Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 35

Muziona Okalamba Okhulupilika Kuti ni Ofunika

Muziona Okalamba Okhulupilika Kuti ni Ofunika

“Imvi ndizo cisoti cacifumu ca ulemelelo.”—MIY. 16:31.

NYIMBO 138 Kukongola kwa Imvi

ZIMENE TIKAMBILANE *

1-2. (a) Malinga na Miyambo 16:31, kodi tiyenela kuwaona motani okalamba okhulupilika? (b) Tiyankha mafunso ati m’nkhani ino?

KU AMERICA, kuli paki ina yake imene mungapeze miyala ya dayamondi panthaka. Koma miyala imeneyo si yoyengedwa moti n’kupangila zinthu. Pa cifukwa cimeneci, ambili akaona miyalayo akhoza kuipitilila posadziŵa kuti ni cuma camtengo wapatali.

2 Tingati okalamba okhulupilika, ni cuma camtengo wapatali monga miyala ya dayamondi imeneyo. Mawu a Mulungu amayelekezela imvi za okalamba amenewa na cisoti cacifumu. (Ŵelengani Miyambo 16:31; 20:29) Komabe, tingayambe kuona okalamba kukhala osafunika. Acicepele amene amaona okalamba kuti ni ofunika, amapeza cinthu camtengo wapatali kuposa cuma cakuthupi. M’nkhani ino, tiyankha mafunso atatu aya: N’cifukwa ciani Yehova amaona okalamba okhulupilika kuti ni amtengo wapatali? N’cifukwa ciani okalamba ni ofunika m’gulu la Yehova? Nanga tingacite ciani kuti tipindule mokwanila na citsanzo cawo?

CIFUKWA CAKE YEHOVA AMAONA OKALAMBA OKHULUPILIKA KUKHALA AMTENGO WAPATALI

Okalamba okhulupilika ni amtengo wapatali kwa Yehova, komanso kwa anthu ake (Onani ndime 3)

3. Malinga na Salimo 92:12-15, n’cifukwa ciani okalamba okhulupilika ni amtengo wapatali kwa Yehova?

3 Okalamba okhulupilika ni amtengo wapatali kwa Yehova Mulungu. Iye amaona umunthu wawo wamkati, ndipo amayamikila makhalidwe awo abwino. Amayamikilanso ngati iwo agaŵilako acicepele cidziŵitso cimene akhala naco, pa zaka zonse zimene akhala akutumikila Mulungu mokhulupilika. (Yobu 12:12; Miy. 1:1-4) Yehova amayamikilanso kupilila kwawo. (Mal. 3:16) Olo kuti akhala akukumana na mavuto, cikhulupililo cawo mwa Yehova sicinagwedezeke. Ciyembekezo cawo ca zakutsogolo calimbilako kuposa mmene cinalili atangophunzila coonadi. Ndipo Yehova amawakonda cifukwa copitiliza kulengeza za dzina lake ngakhale pa ukalamba wawo.—Ŵelengani Salimo 92:12-15.

4. N’ciani cingalimbikitse abale na alongo athu okalamba?

4 Ngati mupita mukalamba, dziŵani kuti Yehova amakumbukila zonse zimene munam’citila m’mbuyomu. (Aheb. 6:10) Mwakhala mukucilikiza nchito yolalikila mokangalika, ndipo zimenezi zimam’kondweletsa Atate wathu wakumwamba. Mwakhala mukupilila mayeso osiyana-siyana, kutsatila miyezo ya m’Baibo, kusamalila maudindo aakulu, komanso kuphunzitsa ena. Mwakhala mukuyendela pamodzi na gulu la Yehova limene lili pa liŵilo. Ndipo mwalimbikitsa amene ali mu utumiki wanthawi zonse. Yehova Mulungu amakukondani ngako cifukwa cokhala okhulupilika. Iye analonjeza kuti “sadzasiya anthu ake okhulupilika.” (Sal. 37:28) Analonjezanso kuti: “Munthu wa imvi ndimamunyamula nthawi zonse.” (Yes. 46:4) Conco, musadzione kukhala osafunika m’gulu la Yehova poona kuti lomba mwakalamba. Ndinu ofunikadi kwambili!

