Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Fufuzani Cinthu Camtengo Wapatali Kuposa Golide

Fufuzani Cinthu Camtengo Wapatali Kuposa Golide

Kodi munapezapo golide? Ni anthu ocepa cabe amene amaipeza. Komabe, anthu mamiliyoni ambili apeza cinthu camtengo wapatali kuposa golide. Cinthu cimeneco ni nzelu zocokela kwa Mulungu, zimene ngakhale “golide woyenga bwino sangapelekedwe mosinthana nazo.”—Yobu 28:12, 15.

ANTHU amene amaphunzila Baibulo tingawayekeze ndi ofufuza golide. Ophunzilawo afunika kucita khama kufufuza m’Malemba kuti apeze nzelu zamtengo wapatali. Popeza ndife ophunzila Baibulo, kodi tingaphunzile ciani tikaona mmene anthu amepezela golide?

MUNAPEZA CUMA

Ganizilani kuti muyenda m’mbali mwa mtsinje, ndipo mwaona kanthu kena kooneka ngati kamwala kakang’ono konyezimila. Mwaŵelama ndi kudoba ndipo mukukondwela kwambili kudziŵa kuti mwapeza golide. Kamwalako n’kakang’ono kwambili kuposa kanjele ka thelele lobala, ndipo sikapezeka-pezeka. Mukuyang’ana uku na uku kuti muone ngati mungapeze kamwala kena.

Mofananamo, mwina mukumbukila tsiku limene Mboni ya Yehova inakufikilani panyumba ndi kukulalikilani. Muyenela kuti mukumbukila bwino mmene munamvelela mutazindikila kuti mwapeza golide wa kuuzimu. Mwina zimenezi zinacitika pamene munaona koyamba dzina la Mulungu lakuti Yehova m’Baibulo. (Sal. 83:18) Kapena pamene munadziŵa kuti mungakhale bwenzi la Yehova. (Yak. 2:23) Panthawi imeneyo muyenela kuti munadziŵa kuti mwapeza cinthu camtengo wapatali kuposa golide. Ndipo munapitiliza kufufuza kuti mupeze cuma cina ca kuuzimu.

MUNAPITILIZA KUFUFUZA

Tuzidutswa twa golide nthawi zina tumapezeka m’mitsinje. Nthawi zina, ofufuza golide amapeza golide wambili, umene angaugulitse madola ambili.

Pamene munayamba kuphunzila Baibulo na wa Mboni za Yehova, muyenela kuti munamvela monga mmene munthu amene wapeza golide wambili amamvelela. Mwacionekele, kusinkhasinkha mavesi a m’Baibulo kunawonjezela cidziŵitso canu. Zimenezo zinacititsa kuti mukhale ndi cuma cambili ca kuuzimu. Posinkhasinkha coonadi ca mtengo wapatali cimeneco, munaphunzila mmene mungakhalile bwenzi la Yehova. Munaphunzilanso mmene mungapitilizile kucita zinthu zimene zimakondweletsa Mulungu pamene muyembekezela moyo wosatha.—Yak. 4:8; Yuda 20, 21.

Mofanana na wofufuza golide, kodi mumayesetsa kuphunzila mfundo zamtengo wapatali za coonadi ca m’Baibulo?

Monga mmene ofufuza golide amacitila kuti apeze golide, muyenela kuti inunso munacita khama kuti mupeze cuma cakuuzimu. Mutaphunzila mfundo zofunika za coonadi ca m’Baibulo, munalimbikitsidwa kudzipeleka ndi kubatizidwa.—Mat. 28:19, 20

PITILIZANI KUFUFUZA

Wofufuza golide angapeze tuzidutswa twa golide m’miyala ikulu-ikulu. Golide imeneyo imakhala mkati mwa miyala, ndipo amafunika kukumba ndi kuphwanya miyalayo kuti atengemo golide. Mukangoona mwalawo simungazindikile kuti muli golide. Zili conco cifukwa cakuti m’miyala ina mungapezeke cabe golide wolemela magalamu 10. Ngakhale n’conco, wofufuza amalimbikila kukumba kuti apeze golide imeneyo.

Ngakhale kuti munthu wadziŵa “ciphunzitso coyambilila ca Khiristu,” afunikabe kucita khama kuti apite patsogolo. (Aheb. 6:1, 2) Pocita phunzilo laumwini, muyenela kucita khama kuti mupeze mfundo zatsopano ndi zothandiza. Mungacite ciani kuti muzipindulabe pocita phunzilo laumwini ngakhale kuti mwakhala mukuphunzila Malemba kwa zaka zambili?

Khalanibe ndi mtima wofuna kuphunzila. Muziyesetsa kuzindikila mfundo zatsopano. Pitilizani kucita khama kuti mupeze nzelu na malangizo ocokela kwa Mulungu, zimene ni cuma ca kuuzimu. (Aroma 11:33) Kuti muwonjezele cidziŵitso canu, seŵenzetsani zida zofufuzila zimene zilipo m’cinenelo canu. Moleza mtima fufuzani malangizo amene angakuthandizeni ndi kupeza mayankho a m’Baibulo pa mafunso anu. Funsani anthu ena kuti akuuzeni malemba ndi nkhani zimene zimawathandiza ndi kuwalimbikitsa. Muziuzako ena mfundo zimene mwapeza pophunzila Mau a Mulungu.

Pamene muphunzila, simuyenela kukhala na colinga cowonjezela cabe cidziŵitso. Mtumwi Paulo anacenjeza kuti “kudziŵa zinthu kumacititsa munthu kudzitukumula.” (1 Akor. 8:1) Pacifukwa cimeneci, pitilizani kukhala wodzicepetsa ndi kulimbitsa cikhulupililo canu. Kucita kulambila kwa pa banja ndi phunzilo laumwini nthawi zonse kudzakuthandizani kutsatila miyezo ya Yehova pa umoyo wanu ndi kuthandiza ena. Koposa zonse, mudzakhala wokondwela podziŵa kuti mwapeza cinthu camtengo wapatali kuposa golide.—Miy. 3:13, 14.