Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MBILI YANGA

Nakhala Nikusangalala Kuphunzila za Yehova na Kuphunzitsako Ena

Nakhala Nikusangalala Kuphunzila za Yehova na Kuphunzitsako Ena

PAMENE n’nali kukula m’tauni ya Easton, Pennsylvania, ku America, colinga canga cinali kupata maphunzilo a ku yunivesite, kuti nikakhale munthu wochuka. Kuphunzila n’nali kukukonda kwambili, ndipo n’nacita bwino m’masamu komanso sayansi. Mu 1956, gulu lomenyela ufulu wa anthu linanipatsa madola 25. Linacita zimenezo cifukwa n’napambana mayeso kuposa ophunzila ena akuda pa sukulupo. Pambuyo pake, zolinga zanga zinasintha. Cifukwa ciyani?

MMENE N’NAPHUNZILILA ZA YEHOVA

Kumayambililo kwa ma 1940, makolo anga anali kuphunzila Baibo na Mboni za Yehova. Phunzilo limenelo linaima. Koma amayi anapitiliza kulandila magazini a Nsanja ya Mlonda na Galamuka! Mu 1950, kunacitika msonkhano wamaiko mu mzinda wa New York City, ndipo banja lathu litaitanidwa, linapezekapo.

Posakhalitsa, M’bale Lawrence Jeffries anayamba kuticezela. Iye anayesetsa kunithandiza kuti niphunzile coonadi. Poyamba, sin’nagwilizane nazo zakuti Mboni za Yehova siziyenela kutengako mbali iliyonse m’zandale komanso kuloŵa usilikali. N’nauza m’baleyo kuti ngati aliyense mu America angakane kukhala msilikali, adani angabwele na kulanda dziko lonseli. Moleza mtima m’bale Jeffries ananifunsa kuti: “Anthu onse mu America akanakhala kuti anali kutumikila Yehova Mulungu, kodi uganiza iye akanacita ciyani adani akanati awaukila?” Zimene ananiyankha pa nkhaniyo komanso pa nkhani zina, zinanithandiza kuona kuti n’nali na maganizo olakwika. Izi zinakulitsa cidwi canga cofuna kuphunzila Baibo.

Pa tsiku la ubatizo wanga

N’nali kuthela maola ambili pa kuŵelenga magazini akale a Nsanja ya Mlonda na Galamuka! amene amayi anali kusunga m’cipinda capansi m’nyumba yathu. M’kupita kwa nthawi, n’nazindikila kuti zimene n’nali kuphunzila cinali coonadi. Conco, n’navomela kuti M’bale Jeffries aziniphunzitsa Baibo. Cina, n’nayamba kupezeka pa misonkhano nthawi zonse. Zimene n’nali kuphunzila zinanifika pa mtima, moti n’nakhala wofalitsa wa uthenga wabwino. N’nasintha zolinga zanga pamene n’namvetsetsa kuti “tsiku lalikulu la Yehova [linali] pafupi.” (Zef. 1:14) Apa, maganizo opita ku yunivesite anathelatu. M’malo mwake, n’nafuna kuthandiza anthu kuphunzila coonadi ca m’Baibo.

N’natsiliza maphunzilo anga a ku sekondale pa June 13, 1956, ndipo patapita masiku atatu, n’nabatizika pa msonkhano wadela. Pa nthawiyo, sin’nadziŵe kuti n’dzapeza madalitso ambili kucokela kwa Yehova cifukwa cosankha kugwilitsa nchito moyo wanga pa kuphunzila za iye na kuphunzitsako ena.

KUPHUNZILA ZA YEHOVA NA KUPHUNZITSAKO ENA MONGA MPAINIYA

Pambuyo pa miyezi 6 n’tabatizika, n’nayamba upainiya wa nthawi zonse. Mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa December 1956 munali nkhani yakuti “Kodi Mungakatumikile Kumalo Osoŵa?” N’naona kuti ine n’kanatha kucita zimenezo. N’nali kufuna kukathandiza kumalo kumene kunali alengezi ocepa a uthenga wabwino.—Mat. 24:14.

