NKHANI YOPHUNZILA 37
Muzidalila Yehova Mmene Samisoni Anacitila
“Yehova Ambuye Wamkulu Koposa, conde, ndikumbukileni ndi kundipatsa mphamvu.”—OWER. 16:28.
NYIMBO 30 Tate Wanga, Mulungu Wanga, Bwenzi Langa
ZIMENE TIKAMBILANE a
1-2. N’cifukwa ciyani nkhani ya Samisoni tiyenela kucita nayo cidwi?
N’CIYANI cimabwela m’maganizo mwanu mukamva dzina lakuti Samisoni? Ngati mumaganizila za mwamuna wamphamvu zodabwitsa, simunaphonye. Koma Samisoni anapanga cisankho coipa cimene pambuyo pake cinam’bweletsela mavuto aakulu kwambili. Ngakhale n’conco, Yehova anayang’ana pa kukhulupilika kumene Samisoni anaonetsa pom’tumikila. Anaonetsetsanso kuti nkhani yake yalembedwa m’Baibo kuti itipindulile.
2 Yehova anaseŵenzetsa Samisoni kucita zinthu zodabwitsa kuti athandize anthu ake osankhidwa Aisiraeli. Patapita zaka mahandiledi Samisoni atamwalila, Yehova anauzila mtumwi Paulo kuti aphatikize dzina la Samisoni pa mndandanda wa maina a anthu a cikhulupililo colimba. (Aheb. 11:32-34) Citsanzo ca Samisoni cingatilimbikitse. Iye anadalila Yehova ngakhale panthawi zovuta. M’nkhani ino, tikambilane zimene tingaphunzile kwa Samisoni, komanso mmene citsanzo cake cingatilimbikitsile.
SAMISONI ANADALILA YEHOVA
3. Kodi Samisoni anapatsidwa utumiki wotani?
3 Pamene Samisoni anabadwa, Afilisiti ndiwo anali kulamulila Aisiraeli mowapondeleza. (Ower. 13:1) Ulamulilo wawo wankhanza unabweletsa mavuto ambili kwa Aisiraeli. Yehova anasankha Samisoni kuti ‘akhale patsogolo populumutsa Aisiraeli m’manja mwa Afilisiti.’ (Ower. 13:5) Unali utumiki wovuta kwambili! Kuti aukwanilitse, Samisoni anafunika kudalila Yehova.
4. Kodi Yehova anam’thandiza bwanji Samisoni kuti adzipulumutse m’manja mwa Afilisiti? (Oweruza 15:14-16)
4 Onani citsanzo ca mmene Samisoni anaonetsela cidalilo cake mwa Yehova komanso pa thandizo lake. Panthawi ina, asilikali Acifilisiti anabwela kuti adzagwile Samisoni ku Lehi komwe mwina ni ku Yuda. Amuna a ku Yuda anacita mantha, conco anapeleka Samisoni m’manja mwa Afilisiti. Anthu a mtundu wake anam’manga na zingwe ziŵili zatsopano, ndipo anam’peleka m’manja mwa Afilisiti. (Ower. 15:9-13) Komabe, “mzimu wa Yehova unayamba kugwila nchito pa iye,” ndipo Samisoni anadula zingwezo. “Zitatelo, anapeza fupa laliŵisi la nsagwada za bulu wamphongo, n’kukantha nalo amuna 1,000” Acifilisiti!—Ŵelengani Oweruza 15:14-16.
5. Kodi Samisoni anaonetsa bwanji kuti anali kudalila Yehova?
5 N’cifukwa ciyani Samisoni anaseŵenzetsa fupa la nsagwada za bulu, cimene sicinali cida comenyela nkhondo? Mosakaikila, Samisoni anadziŵa kuti Yehova angamuthandize kugonjetsa Afilisiti, mosasamala kathu za cida cimene angaseŵenzetse. Inde, mwamuna wokhulupilikayu anangoseŵenzetsa cimene cinali pafupi kuti akwanilitse cifunilo ca Yehova. N’zoonekelatu kuti kudalila Yehova n’kumene kunapangitsa kuti Samisoni apeze cipambano cacikulu!
6. Kodi tingaphunzile ciyani kwa Samisoni pamene tikucita utumiki wathu?
6 Nafenso, Yehova angatilimbikitse kuti tikwanilitse utumiki wathu, ngakhale uoneke wovuta. Iye angacite zimenezi m’njila imene sitikuiyembekezela. Khalani na cidalilo kuti Yehova amene anathandiza Samisoni angakuthandizeni inunso kucita cifunilo cake ngati mudalila thandizo lake.—Miy. 16:3.
