NKHANI YOPHUNZILA 37
“Ndigwedeza Mitundu Yonse Ya Anthu”
“Ndigwedeza mitundu yonse ya anthu, ndipo zinthu zamtengo wapatali zocokela ku mitundu yonse ya anthu zidzaloŵa m’nyumba imeneyi.”—HAG. 2:7.
NYIMBO 24 Bwelani ku Phili la Yehova
ZIMENE TIKAMBILANE *
1-2. Kodi ni gwede-gwede wophiphilitsa uti, amene mneneli Hagai analosela kuti adzacitika m’masiku athu ano?
“M’MPHINDI zocepa cabe, mashopu na zimango zakale zinayamba kuundumuka n’kugwa ngati zidina zosalimba.” “Aliyense anali na nkhawa . . . Anthu ambili anati gwede-gwede ameneyo anacitika m’mamineti aŵili cabe. Koma kwa ine, n’naona kuti anatenga nthawi yaitali.” Izi n’zimene ena anakamba pambuyo pa civomezi cimene cinacitika ku Nepal, mu 2015. Sembe cocitika cocititsa mantha cimeneci cinacitikila imwe, simukanaciiŵala.
2 Komabe, pano tinena, pakucitika gwede-gwede wa mtundu wina, ndipo sakukhudza mzinda umodzi kapena dziko limodzi lokha ayi. Koma akukhudza mitundu yonse ya anthu, ndipo wakhala akucitika kwa zaka zambili. Mneneli Hagai analosela za gwede-gwede ameneyu. Iye anati: “Yehova wa makamu wanena kuti, ‘Posacedwapa ndigwedezanso kumwamba, dziko lapansi, nyanja ndi mtunda.’”—Hag. 2:6.
3. Kodi kugwedeza kophiphilitsa kusiyana bwanji na civomezi ceniceni?
3 Kugwedeza kumene Hagai anakamba, si kuli monga civomezi cimene cimangowononga zinthu cabe. Koma kugwedeza kumeneku, kuli na zotulukapo zabwino. Yehova amatiuza kuti: “Ndigwedeza mitundu yonse ya anthu, ndipo zinthu zamtengo wapatali zocokela ku mitundu yonse ya anthu zidzaloŵa m’nyumba imeneyi. Ine ndidzadzaza nyumbayi ndi ulemelelo.” (Hag. 2:7) Kodi ulosiwu unatanthauza ciani kwa anthu a m’nthawi ya Hagai? Nanga utanthauza ciani kwa ife masiku ano? Nkhani ino, iyankha mafunso amenewa, komanso tiphunzila mmene tingatengeleko mbali pa kugwedeza mitundu masiku ano.
UTHENGA WOLIMBIKITSA M’NTHAWI YA HAGAI
4. N’cifukwa ciani Yehova anatumiza mneneli Hagai kwa anthu ake?
4 Yehova anapatsa mneneli Hagai nchito yofunika kwambili. Ganizilani zinacitika Hagai asanapatsidwe nchitoyo. Hagai ayenela kuti anali pagulu la Ayuda amene anabwelela ku Yerusalemu, atamasulidwa ku ukapolo ku Babulo mu 537 B.C.E. Atangofika kumeneko, alambili okhulupilika amenewo anayala maziko a nyumba ya Yehova, kapena kuti kacisi. (Ezara 3:8, 10) Koma pasanapite nthawi, panabuka vuto linalake. Iwo analefulidwa na kuleka kugwila nchitoyo cifukwa ca anthu owatsutsa. (Ezara 4:4; Hag. 1:1, 2) Conco, mu 520 B.C.E., Yehova anauza Hagai kuti akadzutsenso cangu ca Ayuda amenewo, na kuwalimbikitsa kuti amalize nchito yomanga kacisi. *—Ezara 6:14, 15.
5. N’cifukwa ciani uthenga wa Hagai unali wolimbikitsa kwa anthu a Mulungu?
5 Colinga ca uthenga wa Hagai cinali kulimbitsa cikhulupililo ca Ayuda mwa Yehova. Mneneliyo molimba mtima anauza Ayuda olefukawo kuti: “‘Limbani mtima anthu nonse a m’dzikoli ndipo gwilani nchito,’ watelo Yehova. ‘Pakuti ine ndili ndi inu,’ watelo Yehova wa makamu.” (Hag. 2:4) Mawu akuti “Yehova wa makamu,” ayenela kuti anawalimbikitsa kwambili. Yehova ali na ulamulilo pa makamu a angelo amphamvu. Conco, Ayuda anayenela kum’dalila kuti apambane.
