Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Mumaona Kufunika Kophunzitsa Ena?

Kodi Mumaona Kufunika Kophunzitsa Ena?

“Ndidzakupatsani malangizo abwino.”—MIY. 4:2.

NYIMBO: 93, 96

1, 2. N’cifukwa ciani tifunika kuphunzitsa ena kuti akwanilitse utumiki wawo?

KULALIKILA uthenga wabwino wa Ufumu inali nchito yofunika kwambili kwa Yesu. Komabe, anapatula nthawi yophunzitsa ena kuti akhale abusa ndi aphunzitsi. (Mat. 10:5-7) Ngakhale kuti Filipo anali wotangwanika ndi ulaliki, anapatula nthawi yophunzitsa ana ake akazi anayi kulalikila mogwila mtima coonadi ca m’Baibulo. (Mac. 21:8, 9) Kodi kuphunzitsa ena n’kofunika bwanji masiku ano?

2 Pa dziko lonse, ciŵelengelo ca anthu amene akulandila coonadi cikuwonjezeleka. Ofalitsa atsopano amene akalibe kubatizika ayenela kudziŵa cifukwa cake kucita phunzilo laumwini n’kofunika. Afunika kuphunzitsidwa kulalikila uthenga wabwino, ndi mmene angaphunzitsile ena coonadi. M’mipingo yambili, abale ayenela kulimbikitsidwa kuti ayenelele kukhala atumiki othandiza kapena akulu. Akhiristu ofikapo kuuzimu angathandize acatsopano kupita patsogolo mwa kuwapatsa “malangizo abwino.”—Miy. 4:2.

THANDIZANI ACATSOPANO KUPEZA NZELU NDI MPHAMVU M’MAU A MULUNGU

3, 4. (a) Kodi Paulo anagwilizanitsa bwanji kuphunzila Baibulo ndi kubala zipatso mu ulaliki? (b) Tiyenela kucita ciani coyamba tikalibe kulimbikitsa ophunzila Baibulo kuti azicita phunzilo laumwini?

3 Kodi kucita phunzilo laumwini n’kofunika bwanji? Yankho tilipeza m’mau amene mtumwi Paulo anauza Akhiristu anzake a ku Kolose. Iye anati: “Sitinaleke kukupemphelelani. Takhala tikupemphanso kuti mukhale odziŵa molondola cifunilo cake [Mulungu], ndiponso kuti mukhale ndi nzelu zonse komanso muzimvetsetsa zinthu zauzimu. Tikupemphelelanso kuti muziyenda mogwilizana ndi zimene Yehova amafuna, kuti muzimukondweletsa pa ciliconse, pamene mukupitiliza kubala zipatso m’nchito iliyonse yabwino, ndi kuwonjezela kumudziŵa Mulungu molondola.” (Akol. 1:9, 10) Cidziŵitso colondola cimeneco kapena kuti colongosoka, cikanathandiza Akhiristu a ku Kolose ‘kuyenda mogwilizana ndi zimene Yehova amafuna, kuti azimukondweletsa pa ciliconse.’ Kucita zimenezi kukanawathandiza kupitiliza ‘kubala zipatso m’nchito iliyonse yabwino,’ makamaka panchito yolalikila uthenga wabwino. Kuti azitumikila bwino, wolambila Yehova aliyense afunika kukhala na cizoloŵezi cophunzila Baibulo. Tiyenela kuthandiza anthu amene timaphunzila nawo Baibulo kudziŵa mfundo imeneyi.

4 Ngati ife eni sitiphunzila Baibulo patokha, sitingakwanitse kuthandiza anthu amene timaphunzila nawo Baibulo kuona ubwino wocita phunzilo laumwini. Ife coyamba tiyenela kukhala na cizoloŵezi cophunzila Baibulo. Conco, dzifunseni kuti: ‘Ngati mwininyumba wakambapo maganizo ake amene sagwilizana ndi zimene Baibulo imaphunzitsa, kapena ngati wafunsa mafunso ovuta, kodi nimakwanitsa kupeleka mayankho ocokela m’Baibulo? Pamene niŵelenga mmene Yesu, Paulo, ndi ena anapililila polalikila, kodi nimasinkhasinkha mmene citsanzo cawo cingakhudzile utumiki wanga kwa Yehova?’ Ife tonse tifunikila malangizo ndi uphungu wocokela m’mau a Mulungu. Ndipo ngati tiuza ena mmene tapindulila pocita phunzilo laumwini, tingawalimbikitse kuti nawonso aziphunzila Baibulo mwakhama kuti apindule.

