Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 39

Kodi Dzina Lanu Lilimo “M’buku la moyo”?

Kodi Dzina Lanu Lilimo “M’buku la moyo”?

“Buku la cikumbutso linayamba kulembedwa pamaso pake. Buku limeneli linali lonena za anthu oopa Yehova.”—MAL. 3:16.

NYIMBO 61 Patsogolo! Inu Mboni Zake

ZIMENE TIKAMBILANE *

Kuyambila m’nthawi ya Abele, Yehova wakhala akuwonjezela maina ena “m’buku la moyo” (Onani ndime 1-2)

1. Malinga n’kunena kwa Malaki 3:16, kodi Yehova wakhala akulemba buku liti? Nanga m’bukulo muli ciyani?

 KWA zaka masauzande, Yehova wakhala akulemba buku lapadela. M’buku limeneli muli mndandanda wa maina, ndipo dzina loyamba ni la Abele, mboni yokhulupilika. * (Luka 11:50, 51) Kuyambila nthawiyo, Yehova wakhala akuwonjezela maina ena m’bukulo. Ndipo masiku ano, mainawo afika m’mamiliyoni. M’Baibo, bukulo limachedwa “buku la cikumbutso,” “buku la moyo,” komanso “mpukutu wa moyo.” Koma m’nkhani ino, tigwilitse nchito mawu akuti “buku la moyo.”—Ŵelengani Malaki 3:16; Chiv. 3:5; 17:8.

2. Ni maina andani amene amalembedwa m’buku la moyo? Nanga tingacite ciyani kuti dzina lathu lilembedwe m’buku limeneli?

2 M’buku lapadela limeneli, muli maina a anthu amene amalambila Yehova momuopa, kapena kuti na ulemu waukulu, ndiponso amene amakonda dzina lake. Iwo ali pa mzele wokalandila moyo wosatha. Ifenso masiku ano, dzina lathu lingalembedwe m’buku la moyo limenelo ngati tipitiliza kukhala pa ubale wolimba na Yehova na kuukulitsa. Zimenezi zimatheka pa maziko a nsembe ya dipo la Mwana wake, Yesu Khristu. (Yoh. 3:16, 36) Tonsefe timafuna dzina lathu litalembedwa m’buku limenelo—kaya ciyembekezo cathu n’cokakhala kumwamba, kapena pano padziko lapansi.

3-4. (a) Ngati palipano dzina lathu lilimo m’buku la moyo, kodi ndiye kuti basi tidzalandila moyo wosatha? Fotokozani. (b) Nanga tikambilane ciyani m’nkhani ino komanso yotsatila?

3 Kodi izi zitanthauza kuti onse amene maina awo alembedwa m’buku limeneli ndiye kuti basi adzalandila moyo wosatha? Yankho la funso limeneli timalipeza m’mawu amene Yehova anauza Mose pa Ekisodo 32:33. Yehova anati: “Amene wandicimwilayo ndi amene ndim’fafanize m’buku langa.” Conco, maina amene palipano alimo m’bukulo akhoza kufafanizidwa, kapena kuti kucotsedwamo. Zili ngati kuti Yehova poyamba analemba mainawo na pensulo. (Chiv. 3:5) Tiyenela kuyesetsa kuti dzina lathu likhalebe m’buku la moyo limenelo mpaka pamene lidzalembedwe mwacikhalile na colembela ca inki, titelo kunena kwake.

4 Koma izi zingabutse mafunso. Mwacitsanzo, kodi Baibo imati ciyani za anthu amene maina awo analembedwa m’buku la moyo, komanso za aja amene maina awo sanalembedwemo? Kodi anthu amene maina awo analembedwa m’bukulo adzalandila liti moyo wosatha? Nanga bwanji za awo amene anafa asanadziŵe Yehova? Kodi n’zotheka maina awo kulembedwa m’buku la moyo limenelo? Mafunso amenewa adzayankhidwa m’nkhani ino komanso yotsatila.

NI MAINA ANDANI ALI M’BUKU LA MOYO?

