Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 35

Yehova Amaona Atumiki Ake Odzicepetsa Kukhala Amtengo Wapatali

Yehova Amaona Atumiki Ake Odzicepetsa Kukhala Amtengo Wapatali

“Yehova . . . amaona wodzicepetsa.”​SAL. 138:6.

NYIMBO 48 Kuyenda ndi Yehova Tsiku na Tsiku

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Kodi Yehova amawaona bwanji anthu odzicepetsa? Fotokozani.

YEHOVA amakonda anthu odzicepetsa. Ndipo anthu okhawo amene ali odzicepetsadi, ndiwo angakhale naye pa ubale wolimba. Koma anthu ‘odzikuza sawayandikila.’ (Sal. 138:6) Tonse timafuna kukondweletsa Yehova. Timafunanso kuti iye azitikonda. Conco, tili na zifukwa zabwino zokulitsila khalidwe la kudzicepetsa.

2. Tikambilane ciani m’nkhani ino?

2 M’nkhani ino, tikambilane mafunso atatu aya: (1) Kodi kudzicepetsa kumatanthauza ciani? (2) N’cifukwa ciani tiyenela kukhala na khalidwe limeneli? (3) Nanga ni zocitika ziti zimene zingayese kudzicepetsa kwathu? Monga mmene tiphunzilile m’nkhani ino, tikakhala odzicepetsa, timakondweletsa mtima wa Yehova, ndipo zinthu zimatiyendela bwino.—Miy. 27:11; Yes. 48:17.

KODI KUDZICEPETSA KUMATANTHAUZA CIANI?

3. Kodi kudzicepetsa kumatanthauza ciani?

3 Kudzicepetsa kumatanthauza kusadziona wapamwamba kuposa ena, komanso kusakhala odzikuza kapena odzitukumula. Baibo imaonetsa kuti munthu wodzicepetsa amadziŵa kuti Yehova ni wapamwamba kwambili kuposa iye, ndipo amalemekeza anthu ena. Munthu wodzicepetsa amadziŵa kuti munthu aliyense ni wom’posa m’njila inayake.—Afil. 2:3, 4.

4-5. N’cifukwa ciani tingakambe kuti kudzicepetsa kweni-kweni sikudalila cabe mmene munthu amaonekela?

4 Pali anthu ena amene amaoneka ngati odzicepetsa, koma m’ceni-ceni si odzicepetsa. Amakhala a zii. Mwina angamacite zinthu mwaulemu ndi anthu cifukwa ca mmene analeledwela, kapena cifukwa ca cikhalidwe cawo. Koma mkati mwa mtima, angakhale odzikudza kwambili. M’kupita kwa nthawi, umunthu wawo weni-weni umaonekela.—Luka 6:45.

5 Kumbali ina, ngati munthu ni wopanda mantha, wansangala, kapena amakamba zinthu mosapita mbali, sindiye kuti basi ni wodzikuza. (Yoh. 1:46, 47) Komabe, anthu opanda mantha komanso ansangala afunika kukhala osamala kuti asayambe kudalila maluso awo. Kaya ndife opanda mantha komanso ansangala kapena ayi, tonse tifunika kuyesetsa kukhala wodzicepetsa.

Mtumwi Paulo anali wodzicepetsa(Onani ndime 6) *

6. Monga mmene taonela pa 1 Akorinto 15:10, tiphunzilapo ciani pa citsanzo ca mtumwi Paulo?

6 Ganizilani citsanzo ca mtumwi Paulo. Yehova anamuseŵenzetsa kwambili pokhazikitsa mipingo yatsopano m’mizinda yosiyana-siyana. Iye ayenela kuti anacita zambili potumikila Yehova kuposa mtumwi wina aliyense wa Yesu Khristu. Ngakhale n’conco, Paulo sanadzione kukhala wapamwamba kuposa atumwi anzake. Modzicepetsa, iye anati: “Ndine wamng’ono kwambili mwa atumwi onse, ndipo si ine woyenela kuchedwa mtumwi, cifukwa ndinazunza mpingo wa Mulungu.” (1 Akor. 15:9) Ndiyeno, Paulo anakamba kuti anali pa ubale wolimba na Yehova cifukwa ca cisomo ca Mulungu, osati cifukwa ca makhalidwe ake kapena cifukwa ca zimene anacita potumikila Mulungu. (Ŵelengani 1 Akorinto 15:10.) Ndithudi! Paulo anapeleka citsanzo cabwino kwambili ca kudzicepetsa. M’kalata imene analembela Akhristu anzake a ku Korinto, iye sanakambe modzikuza, olo kuti ena mu mpingowo anafuna kudzionetsa apamwamba kuposa iye.—2 Akor. 10:10.

