Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 38

Onetsani Kuti Ndinu Wodalilika

Onetsani Kuti Ndinu Wodalilika

“Wokhulupilika amabisa nkhani.”—MIY. 11:13.

NYIMBO 101 Tisunge Umodzi Wathu

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Kodi munthu wodalilika tingam’dziŵe bwanji?

 MUNTHU wodalilika amayesetsa kusunga malonjezo ake, ndipo amakamba zoona. (Sal. 15:4) Munthu woteloyo anthu amam’dalila. Umu ni mmene timafunila kuti abale na alongo athu azitidziŵila. Kodi tingacite ciyani kuti iwo azitidalila?

2. Kodi tingaonetse bwanji kuti ndife odalilika?

2 Sitingaumilize anthu ena kuti azitidalila. Anthu amatidalila cifukwa ca zocita zathu. Ena amati kudalilika kuli ngati ndalama. Kuipeza n’kovuta, koma kuiwononga n’kosavuta. Kukamba zoona, Yehova amatidalila. Nafenso tingam’dalile nthawi zonse cifukwa “nchito zake zonse ndi zodalilika.” (Sal. 33:4) Ndipo amafuna kuti tizitengela citsanzo cake. (Aef. 5:1) Tiyeni tione zitsanzo za atumiki a Yehova amene anatengela citsanzo cake, na kuonetsa kuti iwo ni odalilika. Tionenso makhalidwe asanu amene adzatithandiza kukhala odalilika.

PHUNZILANI KWA ATUMIKI A YEHOVA ODALILIKA

3-4. Kodi mneneli Danieli anaonetsa bwanji kuti ni wodalilika? Nanga zimenezi ziyenela kutipangitsa kudzifunsa ciyani?

3 Mneneli Danieli ni citsanzo cabwino ngako pa nkhani ya kudalilika. Iye anatengedwa ku ukapolo na Ababulo. Koma posakhalitsa, anthu anam’dziŵa kuti anali wodalilika. Iye atamasulila maloto a Mfumu Nebukadinezara ya Babulo mothandizidwa na Yehova, anthu anayamba kum’dalila kwambili Danieli. Pa nthawi ina, Danieli anauza mfumu Nebukadinezara kuti Yehova sanali kukondwela na zocita za zake. Uwu sunali uthenga wokondweletsa kwa mfumu. Ndipo kuuza mfumu zimenezi kunafuna kulimba mtima, cifukwa Nebukadinezara anali na mtima wapacala. (Dan. 2:12; 4:20-22, 25) Koma patapita zaka, Danieli anaonetsanso kuti ni wodalilika, pamene anamasulila molondola uthenga wodabwitsa umene unaonekela pa cipupa m’nyumba yacifumu ku Babulo. (Dan. 5:5, 25-29) Patapita nthawi, Dariyo Mmedi na nduna zake nawonso anazindikila kuti Danieli anali na “luso lodabwitsa.” Iwo anapeza kuti iye “anali wokhulupilika. . . . Sanali kunyalanyaza kanthu kapena kucita zacinyengo zilizonse.” (Dan. 6:3, 4) Inde, ngakhale olamulila acikunja amenewa anazindikila kuti mlambili wa Yehova ameneyu, anali munthu woyenela kum’dalila.

4 Poganizila citsanzo ca Danieli, ni bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi anthu amene si Mboni amanidziŵa kuti ndine munthu wotani? Kodi nimadziŵika kuti nimakwanilitsa maundindo anga komanso malonjezo? Ndipo kodi kuti ndine munthu amene anthu angam’dalile?’ N’cifukwa ciyani kudzifunsa mafunsowa n’kofunika? Cifukwa tikakhala odalilika, timabweletsa citamando kwa Yehova.

Nehemiya anasankha amuna odalilika kuti agwile nchito zofunika kwambili (Onani ndime 5)

5. N’ciyani cinathandiza Hananiya kukhala munthu wodalilika?

5 Ataumanganso mpanda wa Yerusalemu mu 455 B.C.E., Bwanamkubwa Nehemiya anasankha amuna odalilika amene akanasamalila bwino mzindawo. Mmodzi wa amunawo anali Hananiya, kalonga wa m’Nyumba ya Citetezo Camphamvu. Baibo imakamba kuti Hananiya anali “munthu wodalilika ndipo anali woopa kwambili Mulungu woona kuposa anthu ena ambili.” (Neh. 7:2) Cikondi pa Yehova komanso mantha oopa kumukhumudwitsa, n’zimene zinathandiza Hananiya kugwila molimbika nchito iliyonse imene anapatsidwa. Makhalidwe amenewa adzatithandiza nafenso kukhala odalilika potumikila Mulungu.

