Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 37

“Dzanja Lako Lisapume”

“Dzanja Lako Lisapume”

“Bzala mbewu zako m’mawa, ndipo dzanja lako lisapume mpaka madzulo.”—MLAL. 11:6.

NYIMBO 68 Fesani Mbewu za Ufumu

ZIMENE TIKAMBILANE *

1-2. Kodi lemba la Mlaliki 11:6 ligwilizana bwanji na nchito yolalikila uthenga wabwino wa Ufumu?

M’MAIKO ena, anthu amaonetsa cidwi kwambili akamvela uthenga wabwino. Amacita kulaka-laka kuti kubwele munthu amene angawauzeko uthenga wabwino. Koma m’maiko ena, anthu sacita cidwi kweni-kweni ndi za Mulungu kapena Baibo. Kodi anthu ambili m’gawo lanu amaulandila motani uthenga wabwino? Kaya anthu ni acidwi kapena ayi, Yehova amafuna kuti tipitilize kugwila nchito yolalikila mpaka pamene adzatiuze kuti yatha.

2 Yehova anaika kale nthawi pamene nchito yolalikila idzatha. Ndipo nchitoyo ikadzatha, “mapeto adzafika.” (Mat. 24:14, 36) Pamene tikuyembekezela nthawiyo, kodi tingaonetse bwanji kuti tikulabadila malangizo akuti “dzanja lako lisapume”? *Ŵelengani Mlaliki 11:6.

3. Kodi tikambilana ciani m’nkhani ino?

3 M’nkhani yapita, tinakambilana zinthu zinayi zimene tifunika kucita kuti tikhale aluso pa nchito yathu yosodza anthu. (Mat. 4:19) M’nkhani ino, tikambilana zinthu zitatu zimene zingatithandize kutsimikiza mtima kupitiliza kugwila nchito yolalikila, olo tikumane na mavuto otani. Tiona cifukwa cake kucita zotsatilazi n’kofunika: (1) Kuikabe maganizo athu pa nchito yolalikila, (2) kukhala oleza mtima, komanso (3) kukhalabe na cikhulupililo colimba.

IKANIBE MAGANIZO ANU PA NCHITO YOLALIKILA

4. N’cifukwa ciani tifunika kuikabe maganizo athu pa nchito imene Yehova anatipatsa?

4 Yesu anakambilatu zocitika zimene zidzaonetsa kuti tili m’masiku otsiliza. Iye anadziŵa kuti zocitika zimenezo zingathe kulepheletsa otsatila ake kuikabe maganizo awo pa nchito yolalikila. Pa cifukwa cimeneci, iye anawalangiza kuti ayenela ‘kukhalabe maso.’ (Mat. 24:42) M’masiku a Nowa, panali zinthu zambili zimene zinalepheletsa anthu kumvela macenjezo amene iye anali kupeleka. Masiku anonso, zinthu zofanana na zimenezo zingatilepheletse kukhalabe maso. (Mat. 24:37-39; 2 Pet. 2:5) Conco, tifunika kuikabe maganizo athu pa nchito imene Yehova anatipatsa.

5. Kodi lemba la Machitidwe 1:6-8 limaonetsa kuti nchito yolalikila idzakula kufika pati?

5 Masiku ano, tifunika kuyesetsa kuika mtima wathu pa nchito yolalikila. Yesu anakambilatu kuti iye akadzamwalila, otsatila ake adzapitiliza kugwila nchitoyi komanso kuti idzakula kwambili. (Yoh. 14:12) Yesu atamwalila, ena mwa ophunzila ake anabwelelanso ku nchito yawo ya usodzi. Iye ataukitsidwa, anacita cozizwitsa mwa kuthandiza ophunzila ake ena kugwila nsomba zambili. Pambuyo pa cozizwitsa cimeneco, Yesu anathandiza ophunzila ake kuona kuti nchito yosodza anthu ndiyo inali yofunika kwambili kuposa nchito ina iliyonse. (Yoh. 21:15-17) Iye atatsala pang’ono kupita kumwamba, anauza ophunzila ake kuti nchito yolalikila imene anayambitsa idzakula kwambili mpaka kupitilila malile a dziko la Isiraeli. (Ŵelengani Machitidwe 1:6-8.) Patapita zaka, Yesu anaonetsa mtumwi Yohane masomphenya a zimene zidzacitika “m’tsiku la Ambuye.” * Cimodzi mwa zinthu zimene Yohane anaona m’masomphenyawo ni cocitika ici cocititsa cidwi: Anaona mngelo akulengeza “uthenga wabwino wosatha . . . kudziko lililonse, fuko lililonse, cinenelo ciliconse, ndi mtundu uliwonse.” (Chiv. 1:10; 14:6) N’zoonekelatu kuti Yehova amafuna kuti tizigwila nawo nchito ya padziko lonse imeneyi yolalikila mpaka pamene idzathe.

