NKHANI YOPHUNZILA 38
Acinyamata—Kodi Mudzakhala na Tsogolo Lotani?
“Kuzindikila kudzakuteteza.”—MIY. 2:11.
NYIMBO 135 Yehova Akulangiza Mwacikondi Kuti: “Mwana Wanga, Khala Wanzelu”
ZIMENE TIKAMBILANE a
1. Kodi Yehoasi, Uziya, na Yosiya anakumana na covuta cotani?
MUNGAMVE bwanji mukanakhala mfumu ya anthu a Mulungu muli wacicepele! Kodi mukanaseŵenzetse bwanji mphamvu zanu monga mfumu? Baibo imasimba za acicepele angapo amene anakhalapo mafumu ku Yuda. Mwacitsanzo, Yehoasi anali na zaka 7 zokha pamene anakhala mfumu, Uziya anali na zaka 16, ndipo Yosiya anali na zaka 8. Ziyenela kuti zinali zovuta kwa iwo! Ngakhale n’telo, Yehova na anthu ena anawathandiza kucita zinthu zambili zabwino.
2. N’cifukwa ciyani m’pofunika kuzidziŵa nkhani za Yehoasi, Uziya, na Yosiya?
2 N’zoona kuti sindife mafumu, koma tingaphunzile zambili kwa anthu atatu ochulidwa m’Baibo amenewa. Iwo anapangapo zisankho zabwino komanso zoipa. Zitsanzo zawo zitionetsa cifukwa cake tiyenela kusankha bwino mabwenzi, kukhalabe odzicepetsa, na kupitiliza kufuna-funa Yehova
SANKHANI MABWENZI MWANZELU
3. Kodi Mfumu Yehoasi anatani na malangizo a Mkulu wa Ansembe Yehoyada?
3 Pangani zisankho zanzelu monga Yehoasi. Ali wacicepele, Mfumu Yehoasi anapanga cisankho cabwino. Popeza analibe tate, iye anatsatila citsogozo ca Mkulu wa Ansembe wokhulupilika Yehoyada. Mkulu wa a ansembeyo analangiza Yohoasi monga mwana wake wodzibalila. Zotulukapo zake, Yehoasi anasankha kutumikila Yehova na kutsogolela pa kulambila koona. Iye anafika mpaka pokonzanso kacisi wa Yehova.—2 Mbiri 24:1, 2, 4, 13, 14.
4. Kodi timapindula bwanji tikamamvela malamulo a Yehova? (Miyambo 2:1, 10-12)
4 Ngati wina akukuphunzitsani kukonda Yehova na kutsatila miyeso yake, ndiye kuti akukupatsani mphatso ya mtengo wapatali. (Ŵelengani Miyambo 2:1, 10-12.) Makolo angaphunzitse ana awo m’njila zambili. Onani mmene atate a mlongo Katya anam’thandizila kupanga zisankho zabwino. Tsiku lililonse pom’peleka kusukulu, atate ake anali kukambilana naye lemba la tsiku. Mlongoyo anati: “Makambilanowo anali kunithandiza kuthana na zovuta zimene n’nali kukumana nazo.” Koma bwanji ngati muona kuti malangizo a m’Baibo amene makolo amakupatsani amakuphelani ufulu? N’ciyani cingakuthandizeni kulandilabe malangizowo? Mlongo Anastasia amakumbukila kuti makolo ake pom’patsa malamulo anali kum’fotokozelanso cifukwa cake. Iye anati: “Izi zinanithandiza kuona kuti anali kunipatsa malamulowo, osati kuti aniphele ufulu, koma kuti aniteteze cifukwa conikonda.”