5. Pelekani malingalilo a mmene mungathandizile acatsopano kukhala na cizoloŵezi cocita phunzilo laumwini.

5 Dzifunseni kuti, ‘Ningaphunzitse bwanji wophunzila Baibulo kuti azicita phunzilo laumwini nthawi zonse?’ Mungayambe mwa kumuonetsa mmene angakonzekelele zimene mumaphunzila naye. Mungam’pemphe kuti aziŵelenga zakumapeto m’buku la Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni, kuphatikizapo malemba osagwila mawu. Mungamuthandize kukonzekela misonkhano kuti akayankhepo. Mungamulimbikitse kuti aziŵelenga magazini iliyonse yatsopano ya Nsanja ya Mlonda ndi Galamukani! Ngati Watchtower Laibulale kapena Laibulale ya pa Intaneti ilipo m’cinenelo cake, mungamuonetse mmene angaiseŵenzetsele pofufuza mayankho a m’Baibulo. Ngati mwamuthandiza mwa njila imeneyi, mudzaona kuti wophunzila Baibulo adzayamba kusangalala pophunzila Mau a Mulungu payekha.

6. (a) Mungathandize bwanji wophunzila wanu kuti azikonda kuŵelenga Baibulo? (b) Kodi wophunzila Baibulo adzapindula bwanji ngati wayamba kukonda kuŵelenga Baibulo?

6 Komabe, sitiyenela kukakamiza anthu kuti adziŵelenga ndi kuphunzila Baibulo. M’malomwake, tiyenela kuseŵenzetsa zida zimene gulu la Yehova latipatsa kuti tiwathandize kukonda kwambili kuŵelenga Baibulo. M’kupita kwanthawi, wophunzila wacidwi ameneyo adzamvela monga mmene wamasalimo anamvelela. Iye anaimba kuti: “Kuyandikila kwa Mulungu ndi cinthu cabwino. Yehova Ambuye Wamkulu Koposa ndiye pothaŵilapo panga.” (Sal. 73:28) Mzimu wa Yehova udzayamba kugwila nchito pa wophunzila Baibulo wacidwi ameneyo.

THANDIZANI ACATSOPANO KUTI ADZIŴE KULALIKILA NDI KUPHUNZITSA

7. Kodi Yesu anaphunzitsa bwanji atumwi ake kulalikila? (Onani cithunzi kuciyambi kwa nkhani ino.)

7 M’buku la Mateyu caputala 10, muli malangizo amene Yesu anapatsa atumwi ake 12. Iye anachula mfundo zofunika m’malo mongokamba mwacisawawa. [1] Atumwiwo anamvetsela bwino-bwino pamene Yesu anali kuwaphunzitsa kulalikila mogwila mtima. Pambuyo polandila malangizo, iwo anapita kukalalikila. Anakwanitsa kuphunzitsa coonadi ca m’Baibulo mwaluso cifukwa coona mmene Yesu anali kuphunzitsila. (Mat. 11:1) Nafenso tingathandize ophunzila Baibulo kukhala alaliki aluso. Lomba tiyeni tikambilane njila ziŵili za mmene tingawathandizile.

8, 9. (a) Kodi Yesu anali kukambilana nawo bwanji anthu mu ulaliki? (b) Tingathandize bwanji acatsopano kuti azikambilana ndi anthu mu ulaliki monga mmene Yesu anacitila?

8 Kukambilana ndi anthu momasuka. Yesu anali kukonda kuuza anthu za Ufumu wa Mulungu. Mwacitsanzo, anakambilana momasuka ndi mkazi pacitsime pafupi na mzinda wa Sukari. (Yoh. 4:5-30) Anakambilananso ndi Mateyu wokhometsa msonkho, amene anali kuchedwanso kuti Levi. Mauthenga Abwino safotokoza zonse zimene Yesu anakambilana na Mateyu. Komabe, iye anavomela ciitano ca Yesu cakuti akhale wotsatila wake. Mateyu pamodzi ndi ena, anamvetsela pamene Yesu anali kuphunzitsa panthawi ya cakudya m’nyumba ya Mateyu.—Mat. 9:9; Luka 5:27-39.

9 Natanayeli anali kuona anthu a ku Nazareti mosayenela. Koma Yesu anakambilana naye mwaubwenzi. Zimenezi zinacititsa kuti Natanayeli asinthe mmene anali kuonela anthuwo. Iye anaganiza zophunzila zambili kwa Yesu wa ku Nazareti. (Yoh. 1:46-51) Motelo, nafenso tiyenela kuphunzitsa acatsopano kuti azikambilana ndi anthu mwaubwenzi ndi momasuka. [2] Tikaphunzitsa acatsopano kukambilana ndi anthu mwa njila imeneyi, iwo adzakonda kwambili ulaliki.

10-12. (a) Kodi Yesu anakulitsa bwanji cidwi ca anthu mu ulaliki? (b) Tingathandize bwanji ofalitsa atsopano kuwonjezela luso lawo?