6. Kodi Tukiko anaonetsa bwanji kuti anali mnzake wodalilika wa mtumwi Paulo?

6 Citsanzo cina ni ca Tukiko, mnzake wodalilika wa mtumwi Paulo. Pamene Paulo anali pa ukaidi wosacoka panyumba, anali kudalila Tukiko, ndipo anam’chula kuti “mtumiki wokhulupilika.” (Aef. 6:21, 22) Paulo anali kum’dalila mwamunayu moti anam’tuma kukapeleka makalata kwa Akhristu a ku Efeso na ku Kolose, komanso kuti akawalimbikitse na kuwatonthoza. Citsanzo ca Tukiko citikumbutsa amuna okhulupilika, komanso odalilika amene amasamalila zosoŵa zathu zauzimu masiku ano.—Akol. 4:7-9.

7. Pa nkhani yokhala wodalilika, kodi mungaphunzile ciyani kwa akulu na atumiki othandiza mu mpingo wanu?

7 Masiku ano, timayamikila kwambili kuti akulu na atumiki othandiza ni amuna odalilika. Mofanana na Danieli, Hananiya, komanso Tukiko, iwo sautenga mopepuka udindo wawo. Mwacitsanzo, pa msonkhano wa mkati mwa mlungu, sitimakayikila kuti mbali zonse za msonkhanowu zinagaŵilidwa. Ndipo akulu amayamikila kwambili ngati abale na alongo amene anagaŵilidwa mbalizo, akonzekela bwino na kuzikamba ku mpingo. Cina, sitidodoma kuitanila wophunzila wathu ku msonkhano wa kumapeto kwa mlungu poganiza kuti mwina sikudzakhala m’bale wokamba nkhani ya anthu onse. Timadziŵanso kuti zofalitsa zogaŵila mu ulaliki ziliko. Conco, timasamalidwa bwino na abale odalilika amenewo. Ndipo timayamikila Yehova potipatsa abalewo. Koma kodi ni m’njila ziti zimene tingaonetsele kuti ndife odalilika?

TIZIKHALA ODALILIKA PA KUSUNGA CINSINSI

8. Kodi tiyenela kusamala ciyani pofuna kudziŵa za umoyo wa ena? (Miyambo 11:13)

8 Timawakonda abale na alongo athu, ndipo timafuna kudziŵa za umoyo wawo. Komabe, tiyenela kusamala kuti tisamaloŵelele nkhani zawo zacinsinsi. Mu mpingo wacikhristu m’nthawi ya atumwi, anthu ena anali “amisece ndi oloŵelela nkhani za eni, n’kumalankhula zimene sayenela kulankhula.” (1 Tim. 5:13) Ife sitifuna kukhala monga iwo. Tiyelekeze kuti munthu wina watiuzako nkhani yake yacinsinsi, ndipo watipempha kuti tisauze aliyense. Mwacitsanzo, mlongo angatiuze nkhani yokhudza thanzi lake, kapena vuto lina lake limene akupitamo. Ndipo watipempha kuti tisauzeko aliyense nkhaniyo. Tiyenela kumusungila cinsinsi cake. * (Ŵelengani Miyambo 11:13.) Tsopano, tiyeni tikambilane mbali zina zimene n’zofunika kwambili kuti tizisunga cinsinsi.

9. Kodi aliyense m’banja angaonetse bwanji kuti ni wodalilika?

9 M’banja. Aliyense m’banja ali na udindo wosunga nkhani zacinsinsi za banja lawo. Mwacitsanzo, mkazi wacikhristu angakhale na kacizolowezi kamene mwamuna wake amakaona kuti n’koseketsa. Kodi mwamunayo ayenela kuuzako ena zimenezo, na kunyazitsa mkazi wake? Ayi. Cifukwa comukonda mkazi wake, sangacite zinthu zimene zingam’kwiyitse akazimva. (Aef. 5:33) Anyamata na atsikana amafunikila ulemu wowayenelela, ndipo makolo ayenela kuikumbukila mfundo imeneyi. Iwo sayenela kucititsa manyazi ana awo amenewo pomauza ena zimene amalakwitsa. (Akol. 3:21) Ana nawonso ayenela kukhala osamala kuti asamaulule nkhani zacinsinsi za m’banja mwawo, kuti asacititse manyazi a m’banja mwawo. (Deut. 5:16) Aliyense m’banja akamacita mbali yake mwa kusunga nkhani zacinsinsi zokhudza banja, banjalo limakhala logwilizana kwambili.

