Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 38

Citani Zinthu Mwanzelu Panthawi ya Mtendele

Citani Zinthu Mwanzelu Panthawi ya Mtendele

“M’dzikolo munalibe cosokoneza ciliconse, komanso palibe anacita naye nkhondo pa zaka zimenezi, cifukwa Yehova anam’patsa mpumulo.”—2 MBIRI 14:6.

NYIMBO 60 Ni Moyo Wawo

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Ni nthawi iti pamene kutumikila Yehova kungakhale kovuta?

KODI muganiza ni nthawi iti pamene kutumikila Yehova kungakhale kovuta kwambili—pamene mukukumana na mavuto aakulu kapena pamene muli pa mtendele? Ngati tikumana na mavuto, cimakhala cosavuta kudalila Yehova. Nanga bwanji ngati tili pa mtendele? Kodi n’kutheka kuti tingayambe kutangwanika na zinthu zina n’kuiŵala kutumikila Mulungu? Yehova anacenjeza Aisiraeli kuti anafunika kusamala kuti zaconco zisawacitikile.—Deut. 6:10-12.

Mfumu Asa anacita zinthu mwamphamvu komanso molimba mtima pothetsa kulambila konama (Onani ndime 2) *

2. Kodi Mfumu Asa anapeleka citsanzo cotani?

2 Mfumu Asa anacita zinthu mwanzelu mwa kudalila Yehova na mtima wonse. Iye ni citsanzo cabwino kwambili kwa ife. Asa anatumikila Yehova panthawi yovuta komanso panthawi ya mtendele. Kuyambila ali mwana, “Asa anatumikila Yehova ndi mtima wathunthu.” (1 Maf. 15:14) Njila imodzi imene Asa anaonetsela kuti anali wodzipeleka potumikila Yehova ni mwa kuthetsa kulambila konama mu Yuda. Baibo imati “iye anacotsa maguwa ansembe acilendo, anagwetsa malo okwezeka, anaphwanya zipilala zopatulika ndi kudula mizati yopatulika.” (2 Mbiri 14:3, 5) Iye anacotsa ngakhale ambuye ake aakazi a Maaka pa udindo wawo wapamwamba mu ufumu wa Yuda. Cifukwa ciani? Cifukwa anali kulimbikitsa anthu kulambila fano.—1 Maf. 15:11-13.

3. Kodi tikambilana ciani m’nkhani ino?

3 Kuwonjezela pa kuthetsa kulambila konama, palinso zina zimene Asa anacita. Iye analimbikitsa kulambila koona, ndipo anathandiza Ayuda kuyambanso kulambila Yehova. Yehova anadalitsa Asa ndi Aisiraeli mwa kucititsa dziko lawo kukhala pa mtendele. * Kwa zaka 10 mu ulamulilo wa Asa, “m’dzikolo munalibe cosokoneza ciliconse.” (2 Mbiri 14:1, 4, 6) M’nkhani ino, tikambilana mmene Asa anaseŵenzetsela nthawi ya mtendele imeneyo. Pambuyo pake, tikambilana citsanzo ca Akhristu a m’nthawi ya atumwi, amene monga Asa, anagwilitsila nchito bwino nthawi yawo ya mtendele. Pothela pake, tiyankha funso ili: Ngati mukhala m’dziko limene muli ufulu wolambila Yehova, kodi mungaigwilitsile nchito bwanji mwanzelu nthawi ya mtendele imeneyo?

MMENE ASA ANASEŴENZETSELA NTHAWI YA MTENDELE

4. Malinga na 2 Mbiri 14:2, 6, 7, kodi Asa anaiseŵenzetsa bwanji nthawi ya mtendele?

4 Ŵelengani 2 Mbiri 14:2, 6, 7. Asa anauza Ayuda kuti Yehova ndiye ‘anawapatsa mpumulo pakati pa adani awo onse owazungulila.’ Koma iye sanaone kuti nthawi ya mtendele imeneyo ni yofunika kungokhala phee osacita kalikonse. M’malomwake, anayamba kumanga mizinda, mipanda, nsanja, komanso makomo a zitseko ziŵili-ziŵili. Iye anauza Ayuda kuti: ‘Malo m’dzikoli akalipo.’ Kodi Asa anatanthauza ciani pamenepa? Anatanthauza kuti Ayuda anali na ufulu woyenda m’dziko limene Mulungu anawapatsa na kumanga popanda kuvutitsidwa na adani awo. Iye analimbikitsa anthuwo kuseŵenzetsa bwino nthawi ya mtendele imeneyo.

