Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 41

Zimene Tingaphunzile M’makalata Aŵili a Petulo

Zimene Tingaphunzile M’makalata Aŵili a Petulo

“Nthawi zonse ndizikukumbutsani zinthu zimenezi.”—2 PET. 1:12.

NYIMBO 127 Mtundu wa Munthu Amene Niyenela Kukhala

ZIMENE TIKAMBILANE a

1. Cakumapeto kwa moyo wake, kodi Petulo anauzilidwa kulemba ciyani?

 Mtumwi Petulo anatumikila Yehova mokhulupilika kwa zaka zambili. Anatsagana na Yesu pa nchito yake yaulaliki. Anayambitsa nchito yolalikila kwa anthu a mitundu ina, ndipo anatumikila mu bungwe lolamulila. Koma sizokhazo, ca m’ma 62 kapena 64 C.E., Yehova anauzila Petulo kulemba makala aŵili a m’Baibo—yomwe ni 1 na 2 Petulo. Iye anali na ciyembekezo cakuti makalatawo adzathandiza Akhristu pambuyo pa imfa yake.—2 Pet. 1:​12-15.

2. N’cifukwa ciyani tinganene kuti makalata a Petulo anali a panthawi yake?

2 Petulo analemba makalatawa, panthawi imene okhulupilila anzake anali ‘acisoni cifukwa ca mayeso osiyana-siyana.’ (1 Pet. 1:6) Aneneli onyenga anafuna kubweletsa ziphunzitso zabodza komanso makhalidwe oipa mu mpingo wa Cikhristu. (2 Pet. 2:​1, 2, 14) Akhristu amene anali kukhala mu Yerusalemu posakhalitsa anali kudzaona “mapeto a zinthu zonse”—zomwe zinaphatikizapo kuwonongedwa kwa mzindawo na asilikali Aciroma, komanso kuthetsedwa kwa dongosolo la Ciyuda. (1 Pet. 4:7) Mosakaikila, makalata a Petulo anathandiza Akhristu kuona zimene angacite kuti apilile mayeso a panthawiyo komanso amtsogolo. b

3. N’cifukwa ciyani tifunika kukambilana makalata ouzilidwa a Petulo?

3 Ngakhale kuti Petulo analembela Akhristu oyambilila makalatawo, Yehova anawaika m’Mawu Ake kuti nafenso tipindule nawo. (Aroma 15:4) Nafenso tikukhala m’dziko limene limalimbikitsa makhalidwe oipa, ndipo timakumananso na mavuto amene amacititsa kuti zikhale zovuta kutumikila Yehova. Kuwonjezela apo, posacedwa tidzakumana na cisautso cimene ni cacikulu kuposa cimene Ayuda anakumana naco. Timapeza zikumbutso zofunika mu makalata aŵili a Petulo, zimene zimatithandiza kuyembekezelabe tsiku la Yehova, kupewa kuopa anthu na kulimbitsa cikondi cathu pa wina na mnzake. Zikumbutso zimenezi zingathandizenso akulu kuona mmene angasamalile zosoŵa za nkhosa.

MUZIYEMBEKEZELABE

4. Malinga na 2 Petulo 3:​3, 4, n’ciyani cingaike cikhulupililo cathu pangozi?

4 Tikukhala m’dziko mmene anthu ambili sakhulupilila zimene Baibo imakamba ponena za mtsogolo. Otsutsa angamatiseke cifukwa takhala tikuyembekezela mapeto kwa zaka zambili. Anthu ena amanena kuti mapeto sadzafika. (Ŵelengani 2 Petulo 3:​3, 4.) Cikhulupililo cathu cingakhale pangozi, ngati tamvela mawu aconco kucokela kwa mwini nyumba, anzathu a ku nchito, kapena anthu a m’banja lathu. Petulo anafotokoza zimene zingatithandize.