6. Kodi kugwedeza kumene Hagai anakamba kunali na zotulukapo zotani?
6 Yehova anatuma Hagai kukalengeza uthenga woonetsa kuti mophiphilitsa adzagwedeza mitundu yonse. Uthengawo unalimbikitsa Ayuda olefukawo, cifukwa anadziŵa kuti Yehova anali kudzagwedeza Perisiya, umene unali ulamulilo wamphamvu pa nthawiyo. Kodi kugwedeza kumeneko kunakhala na zotulukapo zotani? Coyamba, anthu a Mulungu anali kudzatsiliza kumanga kacisi. Kenako, anthu amene sanali Ayuda anali kudzagwilizana nawo pa kulambila Yehova pa kacisi womangidwanso. Uwu unali uthenga wolimbikitsa ngako kwa anthu a Mulungu!—Zek. 8:9.
NCHITO YOGWEDEZA DZIKO MASIKU ANO
7. Ni nchito yogwedeza iti imene timagwila masiku ano? Fotokozani.
7 Kodi ulosi wa Hagai utanthauza ciani kwa ife masiku ano? Masiku anonso, Yehova akugwedeza mitundu yonse, ndipo ife tikuthandiza pa nchito imeneyi. Ganizilani mfundo iyi: Mu 1914, Yehova anaika Yesu Khristu kukhala Mfumu ya Ufumu wake wakumwamba. (Sal. 2:6) Koma kukhazikitsidwa kwa Ufumuwo kunali uthenga woipa kwa olamulila a dzikoli. Zinali conco cifukwa ‘nthawi za amitundu zoikidwilatu’ zinali zitatha, kutanthauza nthawi imene panalibe wolamulila woimilako Yehova. (Luka 21:24) Pozindikila zimenezi, maka-maka kuyambila mu 1919, anthu a Yehova akhala akuuza ena kuti ni Ufumu wa Mulungu wokha umene udzathetsa mavuto a anthu. Kulalikila “uthenga wabwino wa Ufumu” kumeneku kwagwedeza dziko lonse lapansi.—Mat. 24:14.
8. Malinga na Salimo 2:1-3, kodi anthu ambili aulandila motani uthenga umenewu?
8 Kodi anthu aulandila motani uthenga umenewu? Ambili amaukana. (Ŵelengani Salimo 2:1-3.) Mitundu ya anthu ni yokwiya kwambili. Iwo amam’kana Wolamulila woikidwa na Yehova. Uthenga wa Ufumu umene timalalikila sauona kukhala “uthenga wabwino.” Ndipo maboma ena afika ngakhale poletsa nchito yathu yolalikila. Ngakhale kuti olamulila a dzikoli amati amatumikila Mulungu, iwo safuna kutula pansi udindo wawo. Conco, monga anacitila olamulila m’nthawi ya Yesu, olamulila masiku ano amatsutsa Wodzozedwa wa Yehova mwa kuzunza otsatila ake okhulupilika.—Mac. 4:25-28.
9. Kodi Yehova akuwapatsa mwayi wotani anthu amene amakana uthenga wake?
9 Kodi Yehova amacita ciani na mitundu imene imakana uthenga wake? Salimo 2:10-12 imati: “Tsopano inu mafumu, sonyezani kuzindikila, lolani kuti maganizo anu akonzedwe, inu oweluza a dziko lapansi. Tumikilani Yehova mwamantha. Kondwelani ndipo nthunthumilani. Psompsonani mwanayo kuopela kuti Mulungu angakwiye, ndipo mungawonongeke ndi kucotsedwa panjilayo. Pakuti mkwiyo wake umatha kuyaka mofulumila. Odala ndi onse amene akuthawila kwa iye.” Yehova mokoma mtima wapatsa otsutsa amenewa mwayi wakuti apange cisankho canzelu. Iwo angasinthe maganizo awo na kusankha Ufumu wa Yehova. Komabe, nthawi yotsalayi ni yocepa. Tikukhala “m’masiku otsiliza” a dongosolo la zinthu. (2 Tim. 3:1; Yes. 61:2) Kuposa kale lonse, ino ndiye nthawi yakuti anthu aphunzile coonadi, na kusankha kutumikila Mulungu.