OKALAMBA NI OFUNIKA M’GULU LA YEHOVA

5. Kodi okalamba ayenela kukumbukila ciani?

5 Okalamba amathandiza m’njila zambili. Olo kuti tsopano alibe mphamvu poyelekezela na kale, iwo ali na cidziŵitso cokulilapo. Yehova angapitilize kuwagwilitsila nchito, monga mmene tionele pa zitsanzo zakale komanso zamakono.

6-7. Fotokozani zitsanzo za m’Baibo za okalamba amene anadalitsidwa cifukwa cocita utumiki wawo mokhulupilika.

6 M’Baibo muli zitsanzo za anthu okhulupilika amene anatumikila Yehova mokangalika mpaka pa ukalamba wawo. Mwacitsanzo, Mose anali na zaka pafupifupi 80 pamene anakhala mneneli wa Yehova, komanso mtsogoleli wa Aisiraeli. Pamene Danieli anali na zaka mwina zoposa 90, Yehova anapitiliza kumugwilitsila nchito monga mneneli. Nayenso mtumwi Yohane ayenela kuti anali za zaka m’ma 90 pamene anauzilidwa kulemba buku la chivumbulutso.

7 Pali okhulupilika enanso oculuka amene Baibo siikamba zambili zokhudza iwo. Conco, cingakhale cosavuta kuwaiŵala. Ngakhale n’telo, Yehova anali kuwadziŵa, ndipo anawafupa cifukwa ca kukhulupilika kwawo. Mwacitsanzo, Simiyoni munthu “wolungama ndi woopa Mulungu,” amachulidwa mwacidule m’Baibo, koma Yehova anali kum’dziŵa bwino kuti iye anali ndani. Ndipo anam’patsa mwayi woona Yesu ali khanda, komanso kulosela zokhudza Yesu ameneyo na mayi ake. (Luka 2:22, 25-35) Ganizilaninso za mneneli wamkazi wamasiye Anna. Anali na zaka 84, koma “sanali kusoŵa pakacisi.” Cifukwa copezeka pakacisi nthawi zonse, Yehova anam’dalitsa, ndipo anakhala na mwayi woona Yesu ali khanda. Simiyoni komanso Anna anali amtengo wapatali kwa Yehova.—Luka 2:36-38.

Mlongo Didur, amene tsopano ali m’zaka za m’ma 80, akali kutumikila mokhulupilika (Onani ndime 8)

8-9. Kodi mlongo wina wamasiye akupitiliza kucita ciani?

8 Masiku ano, okalamba ambili okhulupilika akhala zitsanzo zabwino kwambili kwa acicepele. Ganizilani citsanzo ca mlongo Lois Didur. Iye anali na zaka 21 pamene anakhala mpainiya wapadela ku Canada. Pambuyo pake, iye na mwamuna wake John, anatumikila m’nchito ya m’dela kwa zaka zambili. Pambuyo pake, iwo anatumikila pa Beteli ku Canada kwa zaka zoposa 20. Pamene mlongo Lois anali na zaka 58, iye na mwamuna wake anapemphedwa kukatumikila ku dziko la Ukraine. Kodi iwo anacita ciani? Kodi anadziona kuti ni okalamba cakuti sangatumikile ku dziko lina? Ayi. Iwo anavomela utumikiwo, ndipo m’bale John anaikidwa kukhala ciwalo ca Komiti ya Nthambi kumeneko. Atatumikila kwa zaka 7, m’bale John anamwalila. Koma mlongo Lois anasankha kupitiliza utumiki wake. Pano tikunena, mlongoyu ali na zaka 81, ndipo akali kutumikilabe pa Beteli ku Ukraine. Iye amakondedwa kwambili.