5-6. (a) Malinga na Afilipi 4:3, ni maina andani amene analembedwa m’buku la moyo? (b) Ni liti pamene maina awo adzalembedwa mwacikhalile m’buku la moyo?

5 Ni maina andani amene analembedwa m’buku lophiphilitsa limeneli? Kuti tiyankhe funso limeneli, tiyeni tikambilane magulu asanu a anthu. Pa magulu amenewa, ena maina awo ni olembedwa m’buku la moyo, koma ena sanalembedwe.

6 Gulu loyamba ni aja amene anasankhidwa kuti akalamulile pamodzi na Yesu kumwamba. Kodi maina awo palipano ni olembedwa m’buku la moyo? Inde. Malinga na mawu a mtumwi Paulo kwa ‘anchito anzake’ ku Filipi, maina a odzozedwa, amene anaitanidwa kuti akalamulile na Yesu alimo m’buku la moyo. (Ŵelengani Afilipi 4:3.) Koma kuti maina awo akhalemobe m’buku lophiphilitsa limeneli, ayenela kukhalabe okhulupilika. Iwo akadzalandila cidindo cothela, kaya asanamwalile kapena cisautso cacikulu cisanayambe, maina awo adzalembedwa mwacikhalile m’buku limeneli.—Chiv. 7:3.

7. Malinga n’kunena kwa Chivumbulutso 7:16, 17, ni liti pamene maina a khamu lalikulu la nkhosa zina adzalembedwa mwacikhalile m’buku la moyo?

7 Gulu laciŵili ni khamu lalikulu la nkhosa zina. Kodi maina awo ni olembedwa m’buku la moyo? Inde. Kodi maina awo adzakhalamobe m’buku la moyo pambuyo pa Aramagedo? Inde. (Chiv. 7:14) Yesu anakamba kuti anthu onga nkhosa amenewa adzacoka kupita “ku moyo wosatha.” (Mat. 25:46) Koma opulumuka Aramagedo amenewo sikuti adzalandila moyo wosatha nthawi yomweyo. Maina awo adzakhalabe olembedwa m’buku la moyo na pensulo, titelo kukamba kwake. Mu Ulamulilo wa Zaka Cikwi (1,000), Yesu “adzawaweta ndi kuwatsogolela ku akasupe a madzi a moyo.” Anthu amene adzatsatila citsogozo ca Yesu na kuweluzidwa pamapeto pake kuti ni okhulupilika kwa Yehova, maina awo adzalembedwa mwacikhalile m’buku la moyo.—Ŵelengani Chivumbulutso 7:16, 17.

8. Ni maina andani amene sanalembedwe m’buku la moyo? Nanga n’ciyani cidzawacitikile?

8 Gulu lacitatu ni anthu onga mbuzi, amene adzawonongedwa pa Aramagedo. Maina awo mulibe m’buku la moyo. Yesu anakamba kuti “adzacoka kupita ku ciwonongeko cothelatu.” (Mat. 25:46) Mouzilidwa na mzimu woyela, Paulo anakamba kuti “amenewa adzawaweluza kuti alandile cilango ca ciwonongeko camuyaya.” (2 Ates. 1:9; 2 Pet. 2:9) Zidzakhalanso cimodzimodzi kwa awo amene akhala akucimwila mzimu woyela mwadala. Nawonso adzalandila ciwonongeko cofafaniza kothelatu, osati moyo wosatha. Mwacionekele iwo sadzaukitsidwa. (Mat. 12:32; Maliko 3:28, 29; Aheb. 6:4-6) Tsopano, tiyeni tione magulu aŵili a anthu amene adzaukitsidwa pano padziko lapansi.

ANTHU AMENE ADZAUKITSIDWA

9. Malinga na Machitidwe 24:15, ni magulu aŵili ati amene adzaukitsidwa pano padziko lapansi? Nanga pali kusiyana kotani pakati pa magulu aŵili amenewa?