ANTHU ENA AILANDILA BWINO NCHITO YOGWEDEZA
10. Kodi nchito yogwedeza yochulidwa pa Hagai 2:7-9, ili na zotulukapo zabwino zotani?
10 Kugwedeza kophiphilitsa kumene Hagai anakambilatu, kwakhala na zotulukapo zabwino. Iye anati cifukwa ca kugwedeza kumeneko, “zinthu zamtengo wapatali [anthu oona mtima] zocokela ku mitundu yonse ya anthu,” zidzalambila Yehova. * (Ŵelengani Hagai 2:7-9.) Nayenso Yesaya komanso Mika, anakambilatu kuti zimenezi zidzacitika “m’masiku otsiliza.”—Yes. 2:2-4, Mika 4:1, 2.
11. Kodi m’bale wina anacita ciani atamva za uthenga wa Ufumu kwa nthawi yoyamba?
11 Onani zimene uthenga wogwedeza dziko unacita kwa m’bale Ken, amene akutumikila
ku likulu lathu. Olo kuti papita zaka 40, iye amakumbukila bwino-bwino nthawi yoyamba pamene anamva za uthenga wa Ufumu. M’bale Ken anati: “Kwa nthawi yoyamba n’tamva coonadi ca Mawu a Mulungu, n’nakondwela ngako kudziŵa kuti tikukhala m’masiku otsiliza a dongosolo lino la zinthu. N’nadziŵa kuti, kuti niyanjidwe na Mulungu na kukapeza moyo wamuyaya, n’nafunika kusiya kugwilizana na dzikoli losadalilika na kuima nji kumbali ya Yehova. Mwapemphelo n’nacitadi zimenezi. N’naleka kucilikiza zocitika za m’dzikoli. Kenaka n’nayamba kucilikiza Ufumu wa Mulungu umene sungagwedezeke.”12. Kodi kacisi wauzimu wa Yehova wakhala na ulemelelo wotani m’masiku ano otsiliza?
12 N’zoonekelatu kuti Yehova wakhala akudalitsa anthu ake. M’masiku ano otsiliza, taona kuwonjezeleka kwakukulu kwa anthu omulambila. Mu 1914 tinali masauzande ocepa cabe. Koma lomba tiposa 8 miliyoni, ndipo caka ciliconse anthu mamiliyoni amacita nafe Cikumbutso. Pa cifukwa cimeneci, m’mabwalo a padziko lapansi a kacisi wauzimu wa Yehova, kutanthauza makonzedwe ake a kulambila koona, mwadzala na “zinthu zamtengo wapatali zocokela ku mitundu yonse ya anthu.” Cina, dzina la Mulungu limalemekezedwa pamene anthuwa apanga masinthidwe na kuvala umunthu watsopano.—Aef. 4:22-24.
13. Cifukwa ca kukula kocititsa cidwi kwa gulu la Mulungu, ni maulosi ena ati amene akwanilitsidwa? (Onani cithunzi pacikuto.)
13 Kukula kocititsa cidwi kwa gulu la Mulungu kumeneku, kwakwanilitsanso maulosi ena, monga ulosi wochulidwa pa Yesaya caputala 60. Vesi 22 ya caputala imeneyi imati: “Wamng’ono adzasanduka anthu 1,000, ndipo wocepa adzasanduka mtundu wamphamvu. Ineyo Yehova ndidzafulumizitsa zimenezi pa nthawi yake.” Cifukwa ca kuculuka kwa alambili oona, pacitika cinthu cokondweletsa kwambili. “Zinthu zamtengo wapatali” zimenezi, kapena kuti anthu amenewa, amabwela m’gulu la Mulungu na maluso osiyana-siyana, komanso amakhala ofunitsitsa kutengapo gawo pa nchito yolalikila “uthenga wabwino wa Ufumu.” Conco, monga ananenela Yesaya, “mkaka wa mitundu ya anthu” ukupelekedwa kwa anthu a Yehova. (Yes. 60:5, 16) Ndipo mwa thandizo la amuna komanso akazi amtengo wapatali amenewa, nchito yolalikila ikugwilidwa m’maiko 240, ndipo mabuku akufalitsidwa m’zinenelo zoposa 1,000.
