NKHANI YOPHUNZILA 40
‘Kuthandiza Anthu Ambili Kukhala Olungama’
“Amene akuthandiza anthu ambili kukhala olungama adzawala ngati nyenyezi mpaka kalekale, inde, kwamuyaya.”—DAN. 12:3.
NYIMBO 151 Adzaitana
ZIMENE TIKAMBILANE *
1. Ni zocitika zokondweletsa ziti zimene tikuyembekezela mu Ulamulilo wa Zaka Cikwi?
IDZAKHALA nthawi yokondweletsa ngako anthu akadzayamba kuukitsidwa pano padziko lapansi mu Ulamulilo wa Khristu wa Zaka 1,000. Onse amene okondedwa awo anamwalila amalakalaka kudzawaonanso. Nayenso Yehova amalakalaka kudzawaonanso. (Yobu 14:15) Tangoganizani cimwemwe cimene aliyense padziko lapansi adzakhala naco podzawaonanso okondedwa ake. Monga tinaphunzilila m’nkhani yapita, “olungama,” amene maina awo analembedwa m’buku la moyo, “adzauka kuti alandile moyo.” (Mac. 24:15; Yoh. 5:29) N’kutheka kuti ambili mwa okondedwa athu amene anamwalila, adzakhala pakati pa anthu oukitsidwa koyambilila pano padziko lapansi. * Kuwonjezela apo, “osalungama,” amene analibe mwayi wodziŵa Yehova kapena kum’tumikila mokhulupilika asanamwalile, “adzauka kuti aweluzidwe.”
2-3. (a) Malinga na Yesaya 11:9, 10, ni pulogilamu yophunzitsa yotani imene idzacitike, yoposa iliyonse m’mbili ya anthu? (b) Kodi tikambilane ciyani m’nkhani ino?
2 Anthu onse oukitsidwa adzafunika kuphunzitsidwa. (Yes. 26:9; 61:11) Motelo, padzakhazikitsidwa pulogilamu yaikulu yophunzitsa imene sinacitikepo m’mbili yonse ya anthu. (Ŵelengani Yesaya 11:9, 10.) N’cifukwa ciyani? Cifukwa osalungama amene adzaukitsidwa adzafunika kuphunzila za Yesu Khristu, makonzedwa a Ufumu, dipo, komanso kufunika kwa dzina lakuti Yehova ndiponso cifukwa cake iye yekha ndiye woyenela kulamulila. Ngakhalenso olungama adzafunika kudziŵa zimene Yehova wakhala akuphunzitsa anthu ake ponena za colinga cake ca dziko lapansi. Ena mwa okhulupilika amenewa anamwalila mawu a Yehova asanathe kulembedwa m’Baibo. Onse, olungama na osalungama, adzakhala na zambili zofunika kuphunzila.
3 M’nkhani ino, tikambilane mafunso otsatilawa: Kodi pulogilamu yaikulu yophunzitsa imeneyi idzacitika motani? Nanga idzapangitsa bwanji kuti maina ena akalembedwe mwacikhalile m’buku la moyo pamene ena sadzatelo? Mayankho a mafunso amenewa ni ofunika kwambili kwa ife masiku ano. Monga tionele, maulosi ena ocititsa cidwi a m’buku la Danieli na Chivumbulutso, atithandiza kusintha kamvedwe kathu pa zimene zidzacitike akufa akadzaukitsidwa. Coyamba, tiyeni tikambilane zocitika zokondweletsa zofotokozedwa mu ulosi wa pa Danieli 12:1, 2.
“AMENE AGONA MUNTHAKA ADZAUKA”
4-5. Kodi Danieli 12:1 imati ciyani ponena za nthawi ya mapeto?
4 Ŵelengani Danieli 12:1. Buku la Danieli limafotokoza ndondomeko ya zocitika zokondweletsa zimene zidzacitika m’nthawi yamapeto. Mwacitsanzo, Danieli 12:1 imakamba kuti Mikayeli, amene ni Yesu Khristu, “waimilila [kutanthauza kuti ali ciimilile] kuti athandize anthu a [Mulungu].” Kuimilila kophiphilitsa kumeneku kunayamba mu 1914 pamene Yesu anaikidwa kukhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu kumwamba.
5 Komabe, Danieli anauzidwanso kuti Yesu “adzaimilila” pa “nthawi ya masautso imene sinakhalepo kuyambila pamene mtundu woyambilila wa anthu unakhalapo kufikila nthawi imeneyo.” “Nthawi ya masautso” imeneyi ni “cisautso cacikulu” cochulidwa pa Mateyu 24:21. Yesu adzaimilila, kapena kuti adzacitapo kanthu kuti ateteze anthu a Mulungu kumapeto kwa nthawi ya masautso imeneyi, kutanthauza pa Aramagedo. Buku la Chivumbulutso limachula anthu a Mulungu amenewa kuti a “khamu lalikulu amene atuluka m’cisautso cacikulu.”—Chiv. 7:9, 14.