5. N’ciyani cingatithandize kuyembekezela moleza mtima mapeto a dongosolo lino la zinthu? (2 Petulo 3:​8, 9)

5 Kwa ena zingaoneke ngati Yehova akucedwa kuthetsa dongosolo loipali la zinthu. Mawu a Petulo angatithandize kukhala na kaonedwe koyenela, amatikumbutsa kuti Yehova amaona nthawi mosiyana kwambili ndi anthu. (Ŵelengani 2 Petulo 3:​8, 9.) Kwa Yehova, zaka 1000 zili ngati tsiku limodzi. Yehova ni woleza mtima, safuna kuti wina aliyense akawonongeke. Ngakhale n’telo pa tsiku lake loikika adzawononga dongosolo loipali. Uyu ni mwayi wathu wogwilitsa nchito nthawi yotsalayi kulalikila uthenga wabwino kwa anthu a mitundu yonse.

6. Kodi tingaonetse bwanji kuti ‘nthawi zonse timakumbukila’ tsiku la Yehova? (2 Petulo 3:​11, 12)

6 Petulo anatilimbikitsa kuti ‘nthawi zonse tidzikumbukila’ tsiku la Yehova. (Ŵelengani 2 Petulo 3:​11, 12.) Tingacite zimenezi mwa kusinkhasinkha za madalitso a m’dziko latsopano nthawi zonse. Muziyelekezela kuti muli m’dziko latsopano mukupuma kamphepo kabwino, mukudya zakudya zopatsa thanzi, mukulandilanso okondedwa anu amene anamwalila. Komanso mukuphunzitsa anthu amene anakhalako zaka zambili m’mbuyomu za kukwanilitsidwa kwa maulosi a m’Baibo. Kusinkhasinkha zimenezi kudzakuthandizani kuyembekezela mwacidwi nthawiyo na kukhala otsimikiza kuti mapeto a dzikoli ali pafupi. Conco popeza ‘tikudziŵilatu’ zimenezi ponena zatsogolo lathu, ‘sitidzasoceletsedwa’ na aphunzitsi onyenga.—2 Pet. 3:17.

MUSAMAOPE ANTHU

7. Kodi kuopa anthu kungatikhuze motani?

7 Cifukwa cakuti tidziŵa kuti tsiku la Yehova lili pafupi, timalimbikitsidwa kulalikila uthenga wabwino. Ngakhale n’telo, nthawi zina zimativuta kulalikila cifukwa coopa anthu. Izi zinamucitikilapo Petulo. Usiku umene Yesu anali kuzengedwa mlandu, Petulo anaopa kuzidziŵikitsa kuti anali mmodzi mwa ophunzila a Yesu, ndipo katatu konse anakana kuti sanali kumudziŵa Yesu. (Mat. 26:​69-75) Patapita nthawi, mtumwiyu ananena motsimikiza kuti: “Musaope zimene iwo amaopa, ndipo musade nazo nkhawa.” (1 Pet. 3:14) Mawu a Petulo amenewa amatitsimikizila kuti tingagonjetse mantha oopa anthu.

8. Tingawagonjetse motani mantha oopa anthu? (1 Petulo 3:15)

8 N’ciyani cingatithandize kugonjetsa mantha oopa anthu? Petulo anati: “Vomelezani m’mitima mwanu kuti Khristu ndi Ambuye.” (Ŵelengani 1 Petulo 3:15.) Izi ziphatikizapo kusinkhasinkha za udindo na mphamvu za Ambuye na Mfumu yathu, Khristu Yesu. Mukacita mantha kuti mulalikile uthenga wabwino mpata ukapezeka, muzikumbukila Mfumu yathu. M’maganizo mwanu muzimuona akulamulila kumwamba atazungulidwa na angelo ambili-mbili. Kumbukilani kuti ali na “ulamulilo wonse kumwamba ndi padziko lapansi” ndiponso kuti ali “pamodzi ndi inu masiku onse mpaka m’nyengo ya mapeto a nthawi ino.” (Mat. 28:​18-20) Petulo anatilimbikitsa kuti ‘tizikhala okonzeka nthawi zonse’ kuikila kumbuyo cikhulupililo cathu. Kodi mungakonde kulalikila ku nchito, ku sukulu, kapena kucita ulaliki wina wa mwayi? Ganizilani tsiku limene mungakonde kucita ulaliki umenewu, ndipo konzekelani zoti mukakambe. Pemphelani kuti mukhale olimba mtima, ndipo khalani na cidalilo kuti Yehova adzakuthandizani kugonjetsa mantha oopa anthu.—Mac. 4:29.

