NKHANI YOPHUNZILA 39
Khalani Wamphamvu Pokhala Wofatsa
“Kapolo wa Ambuye sayenela kukangana ndi anthu, koma ayenela kukhala wodekha kwa onse.”—2 TIM. 2:24.
NYIMBO 120 Tengelani Kufatsa kwa Khristu
ZIMENE TIKAMBILANE a
1. Kodi anthu ku sukulu kapena ku nchito angatifunse ciyani?
Mumamva bwanji ngati mnzanu wa kunchito kapena kusukulu wakufunsani pa zimene mumakhulupilila? Ambili a ife timacita mantha. Koma funso lake lingatithandize kudziŵa maganizo a munthuyo kapena zimene amakhulupilila. Zimenezi zingatipatse mpata wom’gaŵilako uthenga wabwino. Koma nthawi zina, ena angafunse funso pofuna kukangana nafe. Izi siziyenela kutidabwitsa cifukwa anthu ambili amauzidwa mabodza pa zimene timakhulupilila. (Mac. 28:22) Kuwonjezela apo, tikukhala ‘m’masiku otsiliza,’ nthawi imene ambili ni “osafuna kugwilizana ndi anzawo,” komanso “oopsa.”—2 Tim. 3:1, 3.
2. N’cifukwa ciyani kufatsa ni khalidwe labwino kwambili?
2 Mwina mungadzifunse kuti, ‘N’ciyani cinganithandize kukhala wodekha komanso wokoma mtima ngati wina ali na colinga coyambitsa mkangano pa zimene nimakhulupilila?’ Ni kukhala wofatsa. Munthu wofatsa sakwiya msanga akakumana na zokhumudwitsa kapena zodetsa nkhawa. (Miy. 16:32). Koma kucita zimenezi sikopepuka. Kodi mungakulitse bwanji khalidwe la kufatsa? Kodi mungayankhe bwanji mofatsa ngati wina watsutsa zimene mumakhulupilila? Ngati ndinu kholo, kodi mungathandize bwanji ana anu kukhala ofatsa pamene akhalila kumbuyo cikhulupililo cawo? Tiyeni tione.
MMENE TINGAKULITSILE KHALIDWE LA KUFATSA
3. N’cifukwa ciyani tingati anthu ofatsa ni amphamvu osati ofooka? (2 Timoteyo 2:24, 25)
3 Munthu akakhala wofatsa sindiye kuti ni wofooka. Zimafuna mphamvu kuti munthu akhalebe wodekha akaputidwa. Kufatsa ni ‘khalidwe limene mzimu woyela umatulutsa.’ (Agal. 5:22, 23) Liwu la Cigiriki lomasulidwa kuti “kufatsa” nthawi zina anali kuliseŵenzetsa pofotokoza za hachi yakuchile imene yayamba kuwetedwa. Hachiyo imakhala yodekha koma imakhalabe yamphamvu. Nanga ife tingakulitse bwanji khalidwe la kufatsa, koma pa nthawi imodzimodzi n’kukhalanso olimba? Izi sizingatheke mwa mphamvu zathu zokha. Koma zingatheke mwa kupempha mzimu wa Mulungu kuti utithandize kukulitsa khalidwe limeneli. Pali umboni woonetsa kuti zimenezi n’zotheka. Mboni zambili zimayankha mofatsa anthu akaziputa. Kutelo kwathandiza anthu kukhala na kaonedwe kabwino ka gulu lathu. (Ŵelengani 2 Timoteyo 2:24, 25.) Kodi mungakhale nalo bwanji khalidwe la kufatsa?
4. Tingaphunzile ciyani za kufatsa pa citsanzo ca Isaki?
4 M’Baibo muli nkhani zambili zoonetsa kufunika kwa khalidwe la kufatsa. Ganizilani citsanzo ca Isaki. Atakhazikika m’dela la Afilisiti ku Gerari, Afilisitiwo anafocela zitsime zimene anchito a bambo ake anakumba. M’malo mokangana nawo, Isaki na banja lake anasamukako kumeneko ndipo anakumba zitsime zina. (Gen. 26:12-18) Koma Afilisiti ananena kuti madzi a m’zitsimezo analinso awo. Apanso, Isaki anacita zinthu mwa mtendele. (Gen. 26:19-25) N’ciyani cinam’thandiza kukhalabe wofatsa, ngakhale kuti anthu anapitiliza kum’puta? Mosakayika, anaona mmene atate ake Abulahamu anali kucitila zinthu mwa mtendele, komanso “mzimu wabata ndi wofatsa” wa Sara.—1 Pet. 3:4-6; Gen. 21:22-34.