9 Alongo amasiye monga mlongo Lois, cingakhale cosavuta kuwaona kuti ni osafunika, poyelekezela na mmene tinali kuwaonela amuna awo akali moyo. Komabe, umasiye wawo suwapangitsa kukhala osafunika. Yehova amawakonda ngako alongo amene anacilikiza amuna awo kwa zaka zambili, ndipo akupitiliza kum’tumikila mokhulupilika. (1 Tim. 5:3) Cina, iwo amalimbikitsanso acicepele.

10. Kodi m’bale Tony ni citsanzo cabwino motani?

10 Okalamba okhulupilika ambili amene akhala m’nyumba zosungilamo okalamba, nawonso ni amtengo wapatali. Mwacitsanzo, m’bale Tony ni mmodzi wa okalamba amenewa. Iye anabatizikila ku Pennsylvania, U.S.A., mu August 1942 ali na zaka 20. Cifukwa cokana kungena usilikali, anaponyedwa m’ndende kwa zaka ziŵili na hafu. Iye na mkazi wake Hilda, anaphunzitsa ana awo aŵili coonadi. Kwa zaka, mbale Tony anatumikila m’mipingo itatu monga woyang’anila wotsogolela (amene tsopano timati mgwilizanitsi wa bungwe la akulu), komanso monga woyang’anila msonkhano wadela. Iye anali kupita ku ndende kukacititsa misonkhano, na kutsogoza maphunzilo a Baibo. Olo kuti ali na zaka 98, iye akali kutumikila Yehova. Amayesetsa kucita zimene angathe potumikila Yehova pamodzi na abale na alongo mu mpingo.

11. Kodi okalamba amene akhala okha, kapena amene asungidwa na ŵana ŵawo, tingaŵaonetse bwanji kuti ni ofunika?

11 Kodi okalamba amene akhala okha, kapena amene asungidwa na ŵana ŵawo, tingaŵaonetse bwanji kuti ni ofunika? Akulu mu mpingo angawathandize m’njila zambili, monga kupezeka pa misonkhano, komanso kutengako mbali mu ulaliki. Tingapite kukaceza nawo kapena kulankhula nawo kupitila pa vidiyo, poonetsa kuti timawakonda. Tiziikila nzelu kwambili okalamba amene akhala kutali na mpingo wa kwawo. Tizionetsetsa kuti sitikuŵaiŵala. Okalamba ena cingakhale covuta kufotokoza za iwo eni. Koma tidzapindula ngako ngati tipatula nthawi yoceza nawo, na kuŵamvetsela pamene akufotokoza madalitso amene apeza m’gulu la Yehova.

12. Kodi tingapeze ciani mu mpingo mwathu?

12 Tingadabwe kudziŵa kuti mu mpingo mwathu, muli okalamba okhulupilika amene ni zitsanzo zabwino. Mwacitsanzo, kwa zaka zambili, mlongo Harriette anatumikila Yehova mokhulupilika mu mpingo wa kwawo ku New Jersey, U.S.A. Kenako, anasamuka n’kupita kukakhala na mwana wake wamkazi. Abale na alongo mu mpingo wake watsopano, anayamba kuceza naye kuti am’dziŵe bwino. Iwo anaona kuti mlongoyu ni cuma camtengo wapatali. Iye anawalimbikitsa powasimbilako zocitika za mu utumiki wake, atangophunzila coonadi m’ma 1920. Panthawiyo, iye nthawi zonse anali kunyamula mswaci poyenda mu ulaliki, cifukwa anali kudziŵa kuti nthawi iliyonse angamangidwe. Ndipo mu 1933, anaponyedwa m’ndende kaŵili konse kwa mlungu umodzi. Akamangiwa, mwamuna wake amene sanali Mboni, anali kum’cilikiza na kusamalila ana awo atatu aang’ono. Ndithudi, okalamba okhulupilika monga Harriette tiziwalemekeza.

13. Kodi taphunzila ciani zokhudza okalamba m’gulu la Yehova?

13 Abale na alongo athu okalamba ni ofunika kwambili kwa Yehova komanso ku gulu lake. Iwo akhala akuona mmene Yehova wadalitsila gulu lake, komanso iwo eni m’njila zosiyana-siyana. Okalamba amenewo aphunzilapo kanthu pa zophophonya zawo. Conco, muziwaona kuti ni “citsime ca nzelu.” (Miy. 18:4) Mukamapatula nthawi kuti muwadziŵe bwino, cikhulupililo canu cidzalimba, ndipo mudzaphunzila zambili kwa iwo.