“KHALANI OKONDANA KWAMBILI”

Petulo analandila uphungu wa Paulo. Makalata aŵili a Petulo amatiphunzitsa kuonetsa cikondi abale na alongo athu (Onani ndime 9)

9. Kodi Petulo analephela bwanji kuonetsa cikondi panthawi ina? (Onaninso cithunzi)

9 Petulo anaphunzila moonetsela cikondi. Iye analipo pamene Yesu anati: “Ndikukupatsani lamulo latsopano, kuti muzikondana. Mmene ine ndakukondelani, inunso muzikondana.” (Yoh. 13:34) Patapita nthawi, Petulo anakana kudya na abale na alongo amene sanali Ayuda cifukwa coopa anthu. Mtumwi Paulo anauza Petulo kuti zimene anali kucita zinali “zaciphamaso.” (Agal. 2:​11-14) Petulo analandila uphunguwo ndipo anawongolela. M’makalata ake onse, iye anagogomeza kuti cikondi ceniceni si mmene tikumvela mumtima, koma tiyenela kucionetsa cikondico.

10. Fotokozani cimene cingatithandize kuti ‘tizikondana kwambili’. (1 Petulo 1:22)

10 Petulo anati tifunika ‘kukonda abale mopanda cinyengo.’ (Ŵelengani 1 Petulo 1:22.) Timakhala na cikondi cimeneci cifukwa cokhala “omvela coonadi,” cimene cimaphatikizapo ciphunzitso cakuti “Mulungu alibe tsankho.” (Mac. 10:​34, 35) Sitingamvele lamulo la Yesu lakuti tizikondana ngati timakonda ena mu mpingo na kupewa kukonda ena. Monga mmene zinalili kwa Yesu, nafenso sitingakhale omasuka kwa onse. (Yoh. 13:23; 20:2) Koma Petulo akutikumbutsa kuti tiyenela kuyesetsa ‘kukonda gulu lonse la abale,’ cifukwa ni mbali ya banja lathu.—1 Pet. 2:17.

11. Kodi kukonda ena ‘kwambili kucokela mumtima’ kumaphatikizapo ciyani?

11 Petulo anatilimbikitsa kuti tiyenela ‘kukondana kwambili kucokela mu mtima.’ Palembali, mawu akuti kukonda “kwambili” aphatikizapo kuonetsa cikondi kwa munthu wina ngakhale kuti zingakhale zovuta kucita zimenezo. Mwacitsanzo, ngati m’bale watikhumudwitsa m’njila ina yake, mwacibadwa tingafune kubwezela m’malo moonetsa cikondi. Komabe, Petulo anaphunzila kuti kubwezela sikukondweletsa Mulungu. (Yoh. 18:​10, 11) Petulo analemba kuti: “Osabwezela coipa pa coipa kapena cipongwe pa cipongwe, koma m’malomwake muzidalitsa.” (1 Pet. 3:9) Lolani cikondi kukusonkhezelani kukhala okoma mtima komanso oganizila ena ngakhale kwa amene anakukhumudwitsani.

12. (a) Kodi kukondana kwambili kudzatilimbikitsanso kucita ciyani? (b) Kodi vidiyo yakuti Sungani Mgwilizano Monga Mphatso Yamtengo Wapatali yakulimbikitsani kucita ciyani?

