Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 39

Munthu Amene Timakonda Akasiya Yehova

Munthu Amene Timakonda Akasiya Yehova

“Iwo . . . kaŵili-kaŵili, anali kumukhumudwitsa.”—SAL. 78:40.

NYIMBO 102 “Thandizani Ofooka”

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Kodi ena amamvela bwanji wa m’banja mwawo akacotsedwa mu mpingo?

KODI pali wa m’banja mwanu amene anacotsedwa mu mpingo? Izi zimakhala zomvetsa cisoni kwambili! Mlongo wina dzina lake Hilda, anati: “Mwamuna wanga wokhulupilika atamwalila pambuyo pokhala m’cikwati zaka 41, n’naona monga palibe cinthu coŵaŵa ngati cimeneci. * Koma mwana wanga atacotsedwa mu mpingo, kusiya mkazi wake na ŵana, cinaniŵaŵa kwambili kuposa imfa ya mwamuna wanga.”

Yehova amamvetsa cisoni cimene mumakhala naco wokondedwa wanu akasiya kum’tumikila (Onani ndime 2-3) *

2-3. Malinga na Salimo 78:40, 41, kodi Yehova amamvela bwanji atumiki ake akaleka kum’tumikila?

2 Ganizilani cabe mmene cinamuŵaŵila Yehova, pamene angelo ena m’banja lake anam’pandukila. (Yuda 6) Ndipo ganizilaninso mmene cinamuŵaŵila kuona anthu ake okondeka, Aisiraeli, akum’pandukila mobweleza-bweleza. (Ŵelengani Salimo 78:40, 41.) Dziŵani kuti Atate wathu wakumwamba, cimamupweteka wa m’banja lanu akaleka kum’tumikila. Iye amamvetsa cisoni cimene mumakhala naco. Ndipo mwacikondi adzakulimbikitsani na kukuthandizani.

3 M’nkhani ino, tikambilane zimene tingacite kuti tilandile thandizo la Yehova wa m’banja mwathu akacotsedwa. Tikambilanenso mmene tingathandizile ena mu mpingo wacibale wawo akacotsedwa. Koma coyamba, tiyeni tikambilane maganizo olakwika amene tiyenela kupewa.

PEWANI KUDZIIMBA MLANDU

4. Kodi makolo amamvela bwanji mwana wawo akacotsedwa mu mpingo?

4 Mwana akacotsedwa mu mpingo, makolo amakonda kuganizila zina zimene akanacita, pothandiza mwanayo kukhalabe m’coonadi. M’bale wina dzina lake Luke, mwana wake atacotsedwa anati: “N’nadziimba mlandu, ndipo n’nali kulota maloto oipa. Nthawi zina n’nali kulila, ndipo cinali kunipweteka mu mtima.” Mlongo Elizabeth, amene nayenso anakumanapo na vutoli, anali kudzifunsa kuti: “Pokhala kholo, kodi n’nalakwitsa ciani? N’naona kuti n’nalephela kukhomeleza coonadi mwa mwana wanga.”

5. Ni mlandu wa ndani munthu akasiya Yehova?

5 Tizikumbukila kuti Yehova anapatsa aliyense ufulu wodzisankhila zocita. Izi zitanthauza kuti tingasankhe kumumvela kapena kusamumvela. Ana ena makolo awo si citsanzo cabwino, koma anawo asankha kutumikila Yehova na kukhalabe okhulupilika kwa iye. Ndipo ana ena amene makolo awo anayesetsa kuwaphunzitsa coonadi, analeka kutumikila Yehova atakula. Conco, ni ufulu wake munthu kusankha kaya kupitiliza kutumikila Yehova kapena ayi. (Yos. 24:15) Motelo, inu makolo, musamadziimbe mlandu mwana wanu akaleka kutumikila Yehova.

6. Kodi ŵana amamvela bwanji kholo likaleka kutumikila Mulungu?

6 Nthawi zina, kholo lingasiye coonadi, ngakhalenso kusiya banja lake. (Sal. 27:10) Ndipo cimakhala covuta kwa ana amene anali kuona kholo limenelo kukhala citsanzo cabwino. Esther, amene atate ake anacotsedwa, anati: “Kambili n’nali kulila cifukwa atate anacita kusankha kuleka kutumikila Yehova. Nimawakonda atate, conco pamene anacotsedwa mu mpingo, n’nali kudela nkhawa kuti umoyo wawo udzakhala bwanji. Izi zinali kunisoŵetsa tulo.”