5. N’cifukwa ciani Asa anawonjezela mphamvu ya gulu lake lankhondo?

5 Asa anaseŵenzetsanso nthawi ya mtendele imeneyo kuwonjezela mphamvu ya gulu lake lankhondo. (2 Mbiri 14:8) Kodi izi zitanthauza kuti iye sanali kudalila Yehova? Iyai. Koma anacita izi cifukwa anadziŵa kuti iye monga mfumu, anali na udindo wokonzekeletsa anthu ake kaamba ka mavuto obwela m’tsogolo. Asa anali kudziŵa kuti nthawi ya mtendele imene Ayuda anali kusangalala nayo siidzakhalitsa, ndipo ni mmenedi zinakhalila.

MMENE AKHRISTU A M’NTHAWI YA ATUMWI ANASEŴENZETSELA NTHAWI YA MTENDELE

6. Kodi Akhristu a m’nthawi ya atumwi anaiseŵenzetsa bwanji nthawi ya mtendele?

6 Ngakhale kuti Akhristu a m’nthawi ya atumwi anali kuzunzidwa kaŵili-kaŵili, nthawi zina anali kukhala pa mtendele. Kodi ophunzila okhulupilikawo anali kuigwilitsila nchito bwanji nthawi ya mtendele imeneyo? Anali kulalikila uthenga wabwino mwakhama. Buku la Machitidwe limakamba kuti iwo anali “kuyenda moopa Yehova.” Akhristuwo anapitiliza kulalikila uthenga wabwino, ndipo zotulukapo zake zinali zakuti mpingo “unali kukulilakulila.” N’zoonekelatu kuti Yehova anawadalitsa cifukwa cogwila nchito yolalikila mwakhama pa nthawi ya mtendele.—Mac. 9:26-31.

7-8. Kodi Paulo na Akhristu ena anaugwilitsila nchito bwanji mwayi umene anapeza? Fotokozani.

7 Ophunzila a m’nthawi ya atumwi anali kulalikila uthenga wabwino pa mpata uliwonse umene apeza. Mwacitsanzo, pamene mtumwi Paulo anaona kuti khomo lalikulu la utumiki lamutsegukila ali ku Efeso, anayamba kulalikila na kupanga ophunzila mumzindawo.—1 Akor. 16:8, 9.

8 Paulo na Akhristu ena anakhalanso na mwayi wolalikila anthu ambili pamene nkhani ya mdulidwe inathetsedwa mu 49 C.E. (Mac. 15:23-29) Cigamulo pa nkhani ya mdulidwe citalengezedwa ku mipingo, ophunzilawo anawonjezela cangu cawo polalikila “uthenga wabwino wa mawu a Yehova.” (Mac. 15:30-35) Kodi panakhala zotulukapo zotani? Baibo imakamba kuti “mipingo inapitiliza kulimba m’cikhulupililo ndipo ciŵelengelo cinapitiliza kuwonjezeka tsiku ndi tsiku.”—Mac. 16:4, 5.

KUSEŴENZETSA NTHAWI YA MTENDELE MASIKU ANO

9. Kodi masiku ano zinthu zili bwanji m’maiko ambili? Nanga ni funso liti limene tingadzifunse?

9 M’maiko ambili masiku ano, Mboni za Yehova zili na ufulu wolalikila popanda cosokoneza ciliconse. Kodi imwe mukhala m’dziko limene muli ufulu wa kulambila? Ngati n’conco, dzifunseni kuti, ‘Kodi ufulu umenewu nimauseŵenzetsa bwanji?’ M’masiku otsiliza ano, gulu la Yehova lakhala likutsogolela pa nchito yaikulu yolalikila na kuphunzitsa imene siinacitikepo n’kale lonse padzikoli. (Maliko 13:10) Ndipo anthu a Yehova ali na mwayi wocita mautumiki ambili osiyana-siyana.