6. N’ciani cingatithandize kuikabe maganizo athu pa nchito yolalikila?

6 Kodi n’ciani cingatithandize kuikabe maganizo athu pa nchito yolalikila? Cimodzi cimene cingatithandize ni kuganizila zimene Yehova akucita pofuna kutithandiza mwauzimu. Mwacitsanzo, watipatsa cakudya cauzimu coculuka kupitila m’zofalitsa zopulintidwa na za pazipangizo, mavidiyo na zofalitsa zongomvetsela, komanso pa JW Broadcasting. Tangoganizilani! Pa webusaiti yathu pali zofalitsa na zinthu zina m’zitundu zopitilila 1,000. (Mat. 24:45-47) Pamene anthu m’dzikoli ali osagwilizana cifukwa ca kusiyana pa zandale, zacipembedzo, komanso zacuma, atumiki a Mulungu oposa 8 miliyoni ali m’gulu logwilizanadi la abale a padziko lonse. Mwacitsanzo, pa Cisanu pa April 19, 2019, Mboni za Yehova padziko lonse zinatamba vidiyo yofotokoza lemba la tsiku limenelo. Izi zinaonetsa kuti iwo ni ogwilizana. Ndipo m’madzulo pa tsikulo, anthu okwana 20,919,041 anasonkhana na kucita mwambo wokumbukila imfa ya Yesu. Ndithudi, ni mwayi waukulu kuona zocitika zapadela zimenezi, komanso kukhala m’gulu la abale a padziko lonse amene ni ogwilizana. Izi zimatisonkhezela kuikabe maganizo athu pa nchito yolalikila za Ufumu.

Yesu sanalole ciliconse kumulepheletsa kuikabe maganizo ake pa nchito yocitila umboni coonadi (Onani ndime 7)

7. Kodi citsanzo ca Yesu cingatithandize bwanji kuikabe maganizo pa nchito yolalikila?

7 Cina cimene cingatithandize kuikabe maganizo athu pa nchito yolalikila ni kutengela citsanzo ca Yesu. Iye sanalole ciliconse kumuceutsa pa nchito yake yocitila umboni coonadi. (Yoh. 18:37) Iye sanakopeke pamene Satana anamuonetsa “maufumu onse a padziko ndi ulemelelo wawo.” Sanakopekenso pamene anthu anafuna kumulonga ufumu. (Mat. 4:8, 9; Yoh. 6:15) Iye sanakopeke na zinthu zakuthupi, kapena kucita mantha cifukwa ca citsutso coopsa. (Luka 9:58; Yoh. 8:59) Ngati cikhulupililo cathu cayesedwa, cimene cingatithandize kuikabe maganizo pa nchito yolalikila ni kukumbukila malangizo a mtumwi Paulo. Iye analangiza Akhristu kuti ayenela kutengela citsanzo ca Yesu kuti ‘asatope ndiponso kuti asalefuke.’—Aheb. 12:3.

KHALANI OLEZA MTIMA

8. Kodi kuleza mtima n’kutani? Nanga n’cifukwa ciani khalidwe limeneli n’lofunika?

8 Kuleza mtima ni kuyembekezela modekha kuti zinthu zidzakhala bwino. Timafunika kukhala oleza mtima pa zocitika zosiyana-siyana. Mwacitsanzo, mwina tikukumana na vuto linalake ndipo tikufuna kuti vuto limenelo lithe, kapena mwina takhala tikuyembekezela zinthu zinazake zabwino kwa nthawi yaitali. Mneneli Habakuku anali kulaka-laka kuti khalidwe laciwawa lithe mu Yuda. (Hab. 1:2) Ophunzila a Yesu anali kuyembekezela kuti ufumu wa Mulungu “uonekela nthawi yomweyo” kuti uwapulumutse ku ulamulilo wopondeleza wa Aroma. (Luka 19:11) Na ife timalaka-laka tsiku limene Ufumu wa Mulungu udzacotsapo zoipa zonse na kutiloŵetsa m’dziko latsopano mmene mudzakhala cilungamo. (2 Pet. 3:13) Koma tifunika kukhala oleza mtima pamene tikuyembekezela nthawi pamene Yehova adzakonza zinthu. Tiyeni tione njila zina zimene Yehova amaseŵenzetsa potiphunzitsa kukhala oleza mtima.