5. Kodi zocita zanu zingakhuze bwanji makolo anu na Yehova? (Miyambo 22:6; 23:15, 24, 25)
5 Mukamaseŵenzetsa ulangizi wa m’Malemba umene makolo anu amapeleka, mudzawasangalatsa kwambili. Koma koposa zonse, mudzakondweletsa Mulungu ndipo ubwenzi wanu na iye udzalimba. (Ŵelengani Miyambo 22:6; 23:15, 24, 25.) Izi ni zifukwa zabwino kwambili zotipangitsa kutengela citsanzo ca Yehoasi ali mwana.
6. Kodi Yehoasi anayamba kumvela malangizo a ndani, nanga panakhala zotulukapo zotani? (2 Mbiri 24:17, 18)
6 Tengam’poni cenjezo pa zisankho zoipa za Yehoasi. Yehoyada atamwalila, Yehoasi anasankha mabwenzi oipa. (Ŵelengani 2 Mbiri 24:17,18.) Anasankha kumvela akalonga a ku Yuda amene sanali kumvela Yehova. Mungavomeleze kuti Yehoasi anayenela kuwapewa cifukwa anali kucita zoipa. (Miy. 1:10) M’malo mwake, iye anatsatila ulangizi wawo. Kuwonjezela apo, msuweni wake Zekariya atayesa kumuwongolela, Yehoasi analamula kuti aphedwe. (2 Mbiri 24:20, 21; Mat. 23:35) Ati kupusa kwake ŵati! Yehoasi anayamba bwino, koma n’zacisoni kuti m’kupita kwa nthawi anakhala wampatuko komanso wopha anthu. Pothela pake atumiki ake anamupha. (2 Mbiri 24:22-25) Akanapitiliza kumvela Yehova na anthu okonda Yehova, zinthu zikanamuyendela bwino ngako! Kodi mwaphunzilanji pa citsanzoci?
7. Kodi muyenela kusankha anthu otani kuti akhale mabwenzi anu? (Onaninso cithunzi)
7 Phunzilo limodzi limene tingatengepo pa cisankho coipa ca Yehoasi n’lakuti tiyenela kusankha mabwenzi amene amakonda Yehova, komanso amene amafuna kumukondweletsa. Mabwenzi aconco angatithandize kucita zinthu mwanzelu. Sitiyenela kusankha anthu a msinkhu wathu okha-okha kukhala mabwenzi athu. Kumbukilani kuti Yehoasi anali wamng’ono kwambili poyelekezela na mnzake Yehoyada. Ponena za mabwenzi anu, dzifunseni kuti: ‘Kodi amanithandiza kulimbikitsa cikhulupililo canga mwa Yehova? Kodi amanilimbikitsa kutsatila miyeso ya Yehova? Kodi amakonda kukamba za Yehova na coonadi cake ca mtengo wapatali? Kodi amalemekeza miyeso ya Mulungu? Kodi amangoniuza zonikomela m’khutu, kapena amalimba mtima na kuniwongolela nikalakwitsa?’ (Miy. 27:5, 6, 17) Kunena zoona, ngati mabwenzi anu sakonda Yehova, pezani ena. Koma ngati amakonda Yehova, akangamileni—cifukwa adzakuthandizani ngako!—Miy. 13:20.
8. Ngati timaseŵenzetsa soshomidiya, kodi n’ciyani cimene tiyenela kukumbukila?
8 Soshomidiya ni njila yothandiza kwambili yokambilana na acibale komanso mabwenzi. Komabe anthu ena amaseŵenzetsa masamba amcezo amenewa pofuna kukondweletsa anzawo. Amatelo mwa kuika zithunzi kapena mavidiyo a zimene agula kapena zimene acita. Ngati mumaseŵenzetsa soshomidiya, dzifunseni kuti: ‘Kodi nimangofuna kukondweletsa anthu ena? Kodi colinga canga ni kuwalimbikitsa kapena kufuna kuti anitamande? Kodi nimalola kuti zimene ena amaika pa soshomidiya zisonkhezele kaganizidwe kanga, kakambidwe na zocita zanga?’ M’bale Nathan Knorr, amene anatumikilapo m’bugwe lolamulila, anapeleka upangili wakuti: “Colinga canu cisakhale kukodweletsa anthu. Cifukwa simungakwanitse kukondweletsa aliyense. Koma ngati mumakodweletsa Yehova, mudzakondweletsanso amene amamukonda.”
