Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Cikwati—Ciyambi na Cifuno Cake

Cikwati—Ciyambi na Cifuno Cake

“Yehova Mulungu anati: ‘Si bwino kuti munthu [mwamuna] akhale yekha. Ndimupangila womuthandiza, monga mnzake womuyenelela.’”—GEN. 2:18.

NYIMBO: 36, 11

1, 2. (a) Kodi cikwati cinayamba kwanji? (b) N’ciani cimene mwamuna ndi mkazi oyamba anazindikila ponena za cikwati? (Onani cithunzi pamwambapa.)

CIKWATI ni mbali ya umoyo. Tiyeni tikambilane za ciyambi ca cikwati na cifuno cake kuti tikhale na kaonedwe kabwino ka mgwilizano umenewu, ndi kutinso tione madalitso ake. Mulungu atalenga mwamuna woyamba Adamu, anam’patsa nchito yopatsa maina vinyama. Koma Adamu analibe “womuthandiza.” Conco, Mulungu anam’gonetsa tulo tofa nato, n’kumucotsa nthiti imodzi imene anapangila mkazi, na kum’bweletsa kwa iye. (Ŵelengani Genesis 2:20-24.) Mwa ici, cikwati cinacokela kwa Mulungu.

2 Yesu anatsimikizila mau a Yehova akuti: ‘Mwamuna adzasiya atate wake ndi amake, ndi kuphatikana ndi mkazi wake, ndipo aŵiliwo adzakhala thupi limodzi?’ (Mat. 19:4, 5, Buku Lopatulika) Cimene Mulungu anapangila mkazi kucokela ku nthiti ya mwamuna n’kufuna kuti aŵiliwo aone umodzi wawo. Panalibe makonzedwe a kusudzulana kapena kukwatila cipali yayi.

MMENE CIKWATI CIMAKWANILITSILA CIFUNILO CA YEHOVA

3. Kodi cifuno cina cacikulu ca cikwati cinali ciani?

3 Adamu anakondwela kwambili na mkazi wake wokongola, ndipo anamucha dzina lakuti Hava. Pokhala “womuyenelela” wa Adamu, mkaziyo anali ‘wom’thandiza’ wake. Mwa ici, onse aŵili anabweletsa cimwemwe m’banja tsiku ndi tsiku pocita mbali zawo monga mwamuna ndi mkazi. (Gen. 2:18) Cifuno cina cacikulu ca cikwati cinali kubala ana kuti padziko lapansi pakhale anthu. (Gen. 1:28) Ngakhale kuti anawo akanakonda makolo awo, akanafunikila kucoka kuti akayambe mabanja awo-awo. M’kupita kwa nthawi, dziko lapansi likanadzala na ŵanthu pamlingo woyenelela, ndipo akanafutukula paradaiso kufika kumalekezelo a dziko lapansi.

4. Cinacitika n’ciani ndi cikwati coyamba?

4 Cikwati coyamba cinapeza tsoka cifukwa Adamu na Hava anapandukila Yehova pogwilitsila nchito molakwa ufulu wawo wosankha. “Njoka yakale ija,” Satana Mdyelekezi, inanyenga Hava pom’pangitsa kukhulupilila kuti kudya cipatso ca “mtengo wodziŵitsa cabwino ndi coipa” kudzam’patsa nzelu zapadela, cakuti azitha kudzigamulila yekha cabwino ndi coipa. Posayamba wafunsila kwa mwamuna wake, iye ananyozela umutu wa Adamu. Nayenso Adamu m’malo momvela Mulungu, analandila cipatso kwa Hava.—Chiv. 12:9; Gen. 2:9, 16, 17; 3:1-6.

5. Malinga ndi mmene Adamu na Hava anayankhila kwa Yehova, kodi tiphunzilapo ciani?

5 Adamu pofunsidwa na Mulungu, anakankhila mlandu kwa mkazi wake, amvekele: “Mkazi amene munandipatsayu ndi amene wandipatsa cipatso ca mtengowo, ndipo ine ndadya.” A Hava nawonso anakankhila mlandu kwa njoka, kuti ni imene inamunyenga. (Gen. 3:12, 13) Onse anapeleka zifukwa zodzikhululukila, koma zosamveka. Cifukwa cosamvela Yehova, Adamu na Hava anakanidwa na Mulungu monga opanduka. Imeneyi ni cenjezo yamphamvu kwa ife! Kuti cikwati cikhale copambana, aliyense wa aŵiliwo m’banja afunika kucita mbali yake na kumvela Yehova.