9. Fotokozani zitsanzo zoonetsa kuti Yehova ni woleza mtima.

9 Yehova ni citsanzo cabwino ngako pa nkhani ya kuleza mtima. Iye anapatsa Nowa nthawi yokwanila yomanga cingalawa komanso yogwila nchito yolalikila monga “mlaliki wa cilungamo.” (2 Pet. 2:5; 1 Pet. 3:20) Yehova anamvetsela pamene Abulahamu anamufunsa mafunso mobweleza-bweleza ponena za cosankha cake cakuti adzawononga anthu okhala m’mizinda yoipa ya Sodomu na Gomora. (Gen. 18:20-33) Kwa zaka zambili, Yehova analeza mtima kwambili na mtundu wosakhulupilika wa Aisiraeli. (Neh. 9:30, 31) Masiku ano, Yehova waonetsanso kuti ni woleza mtima. Iye wapatsa anthu onse amene afuna kukhala mabwenzi ake nthawi yokwanila yakuti “alape.” (2 Pet. 3:9; Yoh. 6:44; 1 Tim. 2:3, 4) Citsanzo ca Yehova cimeneci citiphunzitsa kuti nafenso tifunika kukhala oleza mtima pamene tikupitiliza kugwila nchito yolalikila na kuphunzitsa. Iye amatiphunzitsanso kukhala oleza mtima kupitila m’fanizo linalake lopezeka m’Mawu ake, Baibo.

Monga mlimi amene amagwila nchito mwakhama komanso moleza mtima, nafenso timayembekezela zotulukapo za nchito yathu imene tagwila mwakhama (Onani ndime 10-11)

10. Kodi citsanzo ca mlimi cochulidwa pa Yakobo 5:7, 8, citiphunzitsa ciani?

10 Ŵelengani Yakobo 5:7, 8. Citsanzo ca mlimi amene wabyala mbewu, cimatiphunzitsa kukhala oleza mtima. N’zoona kuti mbewu zina zimakula mwamsanga. Koma mbewu zambili, maka-maka zija zimene zimabala zipatso zimatenga nthawi yaitali kuti zikhwime. Kale ku Isiraeli, mbewu zikabyalidwa panali kutenga miyezi 6 kuti zikhwime mpaka kuzikolola. Mlimi anali kubyala mbewu zake mvula yoyamba ikagwa, capakati pa mwezi wa October, ndipo anali kukolola mbewuzo pambuyo pa mvula yothela, capakati pa mwezi wa April. (Maliko 4:28) Ndithudi, ni cinthu canzelu kutengela citsanzo ca mlimi ca kuleza mtima. Komabe, kucita zimenezi nthawi zina kungakhale kovuta.

11. Kodi kuleza mtima kungatithandize bwanji mu ulaliki?

11 Nthawi zambili, ife anthu opanda ungwilo timafuna kuonelatu nthawi yomweyo phindu la nchito imene tagwila. Koma tifunika kukumbukila citsanzo ca mlimi. Ngati mlimi afuna kuti mbewu zake zikule bwino na kubala zipatso, amafunika kukhala woleza mtima. Amafunika kugaula, kubyala, na kulimilila. Nafenso timafunika kukhala oleza mtima pogwila nchito yolalikila. Mwacitsanzo, tikakhala oleza mtima sitidzalefuka ngati anthu samvetsela uthenga wathu. M’malomwake, tidzapitiliza kusakila anthu omvetsela uthengawo. Ndiponso, timafunika kukhalabe oleza mtima olo kwa anthu omvetsela uthenga wathu. Sitingakakamize wophunzila Baibo kuti akule m’cikhulupililo. Nthawi zina, ngakhale ophunzila a Yesu anali kucedwa kugwila tanthauzo la zimene iye anali kuwaphunzitsa. (Yoh. 14:9) Timafunika kucita khama kuti tithandize ophunzila Baibo athu kuthetsa tsankho m’mitima yawo na kukhala acikondi. Conco, tiyeni tizikumbukila kuti kwathu ni kubyala na kuthilila, koma wokulitsa ni Mulungu.—1 Akor. 3:6.

