Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kupangitsa Cikwati Cacikhiristu Kukhala Cacimwemwe

Kupangitsa Cikwati Cacikhiristu Kukhala Cacimwemwe

“Aliyense . . . akonde mkazi wake ngati mmene amadzikondela yekha, komanso mkazi azilemekeza kwambili mwamuna wake.”—AEF. 5:33.

NYIMBO: 87, 3

1. Ngakale kuti cikwati cimayamba ndi cisangalalo, kodi omanga banja ayenela kuyembekezela ciani? (Onani cithunzi pamwambapa.)

PAMENE ciphadzuŵayo—mkwatibwi—acitoŵala kwa mkwati wake pa tsiku la cikwati, nayenso mwamuna atakongola mocititsa kaso, cimwemwe cawo cimakhala cosaneneka. Kucokela pa nthawi yoyendelana, cikondi cawo cakula mpaka kufika polumbila kuti adzakhulupilika kwa wina ndi mnzake m’cikwati. Komabe, pamene anthu aŵili agwilizana ndi kumanga banja, aliyense afunikila kusintha. Mau a Mulungu amapeleka uphungu wanzelu kwa onse oloŵa m’banja. Ndipo m’pake, cifukwa amene anayambitsa cikwati amafuna kuti onse okwatilana akhale acimwemwe. (Miy. 18:22) Ngakhale n’conco, Malemba amakambilatu kuti anthu opanda ungwilo akamanga banja, “adzakhala ndi nsautso m’thupi mwawo.” (1 Akor. 7:28) Kodi cofunikila n’ciani kuti nsautso imeneyo izicepako? Ndipo n’ciani cingathandize Akhiristu kukhala ndi banja lacimwemwe?

2. Kodi a m’cikwati afunika kuonetsa mitundu iti ya cikondi?

2 Baibulo imagogomeza kufunika kwa cikondi. Pali mitundu inayi ya cikondi. Cikondi ca pamtima (Cigiriki, phi·liʹa) n’cofunika m’cikwati. Cikondi ca pakati pa mwamuna ndi mkazi (eʹros) cimakometsa cikwati, ndipo cikondi ca pacibale (stor·geʹ) cimafunika pamene m’banja mwakhala ana. Komabe, cikondi cozikidwa pa mfundo za m’Baibulo (a·gaʹpe), n’cimene maka-maka cimathandiza kuti cikwati cikhale copambana. Za cikondi cimeneci, mtumwi Paulo anati: “Aliyense wa inu akonde mkazi wake ngati mmene amadzikondela yekha, komanso mkazi azilemekeza kwambili mwamuna wake.”—Aef. 5:33.

KUUNIKA BWINO MBALI YA MWAMUNA NDI YA MKAZI

3. Kodi cikondi m’cikwati ciyenela kukhala camphamvu bwanji?

3 Paulo analemba kuti: “Amuna inu, pitilizani kukonda akazi anu monga mmene Khiristu anakondela mpingo n’kudzipeleka yekha cifukwa ca mpingowo.” (Aef. 5:25) Kuti otsatila a Yesu atengele citsanzo cake, iwonso afunika kukondana ngati mmene iye anawakondela.(Ŵelengani Yohane 13:34, 35; 15:12, 13.) Cikondi ca Akhiristu ali pabanja ciyenela kukhala camphamvu, moti aliyense afunika kukhala wokonzeka kufela mnzake. Zimenezi zimaiŵalika pakakhala mkangano. Komabe, cikodi ca a·gaʹpe “cimakwilila zinthu zonse, cimakhulupilila zinthu zonse, cimayembekezela zinthu zonse, cimapilila zinthu zonse.” Inde, “cikondi sicitha.”(1 Akor. 13:7, 8) Akhiristu oopa Mulungu sayenela kuiŵala lumbilo lawo lakuti adzakondana ndi kukhulupilika kwa wina ndi mnzake. Ici cidzawathandiza kugwilitsila nchito malangizo apamwamba a Yehova pofuna kuthetsa mavuto alionse amene angabwele.

4, 5. (a) Monga mutu, kodi mwamuna afunika kucita mbali yanji m’banja? (b) Nanga mkazi ayenela kukaona bwanji kakonzedwe ka umutu? (c) Kodi a m’cikwati ena anapanga masinthidwe otani?

