

KUWALA KWA COONADI KUWONJEZEKA

Pa msonkhano wacigawo wa mu 1935, khamu la anthu okhala na ciyembekezo ca pa dziko lapansi linabatizika(Onani ndime 9)

9. (a) Kodi a khamu lalikulu pa dziko lapansi amaima bwanji “pamaso pa mpando wacifumu ndi pamaso pa Mwanawankhosa”? (b) N’cifukwa ciani tikamba kuti kamvedwe kameneka n’kolondola?

9 Mu 1935, Mboni za Yehova zinamvetsetsa coonadi ponena za khamu lalikulu limene Yohane anaona m’masomphenya ake. Mboni za Yehova zinadziŵa kuti a khamu lalikulu sacita kufunika kukakhala kumwamba kuti aime “pamaso pa mpando wacifumu ndi pamaso pa Mwanawankhosa.” Kuima kwawo pamaso pa mpando wacifumu ndi pamaso pa Mwanawankhosa n’kophiphilitsa cabe. Olo kuti ali pa dziko lapansi, a khamu lalikulu amaima “pamaso pa mpando wacifumu” mwa kuzindikila ulamulilo wa Yehova na kugonjela ucifumu wake. (Yes. 66:1) Komanso, amaima “pamaso pa Mwanawankhosa” mwa kukhulupilila nsembe ya dipo la Yesu. Izi n’zogwilizana na zimene Mateyu 25:31, 32 imakamba, zakuti mitundu yonse ya anthu,” kuphatikizapo oipa, “idzasonkhanitsidwa kwa” Yesu, kapena kuti pamaso pake ali pa mpando wake wacifumu waulemelelo. N’zodziŵikilatu kuti mitundu yonse ya anthu yochulidwa pa lembali idzasonkhanitsidwa pa dziko lapansi, osati kumwamba. Kamvedwe katsopano kameneka n’kolondola. Kamatithandiza kumvetsetsa cifukwa cake Baibo siikambako zakuti a khamu lalikulu adzatengedwa kupita kumwamba. Gulu limodzi cabe ndilo linalonjezedwa kukakhala na moyo wosatha kumwamba. Gulu limeneli ni a 144,000, amene “adzakhala mafumu olamulila dziko lapansi” pamodzi na Yesu.—Chiv. 5:10.

10. N’cifukwa ciani a khamu lalikulu afunika kuphunzitsidwa njila za Yehova Ulamulilo wa Zaka 1000 usanayambe?

10 Conco, kuyambila mu 1935, ife Mboni za Yehova takhala tikukhulupilila kuti khamu lalikulu limene Yohane anaona m’masomphenya ni gulu la Akhristu okhulupilika, amene ali na ciyembekezo codzakhala na moyo wosatha pano pa dziko lapansi. Kuti a khamu lalikulu akapulumuke cisautso cacikulu, afunika kuphunzitsidwa njila za Yehova Ulamulilo wa Zaka 1000 usanayambe. Iwo adzafunika kuonetsa kuti ali na cikhulupililo colimba, kuti ‘adzathe kuthawa zinthu zonse zimene zikuyembekezeka kucitika’ Ulamulilo wa Khristu wa Zaka 1000 usanayambe.Luka 21:34-36.

11. N’cifukwa ciani Ophunzila Baibo ena anali kuganiza kuti kumapeto kwa Ulamulilo wa Zaka 1000, mwina anthu ena adzapita kumwamba?

11 Nanga bwanji za maganizo akuti kumapeto kwa Ulamulilo wa Zaka 1000, mwina anthu ena okhulupilika pa dziko lapansi adzapita kumwamba? Mfundo yakuti mwina zimenezi zingacitike inalembedwa zaka zambili zapitazo, mu Nsanja ya Mlonda ya February 15, 1913. Ndipo inabwela cifukwa cakuti Ophunzila Baibo ena anali na maganizo akuti, ‘Atumiki a Mulungu okhulupilika akale sangalandile cabe moyo wa pa dziko lapansi, pamene Akhristu ena amene si okhulupilika mofanana na atumiki akalewo adzalandila moyo wa kumwamba.’ Maganizo amenewa anabwela cifukwa cokhulupilila mfundo zolakwika ziŵili izi: (1) yakuti a khamu lalikulu adzakhala kumwamba, na (2) yakuti khamu lalikulu ni gulu la Akhristu amene ali na cikhulupililo cocepelapo.

12-13. Kodi odzozedwa na a khamu lalikulu amadziŵa ciani ponena za mphoto yawo?