M’kupita kwa nthawi, n’nasamukila m’tauni ya Edgefield, ku South Carolina. Mpingo wa kumeneko unali cabe na ofalitsa anayi. Pamodzi na ine tinakwana asanu. Misonkhano tinali kucitila m’cipinda cocezela m’nyumba ya m’bale wina. N’nali kuthela maola 100 mwezi uliwonse mu ulaliki. Komanso n’nali wokangalika pa kutsogolela nchito yolalikila, ndiponso kukamba nkhani pa misonkhano. Cosangalatsa n’cakuti pamene n’nali kucita zimenezi, n’nali kuphunzila zambili za Yehova.

Mayi wina amene n’nali kuphunzila naye Baibo, anali na saini kapena kuti mochale m’tauni ya Johnston, pa mtundu wa makilomita angapo kucoka kumene n’nali kukhala. Iye ananilemba nchito ya maola ocepa, ndipo anatipatsa kanyumba kuti tizicitilamo misonkhano.

M’bale Jolly Jeffries, mwana wa m’bale amene ananiphunzitsa coonadi, anasamuka kucoka ku Brooklyn, New York kubwela kumene ine n’nali kuti tizitumikila pamodzi monga apainiya. Tinali kukhala m’kalavani imene m’bale wina anaticititsa lendi.

Anthu anali kulandila malipilo ocepa ku South Carolina. Munthu akagwila nchito, pa tsiku anali kulandila madola aŵili kapena atatu. Tsiku lina, n’napita ku shopu kukagula cakudya na ndalama yothela imene n’nali nayo. Pamene n’natuluka m’shopu, munthu wina anabwela na kunifunsa kuti: “Kodi ukufunako nchito? Nizikulandilitsa dola imodzi pa ola.” Ananipatsa nchito ya masiku atatu yoyeletsa pamalo a nchito yomanga. Zinali zoonekelatu kuti Yehova anali kunithandiza kuti nipitilize kutumikila ku Edgefield, ndipo n’natelo. Koma mu 1958, n’napita ku msonkhano wamaiko umene unacitikila ku New York City.

Pa tsiku la ukwati wathu

Pa tsiku laciŵili la msonkhanowo, cinacake capadela cinacitika. N’nakumana na mlongo Ruby Wadlington, amene anali mpainiya wa nthawi zonse m’tauni ya Gallatin, ku Tennessee. Popeza tonse tinali na colinga codzakhala amishonale, tinapezeka pa miting’i ya ofunsila utumiki wa umishonale pa msonkhanowo. Pambuyo pake tinayamba kulembelana makalata. Kenako, n’napemphedwa kuti nikakambe nkhani ya onse ku Gallatin. N’napezelapo mwayi womufunsila ukwati. N’nasamukila mu mpingo umene Ruby anali kusonkhana, ndipo tinakwatilana mu 1959.

KUPHUNZILA ZA YEHOVA NA KUPHUNZITSA ENA MU MPINGO

Pamene n’nali na zaka 23, n’nasankhidwa kukhala mtumiki wa mpingo ku Gallatin (umene tsopano timati mgwilizanitsi wa bungwe la akulu.) Mpingo wathu unali woyamba kucezeledwa na woyang’anila dela, m’bale Charles Thompson. M’baleyu anali ciyambakale. Koma anafunsila kwa ine pa zimene abale anali kusoŵekela, na zimene oyang’anila madela anathandizila pa zosoŵa zawozo. N’naphunzila kwa iye kuti coyamba ni bwino kufunsa mafunso na kudziŵa nkhani yonse tisanapange cigamulo.

Mu May 1964, n’naitanidwa ku Sukulu ya Utumiki wa Ufumu ya mwezi umodzi, imene inacitikila ku South Lansing, mu mzinda wa New York. Alangizi a sukuluyo ananithandiza kukulitsa cifuno canga cophunzila zambili, komanso kuti nifike pokhwima mwauzimu.

KUPHUNZILA ZA YEHOVA NA KUPHUNZITSA ENA M’NCHITO YADELA KOMANSO YACIGAWO

Mu 1965, ine na Ruby tinapemphedwa kuyamba nchito ya m’dela. Tinapatsidwa dela lalikulu, kucokela ku Knoxville, ku Tennessee, mpaka kufika ku tauni ya Richmond, ku Virginia. Delalo linaphatikizapo mipingo ya m’tauni ya North Carolina, Kentucky, komanso West Virginia. N’nali kutumikila cabe mipingo ya anthu akuda, cifukwa pa nthawiyo ku America anali kusankhana mitundu. Conco, anthu akuda na azungu sanali kucitila zinthu pamodzi. Abale ambili anali osauka, ndipo tinaphunzila kugaŵana nawo zocepa zimene tinali nazo. Woyang’anila dela wina amene anali ciyambakale, anaphunzitsa mfundo yakuti: “Uzicita zinthu ngati m’bale. Ukamacezela mpingo, usamakhale ngati bwana. N’cosavuta kuwathandiza ngati amakuona kuti ndiwe m’bale wawo.”