4 Pounika mbali ya aliyense m’banja, Paulo analemba kuti: “Akazi agonjele amuna awo ngati mmene amagonjelela Ambuye, cifukwa mwamuna ndiye mutu wa mkazi wake, monganso mmene Khiristu alili mutu wa mpingo.” (Aef. 5:22, 23) Mfundo imeneyi siitanthauza kuti mkazi ni munthu wotsikilapo kwa mwamuna iyai. M’malo mwake, imathandiza mkazi kukwanilitsa mbali imene Mulungu anam’lengela pamene anati: “Si bwino kuti munthu [Adamu] akhale yekha. Ndimupangila womuthandiza, monga mnzake womuyenelela.” (Gen. 2:18) Monga mmene Khiristu, mutu wa mpingo, amakondela kwambili mpingo wake, mwamuna wacikhiristu afunika kukhala mutu wacikondi. Akacita zimenezi, mkazi wake amamva kukhala wotetezeka, amacita kumva bwino kulemekeza mwamuna wake, kum’cilikiza, ndi kum’gonjela.

5 Mlongo Cathy avomeleza kuti cikwati cimafuna munthu kusintha.  [1] Iye anati: “Pamene n’nali mbeta, n’nali kungocita zimene nikufuna. Koma kukwatiwa kunanisintha, cifukwa n’nafunika kuzoloŵela kudalila mwamuna wanga. Cinali cotivuta poyamba, koma tsopano cikondi cathu catiphunzitsa kucita zinthu m’njila ya Yehova.” Naye mwamuna wake, Fred, anati: “N’nali kale ndi vuto lopanga zosankha. Ndiye kukhala aŵili kunangowonjezela vutolo. Koma kupempha citsogozo kwa Yehova, ndi kumvetsela maganizo a mkazi wanga, kwathandiza kucepetsa vutolo. Nimamva kuti mkazi wanga alidi mcilikizi wanga!”

6. Kodi cikondi cimakhala bwanji ‘cogwilizanitsa camphamvu’ mukabuka mavuto m’banja?

6 Kuti cikwati cikhale colimba, aŵiliwo afunika kukhala ololelana pa kupanda ungwilo kwawo. Afunikanso ‘kupitiliza kukhululukilana ndi mtima wonse.’ Izi zili conco cifukwa onse aŵili amalakwa. Motelo, wina akalakwa, tiyeni tizionapo mwayi wotengapo phunzilo pa colakwaco, wokhululukilana, ndi wosonyezana cikondi monga ‘cogwilizanitsa camphamvu.’ (Akol. 3:13, 14) Komanso “cikondi n’coleza mtima ndiponso . . . sicisunga zifukwa.” (1 Akor. 13:4, 5) Mukasiyana maganizo, kambilanani mwamsanga kuti vutolo lithe. Akhiristu apabanja afunika kuyesetsa kuthetsa vuto lililonse tsiku lisanathe. (Aef. 4:26, 27) Kukamba kuti “pepani nakukhumudwitsani,” kumafuna kudzicepetsa na kulimba mtima. Koma kumathandiza kwambili kuthetsa mavuto, na kukulitsa cikondi m’banja.

KUGANIZILANA N’KOFUNIKA

7, 8. (a) Kodi Baibulo imalangiza ciani pa nkhani ya kucipinda? (b) N’cifukwa ninji a m’cikwati afunika kumaonetsana cikondano cawo?

7 M’Baibulo muli uphungu wothandiza a m’cikwati kukhala oganizilana pa nkhani ya kucipinda. (Ŵelengani 1 Akorinto 7:3-5.) Ngati mwamuna saonetsa cikondi ndi kuganizila mkazi wake, n’covuta kuti nkhani ya kucipinda izim’komela wamkazi. Amuna ayenela kucitila akazi awo “mowadziŵa bwino.” (1 Pet. 3:7) Nkhani ya kucipinda siifuna kucitoumiliza kapena kulamula yayi. Ifunika izicitika mwacibadwa. N’zoona kuti kaŵili-kaŵili thupi la mwamuna ndilo limatsogola. Koma onse aŵili afunika kufika poti aikonzekela nkhaniyo m’maganizo ndi mumtima.

8 Ngakhale kuti Baibulo siicita kulongosola mwacindunji macezedwe akucipinda okonzekeletsana nkhani ya mangawa, imachulako tumacitidwe tokopana twa cikondano, inde tuja amati malaving’i. (Nyimbo ya Sol. 1:2; 2:6) Zoona, Akhiristu a m’cikwati afunika ndithu kumaonetsanako cikondano cawo.