12. Tingaonetse bwanji kuleza mtima polalikila acibululu amene si Mboni?

12 Nthawi zina cingakhale covuta kukhala oleza mtima pamene tikulalikila acibululu amene si Mboni. Koma mfundo ya pa Mlaliki 3:2, 7 ingatithandize. Imati: “Pali . . . nthawi yokhala cete ndi nthawi yolankhula.” Khalidwe lathu labwino lingathandize abululu athu kufuna kumvetsela uthenga wathu. Pa nthawi imodzi-modziyo, timakhala chelu kusakila mipata yowauzako za Yehova. (1 Pet. 3:1, 2) Timafunika kulalikila na kuphunzitsa mwakhama. Koma nthawi zonse timafunika kukhala oleza mtima na munthu aliyense, kuphatikizapo a m’banja lathu.

13-14. Ni zitsanzo ziti zina za atumiki a Mulungu oleza mtima zimene tiyenela kutengela?

13 Tingaphunzile kuleza mtima mwa kuona zitsanzo za anthu okhulupilika akale ochulidwa m’Baibo komanso a masiku ano. Mwacitsanzo, Habakuku analaka-laka kuti zinthu zoipa zithe. Koma anaonetsa kuti anali woleza mtima pamene anati: “Ine ndidzaimabe pamalo a mlonda.” (Hab. 2:1) Mtumwi Paulo anakamba kuti anali kungofuna ‘kumaliza’ utumiki wake. Komabe, moleza mtima iye anapitiliza “kucitila umboni mokwanila za uthenga wabwino.”—Mac. 20:24.

14 Ganizilani citsanzo ca banja lina limene linatsiliza maphunzilo a Sukulu ya Giliyadi. Atatsiliza maphunzilowo, anawatumiza ku dziko limene kuli Mboni zocepa komanso kumene anthu ambili si Akhristu. Anthu ambili analibe cidwi cophunzila Baibo. Koma anzawo otsiliza maphunzilo a Giliyadi, amene anali kutumikila ku maiko ena, anali kuwauza kuti anali kutsogoza maphunzilo a Baibo ambili opita patsogolo. Ngakhale kuti anthu ambili m’gawo lawo sanali kumvetsela uthenga wabwino, banjali moleza mtima linapitiliza kulalikila. Pambuyo polalikila m’gawo loumalo kwa zaka 8, mmodzi wa ophunzila Baibo awo anabatizika. Ndipo iwo anakondwela kwambili. Kodi zitsanzo zimene takambilanazi zitiphunzitsa ciani? Atumiki okhulupilika amenewa sanagwe ulesi pa nchito yawo kapena kulola dzanja lawo kupuma, ndipo Yehova anawadalitsa cifukwa ca kuleza mtima kwawo. Conco tiyeni tipitilize kutengela citsanzo ca “anthu amene, mwa cikhulupililo ndi kuleza mtima, akulandila zinthu zimene Mulungu analonjeza monga colowa cawo.”—Aheb. 6:10-12.

KHALANIBE NA CIKHULUPILILO COLIMBA

15. Kodi njila yoyamba imene cikhulupililo cimatithandizila kupitiliza kugwila nchito yolalikila ni iti?

15 Onani njila ziŵili zimene cikhulupililo cimatithandizila kuti tisalole dzanja lathu kupuma. Coyamba, popeza kuti uthenga umene timalalikila timaukhulupilila, timakhala ofunitsitsa kuuzako ena uthenga umenewu mmene tingathele. Timakhulupilila malonjezo opezeka m’Mawu a Mulungu. (Sal. 119:42; Yes. 40:8) Masiku ano, taona maulosi a m’Baibo akukwanilitsidwa. Taona anthu akusintha umoyo wawo pamene ayamba kutsatila malangizo a m’Baibo. Zimenezi zimalimbitsa cikhulupililo cathu cakuti uthenga wabwino wa Ufumu ni uthenga umene munthu aliyense afunika kuumva.

16. Mogwilizana na Salimo 46:1-3, kodi kukhulupilila Yehova na Yesu kumatithandiza bwanji kutsimikiza mtima kupitiliza kugwila nchito yolalikila?

16 Caciŵili, timakhulupilila Yehova amene ni gwelo la uthenga umene timalalikila. Timakhulupililanso Yesu amene Mulungu anamusankha kukhala Mfumu ya Ufumu wake. (Yoh. 14:1) Conco, olo tikumane na mavuto otani, tidziŵa kuti Yehova nthawi zonse adzakhala pothaŵila pathu na mphamvu yathu. (Ŵelengani Salimo 46:1-3.) Kuwonjezela apo, sitikayikila kuti Yesu kucokela kumwamba, akutsogolela pa nchito yolalikila pogwilitsila nchito mphamvu na ulamulilo zimene Yehova anamupatsa.—Mat. 28:18-20.