KHALANIBE ODZICEPETSA
9. Kodi Yehova anathandiza Uziya kucita ciyani? (2 Mbiri 26:1-5)
9 Pangani zisankho zanzelu monga anacitila Uziya. Ali wacicepele, Mfumu Uziya anali wodzicepetsa. Iye anaphunzila ‘kuopa Mulungu woona.’ Uziya anakhala na moyo kwa zaka 68, ndipo kwa zaka zambili pa umoyo wake Yehova anamudalitsa. (Ŵelengani 2 Mbiri 26:1-5.) Uziya anagonjetsa adani ambili a Yuda, ndipo anakhwimitsa citetezo ca Yerusalemu. (2 Mbiri 26:6-15) Mosakaika, Uziya anakondwela ngako cifukwa ca zimene Mulungu anam’thandiza kucita.—Mlal. 3:12, 13.
10. Kodi zinthu zinamuthela bwanji Uziya?
10 Tengam’poni cenjezo pa zisankho zoipa za Uziya. Mfumu Uziya anazoloŵela kuuza ena zoyenela kucita. N’kutheka kuti izi zinam’pangitsa kuona kuti angacite ciliconse cimene afuna. Tsiku lina, Uziya analoŵa m’kacisi wa Yehova, ndipo modzikuza anayamba kufukiza nsembe, cinthu cimene mafumu sanali kuloledwa kucita. (2 Mbiri 26:16-18) Mkulu wa Ansembe Azariya anayesa kumuwongolela, koma Uziya anakwiya zedi. N’zacisoni kuti Uziya anawononga mbili yake yokhulupilika, ndipo anakanthidwa na khate. (2 Mbiri. 26:19-21) Akanakhalabe wodzicepetsa, moyo wake ukanakhala wabwino ngako!
11. Tiyenela kucita zinthu motani poonetsa kuti ndife odzicepetsa? (Onaninso cithunzi.)
11 Uziya atakhala wamphamvu, anaiŵala kuti ni Yehova amene anam’patsa mphamvu na cipambano. Pali phunzilo lanji kwa ife? Tizikumbukila kuti madalitso na mautumiki amene tili nawo amacokela kwa Yehova. M’malo modzitama na zimene takwanitsa kucita, tiyenela kupeleka ulemu wonse kwa Yehova. b (1 Akor. ) Modzicepetsa, tiyenela kukumbukila kuti ndife opanda ungwilo, ndipo timafunikila cilango. M’bale wina wa zaka za m’ma 60 anati: “Naphunzila kusadziona wofunika kwambili kuposa ena. M’malo mokhumudwa na uphungu umene nalandila cifukwa cocita zinthu mwacibwana, nimayesetsa kuwongolela na kupitiliza kutumikila.” Zoona zake n’zakuti, tikamaopa Yehova na kukhalabe odzicepetsa, zinthu zidzatiyendela bwino.— 4:7Miy. 22:4.
MUSALEKE KUFUNA-FUNA YEHOVA
12. Kodi Yosiya anafuna-funa bwanji Yehova ali wacicepele? (2 Mbiri 34:1-3)
12 Pangani zisankho zanzelu monga anacitila Yosiya. Yosiya anayamba kufuna-funa Yehova ali mnyamata. Anali wofunitsitsa kuphunzila za Yehova na kucita cifunilo cake. Komabe, umoyo sunali wopepuka kwa mfumu yacinyamatayi. Anafunika kulimba mtima kuti abwezeletse kulambila koyela panthawi imene kulambila konyenga kunali kofala. Ndipo anatelodi! Asanakwanitse zaka 20, Yosiya anayamba kucotsa kulambila konyenga m’dzikolo.—Ŵelengani 2 Mbiri 34:1-3.