Pamene tinali kuyendela mpingo wina waung’ono, mkazi wanga anayamba kuphunzila Baibo na mayi wina amene anali na mwana wamkazi wa caka cimodzi. Cifukwa cakuti mu mpingomo munalibe munthu amene akanatsogoza phunzilolo, mkazi wanga anapitiliza kutsogoza kupitila m’kalata. Titacezela mpingowo ulendo wotsatila, mayiyo anapezeka ku misonkhano yonse. Pamene alongo aŵili amene anali apainiya apadela anabwela mu mpingowo, anapitiliza kuphunzila Baibo na mayiyo. Ndipo posapita nthawi anabatizika. Mu 1995 patapita zaka 30, mlongo wina wacitsikana anadzidziŵitsa kwa mkazi wanga Ruby pa Beteli ya Patterson. Mlongoyo anali mwana wa mayi uja amene mkazi wanga anali kuphunzila naye Baibo. Mlongo ameneyo na mwamuna wake anali ophunzila m’sukulu ya Giliyadi ya kalasi nambala 100.

Dela lathu laciŵili linali mu mzinda wa Florida. Pa nthawi imeneyo, tinafunikila motoka. Ndipo tinagula motoka pa mtengo wabwino. Komabe, mu mlungu woyamba citsulo cina mu injini ya motokayo cinawonongeka. Tilinabe ndalama iliyonse yoikonzetsela. N’natumila m’bale wina amene n’naganizila kuti angatithandize. M’baleyo anapempha wanchito wake kuti atikonzele motokayo, ndipo sanatilipilitse ndalama iliyonse. M’baleyo anati, “Musavutike, nangokuthandizani cabe.” Ndipo anacita kutipatsa mphatso ya ndalama. Cimeneco cinali citsanzo cabwino coonetsa mmene Yehova amasamalila atumiki ake. Izi zinatikumbutsa kuti tiyenela kukhala opatsa.

Nthawi zonse tikamayendela mipingo, tinali kukhala m’nyumba za abale. Zotuluka zake, tinakhala na mabwenzi abwino kwambili. Tsiku lina, n’nali kulemba lipoti lokhudza mpingo pogwilitsa nchito makina otaipila. Cifukwa cakuti sin’natsilize kulemba, n’nangoisiya pa makina otaipila. N’tabwelako m’madzulo, n’napeza kuti mwana wa zaka zitatu wadiniza-diniza pa makina otaipila na kuwononga lipoti langa. Moseka naye, n’nali kum’kumbutsa zimene anacitazo kwa zaka zambili.

Mu 1971, n’nalandila kalata yoniika kukhala woyang’anila cigawo ku New York City. Tinadabwa kwambili! Pamene tinali kupita kumeneko, n’nali na zaka 34. Titafika, abale anatilandila na manja aŵili, popeza n’nali woyamba kwa iwo kukhala woyang’anila cigawo wacikuda.

Monga woyang’anila cigawo, n’nali na mwayi wophunzitsa za Yehova mlungu uliwonse, komanso pa msonkhano wadela. Oyang’anila madela ambili anali aciyambakale kuposa ine. Mmodzi wa iwo ndiye anakamba nkhani pa ubatizo wanga. M’bale wina dzina lake Theodore Jaracz, pambuyo pake anadzakhala ciwalo ca Bungwe Lolamulila. Panalinso abale ambili aciyambakale amene anali kutumikila pa Beteli ku Brooklyn. N’nayamikila kwambili kuti oyang’anila madela komanso a m’banja la Beteli, ananithandiza kukhala womasuka. N’nadzionela nekha kuti abalewo anali abusa acikondi amene anali kudalila Mawu a Mulungu, komanso amene anali kuthandiza gulu la Mulungu mokhulupilika. Cifukwa ca kudzicepetsa kwawo, cinakhala cosavuta kwa ine kutumikila monga woyang’anila wacigawo.