Karl F. Klein, m’bale wodzicepetsa amene anatumikilapo m’Bungwe Lolamulila(Onani ndime 7)

7. Kodi abale ena audindo m’nthawi yathu ino aonetsa bwanji kudzicepetsa? Fotokozani citsanzo.

7 Atumiki ambili a Yehova amalimbikitsidwa ngako na nkhani yofotokoza mbili ya M’bale Karl F. Klein, amene anatumikilapo m’Bungwe Lolamulila. M’nkhaniyo, M’bale Klein anafotokoza moona mtima komanso modzicepetsa zinthu zambili zimene sanacite bwino, komanso mavuto amene anakumana nawo mu umoyo wake. Mwacitsanzo, iye anakamba kuti anali kuona ulaliki wa ku nyumba na nyumba kukhala wovuta kwambili, cakuti pamene anacita ulalikiwu kwa nthawi yoyamba mu 1922, sanaucitekonso mpaka panatha zaka ziŵili. Anakambanso kuti pa nthawi ina, ali kutumikila pa Beteli, anasungila cakukhosi m’bale wina amene anam’patsa uphungu. Kuwonjezela apo, iye anadwalapo matenda ovutika maganizo cifukwa ca nkhawa, koma pambuyo pake anacila. Ndipo anakhalanso na mwayi wocita mautumiki ambili ofunika kwambili. M’bale Klein anali munthu waudindo. Koma moona mtima, anafotokoza zofooka zake. Kodi si kudzicepetsa kumeneku? Abale na alongo oculuka saiŵala nkhani yogwila mtima komanso yokambidwa moona mtima yofotokoza mbili ya M’bale Klein. *

N’CIFUKWA CIANI TIYENELA KUKHALA ODZICEPETSA?

8. Kodi 1 Petulo 5:6 imaonetsa bwanji kuti kudzicepetsa kumakondweletsa Yehova?

8 Cifukwa cacikulu cimene tiyenela kukhalila odzicepetsa n’cakuti khalidwe limeneli limakondweletsa Yehova. Mtumwi Petulo anamveketsa bwino mfundo imeneyi. (Ŵelengani 1 Petulo 5:6.) Pothilila ndemanga mawu a Petulo, buku lakuti “Bwera Ukhale Wotsatira Wanga” limati: “Kudzikuza kuli ngati poizoni, ndipo kumawononga zinthu kwambili. Munthu amene ali na luso lotha kucita bwino zinthu zosiyana-siyana angakhale wacabe-cabe m’maso mwa Mulungu ngati wayamba kudzikuza. Koma munthu wodzicepetsa, ngakhale atakhala wooneka ngati wonyozeka, amakhala wamtengo wapatali kwa Yehova. . . . [Iye] adzasangalala kukupatsani inunso mphoto cifukwa ca kudzicepetsa kwanu.” * Kunena zoona, palibe cina cabwino cimene tingacite kuposa kukondweletsa mtima wa Yehova.—Miy. 23:15.

9. N’cifukwa ciani anthu amakondwela kukhala nafe ngati ndife odzicepetsa?

9 Kuwonjezela pa kukondweletsa Yehova, timapindulanso m’njila zambili ngati ndife odzicepetsa. Tikakhala odzicepetsa, anthu ena amamasuka nafe. Kuti timvetsetse cifukwa cake, tingacite bwino kuganizila mmene ifeyo timamvelela tikakhala ndi anthu odzicepetsa. (Mat. 7:12) Ambili a ife sitikondwela kukhala na munthu amene nthawi zonse amafuna kuti ena azicita zinthu mmene iye afunila, amenenso safuna kumvelako malingalilo a ena. Mosiyana na zimenezi, timakondwela kukhala na abale na alongo athu “omvelana cisoni, okonda abale, acifundo cacikulu, ndiponso amaganizo odzicepetsa.” (1 Pet. 3:8) Popeza ife timakondwela kukhala ndi anthu odzicepetsa, nawonso adzakondwela kukhala nafe ngati ndife odzicepetsa.

10. Kodi kudzicepetsa kumatithandiza bwanji kuona zinthu moyenela mu umoyo?

10 Kudzicepetsa kumatithandiza kuti tiziona zinthu moyenela mu umoyo wathu. Nthawi zina, tingaone kapena kukumana na zinthu zimene tiona kuti n’zopanda cilungamo. Mfumu yanzelu Solomo anati: “Ndaonapo anchito atakwela pamahachi, koma akalonga akuyenda pansi ngati anchito.” (Mlal. 10:7) Anthu aluso kwambili, nthawi zina sapatsidwa ulemu. Ndipo nthawi zina anthu amene alibe luso kweni-kweni, ni amene amalandila ulemu woculuka. Ngakhale n’conco, Solomo anaonetsa kuti n’cinthu canzelu kungovomeleza mmene zinthu zilili, m’malo mongokhalila kuda nkhawa cifukwa ca zinthu zimene sizinayende bwino. (Mlal. 6:9) Ngati ndife odzicepetsa, cidzakhala cosavuta kungovomeleza mmene zinthu zilili mu umoyo wathu.