12 M’kalata yake yoyamba, Petulo anaseŵenzetsa mawu ofanana na mawu akuti “kukondana kwambili.” Cikondi cotele, “cimakwilila macimo oculuka.” (1 Pet. 4:8) Mwacionekele Petulo anali kukumbukila zimene anaphunzila kwa Yesu pa nkhani yokhululukila ena zaka zingapo m’mbuyomu. Petulo anaona kuti anali wokoma mtima pamene anapeleka malingalilo akuti ayenela kukhululukila m’bale wake “mpaka nthawi 7.” Koma Yesu anaphunzitsa Petulo kuphatikizapo ife kuti tiyenela kukhululukila ena “mpaka nthawi 77,” kutanthauza mopanda malile. (Mat. 18:​21, 22) Ngati zimakuvutani kutsatila uphungu umenewu, musalefuke! Atumiki onse a Yehova opanda ungwilo, nthawi zina zimawavuta kukhululukila ena. Koma cofunika kwa inu tsopano ni kucita zonse zotheka kuti mukhululukile m’bale wanu na kukhalanso naye pa mtendele. c

AKULU WETANI NKHOSA

13. N’ciyani cingacititse kuti zikhale zovuta kwa akulu kusamalila abale na alongo awo?

13 Mwacidziŵikile Petulo sanaiŵale mawu amene Yesu anamuuza atangoukitsidwa akuti: “Weta ana a nkhosa anga.” (Yoh. 21:16) Ngati ndinu mkulu, mudziŵa kuti malangizo amenewa akupitanso kwa inu. Koma nthawi zina, zingakhale zovuta kwa mkulu kupeza nthawi yosamalila udindo wofunika umenewu. Akulu ayenela kuonetsetsa kuti coyamba akusamalila mabanja awo mwakuthupi, mwauzimu, komanso kuwaonetsa cikondi. Iwo amakhala patsogolo pa nchito yolalikila, pokonzekela na kutsogoza misonkhano ya mpingo komanso ikulu-ikulu. Ena amathandiza makomiti a olankhulana na acipatala, ndipo ena amatumikila mu dipatimenti ya za mamangidwe a gulu. Akulu amakhala otangwanika ngako!

Ngakhale kuti amakhala otangwanika, akulu acikondi amacita zonse zotheka kuti asamalile nkhosa za Mulungu (Onani ndime 14-15)

14. N’ciyani ciyenela kulimbikitsa akulu kuweta gulu la nkhosa? (1 Petulo 5:​1-4)

14 “Petulo analimbikitsa akulu anzake kuti “Wetani gulu la nkhosa za Mulungu.” (Ŵelengani 1 Petulo 5:​1-4.) Ngati ndinu mkulu, tidziŵa kuti mumawakonda abale na alongo ndipo mufuna kuwasamalila. Komabe, nthawi zina mungamadzimve kuti simungakwanitse kusamalila udindo umenewu cifukwa cokhala wotopa kapena wotangwanika kwambili. Ngati zakhala conco, khutulilani Yehova nkhawa zanuzo. Petulo analemba kuti: “Ngati wina akutumikila, atumikile modalila mphamvu imene Mulungu amapeleka.” (1 Pet. 4:11) Abale komanso alongo anu angakumane na mavuto amene sangathetsedwe m’dongosolo lino la zinthu. Koma muzikumbukila kuti Yesu ‘mbusa wamkulu,’ angathe kuwathandiza kuposa wina aliyense. Angakwanitse kucita zimenezi palipano ndiponso m’dziko latsopano. Mulungu amafuna kuti akulu azionetsa cikondi kwa abale awo, kuwaweta komanso kuti akhale “zitsanzo kwa gulu la nkhosa.”