Ambili apeza madalitso oculuka mwa kupita kukatumikila ku dziko lina, kapena mwa kulalikila anthu okamba citundu cina (Onani ndime 10-12) *

10. Kodi lemba la 2 Timoteyo 4:2 limatilimbikitsa kucita ciani?

10 Kodi imwe mungaseŵenzetse bwanji mwanzelu nthawi ya mtendele imene muli nayo? (Ŵelengani 2 Timoteyo 4:2.) Bwanji osapenda mmene zinthu zilili pa umoyo wanu na kuona ngati inuyo kapena wina m’banja lanu angathe kuwonjezela zocita pa nchito yolalikila, mwina ngakhale kuyamba kutumikila monga mpainiya? Ino si nthawi yodziunjikila cuma kapena katundu, cifukwa zinthu zimenezi sitidzapulumuka nazo limodzi pa cisautso cacikulu.—Miy. 11:4; Mat. 6:31-33; 1 Yoh. 2:15-17.

11. Kodi ofalitsa ena acita zotani pofuna kufalitsa uthenga wabwino kwa anthu ambili?

11 Ofalitsa ambili aphunzilako citundu cina n’colinga cakuti aziciseŵenzetsa polalikila na kuphunzitsa. Gulu la Mulungu limawacilikiza ofalitsa amenewa mwa kufalitsa mabuku ofotokoza Baibo m’vitundu vambili. Mwacitsanzo, mu 2010 zofalitsa zathu zinali kupezeka m’vitundu pafupi-fupi 500. Koma masiku ano, zofalitsa zathu zimafalitsidwa m’vitundu voposa 1,000!

12. Kodi anthu amapindula bwanji akamvetsela uthenga wa Ufumu m’citundu cawo? Fotokozani citsanzo.

12 Kodi anthu amakhudzidwa bwanji akamvela coonadi ca m’Mawu a Mulungu m’citundu cawo? Ganizilani za mlongo wina amene anapezeka pa msonkhano wacigawo mu mzinda wa Memphis, ku Tennessee, m’dziko la America. Msonkhanowo unali wa mu Cikinyarwanda, citundu cimene cimakambidwa ndi anthu ambili ku Rwanda, ku Congo (Kinshasa), komanso ku Uganda. Msonkhanowo utatha, mlongoyo amene amakamba Cikinyarwanda anati: “N’kuyamba kuumvetsetsa bwino msonkhano wacigawo kucokela pamene n’nabwela kuno ku America zaka 17 zapitazo.” N’zoonekelatu kuti mlongoyu anakhudzidwa kwambili atamvela msonkhano wacigawo umenewo m’citundu cake. Ngati zinthu zili bwino kwa inu, kodi mungaphunzileko citundu cina kuti muthandize ena m’gawo lanu? Kodi m’gawo la mpingo wanu muli ena amene angakonde kumvetsela uthenga wanu ngati mungakambe nawo m’citundu cawo powalalikila? Mukacita zimenezi, mudzadalitsidwa cifukwa ca khama lanu.

13. Kodi abale athu ku Russia anaiseŵenzetsa bwanji nthawi ya mtendele?

13 M’mayiko ena, abale athu alibe mwayi wolalikila mwaufulu. Nthawi zina, maboma amaika ziletso pa nchito yathu. Ndipo izi zapangitsa kuti abale athu ena asamacite zambili pa nchito yolalikila. Mwacitsanzo, ganizilani za abale athu ku Russia. Pambuyo pozunzidwa kwa zaka zambili, mu March 1991, boma linawalola kuti azilambila mwaufulu. Panthawi imeneyo, ku Russia kunali alengezi a Ufumu pafupi-fupi 16,000. Koma patapita zaka 20, ciŵelengelo ca ofalitsa Ufumu cinakwela kuposa pa 160,000! N’zoonekelatu kuti abale athu anacita zinthu mwanzelu pamene anali na mwayi wolalikila mwaufulu. Nthawi ya mtendele imeneyo siinakhalitse. Koma ngakhale kuti zinthu zinasintha m’dziko lawo, cangu cawo pa kulambila koyela sicinazilale. Iwo akupitiliza kutumikila Yehova mmene angathele malinga na mmene zinthu zilili.