10. Kodi kukhala bwenzi lenileni kumafuna ciyani? (Miyambo 17:17)

10 Kwa mabwenzi athu. Nthawi zina, timafuna kuuzako mnzathu wapamtima zakukhosi. Koma kucita zimenezi kungakhale kotivuta. Mwina sitinazoloŵele kuululila munthu wina nkhani zathu zacinsinsi. Mwinanso tikuopa kuti mnzathuyo angakauzeko ena nkhani zathu zacinsinsi, zimene zingatikhumudwitse kwambili. Kumbali ina, timayamikila kwambili ngati mnzathu amatisungila cinsinsi. Ameneyo ndiye “bwenzi lenileni.”—Ŵelengani Miyambo 17:17.

Akulu sayenela kuulula nkhani zacisinsi kwa a m’banja mwawo (Onani ndime 11) *

11. (a) Kodi akulu na akazi awo amaonetsa bwanji kuti ni odalilika? (b) Kodi tiphunzilapo ciyani kwa mkulu amene anali kusamalila nkhani yacinsinsi mu mpingo, kenako akuceza na banja lake? (Onani cithunzi.)

11 Mu mpingo. Akulu amene amasunga cisinsi amakhala “malo obisalilapo mphepo ndi malo ousapo mvula yamkuntho” kwa abale na alongo. (Yes. 32:2) Tiyenela kumasuka kuuza akulu nkhani iliyonse, cifukwa timawadalila kuti adzatisungila cinsinsi. Ndipo sitiyenela kuwaumiliza kuti atifotokozele nkhani zimene n’zacinsinsi. Cina, akazi a akulu timawayamikila cifukwa sakakamiza amuna awo kuti awaululile nkhani zacinsinsi. Kunena zoona, ni dalitso kukhala na mkulu amene saululila mkazi wake nkhani zacinsinsi zokhudza abale na alongo. Mkazi wa mkulu wina anati: “Nimayamikila kuti mwamuna wanga samaniuzako zokhudza maulendo aubusa amene amacita, monga anthu amene amapitako, kapena thandizo lauzimu limene amawapatsa. Samanichulila ngakhale maina awo. Nimayamikila kuti samaniuza nkhani zimene zikhoza kungokhala mtolo kwa ine. Cifukwa ca zimenezi, nimamasuka kumaceza na aliyense mu mpingo. Ndipo inenso nimakhala na cidalilo cakuti nikauzako mwamuna wanga nkhani zakukhosi kwanga kapena mavuto anga, sadzauzako ena.” Inde, tonsefe timafuna kukhala anthu odalilika. Nanga ni makhalidwe ati amene adzatithandiza kucita zimenezi? Tiyeni tikambilane asanu.

MAKHALIDWE OKUTHANDIZANI KUKHALA WODALILIKA

12. N’cifukwa ciyani tingakambe kuti cikondi ndico maziko a kudalilika? Fotokozani citsanzo.

12 Cikondi ndico maziko a kukhala wodalilika. Yesu anapeleka malamulo aŵili aakulu kwambili—kukonda Yehova komanso kukonda mnzako. (Mat. 22:37-39) Cikondi cathu pa Yehova cimatisonkhezela kutengela citsanzo cake ca kudalilika kwake. Mwacitsanzo, ngati abale na alongo timawakonda, tidzawasungila nkhani zawo zacinsinsi. Sitingayese olo pang’ono kuulula zinthu zimene zingawacititse manyazi kapena kuwaika m’mavuto.—Yoh. 15:12.

13. Kodi kudzicepetsa kumatithandiza bwanji kukhala odalilika?

13 Kudzicepetsa kudzatithandiza kukhala odalilika. Mkhristu wodzicepetsa sakhala na maganizo akuti ‘nifuna nizikhala woyamba ndine kuuza anthu nkhani.’ (Afil. 2:3) Komanso, munthu wodzicepetsa sapangitsa ena kumuona kuti amadziŵa nkhani zacinsinsi zimene n’kosaloledwa kuuzako ena. Kudzicepetsa kudzatithandizanso kupewa kufalitsa nkhani zimene Baibo kapena zofalitsa zozikika pa Baibo sizinakambepo.

14. Kodi kuzindikila kumatithandiza bwanji kukhala odalilika?

14 Kuzindikila kumathandiza Mkhristu kudziŵa “nthawi yokhala cete ndi nthawi yolankhula.” (Mlal. 3:7) M’zikhalidwe zina, amati “kulankhula kuli monga siliva, pamene kukhala cete kuli monga golide.” Kunena kwina, kukhala cete nthawi zina kuli bwino kwambili kuposa kulankhula. M’pake kuti Miyambo 11:12 imati: “Munthu wozindikila bwino ndi amene amakhala cete.” Ganizilani citsanzo ici. Mkulu wina kaŵili-kaŵili anali kupemphedwa kuti akathandizile ku mipingo ina pa nkhani zofunika kusamalidwa. Ponena za mkuluyo, mkulu wina anati, “Iye amakhala wosamala kwambili kuti asaulule nkhani zacisinsi zokhudza mipingo ina.” Cifukwa cakuti mkuluyo ni wozindikila, akulu ena pa bungwe lake amam’lemekeza kwambili. Cifukwa ca zimenezi, iwo amam’dalila mkuluyo kuti ngakhale nkhani zacisinsi za m’bungwe lawo sangaziulule kwa ena.