ZIMENE ZINGAYESE KUDZICEPETSA KWATHU

Kodi zinthu monga zimene zicitika apa zingayese bwanji kudzicepetsa kwathu?(Onani ndime 11-12) *

11. N’cifukwa ciani kudzicepetsa n’kofunika tikapatsidwa uphungu?

11 Tsiku lililonse, timakhala na mipata yambili imene tingaonetsele khalidwe la kudzicepetsa. Ganizilani zocitika izi: Tikapatsidwa uphungu. Tiyenela kukumbukila kuti ngati munthu walimba mtima mpaka kubwela kudzatipatsa uphungu, ndiye kuti mwina talakwitsa kwambili kuposa mmene tikuonela. Tikapatsidwa uphungu, nthawi zambili timakhala na maganizo ongofuna kuukana uphunguwo. Tingayambe kudandaula za munthuyo kapena za mmene watipatsila uphunguwo. Koma ngati ndife odzicepetsa, tidzayesetsa kuona uphungu moyenela.

12. Malinga na Miyambo 27:5, 6, n’cifukwa ciani tiyenela kumuyamikila munthu akatipatsa uphungu? Fotokozani citsanzo.

12 Munthu wodzicepetsa amayamikila akapatsidwa uphungu. Tiyelekezele motele: Tinene kuti muli pa msonkhano. Ndiyeno, pambuyo pokamba na abale na alongo angapo, mmodzi wa iwo wakutengelani pa mbali na kukuuzani kuti m’maso mwanu muli manthongo. Mwacionekele, mungacite manyazi na zimenezi. Koma mungam’yamikile munthuyo cifukwa cokuuzani zimenezi. Ndipo mungaone kuti zikanakhala bwino munthu wina akanakuuzani zimenezi mwamsanga. Mofananamo, ngati m’bale kapena mlongo walimba mtima kubwela kudzatipatsa uphungu umene tikufunikila, tiyenela kuyamikila na kukhala wodzicepetsa. Tiyenela kuona munthuyo monga bwenzi lathu, osati mdani wathu.—Ŵelengani Miyambo 27:5, 6; Agal. 4:16.

N’cifukwa ciani kudzicepetsa n’kofunika pamene ena alandila mwayi wa utumiki?(Onani ndime 13-14) *

13. Kodi tingaonetse bwanji kudzicepetsa pamene ena alandila mwayi wa utumiki?

13 Ena akalandila mwayi wa utumiki. M’bale Jason amene ni mkulu, anati: “Nikaona kuti ena apatsidwa mwayi winawake wa utumiki, nthawi zina nimadabwa kuti n’cifukwa ciani ine sinipatsidwako mwayi wotele.” Kodi na imwe munamvelapo conco? Sikulakwa kukhala na colinga cocita zambili potumikila Yehova. (1 Tim. 3:1) Koma tifunika kukhala osamala. Ngati sitingasamale, mzimu wodzikuza ungayambe kukula mu mtima mwathu. Mwacitsanzo, m’bale angayambe kuganiza kuti ndiye woyenelela kwambili kukhala pa udindo winawake. Kapena mlongo mu mtima mwake angayambe kukamba kuti, ‘Amuna anga ndiwo woyenelela kwambili kukhala pa udindo umenewu kuposa m’bale wakuti-wakuti.’ Komabe, ngati ndife odzicepetsadi, tidzapewa maganizo odzitukumula ngati amenewa.

14. Tingaphunzile ciani tikaganizila mmene Mose anacitila zinthu pamene ena analandila mwayi wa utumiki?

14 Tingaphunzile mfundo yofunika kwambili tikaganizila zimene Mose anacita pamene ena analandila mwayi wautumiki. Iye anali kuona kuti ni mwayi wamtengo wapatali kutsogolela mtundu wa Aisiraeli. Koma kodi Mose anacita ciani pamene Yehova anasankha amuna ena kuti azim’thandiza pa nchitoyi? Sanawacitile nsanje. (Num. 11:24-29) Mose anadzicepetsa, ndipo analola kuti ena am’thandize pa nchito yoweluza anthu. (Eks. 18:13-24) Izi zinathandiza kuti Aisiraeli akhale na oweluza ambili, ndipo sanali kuyembekezela nthawi yaitali kuti aweluzidwe. Mwa ici, Mose anaonetsa kuti sanali kuona udindo wake kukhala wofunika kwambili kuposa umoyo wa ena. Iye n’citsanzo cabwino kwambili kwa ife. Tizikumbukila kuti cofunika kwambili kuti Yehova atigwilitsile nchito ni kukhala wodzicepetsa kuposa kukhala na luso. Malemba amati: “Ngakhale kuti Yehova ali pamwamba, amaona wodzicepetsa.”—Sal. 138:6.