6. Kodi mungalifotokoze bwanji lemba la Genesis 3:15?

6 Ngakale kuti Satana anasokoneza zinthu mu Edeni, Yehova anapeleka ciyembekezo kwa mtundu wa anthu mwa ulosi woyamba m’Baibulo. (Ŵelengani Genesis 3:15.) Mulungu anakonza zakuti “mbewu” ya “mkaziyo” ikawononge mngelo woyamba kupanduka ameneyo. Mwa ici, Yehova anaonetsa anthu kuti ali pa unansi wapadela ndi makamu a angelo omutumikila mokhulupilika kumwamba. Malemba anadzavumbulanso kuti Mulungu adzatumiza mmodzi wa m’gulu lakumwamba lili ngati mkazi wake, kuti “akawononge” Mdyelekezi. Komanso kuti ameneyo akapeleke ciyembekezo kwa anthu omvela, cimene makolo oyambilila anataya—inde ciyembekezo ca moyo wamuyaya pa dziko lapansi, malinga ndi zimene Yehova anafuna poyamba.—Yoh. 3:16.

7. (a) Kodi nkhani ya cikwati yakhala ikuyenda bwanji kuyambila pa cipanduko ca Adamu na Hava? (b) Nanga Baibulo imawalangizanji amuna ndi akazi ali pabanja?

7 Kupanduka kwa Adamu na Hava kunabweletsa mavuto aakulu m’banja mwawo, komanso m’mabanja onse am’tsogolo. Mwacitsanzo, Hava anali kuvutika kwambili ndi pakati, komanso popapa. Ni mmenenso zinakhalila kwa akazi onse. Cina, akazi anayamba kukhumba amuna awo, pamene amuna nawonso anayamba kupondeleza akazi awo. Ndipo monga timaonela m’vikwati vambili masiku ano, amuna amacitila nkhanza azikazi awo. (Gen. 3:16) Baibulo imati amuna afunika kucita umutu wawo mwacikondi. Nawonso akazi ayenela kugonjela umutu wa amuna awo. (Aef. 5:33) Ngati a m’cikwati oopa Mulungu akhala mogwilizana, kukwesana m’banja kumacepa, ngakhale kuthelatu.

VIKWATI KUCOKELA PA ADAMU KUDZAFIKA PA CIGUMULA CA NOWA

8. Kodi vikwati vinali bwanji kucokela pa Adamu kudzafika pa Cigumula ca Nowa?

8 Adamu na Hava asanafe cifukwa ca ucimo ndi kupanda ungwilo, anabala ana amuna ndi akazi. (Gen. 5:4) Mwana wawo woyamba, Kaini, anakwatila mkazi wa m’banja mwawo. Ndiponso Lameki, mbadwa yake ya Kaini, ndiye anali woyamba kudziŵika kuti anakwatila akazi aŵili. (Gen. 4:17, 19) Kucokela pa Adamu kudzafika m’masiku a Nowa, ni anthu oŵelengeka cabe amene anali kulambila Yehova. Ena mwa iwo anali Abele, Inoki, Nowa na banja lake. Baibulo imati m’masiku a Nowa, “ana a Mulungu woona anayamba kuona kuti ana aakazi a anthu anali okongola. Cotelo, anayamba kudzitengela okha akazi alionse amene anawasankha.” Vikwati ivi vinali vosemphana ndi cilengedwe. Ndipo ana amene anabadwamo anali vimphona vaciwawa, vochedwa anefili. Komanso, ‘kuipa kwa anthu kunaculuka padziko lapansi’ ndipo “malingalilo onse a m’mitima ya anthu anali oipa okha-okha nthawi zonse.”—Gen. 6:1-5.