7. Fotokozani citsanzo coonetsa kufunika kotsatila citsogozo ca Yehova.
7 Abale na alongo ambili amene ali mu utumiki wa zamamangidwe aonetsa kuti amadalila Yehova. M’zaka zakumbuyoku, abalewa ndiwo anali kupanga mapulani na kumanga Nyumba za Ufumu zatsopano, komanso zimango zina. Komabe, cifukwa cakuti gulu la Yehova linali kukulila-kulila, panafunikila kupanga masinthidwe. Abale oyang’anila anapempha citsogozo ca Yehova pa nkhaniyi na kuyesa njila zatsopano, monga kugula zimango zotha kale na kuzikonzanso. M’bale Robert watumikila pa nchito zambili zamamangidwe za gulu lathu m’zaka zaposacedwa. Iye anati: “Poyamba zinali zovuta kwa ena kuvomeleza masinthidwe amenewa.” Anapitiliza kuti: “Izi zinali zosiyana kwambili na zimene takhala tikucita kwa zaka zambili. Koma abale anali okonzeka kusintha, ndipo umboni waonetsa kuti Yehova akudalitsa makonzedwe amenewo.” Ici n’citsanzo cimodzi cabe ca mmene Yehova akutsogolela anthu ake kuti akwanilitse cifunilo cake. Nthawi na nthawi, tonsefe tingacite bwino kumadzifunsa kuti, ‘Kodi nimaona citsogozo ca Yehova na kuyesetsa kupanga masinthidwe kuti nimutumikile m’njila yabwino koposa?’
SAMISONI ANASEŴENZETSA BWINO ZIMENE YEHOVA ANAMUGAŴILA
8. Kodi Samisoni anatani panthawi ina atamva ludzu?
8 Mwina mukumbukila zodabwitsa zimene Samisoni anacita. Ali yekha anakhadzula mkango, ndipo anapha amuna 30 mu mzinda wa Afilisiti wa Asikeloni. (Ower. 14:5, 6, 19) Samisoni anadziŵa kuti sakanatha kucita zinthu zimenezi popanda thandizo la Yehova. Izi zinaonekela bwino pamene Samisoni anamva ludzu pambuyo pa kupha Afilisiti 1,000. Kodi iye anatani? M’malo modzidalila, iye anafuulila Yehova kuti amuthandize.—Ower. 15:18.
9. Kodi Yehova analiyankha bwanji pemphelo la Samisoni? (Oweruza 15:19)
9 Yehova anayankha pempho la Samisoni. Motani? Mozizwitsa, anam’pangila kasupe watsopano wa madzi. Samisoni atamwa madziwo, “anapezanso mphamvu ndi kutsitsimulidwa.” (Ŵelengani Oweruza 15:19) Mwacionekele, kasupe ameneyu anakhalapobe kwa zaka ngakhale pamene mneneli Samueli anauzilidwa kulemba buku la Oweruza. N’kutheka kuti Aisiraeli amene anaona kasupeyo, anali kukumbukila kuti atumiki okhulupilika a Yehova akhoza kum’dalila akakhala pa mavuto.
10. Kodi tiyenela kucita ciyani kuti tilandile thandizo locokela kwa Yehova? (Onaninso cithunzi.)
10 Nafenso tiyenela kudalila thandizo la Yehova mosasamala kanthu za maluso athu, kapena zimene takwanitsa kucita mu utumiki wake. Modzicepetsa, tiyenela kuvomeleza kuti cipambano ceniceni tingacipeze kokha mwa thandizo la Yehova. Monga mmene Samisoni anapezela mphamvu atamwa madzi amene Yehova anam’patsa, nafenso tingapeze mphamvu mwauzimu ngati tiseŵenzetsa zogaŵila zonse zimene Yehova amapeleka kwa ife.—Mat. 11:28.