5. Fotokozani citsanzo coonetsa kuti makolo angathe kuphunzitsa ana awo kufunika kwa khalidwe la kufatsa.
5 Inu makolo acikhristu, khalani na cidalilo cakuti mungaphunzitse ana anu kuona kufunika kwa khalidwe la kufatsa. Onani citsanzo ici ca Maxence, wa zaka 17. Anali kukumana na anthu okwiya kusukulu komanso mu utumiki. Moleza mtima, makolo ake anam’thandiza kukulitsa khalidwe la kufatsa. Iwo anati, “Lomba, Maxence amamvetsa kuti kubwezela n’kopepuka koma kudziletsa ukaputidwa kumafuna mphamvu zoculuka.” N’zokondweletsa kuti pali pano Maxence ni wofatsa.
6. Kodi pemphelo ingatithandize bwanji kukulitsa khalidwe la kufatsa?
6 Kodi tingatani ngati wina wacita zinthu zotikwiyitsa, monga kunyoza dzina la Mulungu kapena Baibo? Tizipempha Yehova kuti atipatse nzelu na mzimu wake kuti tiyankhe mofatsa. Nanga tingatani ngati tazindikila kuti pa nthawi ina sitinayankhe mofatsa? Tingaipemphelele nkhaniyo na kuona mmene tingayankhile bwino mtsogolo. Tikatelo, Yehova adzatipatsa mzimu wake woyela kuti tiziugwila mtima na kuonetsa kufatsa.
7. Kodi kuwaloŵeza pa mtima malemba ena kungatithandize bwanji kulamulila lilime m’mikhalidwe yovuta? (Miyambo 15:1, 18)
7 Pali mavesi ena a m’Baibo amene angatithandize kulamulila kalankhulidwe kathu pa mikhalidwe yovuta. Mzimu wa Mulungu ungatikumbutse mavesiwo. (Yoh. 14:26) Mwacitsanzo, mfundo zopezeka m’buku la Miyambo zingatithandize kukhala ofatsa. (Ŵelengani Miyambo 15:1, 18) Bukuli limaonetsanso mapindu a kukhalabe wodekha m’mikhalidwe yovuta.—Miy. 10:19; 17:27; 21:23; 25:15.
MMENE KUZINDIKILA KUMATITHANDIZILA KUKHALA OFATSA
8. N’cifukwa ciyani tiyenela kuganizila cimene capangitsa munthu kufunsa funso lina lake?
8 Kuzindikila nakonso kungatithandize kukhala ofatsa. (Miy. 19:11) Munthu wozindikila amakhala wodziletsa anthu akam’tsutsa pa zimene amakhulupilila. Za mumtima wa munthu sizidziŵika. Munthu angatifunse funso, ife osadziŵa ceniceni cimene wafunsila. Mwacitsanzo, si nthawi zonse pamene tingadziŵe cifukwa cimene munthu watifunsila funso. Conco, m’pofunika kumakumbukila mfundoyi tisanamuyankhe.—Miy. 16:23.
9. Kodi Gidiyoni anaonetsa bwanji kuzindikila na kufatsa pocita zinthu na a Efuraimu?
9 Ganizilani mmene Gidiyoni anayankhila amuna a ku Efuraimu. Iwo anam’funsa mwaukali cifukwa cake sanawaitane mwamsanga kuti akam’thandize kumenyana na adani a Isiraeli. Kodi cifukwa cacikulu cinawapangitsa kukwiya n’ciyani? Mwina n’cifukwa cakuti anali kudziona kuti anali ofunika kwambili pa mafuko onse a mu Isiraeli. Mulimonsemo, Gidiyoni sanatsutsane nawo koma anawayankha mofatsa. Zotsatila zake zinali zakuti “mkwiyo wawo unaphwa.”—Ower. 8:1-3.
10. N’ciyani cingatithandize kudziŵa mmene tingayankhile anthu amene amatsutsa cikhulupililo cathu? (1 Petulo 3:15)
10 Nthawi zina, mnzathu wa ku nchito kapena ku sukulu angatifunse cifukwa cake timatsatila miyeso ya m’Baibo. Zikatelo, timayesetsa kum’fotokozela zimene timakhulupilila kwinaku tikulemekeza maganizo ake. (Ŵelengani 1 Petulo 3:15) Nthawi zambili zimakhala bwino kuona funso la munthu ngati njila yodziŵila maganizo ake m’malo moganiza kuti angofuna kuyambitsa mkangano. Mosasamala kanthu cifukwa cimene munthuyo wadzutsila nkhani inayake, zimakhala bwino kumuyankha modekha komanso mokoma mtima. Yankho lathu lingamuthandize kuunikanso zimene amakhulupilila. Ngakhale munthuyo atayankha mwamwano, colinga cathu cizikhalabe kumuyankha mokoma mtima.—Aroma 12:17.