9. N’cifukwa ciani tifunika kupewa kaleya koceza mokopana ndi munthu amene sitili naye pabanja?

9 Ngati tili na cikondi camphamvu kwa Mulungu na munthu mnzathu, sitidzalola munthu kapena cinthu ciliconse kusokoneza cikwati cathu. Vikwati vina vakhala pamavuto, kapena kutha ndithu, cifukwa mmodzi wa aŵiliwo amakonda kutamba zamalisece. Tiyenela kupewelatu mcitidwe umenewu. Tipewenso kaleya kokonda kuceza mokopana ndi wina amene si m’zathu wa m’cikwati. Kucita zimenezi n’kupanda cikondi. Tikamakumbukila kuti Mulungu amaona zili m’maganizo mwathu na zocita zathu, tidzafuna kukhala oyela kuti tim’kondweletse.—Ŵelengani Mateyu 5:27, 28; Aheberi 4:13.

CIKWATI CIKAYAMBA KUVUTA

10, 11. (a) Kodi kusudzulana n’kofala bwanji? (b) Nanga Baibulo imati ciani za kupatukana? (c) N’ciani cingathandize wa m’cikwati kusaganiza msanga zopatukana?

10 Ngati mavuto aakulu apitiliza m’cikwati, mmodzi kapena onse aŵili angaganize zopatukana kapena kusudzulana. M’maiko ena, hafu ya vikwati vonse vimaesila. Zimenezi sizicitika pamlingo waukulu conco mu mpingo wacikhiristu. Ngakhale n’conco, mavuto a m’banja akuwonjezeleka pakati pa anthu a Mulungu. Ndipo nkhani imeneyi ikufika podetsa nkhawa.

11 Baibulo imapeleka malangizo aya: “Mkazi asasiye mwamuna wake, koma ngati angamusiye, akhale conco wosakwatiwa. Apo ayi, abwelelane ndi mwamuna wakeyo. Mwamunanso asasiye mkazi wake.” (1 Akor. 7:10, 11) Kupatukana na mnzathu wa m’cikwati tisakutenge monga nkhani yopepuka. N’zoona kuti kungaoneke kukhala kothandiza zinthu zafika povuta kwambili. Koma kaŵili-kaŵili, kupatukana kumangoitananso mavuto ena. Yesu atabweleza zimene Mulungu anakamba kuti mwamuna adzasiya makolo ake n’kukagwililizana na mkazi wake, anati: “Cimene Mulungu wacimanga pamodzi, munthu asacilekanitse.” (Mat. 19:3-6; Gen. 2:24) Izi zitanthauza kuti ngakhale mwamuna kapena mkazi, ‘sayenela kulekanitsa cimene Mulungu anacimanga pamodzi.’ Kwa Mulungu, cikwati ni mgwilizano wa moyo wonse. (1 Akor. 7:39) Tonse tidzaŵelengeledwa mlandu kwa Mulungu. Mfundo imeneyi iyenela kukumbutsa onse ali m’vikwati kuyesetsa kumathetsa msanga mavuto madzi akali m’nkhongono.

12. N’ciani cingapangitse wa m’cikwati kuganiza zopatukana?

12 Kuyembekezela kukapeza zabwino zokha-zokha m’cikwati ndiye kumakhalanso muzu wina wa mavuto. Munthu akaona kuti maloto ake aja a zabwino sakwanilitsika onse, amakhala wosakhutila, kumva kugwilitsidwa mwala, ndi kukhumudwa. Kaamba ka zimenezi, amayamba kukangana cifukwa ca kusiyana zibadwa ndi makulidwe, ndalama, azipongozi, azilamu, ndi kulela ana. Komabe coyamikilika n’cakuti, Akhiristu ambili amapeza njila zothetsela mavuto amenewa mwamtendele cifukwa coyang’ana kwa Mulungu.

13. Kodi n’ziti zingakhale zifukwa zomveka zopatukilana?

13 Nthawi zina kupatukana kungakhale komveka. Ena aona kuti sangacitile mwina koma kupatukana pa zifukwa izi: kusasamalila banja mwadala, nkhanza zoipitsitsa, ndi ciwopsezo pa umoyo wauzimu. Akhiristu amene ali na mavuto aakulu m’banja afunika kupempha thandizo kwa akulu. Abale ofikapo amenewa angathandize a m’cikwati za mmene angagwilitsile nchito uphungu wa m’Mau a Mulungu. Pokambilana mavuto a m’banja, tisamaiŵale kupemphelela mzimu wa Yehova kuti utithandize kugwilitsila nchito mfundo za m’Baibulo, ndi kuonetsa zipatso za mzimu wake.—Agal. 5:22, 23. [2]