PINDULANI MOKWANILA NA ZITSANZO ZA OKALAMBA

Monga mmene Elisa anapindulila kukhala na Eliya, abale na alongo angapindule na zitsanzo za aja amene atumikila Yehova kwa zaka zambili (Onani ndime 14-15)

14. Kodi Deuteronomo 32:7, ilimbikitsa acicepele kucita ciani?

14 Muzipeza nthawi yoceza na okalamba. (Ŵelengani Deuteronomo 32:7.) N’zoona kuti kuyang’ana kumawavuta, kuyenda nako n’kovutikila, ndipo cimakhala covuta kulankhula bwino-bwino. Koma iwo amafunabe kukhala okangalika, ndipo adzipangila “mbili yabwino” kwa Yehova. (Mlal. 7:1) Muzikumbukila kuti Yehova amawaona kuti ni ofunika ngako. Motelo, pitilizani kuwalemekeza. Khalani monga Elisa. Iye anafunitsitsa kukhalabe na Eliya pa tsiku lawo lothela kukhala pamodzi. Katatu konse Elisa anauza Eliya kuti: “Sindikusiyani.”—2 Maf. 2:2, 4, 6.

15. Tingawafunse mafunso otani okalamba?

15 Muziwaonetsa cidwi ceniceni okalamba mwa kuwafunsa mafunso mokoma mtima. (Miy. 1:5; 20:5; 1 Tim. 5:1, 2) Afunseni mafunso monga akuti: “Pamene munali wacicepele, n’ciani cinakupangitsani kutsimikiza kuti mwapeza coonadi?” “Kodi zocitika mu umoyo wanu zakuthandizani bwanji kuyandikila kwambili Yehova?” “N’ciani cakuthandizani kupitiliza kukhala acimwemwe potumikila Yehova?” (1 Tim. 6:6-8) Ndiyeno mvetselani pamene akufotokoza.

16. Kodi okalamba komanso acicepele amapindula motani akamacezela limodzi?

16 Okalamba akamaceza na acicepele, onse amapindula. (Aroma 1:12) Acicepele adzakulitsa ciyamiko cawo pa Yehova poona mmene amasamalila atumiki ake okhulupilika, ndipo okalamba adzaona kuti amakondewa. Iwo adzakondwela kwambili kukusimbilankoni mmene Yehova waadalitsila.

17. N’cifukwa ciani tingati okalamba okhulupilika amakongolelako m’kupita kwa zaka?

17 Kukongola kwa kuthupi kumatha munthu akamakula, koma anthu okhulupilika kwa Yehova, amakongolelako m’kupita kwa zaka. (1 Ates. 1:2, 3) N’cifukwa ciani zili conco? Cifukwa kwa zaka, iwo alola mzimu wa Mulungu kuwaumba, na kuŵathandiza kukulitsa makhalidwe abwino. Tikafika powadziŵa bwino okalamba athu okondedwa, kuwalemekeza, na kuphunzila kwa iwo, m’pamenenso tiziŵaona kuti ni cuma camtengo wapatali.

18. Tidzakambilana ciani m’nkhani yotsatila?

18 Mpingo umalimbilako ngati nawonso okalamba amaona acicepele kuti ni ofunika. M’nkhani yotsatila, tidzakambilana mmene okalamba angaonetsele kuti amaona acicepele mu mpingo kuti ni ofunika.

NYIMBO 144 Yang’ana pa Mphoto

^ ndime 5 Okalamba okhulupilika ali ngati cuma camtengo wapatali. Nkhani ino, itithandiza kukulitsa ciyamikilo cathu pa okalamba. Cina, tikambilane mmene tingapindulile na nzelu zawo, komanso zimene akwanitsa kucita potumikila Mulungu. Idzalimbikitsanso okalamba kuona kuti ni ofunika m’gulu la Mulungu.