11-12. (a) Kodi tiyenela kuganizila ciyani tisanayankhe funso? (Onaninso cithunzi.) (b) Fotokozani citsanzo coonetsa kuti munthu akatifunsa funso zingatsegule mwayi wa makambilano abwino.
11 Mwacitsanzo, ngati mnzathu wa ku nchito watifunsa cifukwa cake sitimakondwelela masiku akubadwa, kodi angakhale kuti akufunsa funsolo cifukwa coganiza kuti sitimasangalalako? Kapena n’cifukwa coganiza kuti kusakondwelela kwathu kungabweletse magaŵano ku nchitoko? Tingam’khazike mtima pansi mwa kumuyamikila cifukwa coganizila ena na kum’fotokozela kuti nafenso timasangalala kugwila nchito pamalo pamene anthu ake ni ogwilizana. Izi zingatipatse mwayi womufotokozela mwaubwenzi zimene Baibo imakamba pa masiku akubadwa.
12 Tingacite zofananako wina akatifunsa funso lovuta. Mnzanu wa m’kalasi anganene kuti Mboni za Yehova ziyenela kusintha kapenyedwe kawo pa mcitidwe wa mathanyula. Kodi izi zionetsa kuti sadziŵa zenizeni ponena za zimene Mboni za Yehova zimakhulupilila pa nkhaniyi? Kapena kodi zionetsa kuti ali na mnzake kapena wacibale amene ni wa mathanyula? Kodi amaona kuti tilibe cikondi pa anthu amene amacita mathanyula? Tingafunike kum’tsimikizila kuti timakonda anthu onse, ndiponso kuti timalemekeza ufulu wa aliyense wodzisankhila zocita. b (1 Pet. 2:17) Izi zingapeleke mpata wom’fotokozela mfundo za m’Baibo zopindulitsa.
13. Kodi mungam’thandize bwanji munthu amene amatsutsa cikhulupililo cathu mwa Mulungu?
13 Munthu akatsutsa cikhulupililo cathu mwamphamvu, tisamafulumile kuganiza kuti tidziŵa zonse zimene amakhulupilila. (Tito 3:2) Mwacitsanzo, mungatani ngati mnzanu wa ku sukulu wanena kuti n’kupanda nzelu kukhulupilila Mulungu? Kodi muyenela kuganiza kuti amacikhulupilila kwambili ciphunzitso ca cisanduliko ndipo amacidziŵa bwino? Kwenikweni, angakhale kuti sanaiganizilepo mwakuya nkhaniyi. M’malo mokangana naye pa nkhani ya cisanduliko, mungamuuze mfundo yoti aiganizile. Mwina mungamuonetse nkhani za cilengedwe pa jw.org. N’kutheka kuti pa nthawi ina angakhale wofunitsitsa kukambilana nkhani kapena vidiyo imene anapeza. Inde, kukambilana naye mwaulemu kungacititse kuti aunikenso maganizo ake.
14. Kodi Niall anaseŵenzetsa bwanji webusaiti yathu pothandiza mnzake wa m’kalasi kuthetsa maganizo olakwika pa Mboni za Yehova?
14 Mnyamata wina dzina lake Niall, anagwilitsa nchito webusaiti yathu poonetsa ena kuti zimene amakhulupilila ponena za Mboni za Yehova si zoona. Iye anati, “Nthawi zambili mnzanga wa m’kalasi anali kuniuza kuti sinikhulupilila sayansi imene imakamba zenizeni cifukwa nimakhulupilila ‘buku lodzala na nthano.’” Mnzakeyo atakana kuti Niall amufotokozele za cikhulupililo cake, Niall anamuuza kuti aone pa jw.org pa danga yakuti “Baibulo Komanso Sayansi.” Pambuyo pake, iye anazindikila kuti mnzakeyo anaiŵelenga nkhaniyo ndipo anali wofunitsitsa kukambilana za ciyambi ca moyo. Inunso mungakhale na zotulukapo zabwino monga izi.