13. Kodi kudzipatulila kwa Yehova kudzasintha bwanji umoyo wanu?
13 Ngakhale kuti ndinu wacicepele kwambili, mungathe kutengela Yosiya mwa kufuna-funa Yehova na kuphunzila za makhalidwe ake. Izi zingakulimbikitseni kupatulila moyo wanu kwa iye. Kodi kudzipatulila kumeneku kudzakhudza bwanji umoyo wanu wa tsiku na tsiku? Pa tsiku limene anali kubatizika, ali na zaka 14, Luke anati, “Kuyambila lelo, nidzaika kutumikila Yehova patsogolo mu umoyo wanga, ndipo nidzayesetsa kumukondweletsa.” (Maliko 12:30) Ngati ni zimene nanunso mufuna kucita, mudzadalitsika kwambili!
14. Fotokozani zitsanzo za acicepele amene atengela Mfumu Yosiya.
14 Kodi ni zopinga ziti zimene mungakumane nazo monga mtumiki wacicepele wa Yehova? Johan amene anabatizika ali na zaka 12, ananena kuti anzake a m’kalasi anali kum’kakamiza kuti ayambe kukoka fodya. Kuti athe kukaniza mayeselowo, Johan amakumbukila kuti kukoka fodya kungawononge thanzi lake na ubwenzi wake na Yehova. Rachel amene anabatizika na zaka 14, anafotokoza zimene zimam’thandiza kugonjetsa zopinga zimene amakumana nazo ku sukulu. Iye anati: “Nimagwilizanitsa zimene nimaŵelenga m’Baibo na zimene zanicitikila. Mwacitsanzo, kuphunzila mbili yakale kunganikumbutse nkhani ya m’Baibo kapena ulosi. Nthawi zina kuceza na munthu kunganikumbutse lemba lothandiza limene ningakambilane naye.” Ngakhale kuti zopinga zanu zingasiyane na zimene Mfumu Yosiya anakumana nazo, inunso mungakhale wanzelu komanso wokhulupilika monga iye. Kuthana na mayeso muli wacinyamata kudzakukonzekeletsani kudzathana na mavuto obwela m’tsogolo.
15. N’ciyani cinathandiza Yosiya kutumikila Yehova mokhulupilika? (2 Mbiri 34:14, 18-21)
15 Atakula, Mfumu Yosiya anayamba nchito yokonzanso kacisi. Nchitoyo ili mkati, “anapeza buku la cilamulo ca Yehova lopelekedwa ndi dzanja la Mose.” Atamva bukulo likuŵelengedwa, Yosiya anacitapo kanthu mwa kuyamba kutsatila zimene anali kuŵelenga m’bukulo. (Ŵelengani 2 Mbiri 34:14, 18-21.) Kodi mumafuna kuŵelenga Baibo tsiku lililonse? Ngati munayamba kale, kodi zikuyenda bwanji? Kodi mumasungako mavesi ena amene angakuthandizeni pacanu? Luke amene tamuchula uja, amalemba m’buku mfundo zothandiza zimene apeza. Kodi kucita izi kungakuthandizeni nanunso kukumbukila mavesi na mfundo zimene mwakonda? Mukakulitsa cidziŵitso na cikondi canu pa Baibo, cikhumbo canu cofuna kutumikila Yehova naconso cidzakula. Monga mmene Mawu a Mulungu anathandizila Mfumu Yosiya kucita zoyenela, inunso angakuthandizeni kutelo.