9 Baibo imakamba za magulu aŵili a anthu amene adzaukitsidwa kuti adzakhale na moyo kwamuyaya pa dziko lapansi. Magulu aŵili amenewa ni anthu “olungama” komanso “osalungama.” (Ŵelengani Machitidwe 24:15.) “Olungama” ni anthu amene anatumikila Yehova mokhulupilika pamene anali moyo. Kumbali inayo, “osalungama” ni anthu amene sanali kulambila Yehova asanafe. Ndipo makhalidwe awo sanali abwino. Popeza magulu onse aŵiliwa adzaukitsidwa, kodi tingati maina awo analembedwa m’buku la moyo? Kuti tiyankhe funso limeneli, tiyeni tikambilane gulu lililonse palokha.

10. N’cifukwa ciyani “olungama” adzaukitsidwa? Nanga ena a iwo adzapatsidwa mwayi wotani? (Ponena za ciukitso ca odzakhala pano padziko lapansi, onaninso nkhani yakuti, “Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga” m’magazini ino.)

10 Gulu lacinayi ni anthu “olungama.” Anthu amenewa asanafe, maina awo anali atalembedwa kale m’buku la moyo. Kodi maina awo anacotsedwamo m’bukulo atafa? Ayi, cifukwa m’maganizo mwa Yehova, iwo akali “amoyo.” Yehova “ndi Mulungu wa anthu amoyo, osati akufa, pakuti kwa iye onsewa ndi amoyo.” (Luka 20:38) Izi zitanthauza kuti olungama akadzaukitsidwa padziko lapansi, maina awo adzakhala alimobe m’buku la moyo, ngakhale kuti poyamba adzakhala olembedwa na “pensulo.” (Luka 14:14) Mosakayika konse, ena mwa oukitsidwa amenewo adzapatsidwa mwayi wodzatumikila monga “akalonga padziko lonse lapansi.”—Sal. 45:16.

11. Kodi anthu “osalungama” adzafunikila kuphunzila ciyani kuti maina awo akalembedwe m’buku la moyo?

11 Gulu lothela ni anthu “osalungama.” Mwina cifukwa cakuti iwo sanali kudziŵa malamulo a Yehova, anali na makhalidwe oipa asanafe. Conco, maina awo sanalembedwe m’buku la moyo. Koma akadzaukitsidwa, Mulungu adzawapatsa mwayi woti maina awo alembedwe m’buku la moyo. Anthu “osalungama” amenewa adzafunikila thandizo lalikulu cifukwa ena a iwo asanafe, anali kucita zinthu zoipa kwambili. Pa cifukwa cimeneci, adzafunika kuphunzitsidwa mmene angakhalile na moyo motsatila malamulo a Yehova olungama. Kuti izi zikatheke, Ufumu wa Mulungu udzakhazikitsa pulogilamu yaikulu yophunzitsa anthu imene sinacitikepo m’mbili yonse ya anthu.

12. (a) Kodi ndani adzaphunzitsa osalungama amenewo? (b) N’ciyani cidzaciticitikile anthu amene adzakana kuseŵenzetsa zimene adzaphunzila?

12 Koma kodi ndani adzaphunzitsa anthu osalungama amenewo? Ni a khamu lalikulu, komanso anthu olungama amene adzaukitsidwa. Kuti osalungama amenewo akalembedwe m’buku la moyo, adzafunika kukhala pa ubale na Yehova na kudzipatulila kwa iye. Yesu Khristu na oweluza anzake adzakhala chelu kuona mmene osalungama akupitila patsogolo. (Chiv. 20:4) Aliyense amene adzakana kulandila thandizo limenelo, sadzaloledwa kukhala na moyo, olo kuti adzakhale na zaka 100. (Yes. 65:20) Yehova na Yesu amene amaŵelenga mitima ya anthu, sadzalola aliyense kuwononga ciliconse m’dziko latsopano.—Yes. 11:9; 60:18; 65:25; Yoh. 2:25.

KUUKITSIDWA KUTI ALANDILE MOYO, NA KUUKITSIDWA KUTI AWELUZIDWE

13-14. (a) Kodi mawu a Yesu a pa Yohane 5:29 tinali kuwamva motani kumbuyoku? (b) Nanga tiyenela kudziŵa ciyani za mawu amenewa?