NTHAWI YA MTENDELE IDZATHA

Mfumu Asa atapemphela mocokela pansi pa mtima, Yehova anathandiza Ayuda kugonjetsa gulu lankhondo lalikulu kwambili la adani awo (Onani ndime 14-15)

14-15. Kodi Yehova anaonetsa bwanji mphamvu zake pothandiza Asa?

14 M’nthawi ya Asa, mtendele umene Ayuda anali nawo, m’kupita kwa nthawi unatha. Gulu lankhondo lalikulu la asilikali amphamvu okwana 1 miliyoni, linabwela kudzawaukila kucokela ku Itiyopiya. Mtsogoleli wawo Zera, sanali kukayika kuti iye pamodzi na gulu lake lankhondo adzagonjetsa Ayuda. Koma Mfumu Asa anadalila Mulungu wake, Yehova, osati kukula kwa gulu lake lankhondo. Iye anapemphela kwa Yehova kuti: “Tithandizeni Yehova Mulungu wathu cifukwa tikudalila inu, ndipo tabwela m’dzina lanu kudzamenyana ndi khamuli.”—2 Mbiri 14:11.

15 Ngakhale kuti gulu lankhondo la Aitiyopiya linali na asilikali ambili kuwilikiza kaŵili poyelekezela na asilikali a Asa, Asa anali kudziŵa kuti Yehova ali na mphamvu zoculuka moti adzathandiza anthu ake. Ndipo Yehova sanamugwilitse mwala. Anamuthandizadi. Gulu lankhondo la Aitopiya linagonjetsedwa mocititsa manyazi.—2 Mbiri 14:8-13.

16. Tidziŵa bwanji kuti nthawi ya mtendele idzatha?

16 Olo kuti sitidziŵa bwino-bwino zimene zingacitikile aliyense wa ife kutsogolo, cimene tidziŵa n’cakuti mtendele umene tili nawo palipano ni wosakhalitsa. Kumbukilani kuti Yesu anakambilatu kuti m’masiku otsiliza, “mitundu yonse idzadana” na ophunzila ake. (Mat. 24:9) Mofananamo, mtumwi Paulo anakamba kuti “onse ofuna kukhala ndi moyo wodzipeleka kwa Mulungu mwa Khristu Yesu, nawonso adzazunzidwa.” (2 Tim. 3:12) Satana ali na “mkwiyo waukulu,” ndipo kungakhale kudzinamiza kuganiza kuti tingakwanitse kuuthaŵa mkwiyo wake.—Chiv. 12:12.

17. Kodi cikhulupililo cathu cingayesedwe motani?

17 Posacedwapa, tonse cikhulupililo cathu cidzayesedwa. Patsala kanthawi kocepa, padzikoli pakhala “cisautso cacikulu cimene sicinacitikepo kucokela pa ciyambi ca dziko mpaka tsopano.” (Mat. 24:21) Panthawi imeneyo, abululu ŵathu akhoza kudzatiukila, ndipo nchito yathu ingadzaletsedwe. (Mat. 10:35, 36) Mofanana na Asa, kodi aliyense wa ife adzadalila Yehova kuti adzatithandiza na kutiteteza?