11. Tingaonetse bwanji kuti timadalila thandizo la Yehova? Fotokozani citsanzo.
11 Ganizilani citsanzo ca m’bale Aleksey, mmodzi wa abale athu ku Russia amene akupilila mazunzo aakulu. N’ciyani cam’thandiza kukhalabe wolimba pa mikhalidwe yovuta kwambili? Iye na mkazi wake amacita zinthu zauzimu nthawi zonse. Iye ananena kuti: “Nimayesetsa kutsatila ndandanda yanga yocita phunzilo la munthu mwini komanso kuŵelenga Baibo tsiku lililonse. M’mawa uliwonse ine na mkazi wanga timakambilana lemba la tsiku na kupemphela kwa Yehova capamodzi.” Kodi tiphunzilapo ciyani? M’malo modzidalila, tiyenela kudalila Yehova. Motani? Mwa kulimbikitsa cikhulupililo cathu pophunzila Baibo nthawi zonse patokha, komanso kucita zinthu zina zauzimu. Tikatelo, Yehova adzadalitsa khama lathu pom’tumikila. Nafenso angatipatse mphamvu monga anacitila kwa Samisoni.
SAMISONI SANAFOOKE
12. N’cisankho colakwika citi cimene Samisoni anapanga? Nanga kodi cibwenzi cake na Delila cinasiyana bwanji na zibwenzi zina zoyamba?
12 Samisoni nayenso anali wopanda ungwilo. Conco, anapangapo zisankho zolakwika. Panthawi ina, anapanga cisankho cimene cinam’bweletsela mavuto aakulu. Atatumikila monga woweluza kwa kanthawi, “Samisoni anayamba kukonda mkazi wina ku cigwa ca Soreki, ndipo dzina lake anali Delila.” (Ower. 16:4) Kumbuyoko, Samisoni anali atatomela mkazi wina Mfilisiti. “Yehova ndi amene anali kucititsa zimenezi,” kuti apeleke ‘mpata kwa Samisoni kuti amenyane ndi Afilisiti.’ Patapita nthawi Samisoni anapita kukakhala ku nyumba kwa hule inayake mu mzinda wa Afilisiti ku Gaza. Pa cocitikaci, Mulungu anapatse Samisoni mphamvu zoti azule zipata za mzindawo, izi zinapangitsa kuti mzindawo ukhale wosatetezeka. (Ower. 14:1-4; 16:1-3) Koma cocitika ca Delila cinali cosiyanako cifukwa mwacionekele iye anali Mwisiraeli.
13. Kodi Delila anacita ciyani kwa Samisoni?
13 Delila anavomela kulandila ndalama zambili kucokela kwa Afilisiti kuti apeleke Samisoni m’manja mwawo. N’kutheka kuti cikondi cake Samisoni pa Delila cinam’phimba m’maso moti sanazindikile colinga ca mkaziyo. Mulimonsemo, mobweleza-bweleza Delila anapanikiza Samisoni kuti amuuze cinsinsi ca mphamvu zake, ndipo pothela pake Samisoni anaulula. N’zacisoni kuti zimene Samisoni anacita zinapangitsa kuti mphamvu zake zithe, komanso kuti ataye ciyanjo ca Yehova kwa kanthawi.—Ower. 16:16-20.
14. Nanga Samisoni anakumana na mavuto otani cifukwa cokhulupilila Delila?
14 Samisoni anakumana na mavuto aakulu cifukwa cokhulupilila Delila m’malo mwa Yehova. Afilisiti anam’gwila Samisoni na kumuboola maso. Anamuika m’ndende ku Gaza, mzinda umene anali atagonjetsa mounyazitsa, ndipo anakhala woyendetsa mwala wamphelo m’ndendemo. Kenako Afilisiti anamunyazitsa pamene anali kucita cikondwelelo. Iwo anapeleka nsembe yaikulu kwa mulungu wawo wonyenga Dagoni, ngati kuti iye ni amene anapeleka Samisoni m’manja mwawo. Anam’bweletsa ku cikondweleloco ‘kuti adzawasangalatse’ mwa kum’panga coseketsa.—Ower. 16:21-25.
15. Kodi Samisoni anaonetsa bwanji kuti anayambilanso kudalila Yehova? (Oweruza 16:28-30) (Onani Cithunzi pacikuto.)
15 Ngakhale kuti Samisoni anapanga colakwa cacikulu, sanafooke. Iye anali kufuna-funa mpata kuti akwanilitse nchito imene Mulungu anamupatsa yogonjetsa Afilisiti. (Ŵelengani Oweruza 16:28-30.) Iye anacondelela Yehova kuti: “Ndiloleni ndiwabwezele Afilisiti.” Mulungu woona anayankha pemphelo la Samisoni pobwezeletsa mphamvu zake zapadela. Conco pa tsikulo Samisoni anapha Afilisiti ambili kuposa amene anawapha mu umoyo wake wonse.