7. Kodi Yehova amamvela bwanji akaona mwana amene kholo lake linacotsedwa?

7 Imwe ŵana, ngati mmodzi wa makolo anu anacotsedwa mu mpingo, dziŵani kuti nafenso cimatiŵaŵa. Dziŵaninso kuti Yehova amvetsa mmene mumvelela. Iye amakukondani, ndipo amayamikila kukhulupilika kwanu. Nafenso abale anu timakukondani na kukuyamikilani. Dziŵani kuti si mlandu wanu ngati kholo lanu lapanga cisankho colakwika. Monga takambila kale, Yehova anapatsa aliyense ufulu wodzisankhila zocita. Ndipo aliyense amene anadzipatulila na kubatizika, “ayenela kunyamula katundu wake.”—Agal. 6:5.

8. Kodi ena m’banja amene ni okhulupilika, angacite ciani poyembekezela wocotsedwa kubwelela kwa Yehova? (Onaninso bokosi lakuti, “ Bwelelani kwa Yehova.”)

8 Munthu amene mumam’konda akasiya Yehova, mumayembekezela kuti tsiku lina adzabwelela. Koma kodi mungacite ciani pali pano? Muyenela kulimbitsa cikhulupililo canu. Mukatelo, mudzakhala citsanzo cabwino kwa ena m’banja mwanu, mwina ngakhale kwa wocotsedwa amene. Mudzapezanso mphamvu zokuthandizani kupilila cisoni canu. Tiyeni tikambilane zimene mungacite kuti mulimbitse cikhulupililo canu.

ZIMENE MUNGACITE KUTI MUKHALEBE NA CIKHULUPILILO COLIMBA

9. Tingapeze bwanji mphamvu kucokela kwa Yehova? (Onaninso bokosi lakuti, “ Malemba Okutonthozani Munthu Amene Mumakonda Akasiya Yehova.”)

9 Khalani na pulogilamu yokhazikika ya zauzimu. N’kofunika kwambili kupitiliza kulimbitsa cikhulupililo canu, komanso ca ena m’banja mwanu. Mungacite bwanji zimenezi? Pezani mphamvu kucokela kwa Yehova, mwa kuŵelenga Mawu ake na kuwasinkhasinkha, komanso kupezeka ku misonkhano. Joanna, amene atate ake na m’bale wake anasiya coonadi, anati: “Nimamvelako bwino nikaŵelenga za anthu a m’Baibo monga Abigayeli, Esitere, Yobu, Yosefe, komanso Yesu. Zitsanzo zawo zimanilimbikitsa na kunithandiza kucepetsa cisoni. Nazonso nyimbo zopekedwa koyamba zanilimbikitsa ngako.”

10. Kodi Salimo 32:6-8, imatithandiza bwanji kupilila cisoni cimene tingakhale naco?

10 Mukhuthulileni Yehova za mu mtima wanu. Mukakhala na maganizo olefula, pemphelani kwa Yehova. M’pempheni kuti akuthandizeni kuona zinthu mmene iye amazionela, komanso kuti ‘akupatseni nzelu na kukulangizani njila yoti muyendemo.’ (Ŵelengani Salimo 32:6-8.) N’zoona kuti cingakuvuteni kuuza Yehova mmene mumvelela. Koma iye amadziŵa cisoni cimene muli naco mu mtima. Amakukondani kwambili, ndipo amafuna kuti mumukhuthulile za mu mtima mwanu.—Eks. 34:6; Sal. 62:7, 8.

11. Malinga na Aheberi 12:11, n’cifukwa ciani tiyenela kukhulupilila cilango cimene Yehova amatipatsa mwacikondi? (Onaninso bokosi lakuti, “ Kucotsa Munthu mu Mpingo ni Makonzedwe Acikondi a Yehova.”)

11 Gwilizanani na cigamulo ca akulu. Kucotsa munthu mu mpingo ni makonzedwe a Yehova. Iye amatiwongolela mwacikondi ndipo aliyense amapindula, kuphatikizapo wolakwayo. (Ŵelengani Aheberi 12:11.) Ena mu mpingo angayambe kukamba kuti akulu sanagamule bwino kuti uje acotsedwe mu mpingo. Koma dziŵani kuti kambili anthu otelo samachula zoipa zimene wolakwayo anacita. Timakhala kuti sitidziŵa zoona zake pa nkhaniyo. Ndiye n’canzelu kukhulupilila kuti akulu amene anaweluza nkhaniyo, anayesetsa kutsatila mfundo za m’Malemba, podziŵa kuti ‘akuweluzila Yehova.’—2 Mbiri 19:6.