15. Kodi mkulu wina amaweta bwanji nkhosa? (Onaninso cithunzi.)

15 M’bale William amene watumikila monga mkulu kwa zaka zambili, amamvetsa kufunika kwa kucita maulendo a ubusa. Mlili wa COVID-19 utangoyamba, iye na akulu anzake anagwilizana zoti mlungu uliwonse azikambilana na wofalitsa aliyense m’kagulu kake. Pofotokoza cifukwa cake iye anati: “Abale na alongo anali kukhala okha-okha m’nyumba zawo, ndipo cinali capafupi kwa iwo kukhala na maganizo olefula.” Ngati m’bale akukumana na vuto, m’bale William amamvetsela mwacidwi kuti amvetse nkhawa ya m’baleyo komanso zimene akufunikila. Ndipo amapeleka thandizo loyenelela kucokela mu zofalitsa zathu kapena mavidiyo yathu ya pa webusaiti. Iye anati: “Maulendo aubusa ni ofunika kwambili masiku ano kuposa kale lonse. Khama limene timaonetsa pothandiza ena kuphunzila za Yehova, ni limenenso tiyenela kuonetsa pocita maulendo aubusa pothandiza nkhosa za Yehova kukhala m’coonadi.”

LOLANI YEHOVA KUTI AMALIZITSE KUKUPHUNZITSANI

16. Tingaseŵenzetsele motani uphungu umene taphunzila m’makalata a Petulo?

16 Takambilana zocepa pa zimene tingaphunzile ku makalata a Petulo. Mwina mwaona mbali zina zimene mungafunikile kuongolela . Mwacitsanzo, kodi muyenela kumasinkhasinkha kwambili za madalitso a m’dziko latsopano? Kodi mwadziikila colinga kuti mukalalikile ku nchito, kusukulu kapena mu ulaliki wina wa mwai? Kodi mwaona njila zina zimene mungacite kuti muzikonda kwambili abale na alongo anu? Akulu, kodi ndinu okonzeka kuweta gulu la nkhosa la Yehova mofunitsitsa komanso modzipeleka? Kudziunika moona mtima kungakuthandizeni kuti muone pamene muyenela kuongolela, koma musalefuke. “Ambuye ndi wokoma mtima,” ndipo adzakuthandizani kuti muongolele. (1 Pet 2:3) Petulo anatitsimikizila kuti “Mulungu. . . adzamalizitsa kukuphunzitsani. Adzakulimbitsani ndi kukupatsani mphamvu.”—1 Pet 5:10.

17. Padzakhala zotulukapo zotani ngati tiikilapo mtima komanso tilola Yehova kutiphunzitsa?

17 Panthawi ina, Petulo anaziona wosayenela kukhala pamodzi na Mwana wa Mulungu. (Luka 5:8) Koma cifukwa ca thandizo la Yehova komanso la Yesu, anakwanitsa kutsatila Khristu mokhulupilika. Zotsatila zake zinali zakuti Yehova ‘anam’tsegulila khomo kuti aloŵe mwaulemelelo mu ufumu wosatha wa Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu.’ (2 Pet. 1:11) Mphoto yosangalatsa zedi! Ngati mwaikilapo mtima mmene Petulo anacitila komanso kulola Yehova kuti akuphunzitseni, inunso mudzalandila mphoto ya moyo wosatha. Ndipo “cikhulupililo canu cidzacititsa kuti miyoyo yanu ipulumuke.”—1 Pet. 1:9.

NYIMBO 109 Tizikondana ndi Mtima Wonse

a M’nkhani ino tione mmene makalata a Petulo angatithandizile kupilila zovuta. Ithandizenso akulu kuona mmene angakwanilitsile udindo wawo monga abusa.

b Mwina, Akhristu okhala mu Palesitina analandila makalata a Petulo kuukilidwa koyamba kwa Yerusalemu kusanacitike mu 66 C.E.

c Tambani vidiyo yakuti Sungani Mgwilizano Monga Mphatso Yamtengo Wapatali pa jw.org.