12 Komabe, monga takambila kale, kuyambila mu 1935, Mboni za Yehova zinamvetsetsa kuti anthu opulumuka Aramagedo ndiwo a khamu lalikulu amene Yohane anaona m’masomphenya. Iwo ‘adzatuluka m’cisautso cacikulu’ pano pa dziko lapansi. Ndipo adzapitilizabe “kufuula ndi mawu okweza, kuti: ‘Cipulumutso cathu cacokela kwa Mulungu wathu, amene wakhala pampando wacifumu, ndi kwa Mwanawankhosa.’” (Chiv. 7:10, 14) Kuwonjezela apo, Malemba amakamba kuti anthu amene adzaukitsidwa kukakhala na moyo kumwamba, adzalandila “cinthu cabwino kwambili” kuposa zimene anthu akale okhulupilika adzalandile. Conco, panthawiyo Mboni za Yehova zinamvetsa kuti anthu okhulupilika akale ali na ciyembekezo codzakhala na moyo wosatha pano padziko lapansi, osati kumwamba. (Aheb. 11:40) Abale athu atamvetsetsa mfundo imeneyi, anayamba kuitanila anthu ena mokangalika kuti ayambe kutumikila Yehova, ali na ciyembekezo cokakhala na moyo wosatha pano pa dziko lapansi.

13 A khamu lalikulu amakondwela na ciyembekezo cimene ali naco. Amadziŵa kuti Yehova ndiye ali na udindo wosankha kumene olambila ake okhulupilika adzatumikila, kaya kumwamba kapena pa dziko lapansi. Akhristu onse, kaya odzozedwa kapena a khamu lalikulu, amadziŵa kuti adzalandila mphoto yawo kokha kaamba ka cisomo ca Yehova, cimene anacionetsa mwa kupeleka nsembe ya dipo la Yesu Khristu.—Aroma 3:24.

KHAMU LIMENELI NI LALIKULUDI

14. Pambuyo pa 1935, n’cifukwa ciani ambili sanali kudziŵa mmene ulosi wonena za khamu lalikulu udzakwanilitsidwila?

14 Anthu a Yehova atamvetsetsa za khamu lalikulu mu 1935, ambili sanali kudziŵa kuti zidzatheka bwanji kuti anthu oyembekezela kudzakhala pa dziko lapansi akhaledi khamu lalikulu. Mwacitsanzo, m’bale Ronald Parkin anali na zaka 12 pamene atumiki a Mulungu anamvetsetsa kuti khamu lalikulu n’ndani. Iye anati: “Pa nthawiyo, panali ofalitsa pafupi-fupi 56,000 pa dziko lonse lapansi, ndipo odzozedwa analipo ambili, mwinanso kuposa a khamu lalikulu. Conco, khamu lalikulu silinali kuoneka lalikulu kweni-kweni.”

15. Kodi nchito yosonkhanitsa khamu lalikulu yakhala ikupita patsogolo motani?

15 Koma citapita caka ca 1935, amishonale anayamba kutumizidwa m’maiko ambili, ndipo ciŵelengelo ca Mboni za Yehova cinapitiliza kuwonjezeka. Ndiyeno, mu 1968, panayambika pulogilamu yophunzitsa anthu Baibo, poseŵenzetsa buku lakuti Coonadi Cimene Cimatsogolela ku Moyo Wamuyaya. Bukuli linali kufotokoza coonadi m’njila yosavuta kumva. Izi zinacititsa kuti anthu ambili ofatsa abwele m’gulu la Mulungu kuposa kale lonse. Ndipo m’zaka zinayi cabe, anthu oposa 500, 000 anabatizika na kukhala ophunzila a Khristu. Komanso, pamene chechi ya Katolika inayamba kucepa mphamvu ku Latin America na ku maiko ena, ndiponso pamene ziletso pa nchito yathu zinacotsedwa kum’maŵa kwa Europe na m’maiko ena a mu Africa, anthu ofika m’mamiliyoni anabatizika. (Yes. 60:22) M’zaka zaposacedwa, gulu la Yehova lafalitsa mabuku ena othandiza kwambili, n’colinga cothandiza anthu kudziŵa zimene Baibo imaphunzitsa. Ndithudi! Yehova wasonkhanitsa khamu lalikulu, limene lomba lili na anthu oposa 8 miliyoni.

KHAMU LA ANTHU A MITUNDU YOSIYANA-SIYANA

16. Kodi khamu lalikulu likusonkhanitsidwa kucokela kuti?

16 Polemba za masomphenya ake, Yohane anati khamu lalikulu lidzacokela “m’dziko lililonse, fuko lililonse, mtundu uliwonse, ndi cinenelo ciliconse.” Zaka zambili kumbuyoko, nayenso mneneli Zekariya anali atalemba ulosi wofanana na umenewu. Iye anati: “M’masiku amenewo, amuna 10 ocokela m’zilankhulo zonse za anthu a mitundu ina adzagwila covala ca munthu amene ndi Myuda ndi kunena kuti: ‘Anthu inu tipita nanu limodzi, cifukwa tamva kuti Mulungu ali ndi inu.’”—Zek. 8:23.