9. Kodi Yehova anacita nawo bwanji anthu oipa m’masiku a Nowa? Ndipo titengapo punzilo lanji pa zimene zinacitikazo?

9 Pofuna kuwononga anthu oipawo, Yehova anabweletsa Cigumula ca Nowa. Pa nthawiyo, anthu anali otangwanika ndi zocitika za umoyo wa tsiku ndi tsiku, kuphatikizapo kukwatila ndi kukwatiwa. Mwa ici, anthuwo sanasamale na zimene “Nowa, mlaliki wa chilungamo,” anali kuwacenjeza za ciwonongeko cimene cinali kubwela. (2 Pet. 2:5) Yesu anayelekezela zocitika za pa nthawiyo na zimene tiona masiku ano. (Ŵelengani Mateyu 24:37-39.) Masiku ano, anthu ambili amakana kumvetsela uthenga wabwino wa Ufumu umene ulalikidwa pa dziko lonse lapansi, kupeleka umboni ku mitundu yonse, dongosolo la zinthu lino lisanathe. Tiyeni titengepo phunzilo lakuti, ngakhale nkhani zokhudza banja, monga cikwati kapena kulela ana, zisatiiŵalitse mfundo yakuti tsiku la Yehova lili pafupi kwambili.

VIKWATI KUCOKELA PA CIGUMULA KUDZAFIKA M’NTHAWI YA YESU

10. (a) Ni makhalidwe oipa ati amene anafala kwa anthu ambili? (b) Nanga Abulahamu na Sara anapeleka bwanji citsanzo cabwino m’cikwati cawo?

10 Ngakhale kuti onse, Nowa ndi ana ake atatu, aliyense anali na mkazi mmodzi, anthu anali kukwatila cipali m’nthawi imeneyo Cikhiristu cisanayambe. M’zikhalidwe zambili, zaciwelewele zinangokhala mbali ya umoyo wa anthu, cakuti zinaloŵelela mpaka m’miyambo ina ya cipembedzo. Pamene Abulamu (Abulahamu) na mkazi wake Sarai (Sara), anamvelela Mulungu ndi kusamukila ku Kanani, dzikolo linali lodzala na macitidwe onyoza cikwati. Pa cifukwa cimeneci, Yehova analamula kuti mizinda ya Sodomu na Gomora iwonongedwe. Anthu a m’mizindayo anali kucita zaciwelewele zonyansa kwambili, kapena kuzilekelela. Koma Abulahamu anali kuyang’anila bwino banja lake, ndipo Sara nayenso anali citsanzo cabwino pogonjela umutu wa mwamuna wake. (Ŵelengani 1 Petulo 3:3-6.) Abulahamu anaonetsetsa kuti mwana wake Isake akwatile mkazi wolambila Yehova. Maganizo amenewo ofuna kucilikiza kulambila koona, ni amenenso anali na Yakobo mwana wa Isake, amene ana ake anadzakhala makolo a mafuko 12 a Israeli.

11. Kodi Cilamulo ca Mose cinawateteza bwanji Aisiraeli?

11 M’kupita kwa nthawi, Yehova anacita cipangano ndi ana a Yakobo (Isiraeli). Cikwati m’nthawi imeneyo, kuphatikizapo cipali, cinatsogoleledwa ndi Cilamulo ca Mose. Cilamulo cinateteza Aisiraeli mwauzimu powaletsa kukwatilana ndi anthu a cipembedzo conama. (Ŵelengani Deuteronomo 7:3, 4.) M’banja mukabuka mavuto aakulu, kaŵili-kaŵili akulu anali kupeleka thandizo. Anthu osakhulupilika m’cikwati, a nsanje kwambili, ndi ongokaikila anzawo, anali kupatsidwa cilango. Cisudzulo cinali kuloledwa, koma panali malamulo ake. Mwamuna anali kuloledwa kusudzula mkazi wake cifukwa ca “vuto linalake.” (Deut. 24:1) Ngakhale kuti ‘vuto linalakelo’ sanalichule, mwacionekele silinaphatikizepo zolakwa zing’ono-zing’ono.—Lev. 19:18.

OSAYESA KUCITILA CIWEMBU MNZANU WA M’CIKWATI

12, 13. (a) M’masiku a Malaki, kodi azimuna ena anali kuwacitila motani akazi awo? (b) Ngati masiku ano munthu wobatizika athaŵitsana ndi mkazi kapena mwamuna wa mwiniwake, kodi pamakhala zotsatilapo zanji?