13 Yesu anakambanso za anthu amene adzaukitsidwa pano padziko lapansi. Mwacitsanzo, iye anati: “Idzafika nthawi pamene onse ali m’manda acikumbutso adzamva mawu ake ndipo adzatuluka. Amene anali kucita zabwino adzauka kuti alandile moyo. Amene anali kucita zoipa adzauka kuti aweluzidwe.” (Yoh. 5:28, 29) Kodi Yesu anatanthauza ciyani pamenepa?

14 Kumbuyoku, tinali kukhulupilila kuti mawu a Yesu amenewa aonetsa zimene oukitsidwa adzacite pambuyo pa ciukitso. Kutanthauza kuti pambuyo pa kuukitsidwa kwawo, ena adzacita zabwino, pamene ena adzacita zoipa. Komabe, onani kuti Yesu sanakambe kuti anthu amene adzatuluka m’manda acikumbutso adzacita zabwino kapena adzacita zoipa. Iye anagwilitsa nchito mawu oonetsa kuti zinacitika kale. Anafotokoza za anthu amene “anali kucita zabwino,” komanso amene “anali kucita zoipa.” Izi zionetsa kuti zimene anacitazo, anazicita asanafe. Zimenezi n’zomveka cifukwa m’dziko latsopano, palibe aliyense amene adzaloledwa kucita zoipa. N’kutheka kuti osalungama anacita zoipazo asanafe. Ndiye kodi mawu a Yesu akuti “adzauka kuti alandile moyo,” komanso akuti “adzauka kuti aweluzidwe” atanthauza ciyani?

15. Ndani “adzauka kuti alandile moyo”? Nanga n’cifukwa ciyani?

15 Anthu olungama amene anacita zabwino asanafe, “adzauka kuti alandile moyo” cifukwa maina awo adzakhala alimo m’buku la moyo. Izi zitanthauza kuti ciukitso ca anthu “amene anali kucita zabwino” cofotokozedwa pa Yohane 5:29, n’cofanana na ciukitso ca anthu “olungama” ochulidwa pa Machitidwe 24:15. Kamvedwe kameneka n’kogwilizana na mawu a pa Aroma 6:7, amene amati: “Munthu amene wafa wamasuka ku uchimo wake.” Conco, anthu olungama amenewa akafa, Yehova amafafaniza macimo awo onse. M’malo mwake, amasunga mbili yabwino ya kukhulupilika kwawo. (Aheb. 6:10) Ngakhale n’telo, olungama oukitsidwa amenewo adzafunika kukhalabe okhulupilika kuti maina awo asadzafutidwe m’buku la moyo.

16. Kodi mawu akuti “adzauka kuti aweluzidwe” atanthauza ciyani?

16 Nanga bwanji za aja amene anacita zoipa asanafe? Olo kuti nawonso macimo awo anafafanizidwa atafa, iwo sanakhalepo na mbili yabwino yokhala okhulupilika kwa Mulungu. Maina awo mulibe m’buku la moyo. Conco, ciukitso ca “amene anali kucita zoipa” n’cofanana na ciukitso ca “osalungama” ochulidwa pa Machitidwe 24:15. Iwo “adzauka kuti aweluzidwe.” * Osalungama adzaweluzidwa m’lingalilo lakuti Yesu adzaunika zocita zawo. (Luka 22:30) Zidzatenga nthawi kuti zidziŵike bwino ngati ciweluzo cawo n’cakuti maina awo ni oyenelela kulembedwa m’buku la moyo. Anthu osalungama amenewa akadzasiya njila zawo zoipa na kudzipatulila kwa Yehova, m’pamene maina awo adzalembedwe m’buku la moyo.

17-18. Kodi onse amene adzaukitsidwa pano padziko lapansi adzafunikila kudzacita ciyani? Kodi mawu akuti “nchito” pa Chivumbulutso 20:12, 13 atanthauza ciyani?

