Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Johannes Rauthe ali mu ulaliki, mwina ca m’ma 1920

ZA M’NKHOKWE YATHU

“Nikolola Zipatso ndi Kutamanda Yehova”

“Nikolola Zipatso ndi Kutamanda Yehova”

Pofotokoza nkhondo yoyamba ya pa dziko lonse imene inali kucitika ku Ulaya, Nsanja ya Mlonda yacingelezi ya September 1, 1915 inati: “Nkhondo zonse zimene zinacitika m’mbuyomu, zinali zazing’ono kuyelekezela ndi nkhondo imeneyi.” Nkhondoyi inasakaza maiko pafupi-fupi 30. Cifukwa ca mikangano imene inalipo, Nsanja imeneyo inati: “Nchito ya Ufumu yabwelela m’mbuyo makamaka m’maiko a Germany ndi France.”

Pa nthawi ya nkhondo ya pa dziko lonse imeneyo, Ophunzila Baibulo sanamvetsetse mfundo yakuti Akhiristu sayenela kutengako mbali m’nkhondo. Komabe, iwo anali ofunitsitsa kulalikila uthenga wabwino. Pofuna kutengako mbali panchito ya Ufumu, Wilhelm Hildebrandt anaitanitsa tumapepala twauthenga twa masamba anayi tochedwa The Bible Students Monthly m’Cifulenchi. Iye sanali kopotala (mlaliki wa nthawi zonse), koma anali msilikali wacijelemani m’dziko la France. Msilikali ameneyu, amene anali kuonedwa monga mdani, anali kulalikila za mtendele kwa anthu okamba Cifulenchi atavala yunifomu yausilikali. Izi zinadabwitsa anthu amene anali kuwalalikila.

Makalata amene analembedwa mu Nsanja ya Mlonda imeneyo, aonetsa kuti Ophunzila Baibulo acijelemani anali ofunitsitsa kulalikila uthenga wabwino ngakhale kuti anali asilikali. M’bale Lemke, amene anali msilikali wa pamadzi, anapeleka lipoti lakuti anzake asanu anacita cidwi ndi uthenga wabwino. Iye analemba kuti: “Ngakhale kuti ndine msilikali wa pamadzi, nikukolola zipatso ndi kutamanda Yehova.”

Georg Kayser anapita kunkhondo monga msilikali. Koma anabwelela kunyumba ali mtumiki wa Mulungu. N’ciani cinacitika? Ali ku nkhondoko n’kutheka kuti anapeza cofalitsa ca Ophunzila Baibulo na kuciŵelenga. Atamvetsa coonadi, analeka kumenya nkhondo. Ndiyeno, anayamba kugwila nchito imene siinali kukhudzana ndi zausilikali. Pambuyo pa nkhondo, iye anakhala mpainiya wokangalika kwa zaka zambili.

Ngakhale kuti panthawiyo Ophunzila Baibulo sanali kumvetsetsa nkhani ya kusatengako mbali m’nkhondo, zocita zawo zinali kusiyana kwambili ndi za anthu amene anali kucilikiza nkhondo. Atsogoleli andale ndi abusa acipembedzo anali yakali-yakali kucilikiza nkhondo, koma Ophunzila Baibulo anali kulengeza za “Kalonga Wamtendele.” (Yes. 9:6) Ena anaiona mopepuka nkhani ya kusatengako mbali pankhondo. Ngakhale n’conco, anapitiliza kutsatila zimene Wophunzila Baibulo wina dzina lake Konrad Mörtter anali kukhulupilila. Iye anati: “Nazindikila bwino mfundo ya m’Mawu a Mulungu yakuti Mkhiristu sayenela kupha munthu.”—Eks. 20:13 *

Hans Hölterhoff anali kuseŵenzetsa ngolo iyi polengeza za The Golden Age (imene tsopano imachedwa Galamukani!)

M’dziko la Germany, Ophunzila Baibulo oposa 20 anakanilatu kuloŵa usilikali, ngakhale kuti boma linakhwimitsa lamulo lokhudza ufulu wa anthu. Ena anawaganizila kuti acita misala. Mmodzi wa iwo anali Gustav Kujath, amene anapelekedwa ku cipatala ca amisala. Kumeneko anapatsidwa mankhwala a anthu amisala. Hans Hölterhoff nayenso anakana kuloŵa usilikali, ndipo anaikidwa m’ndende. Ali m’ndendemo, anakana kugwila nchito iliyonse yokhudzana ndi nkhondo. Oyang’anila ndende anamuzunza kwambili. Ataona kuti wakana kusintha maganizo ake, anayelekeza monga afuna kumupha. Komabe, Hans anakhalabe wokhulupilika panthawi yonse ya nkhondo.

Abale ena amene anakakamiziwa kuloŵa usilikali, anakana kunyamula zida zankhondo. M’malo mwake, anapempha kuti apatsidwe nchito imene siinali kukhudzana ndi usilikali. * Mwacitsanzo, Johannes Rauthe anapatsidwa nchito yokonza njanji. Konrad Mörtter anamuuza kuti aziseŵenzela kucipatala. Reinhold Weber anapatsidwa nchito ya unesi. August Krafzig, anapatsidwa nchito yosamalila katundu, ndipo anayamikila kwambili nchito imeneyi. Ophunzila Baibulo amenewa ndi enanso ambili anali otsimikiza mtima kutumikila Yehova mokhulupilika cifukwa comukonda.

Cifukwa cakuti Ophunzila Baibulo anakana kuloŵelela m’nkhondo, boma linayamba kuwalonda-londa. Mwacitsanzo, Ophunzila Baibulo m’dziko la Germany anapatsidwa milandu yambili cifukwa colalikila. Pofuna kuwathandiza, ofesi ya nthambi m’dziko la Germany inakhadzikitsa dipatimenti ya zamalamulo pa Beteli mumzinda wa Magdeburg.

M’kupita kwa nthawi, Mboni za Yehova zinasintha kamvedwe kawo pankhani yosatengako mbali m’nkhondo. Pamene nkhondo yaciŵili ya padziko lonse inayamba, iwo sanavomele olo pang’ono kuloŵa usilikali. Pa cifukwa cimeneci, anaonedwa monga adani a Boma la Germany, ndipo anazunzidwa kwambili. Nkhani imeneyi idzafotokozedwa bwino m’nkhani zina za kutsogolo pa mbali yakuti “Za m’Nkhokwe Yathu.”—Za m’nkhokwe yathu ku Central Europe.

^ par. 7 Onani mbili ya Ophunzila Baibulo m’dziko la Britain panthawi ya nkhondo yoyamba ya pa dziko lonse m’nkhani yakuti “Kale Lathu—Anakhalabe Okhulupirika pa ‘Ola la Kuyesedwa.’” Nkhaniyi ipezeka mu Nsanja ya Olonda ya May 15, 2013.

^ par. 9 Malingalilo okhudza kugwila nchitoyi anapelekedwa m’buku lakuti Millennial Dawn Volume 6 (1904) ndi m’magazini ya Zion’s Watch Tower ya August 1906, ya m’Cijelemani. Magazini ya The Watch Tower ya September 1915, inasintha kamvedwe ka mfundo imeneyo, ndipo inafotokoza kuti Ophunzila Baibulo ayenela kupewelatu kuloŵa usilikali. Koma nkhani imeneyi munalibe m’magazini ya Cijelemani.