12. Kodi ena apindula motani cifukwa cocilikiza makonzedwe a Yehova opeleka cilango?

12 Mukagwilizana na cigamulo ca akulu ca kucotsa wacibale wanu mu mpingo, ndiye kuti mukumuthandiza kubwelela kwa Yehova. Mlongo Elizabeth, amene tam’chula m’nkhani ino, anati: “Cinali covuta kwambili kuleka kukamba na mwana wathu wamkulu. Koma atabwelela kwa Yehova, anavomeleza kuti anayeneladi kucotsedwa mu mpingo. Pambuyo pake, iye anati anaphunzilapo kanthu pa zimene zinamucitikilazo. N’nafika poyamikila cilango cimene Yehova amapeleka.” Mwamuna wake Mark anawonjezela kuti: “Patapita nthawi, mwana wathu ananiuza kuti afuna kubwelela mu mpingo, cifukwa coona kuti sitinali kuceza naye olo pang’ono. Ndine wokondwa kuti Yehova anatithandiza kukhalabe omvela.”

13. N’ciani cingakuthandizeni kucepetsa cisoni canu?

13 Uzankoni anzanu apamtima mmene mumvelela. Cina, muziceza na Akhristu okhwima amene angakuthandizeni kuti musataye mtima. (Miy. 12:25; 17:17) Joanna, amene tam’chula poyamba, anati: “N’nali kukhala wosungulumwa. Koma kuuzako mabwenzi anga apamtima kunanithandiza kupilila.” Nanga mungacite ciani ngati ena mu mpingo akamba zinthu zongowonjezela cisoni canu?

14. N’cifukwa ciani tiyenela ‘kupitiliza kulolelana na kukhululukilana na mtima wonse’?

14 Khalani oleza mtima kwa abale na alongo anu. Kukamba zoona, si onse angakambe zinthu zolimbikitsa. (Yak. 3:2) Tonsefe ndife opanda ungwilo. Conco, musadabwe ngati wina wasoŵa conena, kapena mosadziŵa wakamba zinthu zimene zakukwiyitsani. Kumbukilani malangizo a mtumwi Paulo akuti: “Pitilizani kulolelana ndi kukhululukilana ndi mtima wonse, ngati wina ali ndi cifukwa codandaulila za mnzake.” (Akol. 3:13) Mlongo wina amene wacibale wake anacotsedwa, anati: “Yehova wanithandiza kukhululukila Akhristu anzanga amene amayesetsa kunithandiza, koma osazindikila kuti akunikhumudwitsa.” Kodi mpingo ungacite ciani kuti uthandize okhulupilika m’banjalo?

ZIMENE MPINGO UNGACITE

15. Tingacite ciani kuti tithandize banja limene wacibale wawo wacotsedwa?

15 Alandileni na manja aŵili acibale okhulupilika a munthu wocotsedwa. Mlongo wina dzina lake Miriam, anakamba kuti anali kuyopa kupita ku misonkhano mlongosi wake atacotsedwa mu mpingo. Iye anati: “N’nali na mantha kuti kaya anthu azikamba zotani. Koma n’tapita, n’naona kuti nawonso abale na alongo anali acisoni, ndipo sanachulepo zoipa zokhudza mlongosi wanga wocotsedwa. Niyamikila kuti anali nane pa nthawi yovuta imeneyo.” Mlongo wina anati: “Mwana wathu atacotsedwa, mabwenzi athu anabwela kudzatitonthoza. Ena anacita kutiuza kuti anasoŵa conena. Ena analila nane, ndipo enanso ananilembela makalata acilimbikitso. Zimene anacita zinanilimbikitsa zedi!”