10 Kukulitsa cidwi. Yesu anali na nthawi yocepa yolalikila. Ngakhale n’conco, anapatula nthawi yokulitsa cidwi ca anthu amene anali kumvetsela uthenga wabwino. Mwacitsanzo, Yesu anaphunzitsa khamu la anthu atakhala m’boti. Ndiyeno, mozizwitsa anacititsa Petulo kugwila nsomba zambili, ndipo anamuuza kuti: “Kuyambila lelo uzisodza anthu amoyo.” Kodi zimene Yesu anakamba na kucita zinali ndi zotsatilapo zabwanji? Petulo ndi anzake ‘anayendetsa ngalawazo ndi kufika nazo kumtunda, ndipo iwo anasiya ciliconse ndi kutsatila [Yesu].’—Luka 5:1-11.

11 Nikodemo, amene anali membala wa Khoti Yapamwamba ya Ayuda, anacita cidwi ndi zimene Yesu anali kuphunzitsa. Anafuna kuphunzila zambili koma anali kucita mantha ndi zimene ena angakambe akamuona akukamba ndi Yesu. Conco, anapita kwa Yesu usiku. Yesu sanamuuze kuti abwelele iyayi, koma anapatula nthawi kuti amuphunzitse coonadi ca mtengo wapatali. (Yoh. 3:1, 2) Kodi tiphunzilapo ciani pa nkhani zimenezi? Mwana wa Mulungu anapatula nthawi yothandiza anthu kukhala na cikhulupililo colimba. Kodi nafenso sitiyenela kucita khama kubwelelako kwa anthu acidwi ndi kuphunzila nawo Baibulo?

12 Ofalitsa atsopano akhoza kuwonjezela luso lawo lophunzitsa ngati timalalikila nawo. Tingawathandize kuti azibwelelako kwa anthu, ngakhale amene aonetsa cidwi cocepa. Tingapemphe ofalitsa atsopano kuti atipelekeze ku maulendo obwelelako kapena kukatsogoza maphunzilo a Baibulo. Tikawaphunzitsa na kuwalimbikitsa mwa njila imeneyi, iwo adzayamba kuonetsa ena cidwi ndi kutsogoza maphunzilo a Baibulo awo-awo. Adzaphunzila kuti sayenela kubwelela m’mbuyo akapeza anthu opanda cidwi, koma kuti ayenela kuleza mtima ndi kupilila mu ulaliki.—Agal. 5:22; onani bokosi yakuti “ Kuleza Mtima N’kofunika.”

PHUNZITSANI ACATSOPANO KUTI AZITHANDIZA AKHIRISTU ANZAWO

13, 14. (a) Muphunzilapo ciani mukaganizila zitsanzo za m’Baibulo za anthu amene anadzipeleka kuti athandize ena? (b) Mungathandize bwanji ofalitsa atsopano komanso acicepele kuti adzikonda abale ndi alongo?

13 Yehova afuna kuti atumiki ake azikondana ndi kutumikilana monga abale ndi alongo. (Ŵelengani 1 Petulo 1:22; Luka 22:24-27.) Baibulo imafotokoza kuti Yesu anadzipeleka, kuphatikizapo kupeleka moyo wake, kuti athandize ena. (Mat. 20:28) Dorika “anali kucita nchito zabwino zambili, ndi kupeleka mphatso zacifundo zoculuka.” (Mac. 9:36, 39) Mariya, mlongo wa mumpingo wa ku Roma, anacitila Akhiristu anzake nchito zambili. (Aroma 16:6) Kodi tingathandize bwanji acatsopano kudziŵa kuti kuthandiza abale ndi alongo mumpingo n’kofunika kwambili?

Phunzitsani acatsopano kuti azikonda Akhiristu anzawo (Onani ndime 13, 14)

14 Akhiristu ofikapo mwauzimu angapemphe acatsopano kuti awapelekeze kukacezela odwala ndi okalamba. Nawonso makolo angapite ndi ana awo pamaulendo amenewa ngati mpoyenela. Pamene akulu athandiza okalamba monga kuwapezela cakudya kapena kuwakonzela nyumba, angacite bwino kutengako ena. Mbali zonsezi zingathandize acicepele ndi acatsopano kuti aphunzile kuthandiza ena. Mkulu wina anali kukonda kucezela abale a m’gawo lake mwacidule akapita mu ulaliki, kuti adziŵe za umoyo wawo. Wacicepele amene nthawi zambili anali kuyenda ndi mkuluyo, anaphunzila kuti onse mumpingo ayenela kudzimva kuti ni ofunika kwambili.—Aroma 12:10.