16. Tingaphunzilenji pa colakwa ca Samisoni?
16 Ngakhale kuti Samisoni anakumana na mavuto aakulu cifukwa ca colakwa cake, iye sanaleke kuyesetsa kucita cifunilo ca Yehova. Nafenso tikalakwitsa zina zake, kenako n’kudzudzulidwa kapena kucotsedwa paudindo, sitiyenela kuleka kuyesetsa kucita cifunilo ca Yehova. Musaiŵale kuti Yehova ni okonzeka kutikhululukila. (Sal. 103:8-10) Monga zinalili kwa Samisoni, nafenso Yehova angadzapitilize kutigwilitsa nchito ngakhale titalakwitsa zina zake.
17-18. Kodi citsanzo ca Michael cakulimbikitsani motani? (Onaninso cithunzi.)
17 Onani zinacitikila m’bale wina wacinyamata dzina lake Michael. Anali wokangalika pa zinthu zauzimu, ndipo anali kutumikila monga mtumiki wothandiza komanso mpainiya wa nthawi zonse. N’zacisoni kuti analakwitsa zina zake zimene zinapangitsa kuti ataye mwayi wa mautumiki amenewo. Michael anati: “Kumbuyo konseku, zinthu zinali kuniyendela bwino kwambili mu utumiki wanga kwa Yehova. Koma mosayembekezela, ndinamva ngati zonse zaima. N’nadziŵa kuti Yehova sanganisiye, koma n’nali kudzifunsabe ngati ubwenzi wanga na iye ungadzakhalenso mmene unali poyamba, komanso ngati ningadzatumikilenso mu mpingo monga mmene n’nali kucitila kale.”
18 N’zokondweletsa kuti Michael sanabwelele m’mbuyo. Iye anawonjezele kuti: “N’naika maganizo anga pa kukonza ubwenzi wanga na Yehova mwa kupemphela mocokela pansi pa mtima, kucita phunzilo la munthu mwini, komanso kusinkhasinkha.” M’kupita kwa nthawi, Michael anakhalanso na kaimidwe kabwino mu mpingo. Ndipo lomba akutumikila monga mkulu komanso mpainiya wanthawi zonse. Ananenanso kuti: “Thandizo na cilimbikitso zimene n’nalandila makamaka kucokela kwa akulu, zinandithandiza kuona kuti Yehova anali kunikondabe. Pali pano nikutumikilanso mu mpingo na cikhumbumtima coyela. Cocitikaci caniphunzitsa kuti Yehova ni wokonzeka kukhululukila amene walapadi.” Tisakaikile zakuti Yehova angatigwilitsenso nchito na kutidalitsa ngakhale titalakwitsa zina zake, malinga ngati tiyesetsa kukonza zimene tinalakwitsazo, na kupitiliza kum’dalila.—Sal. 86:5; Miy. 28:13.
19. Kodi citsanzo ca Samisoni cakulimbikitsani bwanji?
19 M’phunzilo lino, takambilana zocitika zingapo zocititsa cidwi mu umoyo wa Samisoni. Sanali wangwilo, koma ngakhale n’telo sanafooke potumikila Yehova ngakhale pamene analakwitsa zina zake. Yehova anam’gwilitsanso nchito mwa kum’patsanso mphamvu zapadela. Yehova anamuonabe kuti anali munthu wa cikhulupililo colimba, ndipo anam’phatikiza pa mndandanda wa anthu okhulupilika ochulidwa mu Aheberi caputala 11. N’zolimbikitsa kwambili kudziŵa kuti Atate wathu wacikondi amene tikum’tumikila, amafunitsitsa kutilimbikitsa maka-maka pamene tafooka! Conco monga anacitila Samisoni, tizimucondelela Yehova kuti: “Conde, ndikumbukileni ndi kundipatsa mphamvu.”—Ower. 16:28.
NYIMBO 3 Ndimwe Mphamvu Zathu, Ciyembekezo, na Cidalilo Cathu
a Samisoni ni dzina la munthu wa m’Baibo amene ni wodziŵika kwambili ngakhale kwa anthu osadziŵa zambili za m’Baibo. Nkhani yake aifotokozapo m’maseŵelo, nyimbo komanso m’mafilimu. Ngakhale n’telo, nkhaniyi si nthano cabe. Tingaphunzile zambili kwa mwamuna wa cikhulupililo ameneyu.