16. Kodi mpingo ungapitilize bwanji kupeleka thandizo ku banja la munthu wocotsedwa?

16 Pitilizani kuthandiza okhulupilika m’banjalo. Iwo afunikila cikondi na cilimbikitso canu kuposa kale lonse. (Aheb. 10:24, 25) Nthawi zina, zacitikapo kuti a m’banja la munthu wocotsedwa amasalidwa monga kuti nawonso ni ocotsedwa. Koma tisalole zimenezi kucitika. Ana amene makolo awo anasiya coonadi, ndiwo afunikila kwambili kuwalimbikitsa na kuwayamikila. Maria, amene mwamuna wake anacotsedwa mu mpingo na kusiya banja lake, anati: “Ena a mabwenzi anga anali kubwela kwathu kudzatiphikila cakudya, na kunithandiza kuphunzitsa ŵana ŵanga. Nawonso zinawakhudza kwambili, ndipo anali kulila nane. Anali kunikhalila kumbuyo pamene ena anali kunikambila mabodza. Iwo ananilimbikitsa ngako!”—Aroma 12:13, 15.

Mpingo umathandiza banja la munthu wocotsedwa (Onani ndime 17) *

17. Kodi akulu angacite ciani kuti atonthoze amene ali na cisoni?

17 Imwe akulu, muziyesetsa kulimbikitsa banja la munthu wocotsedwa. Ni udindo wanu kutonthoza alambili anzanu amene wokondedwa wawo wasiya Yehova. (1 Ates. 5:14) Muziwalimbikitsa misonkhano isanayambe komanso ikatha. Muziwayendelako na kupemphela nawo pamodzi. Cina, muzilalikila nawo, komanso kuwaitanilako pa kulambila kwanu kwa pabanja. Abusa auzimu ayenela kuonetsa cifundo na cikondi ku nkhosa ya Yehova imene ili na cisoni.—1 Ates. 2:7, 8.

MUSAFOOKE NDIPO PITILIZANI KUDALILA YEHOVA

18. Malinga na 2 Petulo 3:9, kodi Mulungu afuna kuti anthu ocita zoipa acite ciani?

18 Yehova “safuna kuti wina aliyense adzawonongedwe, koma amafuna kuti anthu onse alape.” (Ŵelengani 2 Petulo 3:9.) Ngakhale munthu acite chimo lalikulu bwanji, moyo wake umakhalabe wamtengo wapatali kwa Mulungu. Kumbukilani kuti Yehova analipila mtengo wapamwamba kwambili, umene ni nsembe ya dipo la Mwana wake wokondeka, kaamba ka miyoyo ya anthu ocimwa. Mwacifundo, Yehova amayesa kuthandiza anthu amene amusiya kubwelela kwa iye. Iye amayembekezela kuti anthuwo adzabwelela kwa iye, monga mmene fanizo la Yesu la mwana wolowelela limaonetsela. (Luka 15:11-32) Ambili amene anasiya coonadi, patapita nthawi anabwelela kwa Atate wawo wacikondi wakumwamba. Ndipo mpingo unawalandila na manja aŵili. Elizabeth, amene tam’chula poyamba, anakondwela ngako mwana wake atabwelela mu mpingo. Iye anati: “Nimayamikila onse amene anali kutilimbikitsa kuti tisafooke.”

19. N’cifukwa ciani tiyenela kupitiliza kudalila Yehova?

19 Tizidalila Yehova nthawi zonse. Malangizo amene amatipatsa amatithandiza nthawi zonse. Iye ni Tate wopatsa komanso wacifundo, ndipo amakonda onse amene amam’konda na kum’lambila. Dziŵani kuti Yehova sadzakusiyani konse pa nthawi yovuta. (Aheb. 13:5, 6) Mark, amene tam’chula poyamba, anati: “Yehova sangatisiye olo pang’ono. Iye sakhala nafe patali tikakumana na mavuto.” Yehova adzapitiliza kukupatsani “mphamvu yoposa yacibadwa.” (2 Akor. 4:7) Inde, n’zotheka kukhalabe wokhulupilika ngakhale pamene wokondedwa wanu wasiya Yehova.

NYIMBO 44 Pemphelo la Munthu Wovutika

^ ndime 5 Cimaŵaŵa kwambili wa m’banja lathu akasiya Yehova. M’nkhani ino, tiona mmene Mulungu wathu amamvelela izi zakacitika. Tikambilane zimene acibale okhulupilika m’banjalo angacite kuti apilile cisoni, na kukhalabe olimba mwauzimu. Tikambilanenso zimene onse mu mpingo angacite kuti atonthoze na kuthandiza banja lokhudzidwalo.

^ ndime 1 Maina ena m’nkhani ino asinthidwa.

^ ndime 79 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: M’bale akasiya banja lake komanso Yehova, mkazi wake na ŵana amavutika.

^ ndime 81 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Akulu aŵili abwela kudzalimbikitsa banjalo mwauzimu.