15. Kodi zinthu zinasintha bwanji mu umoyo wa abale na alongo ambili?

15 Ngati zinthu zasintha mu umoyo. M’zaka zaposacedwapa, abale na alongo ambili amene atumikila Yehova kwa zaka zambili anauzidwa kuti asiye utumiki wawo n’kuyamba kutumikila m’mautumiki ena. Mwacitsanzo, mu 2014, utumiki woyang’anila zigawo utatha, oyang’anila zigawo na azikazi awo anapatsidwa mautumiki ena a nthawi zonse. Kuyambila caka cimodzi-modzico, oyang’anila a madela anauzidwa kuti akafika zaka 70, afunika kusiya utumikiwu. Ndipo abale amene ali na zaka 80 kapena kuposelapo, satumikilanso monga mgwilizanitsi wa bungwe la akulu mu mpingo. Kuwonjezela apo, m’zaka zapitazi, atumiki ambili a pa Beteli anauzidwa kuti akacite upainiya ku mipingo. Palinso abale na alongo ena amene anasiya utumiki wa nthawi zonse wapadela cifukwa ca matenda, maudindo a m’banja, kapena pa zifukwa zina.

16. Kodi abale na alongo ena anaonetsa bwanji kudzicepetsa pamene zinthu zinasintha mu umoyo wawo?

16 Kupanga masinthidwe otelo kunali kovuta kwa abale na alongo amenewa. Mwacionekele, anali kuukonda kwambili utumiki wawo, ndipo ambili anali atakhala mu utumikiwo kwa zaka. Ena utumiki wawo utatha, anali kukhala na cisoni kwambili. Koma m’kupita kwa nthawi, anajaila umoyo wawo watsopano. N’ciani cinawathandiza? Cacikulu cimene cinawathandiza ni kukonda kwawo Yehova. Anali kudziŵa kuti anadzipatulila kwa Mulungu, osati ku nchito, udindo, kapena ku utumiki winawake. (Akol. 3:23) Iwo amakondwela kutumikila Yehova modzicepetsa pa utumiki uliwonse. Abale na alongo amenewa ‘amatulila [Yehova] nkhawa zawo zonse,’ podziŵa kuti iye amawadela nkhaŵa.—1 Pet. 5:6, 7.

17. N’cifukwa ciani ndife oyamikila kuti Mawu a Mulungu amatilimbikitsa kukhala odzicepetsa?

17 Ndife oyamikila kwambili kuti Mawu a Mulungu amatilimbikitsa kukhala odzicepetsa. Tikakulitsa khalidwe labwino limeneli, timapindula ndiponso timapindulitsa ena. Kuwonjezela apo, cimakhala copepukilako kupilila mavuto amene timakumana nawo. Koposa zonse, timayandikila kwambili Atate wathu wakumwamba. Ndipo ndife okondwela kudziŵa kuti ngakhale kuti iye ni “Wapamwamba ndi Wokwezeka,” amakonda atumiki ake odzicepetsa na kuwaona kuti ni amtengo wapatali.—Yes. 57:15.

NYIMBO 45 Kusinkha-sinkha kwa Mtima Wanga

^ ndime 5 Kudzicepetsa ni limodzi mwa makhalidwe ofunika kwambili amene tifunika kukhala nawo. Kodi kudzicepetsa kumatanthauza ciani? N’cifukwa ciani tiyenela kukhala na khalidwe limeneli? Nanga kusintha kwa zinthu mu umoyo wathu kungayese bwanji kudzicepetsa kwathu? M’nkhani ino, tikambilane mafunso ofunika amenewa.

^ ndime 7 Nkhani yofotokoza mbili ya M’bale Klein inatuluka mu Nsanja ya Mlonda ya Cizungu ya October 1, 1984.

^ ndime 8 Onani mutu 3, ndime 23, m’buku limenelo.

^ ndime 53 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Mtumwi Paulo ali m’nyumba ya m’bale winawake, ndipo akuceza momasuka na ena, kuphatikizapo acicepele.

^ ndime 57 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: M’bale akulandila uphungu wa m’Baibo wopelekedwa na m’bale wacinyamata.

^ ndime 59 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: M’bale wacikulile sakucitila nsanje m’bale wacinyamata amene ali na udindo mu mpingo.