KUBWELELANSO M’NCHITO YADELA

Mu 1974, Bungwe Lolamulila linaika oyang’anila madela kukhala oyang’anila cigawo. Conco, n’nabwelelanso m’nchito yadela, koma n’nakatumikila ku South Carolina. Ndipo panthawiyo, abale acikuda na azungu anali atayamba kucitila zinthu pamodzi, ndipo zimenezo zinali zokondweletsa kwa tonsefe.

Cakumapeto kwa 1976, n’natumizidwa ku dela lina ku Georgia, pakati pa Atlanta na Columbus. Nikumbukila bwino kuti n’nakamba nkhani ya malilo ya ana asanu acikuda, amene anafela m’nyumba pambuyo pakuti anthu ena aitentha na moto. Ndipo amayi a anawo anali m’cipatala cifukwa ca kupsa na motowo. Abale na alongo ambili—acikuda komanso azungu, nthawi zonse anali kupita ku cipatala kukawalimbikitsa makolowo. N’naona kuti cikondi cimene abale anali naco cinali capadela. Cikondi cotelo cimathandiza atumiki a Mulungu kupilila mikhalidwe yovuta.

KUPHUNZILA ZA YEHOVA PA BETELI NA KUPHUNZITSAKO ENA

Mu 1977, tinapemphedwa kupita ku Beteli ya Brooklyn kukathandiza pa nchito inayake. Pamene nchitoyo inali kutha, abale aŵili a m’Bungwe Lolamulila ananiitana, na kutipempha ngati tingakonde kutumikila mwacikhalile pa Beteli. Tinavomela utumiki umenewo.

Kwa zaka 24, n’natumikila ku Service Department kumene abale nthawi zonse anali kukambilana mothetsela nkhani zovuta za m’mipingo. Kwa zaka zambili, Bungwe Lolamulila lakhala likupeleka citsogozo mogwilizana na mfundo za m’Baibo. Mfundo zimenezi zimathandiza a ku Service Department kupeza mayankho a mafunso. Zimagwilitsidwanso nchito pophunzitsa oyang’anila madela, akulu, na apainiya. Mfundo zimene amagwilitsa nchito pophunzitsa, zathandiza anthu ambili kukula kuuzimu. Zotulukapo zake n’zakuti gulu la Yehova lakhala lolimba.

Kuyambila mu 1995 mpaka 2018, n’nacezela maofesi a nthambi osiyana-siyana monga woimilako likulu, amene kale anali kuchedwa woyendela nthambi. N’nali kukumana na abale a M’makomiti a Nthambi, atumiki a pa Beteli, ndiponso amishonale kuti niwalimbikitse. Komanso kuwathandiza pa zovuta zimene anali kukumana nazo. Panthawi imodzimodzi, ine na mkazi wanga Ruby tinali kulimbikitsidwa pakumva zocitika zokondweletsa zimene iwo anali kutisimbila. Mwacitsanzo, pamene tinacezela nthambi ya ku Rwanda mu 2000, tinalimbikitsidwa titamva mmene zinthu zinalili kwa abale komanso a m’banja la Beteli panthawi ya nkhondo ya pa ciweniweni mu 1994. Ambili anataikilidwa okondedwa awo. Ngakhale kuti anali kukumana na mavuto onsewo, abale athu amenewo sanataye cikhulupililo, ciyembekezo, na cimwemwe cawo.

Titakwanitsa zaka 50 mu ukwati

Tsopano, tili na zaka za m’ma 80. Kwa zaka 20 zapitazo, nakhala nikumikila m’Komiti ya Nthambi ku America. Sin’nalandilepo maphunzilo aliwonse a ku yunivesite. Koma nalandila maphunzilo apamwamba kwambili ocokela kwa Yehova na gulu lake. Izi zanikonzeletsa kuphunzitsa ena coonadi ca m’Baibo cimene cingawapindulile kwamuyaya. (2 Akor. 3:5; 2 Tim. 2:2) Naona mmene uthenga wa m’Baibo wathandizila anthu kusintha umoyo wawo, na kukhala pa ubale wabwino na Mlengi wawo. (Yak. 4:8) Ine na mkazi wanga Ruby, timayesetsa mmene tingathele kulimbikitsa ena kuti aziyamikila mwayi wophunzila za Yehova, na kuphunzitsako ena coonadi. Uwu ni mwayi waukulu kopambana umene mtumiki wa Yehova angakhale nawo.