6. Kodi cidzacitike n’ciyani a khamu lalikulu akadzapulumuka cisautso cacikulu? Fotokozani. (Ponena za ciukitso ca odzakhala padziko lapansi, onaninso nkhani yakuti “Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga” m’magazini ino.)
6 Ŵelengani Danieli 12:2. Kodi cidzacitike n’ciyani a khamu lalikulu akadzapulumuka nthawi ya masautso imeneyo? Ulosi umenewu sukamba za ciukitso cophiphilitsa, kapena kuti kuuka kwauzimu kwa atumiki a Mulungu kumene kunacitika kumayambililo kwa masiku otsiliza, monga tinali kudziŵila kale. * M’malo mwake, mawu a pa lembali amakamba za kuukitsidwa kwa akufa kumene kudzacitike m’dziko latsopano limene likubwelalo. N’cifukwa ciyani tikutelo? Mawu akuti “nthaka” pa Danieli 12:2 ni ofanana na mawu ochulidwa pa Yobu 17:16 akuti “fumbi.” Mawu onsewa amatanthauza “Manda.” Pa cifukwa cimeneci, Danieli 12:2 imakamba za ciukitso ceniceni cimene cidzacitika pambuyo pakuti masiku otsiliza atha, komanso pambuyo pa nkhondo ya Aramagedo.
7. (a) Kodi anthu ena adzauka kuti ‘akalandile moyo wosatha’ mlingalilo lotani? (b) N’cifukwa ciyani kumeneku kudzakhala “kuuka kwabwino kwambili”?
7 Koma kodi Danieli 12:2 imatanthauza ciyani ponena kuti ena adzauka kuti ‘akalandile moyo wosatha’? Imatanthauza kuti anthu amene adzaukitsidwa kenako n’kupitiliza kuphunzila za Yehova na Yesu na kuwadziŵa bwino, komanso kuwamvela mu ulamulilo wa zaka 1,000, pamapeto pake adzalandila moyo wosatha. (Yoh. 17:3) Uku kudzakhala “kuuka kwabwino kwambili” kuposa kumene kunacitika m’nthawi zakale. (Aheb. 11:35) N’cifukwa ciyani? Cifukwa anthu opanda ungwilo amenewo anamwalilanso.
8. N’ciyani cikapangitse kuti ena akadzaukitsidwa ‘akalandile citonzo na kudedwa mpaka kale-kale’?
8 Koma si onse oukitsidwa amene adzalabadila zimene Yehova adzawaphunzitsa. Ulosi wa Danieli unakamba kuti ena adzauka kuti ‘akalandile citonzo ndipo adzadedwa mpaka kale-kale.’ Cifukwa cakuti adzaonetsa mzimu wacipanduko, maina awo sadzalembedwa m’buku la moyo, ndipo sadzalandila moyo wosatha. M’malo mwake, ‘adzadedwa mpaka kale-kale,’ kutanthauza kuti adzawonongedwa. Conco, Danieli 12:2 imakamba zimene pamapeto pake zidzacitika kwa onse oukitsidwa, malinga na zimene adzacita pambuyo pa ciukitso cawo. * (Chiv. 20:12) Ena adzalandila moyo wosatha, koma ena adzawonongedwa.
‘KUTHANDIZA ANTHU AMBILI KUKHALA OLUNGAMA’
9-10. N’ciyani cina cidzacitike cisautso cacikulu cikadzatha? Nanga ndani “adzawala ngati kuwala kwa kuthambo”?
9 Ŵelengani Danieli 12:3. N’ciyani cina cidzacitika “nthawi ya masautso” ikadzatha? Kuwonjezela pa zimene Danieli 12:2 imakamba, vesi 3 imafotokoza zina zimene zidzacitika pambuyo pa cisautso cacikulu.
10 Ndani “adzawala ngati kuwala kwa kuthambo”? Timapeza yankho m’mawu a Yesu a pa Mateyu 13:43 akuti: “Pa nthawi imeneyo olungama adzawala kwambili ngati dzuŵa mu Ufumu wa Atate wawo.” Ponena mawu amenewa, Yesu anali kukamba za “ana a Ufumu,” abale ake odzozedwa amene adzatumikila naye limodzi mu Ufumu wakumwamba. (Mat. 13:38) Conco, Danieli 12:3 iyenela kuti imakamba za odzozedwa, komanso nchito imene adzagwila mu Ulamulilo wa Zaka Cikwi.