15. N’cifukwa ciani akulu ayenela kuyesetsa kuthandiza abale kupita patsogolo mumpingo?

15 Yehova amaseŵenzetsa abale kuti aziphunzitsa mumpingo. Conco, abale onse ayenela kunola luso lawo lokamba nkhani. Ngati ndinu mkulu, kodi mumapatula nthawi yomvetsela pamene mtumiki wothandiza ayeseza nkhani yake? Mukamuthandiza, iye angakulitse luso lake monga mphunzitsi wa Mawu a Mulungu.—Neh. 8:8. [3]

16, 17. (a) N’ciani cimene Paulo anacita kuti athandize Timoteyo kupita patsogolo? (b) Kodi akulu angaphunzitse bwanji abale kuti ayenelele kukhala akulu mumpingo?

16 Abale ambili akufunikabe kuti akhale akulu mumpingo wacikhiristu. Ndipo onse amene adzayenelela kugwila nchito imeneyi kutsogolo, afunika kupitilizabe kuphunzitsidwa. Paulo anaphunzitsa Timoteyo, ndipo anam’limbikitsa kuti nayenso aziphunzitsako ena. Anauza Timoteyo kuti: “Iwe mwana wanga, pitiliza kupeza mphamvu m’kukoma mtima kwakukulu kumene kuli mwa Khiristu Yesu. Zinthu zimene unazimva kwa ine ndi kwa mboni zambili zokhudza ine, zimenezo uziphunzitse kwa anthu okhulupilika amene nawonso, adzakhala oyenelela bwino kuphunzitsa ena.” (2 Tim. 2:1, 2) Timoteyo anaphunzila zambili cifukwa cotumikila pamodzi ndi mtumwi wacikulile. Ndiyeno, iye anagwilitsila nchito malangizo a Paulo mu ulaliki ndiponso m’mbali zina za utumiki.—2 Tim. 3:10-12.

17 Paulo anapatula nthawi yambili yoceza ndi Timoteyo. Anacita izi kuti atsimikizile kuti Timoteyo waphunzitsidwa bwino. (Mac. 16:1-5) Akulu angatengele citsanzo ca Paulo cimeneci mwa kuyenda ndi atumiki othandiza ku maulendo aubusa ngati mpoyenela. Mwakutelo, akulu amaphunzitsa abalewo kukhala na makhalidwe ofunika kwa akulu monga cikhulupililo, kuleza mtima, na cikondi. Zimenezi zimakonzekeletsa abalewo kuti adzakwanitse kutumikila bwino monga abusa a “gulu la nkhosa za Mulungu.”—1 Pet. 5:2.

KUPHUNZITSA ENA N’KOFUNIKA KWAMBILI

18. N’cifukwa ciani kuphunzitsa ena n’kofunika kwambili?

18 Kuphunzitsa ena n’kofunika kwambili cifukwa ciŵelengelo ca anthu amene ayamba kutumikila Yehova cikuwonjezeka. Ndiponso, kumatipatsa mwayi wotumikila Yehova. Citsanzo ca Yesu ndi Paulo cophunzitsa ena n’cothandizabe masiku ano. Yehova afuna kuti atumiki ake amasiku ano aphunzitsidwe bwino kuti ayenelele kusenza maudindo m’gulu lake. Mulungu watipatsa mwayi wothandiza acatsopano kuti akwanitse kutumikila bwino mumpingo. Zinthu m’dzikoli zikuipila-ipila, ndipo nchito yolalikila ikupita patsogolo. Conco, kuphunzitsa ena n’kofunika ndipo kuyenela kucitidwa mwamsanga.

19. N’cifukwa ciani tingakhale otsimikiza mtima kuti khama lathu pophunzitsa ena mu utumiki wa Yehova silizapita pacabe?

19 N’zoona kuti kuphunzitsa ena kumafuna nthawi ndi khama. Koma Yehova na Mwana wake wokondedwa, adzatithandiza ndi kutipatsa nzelu kuti tikwanitse kuphunzitsa ena. Ndipo timakondwela kwambili kuona anthu amene taphunzitsa ‘akugwila nchito mwakhama ndiponso mwamphamvu.’ (1 Tim. 4:10) Tiyeni tonse tipitilize kupita patsogolo pocita utumiki wopatulika kwa Yehova.

^ [1] (ndime 7) Zina mwa mfundo zimene Yesu anaphunzitsa ni (1) Kulalikila uthenga woyenela. (2) Kukhala wokhutila na zimene Mulungu amatipatsa. (3) Kupewa kukangana ndi mwininyumba. (4) Kudalila Mulungu tikapeza anthu otsutsa. (5) Kusacita mantha.

^ [2] (ndime 9) M’buku la Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu masamba 62-64, muli malangizo othandiza a mmene mungayambile kukambilana na anthu.

^ [3] (ndime 15) Buku ya Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu masamba 52-61, imafotokoza makhalidwe ofunikila kuti tidziphunzitsa mwaluso.