18. Malinga na Aheberi 10:38, 39, n’ciani cidzatithandiza kukhalabe olimba pamene nthawi ya mtendele idzatha?

18 Yehova wakhala akutikonzekeletsa mwauzimu kaamba ka zinthu zimene tidzakumana nazo kutsogoloku. Pofuna kutithandiza kukhalabe olimba mwauzimu, Yehova akutsogolela “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu” kuti azitipatsa “cakudya [cabwino cauzimu] pa nthawi yoyenela.” (Mat. 24:45) Koma aliyense wa ife ayenela kucita khama kuti alimbitse cikhulupililo cake mwa Yehova.—Ŵelengani Aheberi 10:38, 39.

19-20. Mogwilizana na 1 Mbiri 28:9, ni mafunso ati amene tiyenela kudzifunsa? Nanga n’cifukwa ciani tiyenela kudzifunsa mafunso amenewa?

19 Mofanana na Mfumu Asa, tiyenela ‘kufunafuna Yehova.’ (2 Mbiri 14:4; 15:1, 2) Timafuna-funa Yehova mwa kuphunzila za iye na kubatizika. Ndipo tikabatizika, timacita zonse zimene tingathe kuti tilimbitse cikondi cathu pa Yehova. Kuti tidziŵe mmene tikucitila pa mbali imeneyi, tingadzifunse kuti: ‘Kodi nimapezeka ku misonkhano ya mpingo nthawi zonse?’ Tikamapezeka ku misonkhano imene gulu la Yehova limatikonzela, timatsitsimulidwa mwauzimu komanso timapindula na mayanjano olimbikitsa. (Mat. 11:28) Tingadzifunsenso kuti, ‘Kodi nili na cizoloŵezi cocita phunzilo laumwini? Ngati mukhala pamodzi na a m’banja lanu, kodi wiki iliyonse mumapatula nthawi yocita kulambila kwa pabanja? Kapena ngati mumakhala mwekha, kodi mumapatulabe nthawi yophunzila monga mmene munali kucitila pamodzi na a m’banja lanu? Komanso, kodi mumatengako mbali mokwanila pa nchito yolalikila na kupanga ophunzila?’

20 N’cifukwa ciani tiyenela kudzifunsa mafunso amenewa? Baibo imakamba kuti Yehova amasanthula maganizo athu na zimene zili m’mitima yathu. Izi n’zimene nafenso tifunika kucita. (Ŵelengani 1 Mbiri 28:9.) Ngati taona kuti tifunika kusinthako zinthu zina pa zolinga zathu, khalidwe lathu, kapena maganizo athu, tiyenela kupempha Yehova kuti atithandize kupanga masinthidwe amenewo. Ino ndiyo nthawi yodzikonzekeletsa ku mayeselo amene akubwela kutsogolo. Musalole ciliconse kukulepheletsani kuseŵenzetsa mwanzelu nthawi ya mtendele!

NYIMBO 62 Nyimbo Yatsopano

^ ndime 5 Kodi mukhala m’dziko limene muli ufulu wolambila Yehova? Ngati n’conco, kodi mukuiseŵenzetsa bwanji nthawi ya mtendele imeneyo? Nkhani ino ikuthandizani kudziŵa mmene mungatsatilile citsanzo ca Mfumu Asa ya Yuda komanso ca Akhristu a m’nthawi ya atumwi. Iwo anaseŵenzetsa mwanzelu nthawi ya mtendele pamene m’dziko lawo munalibe cosokoneza ciliconse.

^ ndime 3 KUFOTOKOZELA MAWU ENA: Liwu lakuti “mtendele” silitanthauza cabe kusakhalapo kwa nkhondo. Liwu la Ciheberi lomasulidwa kuti mtendele limaphatikizaponso kukhala na umoyo wathanzi, wotetezeka, komanso wosangalala.

^ ndime 57 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Mfumu Asa anacotsa ambuye ŵake pa udindo wawo cifukwa anali kulimbikitsa kulambila konama. Anthu amene anali kumbali ya Asa anatengela citsanzo cake mwa kuwononga mafano.

^ ndime 59 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Banja lokangalika pa nchito yolalikila likusintha zina na zina mu umoyo wawo n’colinga cakuti likatumikile kumene kuli ofalitsa ocepa.