14. Kodi Baibulo imati ciani kwa Akhiristu amene anzawo a m’cikwati satumikila Yehova?

14 Nthawi zina Mkhiristu angakhale ndi mwamuna kapena mkazi amene si Mboni. Baibulo imapeleka zifukwa zabwino zimene aŵiliwo safunikila kulekana. (Ŵelengani 1 Akorinto 7:12-14.) Kaya amene si Mboniyo adziŵe kapena asadziŵe, iye “amayeletsedwa” cifukwa cokwatilana ndi wokhulupilila. Komanso ana obadwa kwa iwo amaonedwa “oyela,” ndipo ni ovomelezeka kwa Mulungu. Paulo anati: “Mkaziwe, udziŵa bwanji, mwina ungapulumutse mwamuna wako? Kapena mwamunawe, udziŵa bwanji, mwina ungapulumutse mkazi wako?” (1 Akor. 7:16) M’mipingo yambili ya Mboni za Yehova, muli mabanja mmene Mkhiristu ndiye anathandiza ‘kupulumutsa’ mnzakeyo.

15, 16. (a) Kodi Baibulo imapeleka uphungu wanji kwa akazi acikhiristu amene amuna awo si Mboni? (b) Nanga Mkhiristu angacite bwanji ‘ngati wosakhulupililayo asankha kucoka’?

15 Mtumwi Petulo analangiza akazi acikhiristu kugonjela amuna awo. Anati “ngati ali osamvela mawu akopeke, osati ndi mawu, koma ndi khalidwe lanu, poona okha ndi maso awo khalidwe lanu loyela ndi ulemu wanu waukulu.” Inde, mwa “mzimu wabata ndi wofatsa umene uli wamtengo wapatali pamaso pa Mulungu,” mkazi angakopele mwamuna wake ku cipembedzo coona mom’fika pamtima, kusiyana ndi kumamuuza mosam’pita m’bali ziphunzitso za Cikhiristu.—1 Pet. 3:1-4.

16 Koma bwanji ngati wosakhulupilila asankha kupatukana? Baibulo imati: “Ngati wosakhulupililayo wacoka, acoke. M’bale kapena mlongo sakhala womangika zinthu zikatelo, koma Mulungu anakuitanani kuti mukhale mu mtendele.” (1 Akor. 7:15) Apa satanthauza kuti Mkhiristuyo tsopano ni womasuka kukwatila, yayi. Komanso, safunikila kucitoumiliza wosakhulupililayo kuti asacoke, yayinso. Kupatukana kungabweletseko mpumulo winawake. Ndipo Mkhiristuyo angakhale ndi mafuno abwino kwa mnzake wocokayo, akuti m’tsogolo akabweze mtima kuti akapitilize cikwati cawo, ndi kuti akakhale Mboni.

KUIKABE PATSOGOLO ZINTHU ZAUZIMU

Kuika patsogolo zinthu zauzimu kudzawonjezela cimwemwe m’banja mwanu (Onani ndime 17)

17. N’ciani cimene Akhiristu ali pabanja ayenela kuika patsogolo?

17 Pokhala mu “masiku otsiliza,” tili m’nthawi yovuta kucita nayo. (2 Tim. 3:1-5) Kukhala olimba kuuzimu ndiye kungatithandize kulimbana ndi dzikoli. Paulo analemba kuti: “Nthawi yotsalayi yafupika. Conco amene ali ndi akazi azikhala ngati alibe, . . . Amene amagwilitsila nchito dzikoli azikhala ngati amene sakuligwilitsila nchito mokwanila.” (1 Akor. 7:29-31) Paulo sanatanthauze kuti Akhiristu azinyalanyaza maudindo awo a m’banja ayi. Koma cifukwa ca nthawi yofupikayo, anafunika kuika patsogolo zinthu zauzimu.—Mat. 6:33.

18. N’cifukwa ciani n’zotheka Akhiristu kukhala ndi cikwati cacimwemwe ndi copambana?

18 Ngakhale kuti tili m’nthawi yovuta kwambili, ndipo tikuona kuti vikwati vili kupasuka kulikonse, n’zotheka kuti ife tikhale ndi cikwati cacimwemwe ndi copambana. Inde, Akhiristu ali pabanja amene satayana ndi anthu a Yehova, amene amagwilitsila nchito uphungu wa m’Malemba, ndi kulola mzimu woyela wa Yehova kuwatsogolela, akhoza kusunga “cimene Mulungu anacimanga pamodzi.”—Maliko 10:9.

^ [1] (ndime 5) Maina asinthidwa.

^ [2] (ndime 13) Onani kamutu kakuti “Zimene Baibo Imanena pa Kulekana ndi Kupatukana,” m’buku yakuti “Khalanibe m’Cikondi ca Mulungu,” masa. 219-221.