Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mfundo Yothandiza pa Kufufuza Kwanu

Mfundo Yothandiza pa Kufufuza Kwanu

Zida Zophunzitsila Ana

Makolo ali na udindo waukulu wophunzitsa ana awo za Yehova. (Aef. 6:4) Pofuna kuwathandiza, gulu la Yehova lafalitsa zida zambili. Kodi mungaziseŵenzetse motani pophunzitsa ana anu?

  • Pitani pa JW.ORG. pamenepo, mudzapezapo zofalitsa zonse zimene anakonzela ana, kuphatikizapo mavidiyo, na nkhani zoŵelenga. a Kuti muzipeze, lembani mau akuti “Ana” kapena “Acinyamata” m’danga lofufuzila.

  • Sankhani zothandiza. Pansi pa kamutu kakuti “Ana,” mungasankhe nkhani, mavidiyo na nyimbo zimene muona kuti n’zothandiza kwambili kwa ana anu. Kuti muzipeze, lembani mau akuti “Zochita pa Kulambila kwa Pabanja” m’danga lofufuzila ku Chichewa.

  • Kambilanani nawo. Pewani kuseŵenzetsa mavidiyo, kapena nkhani zoŵelenga monga zinthu zotangwanitsila mwana wanu akasoŵa zocita. Koma kambilanani naye nkhanizo, na kum’thandiza kukhala pa ubale wolimba na Yehova.

a Palipano, JW Library® ili na mavidiyo ambili a ana m’Cinyanja, koma ili na nkhani zoŵelenga zocepa cabe.