11-12. Ni nchito iti imene a 144,000 adzagwila mu ulamulilo wa zaka 1,000?
11 Kodi odzozedwa adzathandiza bwanji “anthu ambili kukhala olungama”? Odzozedwa adzaseŵenzela pamodzi na Yesu Khristu pa nchito yophunzitsa imene idzacitika pano padziko lapansi mu ulamulilo wa za 1,000. A 144,000 adzatumikila monga mafumu komanso ansembe. (Chiv. 1:6; 5:10; 20:6) Conco, iwo adzathandiza ‘pocilitsa mitundu ya anthu,’ ndipo pang’ono-m’pang’ono adzathandiza anthu kubwelelanso ku ungwilo. (Chiv. 22:1, 2; Ezek. 47:12) Cidzakhala cinthu cokondweletsa cotani nanga kwa odzozedwa!
12 Kodi ena mwa “ambili” amene adzakhala olungama ndani? Amenewa aphatikizapo oukitsidwa, komanso opulumuka Aramagedo pamodzi na ana amene angadzabadwe m’dziko latsopano. Podzafika kumapeto kwa zaka 1,000, aliyense padziko lapansi adzakhala wangwilo. Ndiye kodi ni liti pamene maina awo adzalembedwa mwacikhalile na colembela ca inki osati na pensulo m’buku la moyo?
MAYESO OTHELA
13-14. Kodi anthu onse angwilo padziko lapansi adzafunika kuonetsa ciyani asanalandile moyo wosatha?
13 Tiyenela kukumbukila kuti kukhala wangwilo pakokha sikutanthauza kuti basi munthu adzalandila moyo wosatha. Ganizilani za Adamu na Hava. Iwo anali angwilo. Koma anafunika kum’khutilitsa Yehova Mulungu kuti ni omvela asanawapatse moyo wosatha. Ndipo zacisoni n’zakuti iwo analephela kumumvela.—Aroma 5:12.
14 Podzafika kumapeto kwa zaka 1,000, kodi anthu padziko lapansi adzakhala otani? Panthawiyo, anthu onse padziko lapansi adzakhala atafika pa ungwilo. Kodi anthu onse angwilo amenewo adzamvela Yehova na mtima wawo wonse kwamuyaya? Kapena kodi ena adzacita monga Adamu na Hava, amene anali angwilo koma anakhala osakhulupilika? Mafunso amenewa ayenela kuyankhidwa. Koma motani?
15-16. (a) Ni liti pamene anthu onse adzapatsidwa mwayi woonetsa kukhulupilika kwawo kwa Yehova? (b) Kodi padzakhala zotulukapo zotani pa mayeso othela amenewo?
15 Satana adzamangidwa kwa zaka 1,000. Panthawiyo, iye sadzakwanitsa kusoceletsa aliyense. Koma zikadzatha zaka cikwi zimenezo, Satanayo adzamasulidwa m’ndende yake. Iye akadzamasulidwa, adzayesa kusoceletsa anthu angwilo. Panthawi ya mayeso amenewo, anthu onse angwilo padziko lapansi adzakhala na mwayi woonetsa poyela kuti amalemekeza dzina la Mulungu na kumvela ulamulilo wake. (Chiv. 20:7-10) Mmene aliyense adzacitila pa mayeso amenewo, n’zimene zidzapangitsa kuti dzina lake lilembedwe mwacikhalile m’buku lamoyo kapena kucotsedwamo.
16 Koma anthu ena adzakana ulamulilo wa Yehova, mofanana na Adamu na Hava. Kodi n’ciyani cidzawacitikila anthu amenewo? Chivumbulutso 20:15 imati: “Aliyense amene sanapezeke atalembedwa m’buku la moyo anaponyedwa m’nyanja yamoto.” Inde, anthu opanduka amenewo adzawonongedwa moti sadzakhalakonso. Koma anthu ambili angwilo adzapambana mayeso othela amenewo. Ndipo maina awo adzalembedwa mwacikhalile m’buku la moyo.