NTHAWI YOPANGA CISANKHO
14. Kodi anthu ayenela kupanga cisankho cotani pali lomba?
14 M’nthawi ino yamapeto, kugwedeza mitundu kumeneku kukupangitsa anthu kukakamizika kupanga cisankho. Kodi iwo adzacilikiza Ufumu wa Mulungu, kapena adzaika cidalilo cawo m’maboma a dzikoli? Ici n’cisankho cimene aliyense ayenela kupanga. Olo kuti anthu a Yehova amamvela malamulo a boma a m’dziko lawo, iwo satengela mbali iliyonse m’ndale za dziko. (Aroma 13:1-7) Amadziŵa kuti ni Ufumu wa Mulungu wokha umene udzathetsa mavuto a anthu. Ndipo Ufumuwo suli mbali ya dziko.—Yoh. 18:36, 37.
15. Kodi buku la Chivumbulutso limaonetsa kuti kukhulupilika kwa anthu a Mulungu kudzayesedwa motani?
15 Buku la Chivumbulutso limaonetsa kuti kukhulupilika kwa anthu a Mulungu kudzayesedwa m’masiku otsiliza. Mayeso amenewo adzapitiliza kubwela mwa zitsutso na mazunzo pa ife. Maboma a dzikoli adzafuna kuti tizilambila iwo, ndipo adzazunza amene adzakana kutelo. (Chiv. 13:12, 15) Mabomawo ‘adzakakamiza anthu onse, olemekezeka ndi onyozeka, olemela ndi osauka, mfulu ndi akapolo, kuti apatsidwe cizindikilo padzanja lawo lamanja kapena pamphumi pawo.’ (Chiv. 13:16) M’nthawi zakale, akapolo anali kudindiwa cizindikilo copseleza coonetsa umwini wa mbuye wawo. Mofananamo, onse masiku ano akuyembekeledwa kukhala na cizindikilo pa dzanja kapena pa mphumi pawo. Mabomawo adzafuna kuti aliyense aonetse mwa maganizo ake, komanso zocita zake kuti akucilikiza ndale m’dzikoli.
16. N’cifukwa ciani tiyenela kulimbitsa cikhulupililo cathu mwa Yehova pali pano?
16 Kodi ife tidzalandila cizindikilo cophiphilitsa cimeneco na kucilikiza maboma a ndale? Awo amene adzakana, adzakumana na mavuto aakulu. Buku la Chivumbulutso limakambanso kuti: “Aliyense asathe kugula kapena kugulitsa, kupatulapo ngati ali ndi cizindikiloco.” (Chiv. 13:17) Koma anthu a Mulungu adziŵa zimene Mulungu adzacita kwa anthu amene ali na cizindikilo cochulidwa pa Chivumbulutso 14:9, 10. M’malo mokhala na cizindikilo cimeneco, zidzakhala ngati iwo alemba pa dzanja lawo kuti, “Wa Yehova.” (Yes. 44:5) Ino ndiye nthawi yolimbitsa cikhulupililo cathu mwa Yehova. Cikhulupililo cathu cikalimba, Yehova adzakhala wonyadila kukamba kuti ndife ake-ake!
KUGWEDEZA KOTSILIZA
17. Kodi tiyenela kukumbukila ciani pa kuleza mtima kwa Yehova?
17 Yehova waonetsa kuleza mtima kwakukulu masiku ano otsiliza. Iye safuna kuti wina aliyense akawonongedwe. (2 Pet. 3:9) Wapatsa anthu onse nthawi yakuti alape, na kusankha kumum’tumikila. Koma kuleza mtima kwake kuli na polekezela. Amene amakana mwayi umenewu mapeto awo adzafanana monga a Farao m’nthawi ya Mose. Yehova anauza Farao kuti: “Pofika pano ndikanatambasula kale dzanja langa ndi kukupha ndi mlili, iweyo ndi anthu ako, kukufafanizani padziko lapansi. Koma ndakusiya ndi moyo kuti ndikusonyeze mphamvu zanga, ndi kuti dzina langa lilengezedwe padziko lonse lapansi.” (Eks. 9:15, 16) Mitundu yonse nayonso idzadziŵa kuti Yehova ndiye Mulungu yekha woona. (Ezek. 38:23) Kodi izi zidzacitika motani?