17. N’ciani cikucitika pofuna kuthandiza anthu ocokela m’mitundu yonse na zinenelo zonse?

17 Ife Mboni za Yehova timadziŵa kuti uthenga wabwino ufunika kulalikidwa m’vitundu vambili, kuti anthu a zinenelo zonse asonkhanitsidwe. Takhala tikumasulila mabuku ophunzilila Baibo kwa zaka zoposa 130. Koma lomba nchito yomasulila yakula kwambili kuposa kale lonse. Tikumasulila mabuku ophunzilila Baibo m’vitundu voposa 900. Inde, Yehova akucita cozizwitsa masiku ano. Akusonkhanitsa khamu lalikulu la anthu kucokela m’mitundu yonse. Ndipo cifukwa cakuti cakudya cauzimu cikupezeka m’vitundu vambili tsopano, a khamu lalikulu amalambila Yehova mogwilizana, olo kuti ali m’maiko osiyana-siyana. Ndiponso Mboni za Yehova ni zodziŵika kwambili cifukwa ca khama lawo pa nchito yolalikila, komanso cifukwa cakuti amakondana. Kodi si zolimbitsa cikhulupililo zimenezi?—Mat. 24:14; Yoh. 13:35.

MMENE MASOMPHENYAWA AMATIKHUDZILA

18. (a) Mogwilizana na Yesaya 46:10, 11, n’cifukwa ciani n’zosadabwitsa kuti Yehova wakwanilitsa ulosi wokamba za khamu lalikulu? (b) N’cifukwa ciani anthu amene ali na ciyembekezo codzakhala pano pa dziko lapansi saona kuti anamanidwa mwayi?

18 Ndife okondwa kwambili na kukwanilitsidwa kwa ulosi wokhudza khamu lalikulu. N’zosadabwitsa kuona kuti Yehova wakwanilitsa ulosi umenewu m’njila yocititsa cidwi. (Ŵelengani Yesaya 46:10, 11.) A khamu lalikulu amayamikila Yehova cifukwa ca ciyembekezo cimene anawapatsa. Saona kuti anamanidwa mwayi cifukwa cakuti sanadzozedwe na mzimu wa Mulungu kuti akatumikile limodzi na Yesu kumwamba. M’Malemba, timaŵelenga za atumiki a Mulungu ambili okhulupilika, amene anali kutsogoleledwa mwapadela na mzimu woyela, koma sali m’gulu la a 144,000. Mmodzi wa iwo ni Yohane M’batizi. (Mat. 11:11) Wina ni Davide. (Mac. 2:34) Atumiki a Mulungu amenewa na ena ambili-mbili, adzaukitsidwa na kukhala na moyo m’paradaiso pano pa dziko lapansi. Onse amenewa, pamodzi na a khamu lalikulu, adzakhala na mwayi woonetsa kukhulupilika kwawo kwa Yehova na ucifumu wake.

19. Ngati tamvetsetsa tanthauzo la ulosi wa Yohane wokamba za khamu lalikulu, kodi tidzacita ciani?

19 Tsopano Mulungu akusonkhanitsa anthu mamiliyoni ocokela m’mitundu yonse kuti am’lambile mogwilizana. Izi sizinacitikepo n’kale lonse. Conco, kaya ciyembekezo cathu n’copita kumwamba kapena cokhala pa dziko lapansi, tifunika kuthandiza anthu ambili mmene tingathele, kuti abwele m’gulu la khamu lalikulu la “nkhosa zina.” (Yoh. 10:16) Posacedwa, Yehova adzabweletsa cisautso cacikulu cimene cinanenedwelatu, ndipo adzawononga maboma na zipembedzo zonse zimene zabweletsa mavuto osaneneka pakati pa anthu. Ha! Ni ciyembekezo cokondweletsa cotani nanga cimene onse a khamu lalikulu ali naco, codzatumikila Yehova pa dziko lapansi kwamuyaya!—Chiv. 7:14.

NYIMBO 139 Yelekeza Uli M’dziko Latsopano

^ ndime 5 M’nkhani ino, tikambilane masomphenya aulosi amene Yohane anaona, okhudza kusonkhanitsa “khamu lalikulu.” Mosakaikila, nkhaniyi idzalimbitsa cikhulupililo ca onse amene ali m’gulu lodalitsika limeneli.

^ ndime 8 Onani buku lakuti Jehovah’s Witnesses—Proclaimers of God’s Kingdom, tsa. 159-163.