15. Fotokozani citsanzo coonetsa kuti kukhala woona mtima kumathandiza ena kuti azitidalila.

15 Kuona mtima ni khalidwe linanso limene lingatithandize kukhala odalilika. Munthu woona mtima timam’dalila cifukwa timadziŵa kuti amakamba zoona nthawi zonse. (Aef. 4:25; Aheb. 13:18) Mwacitsanzo, tinene kuti mufuna kuwonjezela luso lanu la kuphunzitsa. Mukupempha wina kuti amvetsele nkhani yanu, na kukuchulilani mbali zimene muyenela kuwongolela. Ndani amene mungam’dalile kuti adzakuuzani zoona? Kodi ni uja amene adzakuuzani zimene mungakonde kumva, kapena amene mokoma mtima angakuuzeni zoona? Yankho n’lacidziŵikile. Baibo imati: “Kudzudzula munthu mosabisa mawu, kuli bwino kusiyana ndi kumukonda koma osamusonyeza cikondico. Zilonda zovulazidwa ndi munthu wokukonda zimakhala zokhulupilika.” (Miy. 27:5, 6) Ngakhale kuti zimene bwenzi lathu lingatiuze moona mtima zingakhale zosasangalatsa poyamba, m’kupita kwa nthawi tidzaona kuti n’zothandiza.

16. Kodi Miyambo 10:19 imaonetsa bwanji kufunika kokhala odziletsa?

16 Kudziletsa nakonso n’kofunika kwambili kuti anthu ena azitidalila. Khalidwe limeneli limatithandiza kukhala cete pamene mtima wathu walakalaka kukamba nkhani zimene n’zacinsinsi. (Ŵelengani Miyambo 10:19.) Tikamagwilitsa nchito soshomidiya, kudziletsa kwathu kungaikidwe pa mayeso. Tikapanda kusamala, tingafalitse nkhani zacinsinsi kwa anthu oculuka pa Intaneti. Tikatelo, sitingakwanitse kuletsa anthu kuzigwilitsa nchito molakwika nkhanizo, kapena kuvulaza nazo anthu ena. Cina, kudziletsa kudzatithandiza kukhala cete anthu otsutsa akafuna kutipusitsa kuti tiulule zinthu zimene zingaike moyo wa abale na alongo athu pa ciwopsezo. Izi zingacitike pamene apolisi akutifunsa mafunso m’dziko limene nchito yathu ni yoletsedwa. Pa zocitika zimenezi komanso zina, tingatsatile mfundo ya m’Baibo yakuti: “Ndidzamanga pakamwa panga kuti patetezeke.” (Sal. 39:1) Pocita zinthu na a m’banja mwathu, mabwenzi athu, abale na alongo athu, kapena wina aliyense, tiyenela kukhala odalilika. Ndipo kudalilika kumeneku kumafuna kudziletsa.

17. Kodi tingalimbikitse bwanji mzimu wodalilana mu mpingo?

17 Timayamikila kwambili Yehova potibweletsa m’gulu lake mmene anthu ake ni acikondi komanso odalilika. Tonse tili na udindo wopangitsa kuti abale na alongo athu azitidalila. Aliyense payekha akamayesetsa kuonetsa khalidwe la cikondi, kudzicepetsa, kuzindikila, kuona mtima, komanso kudziletsa, timalimbikitsa mzimu wodalilana mu mpingo. Kukhala wodalilika kulibe polekezela. Conco, tiyeni titengele citsanzo ca Mulungu wathu Yehova, na kupitilizabe kuonetsa kuti ndife odalilika.

NYIMBO 123 Gonjelani Dongosolo la Mulungu

^ Ngati tifuna kuti ena azitidalila, coyamba ife eni tiyenela kuonetsa kuti ndife odalilika. M’nkhani ino, tione cifukwa cake kudalilika n’kofunika kwambili. Tionenso makhalidwe amene angatithandize kuti anthu azitidalila.

^ Tikadziŵa kuti wina mu mpingo wacita chimo lalikulu, tiyenela kumuuza kuti akauze akulu nkhaniyo. Ngati iye sakucita zimenezo, kukhulupilika kwathu kwa Yehova komanso ku mpingo wacikhristu, kudzatipangitsa kukawauza abusa auzimu za chimo lakelo.

^ MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Mkulu sayenela kuulula nkhani zacisinsi kwa a m’banja lake zimene anasamalila mu mpingo.