18. (a) Kodi pa Hagai 2:6, 20-22, pakuchula kugwedeza kwina kuti? (b) Nanga tidziŵa bwanji kuti mawu a Hagai adzakwanilitsika kutsogolo?
Hagai 2:6, 20-22 anali kudzakwanilitsidwa m’tsogolo. (Ŵelengani.) Iye analemba kuti: “Koma tsopano walonjeza kuti: ‘Ndidzagwedezanso kumwamba, osati dziko lapansi lokhali.’ Tsopano, mawu akuti ‘ndidzagwedezanso,’ akusonyeza kuti zinthu zimene adzazigwedezezo zidzacotsedwa. Zimenezi ndi zinthu zimene zinapangidwa ndi winawake, ndipo adzazicotsa kuti zimene sizikugwedezeka zitsale.” (Aheb. 12:26, 27) Mosiyana na kugwedeza kochulidwa pa Hagai 2:7, kugwedeza kumeneku kukutanthauza ciwonongeko camuyaya kwa aja amene, mofanana na Farao, amakana kuvomeleza kuti Yehova ndiye woyenela kulamulila.
18 Patapita zaka zambili Hagai atamwalila, mtumwi Paulo mouzilidwa anaonetsa kuti mawu apa19. Kodi cimene sicidzagwedezeka n’ciani? Nanga tidziŵa bwanji?
19 N’ciani cimene sicidzagwedezeka kapena kucotsedwa? Paulo anapitiliza kuti: “Poona kuti tidzalandila Ufumu umene sungagwedezeke, tiyeni tipitilize kulandila kukoma mtima kwakukulu, kuti kudzela m’kukoma mtima kwakukulu kumeneko, ticitile Mulungu utumiki wopatulika m’njila yovomelezeka, ndipo tiucite moopa Mulungu komanso mwaulemu waukulu.” (Aheb. 12:28) Kugwedeza kotsiliza kukadzatha, ni Ufumu wa Mulungu wokha umene udzakhalapo ndipo sudzagwedezeka konse.—Sal. 110:5, 6; Dan. 2:44.
20. Kodi anthu ayenela kupanga cisankho cotani? Nanga tingawathandize bwanji?
20 Ino si nthawi yocita zengelezu! Anthu ayenela asankhe, kaya kupitiliza na moyo umene dzikoli limalimbikitsa, wopita ku ciwonongeko, kapena kutumikila Yehova na makhalidwe awo kuti akapeze moyo wamuyaya. (Aheb. 12:25) Mwa nchito yathu yolalikila, tingathandize anthu kupanga cisankho pa nkhani yofunika kwambili imeneyi. Tiyeni tithandize anthu ambili kusankha kucilikiza Ufumu wa Mulungu. Ndipo nthawi zonse tizikumbukila mawu a Ambuye Yesu akuti: “Uthenga wabwino uwu wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.”—Mat. 24:14.
NYIMBO 40 Kodi Ndife a Ndani?
^ ndime 5 Nkhani ino, ifotokoza kamvedwe katsopano ka lemba la Hagai 2:7. M’nkhani ino, tiphunzile mmene tingatengeleko mbali m’nchito yofunika kwambili imene ikugwedeza mitundu yonse. Tidzaonanso kuti nchito yogwedeza imeneyi imapangitsa anthu ena kumvetsela uthenga wathu, pamene ena amaukana.
^ ndime 4 Tidziŵa kuti Hagai anacita zimene anauzidwa, cifukwa anatsiliza kumanga kacisi mu 515 B.C.E.
^ ndime 10 Kumeneku ni kusintha kwa kamvedwe kathu. Kale tinali kukhulupilila kuti kugwedeza mitundu yonse, si ndiko kupangitsa anthu oona mtima kuyamba kutumikila Yehova. Onani nkhani yakuti “Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga,” mu Nsanja ya Olonda ya May 15, 2006.
^ ndime 63 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Hagai analimbikitsa anthu a Mulungu kuti acilimike pa nchito yomanganso kacisi. Atumiki a Mulungu amakono amafalitsa uthenga wa Mulungu mokangalika. Banja likulalikila uthenga wokhudza kugwedeza kotsiliza.