MU “NTHAWI YAMAPETO”
17. Kodi Danieli anauzidwa kuti n’ciyani cidzacitika m’nthawi yathu ino? (Danieli 12:4, 8-10)
17 N’zosangalatsa cotani nanga kuganizila zocitika zakutsogolo zimenezi! Komabe, Danieli analandilanso uthenga wofunika kwambili wocokela kwa mngelo, wokamba za “nthawi yamapeto.” (Ŵelengani Danieli 12:4, 8-10; 2 Tim. 3:1-5) Mngeloyo anauza Danieli kuti: “[Anthu] adzadziŵa zinthu zambili zoona.” Inde, panthawi imeneyo anthu a Mulungu adzawamvetsa bwino kwambili mawu a ulosi amenewo. Mngeloyo ananenanso kuti m’nthawi ino ya mapeto, “anthu oipa adzacita zinthu zoipa ndipo palibe munthu woipa aliyense amene adzamvetsetse mawu amenewa.”
18. N’ciyani cidzacitikila anthu oipa posacedwa?
18 Masiku ano, zingaoneke kuti anthu oipa amangocita zinthu zoipa popanda kulangidwa. (Mal. 3:14, 15) Koma posacedwa, Yesu adzaweluza anthu onga mbuzi amenewa mwa kuwalekanitsa na anthu onga nkhosa. (Mat. 25:31-33) Anthu oipa amenewa sadzapulumuka cisautso cacikulu kapena kuukitsidwa kuti akhale m’dziko latsopano. Ndipo maina awo sadzalembedwa mu “buku la cikumbutso” lochulidwa pa Malaki 3:16.
19. Kodi ino ni nthawi yofunika kucita ciyani? Nanga n’cifukwa ciyani? (Malaki 3:16-18)
19 Ino ndiyo nthawi yoonetsa mwa zocita zathu kuti sitili pakati pa anthu oipa amenewo. (Ŵelengani Malaki 3:16-18.) Yehova akusonkhanitsa anthu amene amawaona kuti ni “cuma capadela,” kapena kuti anthu amtengo wapatali kwa iye. Kukamba zoona, timafuna titakhala mmodzi wa anthu amenewa.
20. Kodi Mulungu anam’lonjeza ciyani Danieli? Nanga n’cifukwa ciyani muyembekezela mwacidwi kukwanilitsidwa kwa lonjezo limenelo?
20 Ndithudi, tikukhala m’nthawi ya zocitika zocititsa cidwi. Koma posacedwa, kudzacitika zinthu zina zocititsa cidwi kuposa pamenepa. Mwacitsanzo, kuipa konse kudzatha posacedwa. Cotsatila, tidzaona kukwanilitsidwa kwa zimene Yehova analonjeza Danieli kuti: “Udzauka kuti ulandile gawo lako pa mapeto a masikuwo.” (Dan. 12:13) Kodi mumalakalaka kudzaona nthawi pamene Danieli pamodzi na okondedwa anu adzaukitsidwa? Ngati n’conco, citani zonse zotheka kuti mukhalebe wokhulupilika palipano. Mukatelo, mudzakhala otsimikiza kuti dzina lanu silidzacotsedwamo m’buku la moyo la Yehova.
NYIMBO 80 ‘Talaŵani, Muone Kuti Yehova ni Wabwino’
^ Nkhani ino ifotokoza kusintha kwa kamvedwe kathu ponena za nchito yaikulu yophunzitsa anthu yochulidwa pa Danieli 12:2, 3. Tikambilane kuti nchito imeneyi idzacitika liti, komanso amene akuloŵetsedwamo. Tionenso mmene nchito yophunzitsa imeneyo idzathandizila anthu padziko lapansi kukonzekela mayeso othela kumapeto kwa Ulamulilo wa Khristu wa Zaka Cikwi.
^ Mwina ciukitso cidzayamba na anthu amene anamwalila ali okhululupillika m’masiku otsiliza ano, kenako kutsatila mibadwo mibadwo kubwelela m’mbuyo. Ngati zidzakhaladi conco, ndiye kuti m’badwo uliwonse udzakhala na mwayi wolandila anthu oukitsidwa amene anali kuwadziŵa. Mulimonsemo, ponena za ciukitso ca anthu opita kumwamba, Malemba amakamba kuti “aliyense pamalo pake.” Conco, zioneka kuti naconso ciukitso ca anthu pano padziko lapansi cidzacitika mwadongosolo.—1 Akor. 14:33; 15:23.
^ Uku ni kusintha kwa kamvedwe kathu pa zimene zinafotokozedwa m’buku lakuti Samalani Ulosi wa Danieli!, caputala 17, komanso mu Nsanja ya Olonda ya July 1, 1987, mas. 21-25.
^ Komabe, mawu akuti “olungama” komanso “osalungama” opezeka pa Machitidwe 24:15, komanso mawu akuti “amene anali kucita zabwino” ndiponso akuti “amene anali kucita zoipa” a pa Yohane 5:29, kwenikweni amanena za nchito zimene oukitsidwawo anacita asanafe.