16. N’ciyani cinapangitsa Yosiya kucita zolakwa zazikulu, nanga tiphunzilapo ciyani?
16 Tengam’poni cenjezo pa zisankho zoipa za Yosiya. Ali na zaka ngati 39, Yosiya anapanga cisankho colakwika cimene cinam’tayitsa moyo wake. Anadzidalila m’malo modalila Yehova kuti amutsogolele. (2 Mbiri 35:20-25) Tiphunzilapo ciyani? Kaya tili na zaka zingati, kapena takhala tikuphunzila Baibo kwa nthawi yaitali bwanji, sitiyenela kuleka kumufuna-funa Yehova. Izi ziphatikizapo kupempha citsogozo cake nthawi zonse, kuphunzila mawu ake, na kugwilitsa nchito ulangizi wa Akhristu okhwima. Tikamatelo, tidzapewa kupanga zisankho zolakwika, ndipo tidzakhala osangalala.—Yak. 1:25.
INU ACICEPELE—ZINTHU ZINGAKUYENDELENI BWINO
17. Kodi taphunzila ciyani kwa Mafumu atatu a Yuda?
17 Pali zinthu zambili zimene mungacite mukali acicepele. Zitsanzo za Yohoasi, Uziya komanso Yosiya zimaonetsa kuti n’zotheka acicepele kupanga zisankho zanzelu na kukhala umoyo wokondweletsa Yehova. N’zoona kuti acicepelewa anapangapo zisankho zimene zinawabweletsela mavuto. Koma ngati mutengela zabwino zimene anacita na kupewa zisankho zoipa zimene anapanga, mungakhale na umoyo wokondweletsa.
18. Ni zitsanzo ziti za m’Malemba zimene zionetsa kuti zinthu zingakuyendeleni bwino pa umoyo? (Onaninso cithunzi)
18 M’malemba mulinso nkhani za acinyamata ena omwe anakhala mabwenzi a Yehova, anapeza ciyanjo cake, ndipo zinthu zinawayendela bwino. Mmodzi wa iwo ni Davide. Ali wacicepele, anasankha kukhala kumbali ya Mulungu, ndipo m’kupita kwa nthawi anakhala mfumu yokhulupilika. N’zoona kuti analakwitsapo zina zake, koma kwakukulu-kulu Mulungu anamuona kukhala wokhulupilika. (1 Maf. 3:6; 9:4, 5; 14:8) Kuphunzila za umoyo wa Davide na utumiki wake wokhulupilika kungakulimbikitseni ngako. Kapena mungasankhe kuphunzila za acinyamata ena monga Maliko kapena Timoteyo. Anayamba kutumikila Yehova ali acicepele, ndipo anapitiliza kum’tumikila mokhulupilika. Cisankho cawo cinakondweletsa Yehova; ndipo nawonso anakhala okondwela.
19. Kodi zinthu zingakutheleni bwanji mu umoyo?
19 Kuti mukhale na tsogolo labwino, zidalila mmene mukuseŵenzetsela moyo wanu pali pano. Mukamakhulupilila Yehova na kupewa kudzidalila, adzakutsogolelani. (Miy. 20:24) Mungakhale na umoyo wosangalatsa komanso wokhutilitsa. Kumbukilani, Yehova amayamikila zimene mumam’citila. Palibe njila yabwino yoseŵenzetsela umoyo wathu yoposa kutumikila Atate wathu wakumwamba?
NYIMBO 144 Yang’anani pa Mphoto!
a Inu acicepele, Yehova amadziŵa kuti mumakumana na zokhoma zimene zingapangitse kuti cikhale covuta kukhala naye pa ubwenzi. Kodi mungapange bwanji zisankho zanzelu zimene zidzakondweletsa Atate wanu wakumwamba? Tikambilane zitsanzo za anyamata atatu amene anakhala mafumu a Yuda. Onani zimene mungaphunzile pa zisankho zimene anapanga.
b Onani bokosi lakuti “Musamanamizile kukhala odzicepetsa” yopezeka m’nkhani ya pa jw.org yakuti “Kodi Kukhala Munthu Wotchuka pa Intaneti Kuli Ndi Phindu?”