12 M’masiku a mneneli Malaki, azimuna ambili aciyuda anali kucitila ciwembu azikazi awo mwa kuwasudzula pa zifukwa za mtundu uliwonse. Amunawo anali kusiya akazi okula nawo, mwina kuti akwatilenso acitsikana, ngakhale akunja. Pamene Yesu anali pa dziko lapansi, amuna aciyuda anali kusudzula akazi awo mwaciwembu “pa cifukwa ciliconse.” (Mat. 19:3) Kusudzula akazi kumeneko Yehova Mulungu anali kudana nako ngako.—Ŵelengani Malaki 2:13-16.

13 Ngakhale masiku ano, ciwembu ca m’cikwati sicingaloledwe pakati pa anthu a Yehova. Koma bwanji ngati m’bale wobatizika kapena mlongo wathaŵitsana ndi mwamuna kapena mkazi wa mwiniwake n’kukakwatilana, kenako n’kusudzula mnzake wa m’cikwati? Ngati wocimwayo salapa, ayenela kucotsedwa mu mpingo pofuna kusungitsa ciyelo ca mpingo. (1 Akor. 5:11-13) Akalibe kubwezedwa mu mpingo, afunika coyamba aonetse ‘zipatso zosonyeza kuti walapadi.’ (Luka 3:8; 2 Akor. 2:5-10) Palibe nthawi yoikika imene iyenela kupitapo kuti munthu abwezedwe mu mpingo. Ngakhale n’conco, ciwembu ca mtundu umenewu, cimene sicicitika-citika pakati pa anthu a Mulungu, sitingacilekelele. Kuti wocimwayo aonetse umboni wokwana wakuti walapadi zoona, payenela kupita nthawi yokwanila. Ngakhale munthuyo abwezedwe, amakhalabe woŵelengeledwa mlandu ‘ku mpando wa ciweluzo wa Mulungu,’ amene adziŵa bwino ngati kulapa kwake n’kwa zoona kapena ayi.—Aroma 14:10-12; onani Nsanja ya Mlonda ya Cizungu ya November 15, 1979, masa. 31-32.

CIKWATI PAKATI PA AKHIRISTU

14. Kodi Cilamulo cinatumikila mbali iti maka-maka?

14 Umoyo wa Aisiraeli unali kutsogoleledwa ndi Cilamulo ca Mose kwa zaka zopitilila 1,500. Cilamulo cinathandiza anthu a Mulungu kusaiŵala kufunika kwa cilungamo posamalila nkhani za m’banja na zina. Cinalinso monga mlangizi wawo wowatsogolela kwa Mesiya. (Agal. 3:23, 24) Cilamulo citafafanizidwa pa imfa ya Yesu, Mulungu anakhazikitsa makonzedwe atsopano. (Aheb. 8:6) Makonzedwe atsopanowo sanalolenso zina zimene Cilamulo cinali kulolela.

15. (a) Kodi lamulo lokhudza cikwati mu mpingo wacikhiristu n’lakuti ciani? (b) Ngati Mkhiristu alingalila zosudzula mnzake, kodi afunika kuganizila mfundo ziti?

15 Poyankha funso limene Afarisi anafunsa Yesu, iye anati Mose analolela kuti anthu azisudzulana, “koma kuyambila paciyambi sizinali conco ayi.” (Mat. 19:6-8) Motelo, Yesu anaonetsa kuti lamulo la cikwati limene Mulungu anakhazikitsa m’munda wa Edeni liyenela kutsatilidwa mu mpingo wacikhiristu. (1 Tim. 3:2, 12) Pokhala “thupi limodzi,” a m’cikwati afunika kuphatikana pamodzi, ndi kulola cikondi cawo kwa Mulungu ndi kwa wina na mnzake kulimbitsa cikwati cawo. Ngakhale kusudzulana kukhoti, popanda cifukwa ca cigololo, sikungamasule munthu kuti akwatilenso. (Mat. 19:9) Inde, wina angasankhe kukhululukila mnzake wocita cigololo amene walapa, monga mmene mneneli Hoseya anakhululukila mkazi wake waciwelewele, Gomeri. Ngakhalenso mmene Yehova anakhululukila Aisiraeli pamene analapa cigololo cawo cauzimu. (Hos. 3:1-5) Komabe, munthu akadziŵa kuti mnzake wa m’cikwati anacita cigololo, koma n’kugonabe naye, mcitidwe umenewo utanthauza kum’khululukila mzake wocimwayo, ndipo umacotsapo maziko a m’Malemba a cisudzulo.