17 Anthu amene adzaukitsidwewo, olungama kapena osalungama, onse adzafunika kutsatila malamulo a m’mipukutu yatsopano imene idzatsegulidwa mu ulamulilo wa zaka 1,000. Mtumwi Yohane anafotokoza zimene anaona m’masomphenya. Anati: “Ndinaona akufa, olemekezeka ndi onyozeka, ataimilila pamaso pa mpando wacifumuwo, ndipo mipukutu inafunyululidwa. Koma mpukutu wina unafunyululidwa, ndiwo mpukutu wa moyo. Ndipo akufa anaweluzidwa malinga ndi zolembedwa m’mipukutuyo, mogwilizana ndi nchito zawo.”—Chiv. 20:12, 13.

18 Kodi oukitsidwa adzaweluzidwa malinga na “nchito” zawo ziti? Kodi ni nchito zimene anacita asanafe? Ayi. Kumbukilani kuti macimo awo anafafanizidwa pamene iwo anafa. Conco, “nchito zawo” si zija zimene anali kucita asanafe ayi. M’malo mwake, zitanthauza zocita zawo pa zimene adzaphunzitsidwa m’dziko latsopano. Ngakhale amuna okhulupilika monga Nowa, Samueli, Davide, na Danieli, adzafunika kuphunzila za Yesu Khristu, komanso kukhulupilila nsembe ya dipo lake. Ngati zili telo, kuli bwanji osalungama!

19. Kodi anthu amene adzakana mwayi wapadela umenewo zidzawathela bwanji?

19 Kodi anthu amene adzakana mwayi wapadela umenewo zidzawathela bwanji? Chivumbulutso 20:15 imatiuza kuti: “Aliyense amene sanapezeke atalembedwa m’buku la moyo anaponyedwa m’nyanja yamoto.” Inde, iwo adzawonongedwa kothelatu moti sadzakhalakonso. Conco, m’pofunika kwambili kuonetsetsa kuti dzina lathu lalembedwa m’buku la moyo, na kukhalabe mmenemo.

M’bale akugwila nawo nchito yaikulu yophunzitsa anthu, imene idzacitika mu Ulamulilo wa Zaka 1,000 (Onani ndime 20)

20. Ni nchito yokondweletsa iti imene idzacitike mu Ulamulilo wa Zaka Cikwi? (Onani cithunzi pacikuto.)

20 Ndithudi, nthawi ya Ulamulilo wa Zaka Cikwi idzakhala yokondweletsa ngako! Idzaphatikizapo pulogilamu yaikulu yophunzitsa anthu imene sinacitikepo pano padziko lapansi. Koma idzakhalanso nthawi imene olungama komanso osalungama adzaunikidwa bwino-bwino makhalidwe awo. (Yes. 26:9; Mac. 17:31) Kodi pulogilamu yophunzitsa imeneyi idzacitika motani? Nkhani yotsatila, idzatithandiza kudziŵa mmene idzacitikile, komanso kuyamikila makonzedwe abwino amenewa.

NYIMBO 147 Lonjezo la Moyo Wamuyaya

^ Nkhani ino, ifotokoza kusintha kwa kamvedwe kathu pa mawu a Yesu a pa Yohane 5:28, 29 akuti anthu “adzauka kuti alandile moyo,” komanso akuti “adzauka kuti aweluzidwe.” Tikambilane zimene ciukitso ca magulu aŵili amenewa cimatanthauza, komanso anthu amene ali m’magulu amenewa.

^ Bukuli linayamba kulembedwa “kucokela pa kukhazikitsidwa kwa dziko.” Mawu akuti dziko pa lembali, akutanthauza anthu amene ali na mwayi woomboledwa ku uchimo. (Mat. 25:34; Chiv. 17:8) Mwacidziŵikile, munthu wolungama Abele, ndiye woyamba kulembedwa dzina m’buku la moyo limeneli.

^ Kumbuyoko, zofalitsa zathu zinali kufotokoza kuti mawu akuti ‘kuweluza’ pa lembali atanthauza ciweluzo copeleka cilango. N’zoona kuti mawu amenewa angatanthauze zimenezi. Koma pa lembali, zioneka kuti Yesu anagwilitsa nchito mawu amenewa akuti ‘kuweluza’ potanthauza kuunika munthu na kumuyang’anila, kapena kuti “kusanthula khalidwe lake,” malinga na dikishonale ina ya Cigiriki.