17. Fotokozani citsanzo coonetsa cifukwa cake tifunika kupitiliza kulalikila.

17 Cikhulupililo cimatithandiza kukhala otsimikiza kuti Yehova adzadalitsa khama lathu, nthawi zina m’njila zimene sitingayembekezele. (Mlal. 11:6) Mwacitsanzo, tsiku na tsiku, anthu masauzande ambili amabwela pa mathebulo athu a zofalitsa na pa tumasitandi twa ulaliki. Kodi kulalikila mwa njila imeneyi kwakhaladi kothandiza? Inde! Mwacitsanzo, mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa November 2014, muli nkhani ya mtsikana wina wa pa yunivesiti amene anasankha kulemba nkhani yokhudza Mboni za Yehova. Iye sanakwanitse kupeza Nyumba ya Ufumu pafupi. Koma anapeza thebulo la zofalitsa zathu pa yunivesiti pomwepo, ndipo anapezanso zimene anali kufuna zomuthandiza polemba zokhudza Mboni za Yehova. Pamapeto pake, mtsikanayo anabatizika n’kukhala Mboni, ndipo lomba ni mpainiya wanthawi zonse. Zocitika monga zimenezi zimatisonkhezela kupitiliza kugwila nchito yolalikila cifukwa zimaonetsa kuti pakali anthu amene amafuna kumvela uthenga wa Ufumu.

TSIMIKIZANI MTIMA KUSAPUMITSA DZANJA LANU

18. N’cifukwa ciani ndife otsimikiza kuti nchito yolalikila za Ufumu idzatha pa nthawi yake, imene Yehova afuna?

18 Sitikayika konse kuti nchito yolalikila idzatha panthawi yake. Ganizilani zimene zinacitika m’nthawi ya Nowa. M’nthawiyo, Yehova anaonetsa kuti nthawi zonse iye amasunga nthawi. Kukali zaka 120, iye anaikilatu nthawi yobweletsa Cigumula. (Gen. 6:3) Patapita zaka zambili, Yehova anauza Nowa kuti amange cingalawa. Mwina kwa zaka 40 kapena 50 Cigumula cisanayambe, Nowa anapitilizabe kugwila nchitoyo mwakhama. Ngakhale kuti anthu sanali kulabadila uthenga wake, Nowa anapitiliza kulalikila uthenga wocenjeza anthu mpaka pamene Yehova anamuuza kuti nthawi yafika yakuti aloŵetse vinyama m’cingalawa. Ndiyeno, nthawi itakwana, “Yehova anatseka citseko.”—Gen. 6:3; 7:1, 2, 16.

19. Kodi tidzalandila madalitso otani ngati sitilola dzanja lathu kupuma?

19 Posacedwa, Yehova adzatiuza kuti nchito yolalikila yatha. Kenako adzawononga dziko la Satanali, na kubweletsa dziko latsopano limene mudzakhala cilungamo. Conco pamene tikuyembekezela nthawiyo, tiyeni titengele citsanzo ca Nowa, Habakuku, na ena amene sanalole dzanja lawo kupuma. Tiyeni tipitilize kuika maganizo athu pa nchito yolalikila, kukhala oleza mtima, komanso kukhulupilila kwambili Yehova na malonjezo ake.

NYIMBO 75 ‘Ine Nilipo, N’tumizeni!’

^ ndime 5 Nkhani yapita, inalimbikitsa maphunzilo a Baibo opita patsogolo kulabadila ciitano ca Yesu cakuti akhale asodzi a anthu. Nkhani ino ifotokoza zinthu zitatu zimene ofalitsa onse, kaya atsopano kapena aciyambakale ayenela kucita kuti apitilize kugwila nchito yolalikila za Ufumu mpaka pamene Yehova adzanene kuti yatha.

^ ndime 2 KUFOTOKOZELA MAWU ENA: M’nkhani ino, mawu akuti “dzanja lako lisapume” atanthauza kuti tifunika kupitilizabe kugwila nchito yolalikila mpaka pamene Yehova adzatiuze kuti yatha.

^ ndime 5 “Tsiku la Ambuye” linayamba pamene Yesu anakhala Mfumu mu 1914, ndipo lidzatha kumapeto kwa Ulamulilo wake wa Zaka 1,000.