16. Kodi Yesu anati ciani za kukhala mbeta?

16 Yesu ataunika kuti cisudzulo n’cosaloleka kwa Akhiristu oona popanda cifukwa ca cigololo, anakambanso za “awo ali ndi mphatso” yokhala ndi umoyo waumbeta. Iye anawonjezela kuti: “Amene angathe kucita zimenezi acite.” (Mat. 19:10-12) Ni ambili amene asankha kukhala osakwatila kuti atumikile Yehova ndi maganizo amodzi. Ndipo tiwayamikila kwambili pa kudzipeleka kwawo.

17. N’ciani cingathandize Mkhiristu kusankha kuti akwatile kapena asakwatile?

17 Ngati wina asankha kukhalabe mbeta, ni nkhani ya mwiniwake atatsimikiza mu mtima mwake. Ndipo amene wasankha kuloŵa m’banja nayenso n’cosankha cake. Mtumwi Paulo analimbikitsa kukhala mbeta. Komabe anati: “Cifukwa ca kuwanda kwa dama, mwamuna aliyense akhale ndi mkazi wake-wake ndipo mkazi aliyense akhale ndi mwamuna wake-wake.” Ndiyeno anawonjezela kuti: “Koma ngati sangathe kudziletsa, akwatile, pakuti ndi bwino kukwatila kusiyana ndi kuvutika ndi chilakolako.” Munthu akaloŵa m’banja, amatetezeka ku macitidwe monga kudzipukusa (masturbation), kapenanso ciwelewele cifukwa cothenthedwa ndi cilakolako. Komanso, n’cinthu canzelu kuganizilanso msinkhu. N’cifukwa cake Paulo anakamba kuti: “Ngati wina akuona kuti zikumuvuta kukhalabe yekha, ngati wapitilila pachimake pa unyamata, ndipo ngati ziyenela kutelo, acite mmene akufunila, sacimwa. Akwatile.” (1 Akor. 7:2, 9, 36; 1 Tim. 4:1-3) Apa satanthauza kuti wacinyamata kapena wacitsikana akayamba kutenthedwa na cilakolako basi akwatile, yayi. Iye angakhale akalibe kufikapo poti n’kukwanilitsa maudindo a umoyo wa banja.

18, 19. (a) Kodi cikwati cacikhiristu ciyenela kuyamba bwanji? (b) Nanga tidzakambilana ciani m’nkhani yotsatila?

18 Cikwati cacikhiristu ciyenela kuyamba ndi mwamuna ndi mkazi, onse aŵili odzipeleka kwa Yehova, ndiponso omukonda ndi mtima wonse. Afunikanso kukhala okondana mofikapo, cakuti ni ofunitsitsa kudzipeleka kwa wina na mnzake kuti amange banja. Akakhala na ciyambi cimeneci, amadalitsika potsatila uphungu wakuti kwatilani ‘kokha mwa Ambuye.’ (1 Akor. 7:39) Akaloŵa m’banja, nawonso amadzavomeleza kuti Baibulo ndiyo imapeleka uphungu wabwino kuposa munthu aliyense, kuti banja lipambane.

19 M’nkhani yotsatila tidzakambilana mfundo za m’Malemba zothandiza Akhiristu ali pabanja mmene angacitile ndi mavuto a “masiku ano otsiliza.” Maka-maka pamene amuna ndi akazi ambili ali na makhalidwe osoŵetsa cimwemwe m’mabanja awo. (2 Tim. 3:1-5) M’mau ake anzelu, Yehova anatipatsa zonse zofunikila, kuti tikhale ndi zikwati zacimwemwe ndi zopambana—inde, pamene tili paulendo wathu wopita ku moyo wosatha.—Mat. 7:13, 14.