KONZEKELANI MONGA BANJA
15. Kodi makolo angathandize bwanji ana awo kuyankha mofatsa anzawo a kusukulu akatsutsa cikhulupililo cawo?
15 Makolo angaphunzitse ana awo mmene angayankhile modekha cikhulupililo cawo cikatsutsidwa. (Yak. 3:13) Makolo ena amasankha kuyeseza pa kulambila kwa pa banja mmene angayankhile modekha. Amasankha nkhani zimene zingabuke ku sukulu na kuzikambilana. Kenako amacita citsanzo na kuphunzitsa ana awo mmene angayankhile modekha komanso mofika pa mtima.—Onani bokosi lakuti “ Kuyeseza Kungathandize Banja Lanu.”
16-17. Kodi kuyeseza kungawathandize bwanji acicepele?
16 Kuyeseza kungathandize Akhristu kupeleka mayankho okhutilitsa. Kungawathandizenso kutsimikizila paokha kuti zimene amakhulupilila ni coonadi. Nkhani zakuti “Zimene Acinyamata Amafunsa” pa jw.org ku Chichewa, zili na mbali yakuti zoti achinyamata achite. Mbali imeneyi, inakonzedwa kuti ithandize acinyamata kulimbitsa cikhulupililo cawo, na kuwathandiza kukhala okonzeka kuyankha anthu m’mawu awo-awo. Mwa kuŵelenga nkhanizi monga banja, tonse tingaphunzile kukhalila kumbuyo cikhulupililo cathu mofatsa.
17 Mnyamata wina dzina lake Matthew, anafotokoza mmene kuyeseza kunam’thandizila. Pa kulambila kwawo kwa pabanja, iye na makolo ake nthawi zambili anali kufufuza nkhani zimene zingabuke m’kalasi. Iye anati: “Timaganizila mafunso osiyanasiyana amene angakhalepo, ndipo timayeseza mmene tingawayankhile malinga na zimene tafufuza. Nikakhala na cifukwa comveka cokhulupilila zinazake, nimakhala na cidalilo ndipo nimakhala wofatsa pocita zinthu na ena.”
18. Kodi Akolose 4:6 ionetsa kufunika kwa ciyani?
18 Kufotokoza zinthu mosavuta pakokha sikokwanila kuti tiwafike pa mtima anthu ena. Koma kufotokoza zinthu mwaluso komanso mofatsa kungathandize. (Ŵelengani Akolose 4:6.) Kufotokozela wina cikhulupililo cathu tingakuyelekezele na kuponya mpila. Tingauponye mwacikondi kapena mwamphamvu. Tikauponya mwacikondi, amene tikuseŵela naye akhoza kuugwila na kupitiliza kuseŵela. Mofananamo, tikafotokoza cikhulupililo cathu mwaluso komanso mofatsa, anthu angakhale ofunitsitsa kumvetsela na kupitiliza makambilano. Komabe, ngati munthu angofuna kukangana nafe, kapena kutinyodola pa cikhulupililo cathu, sitiyenela kupitiliza makambilanowo. (Miy. 26:4) Koma ni anthu ocepa cabe amene angacite zimenezi, ambili angakhale ofunitsitsa kumvetsela.
19. N’ciyani ciyenela kutilimbikitsa kukhala ofatsa poteteza cikhulupililo cathu?
19 N’zoonekelatu kuti kudziikila colinga cokhala wofatsa kuli na mapindu ambili. Muzipemphela kwa Yehova kuti akupatseni mphamvu zofunikila kuti mukhalebe ofatsa poyankha anthu otsutsa kapena onyodola. Kumbukilani kuti kukhala wofatsa kungathandize kuti kusiyana maganizo kusakule n’kukhala mkangano. Ndipo kuyankha kwanu mofatsa kungalimbikitse anthu ena kusintha kapenyedwe kawo pa ife komanso pa coonadi ca m’Baibo. “Khalani okonzeka nthawi zonse” kuteteza cikhulupililo canu. “Koma ayankheni ndi mtima wofatsa ndiponso mwaulemu kwambili.” (1 Pet. 3:15) Inde, pangani kufatsa kukhala khalidwe lanu lalikulu!
NYIMBO 88 N’dziŵitseni Njila Zanu
a Nkhani ino ipeleka malingalilo a mmene tingakhalile kumbuyo cikhulupililo cathu mofatsa anthu ena akatiputa kapena akatitsutsa.
b Kuti mudziŵe zambili, onani nkhani yakuti “Kodi Baibulo Limalola kuti Akazi Kapena Amuna Okhaokha Azigonana?” Mu Galamukani! ya Chichewa ya Na. 4 2016.
c Mungapeze malingalilo othandiza pa jw.org mu mpambo wa nkhani zakuti, “Zimene Acinyamata Amafunsa” komanso zakuti “Mafunso Amene Amafunsidwa Kaŵili-kaŵili Ponena za Mboni za Yehova.”